Yesu Khristu
Kudalitsa Mkate


Kudalitsa Mkate

O Mulungu, Atate Wamuyaya,
tikukupemphani mu dzina la mwana wanu, Yesu Khristu,
kuti mudalitse ndikuyeretsa mkate uwu,
kwa miyoyo yonse imene idye mkatewu,
kuti adye pokumbukira thupi la mwana wanu,
ndikuchitira umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya,
kuti ndiwofunitsitsa kutenga dzina la mwana wanu,
ndikum’kumbukira iye nthawi zonse
ndikusunga malamulo amene anapereka kwa iwo;
kuti akhale ndi Mzimu wake nthawi zonse.
Amen.

Print