Yesu Khristu
Kudalitsa Madzi


Kudalitsa Madzi

O Mulungu, Atate Wamuyaya,
tikukupemphani mu dzina la mwana wanu, Yesu Khristu,
kuti mudalitse ndikuyeretsa madzi awa,
kwa miyoyo yonse imene imwe madziwa,
kuti achite ichi pokumbukira mwazi wa mwana wanu,
womwe unakhetsedwa mmalo mwa iwo;
kuti achitire umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya,
kuti azimukumbukira iye nthawi zonse,
kuti akhale ndi Mzimu wake.
Amen.

Print