Malembo Oyera
4 Nefi 1


Nefi Wachinayi

Buku la Nefi
Amene ali Mwana wa Nefi—M’modzi wa Ophunzira a Yesu Khristu

Nkhani ya anthu a Nefi, molingana ndi zolemba zake.

Mutu 1

Anefi ndi Alamani onse atembenukira kwa Ambuye—Ali ndi zinthu zonse zofanana, achita zozizwitsa, ndipo achita bwino m’dziko—Pambuyo pa dzaka mazana awiri, migawikano, kuipa, mipingo yabodza, ndi mazunzo ayamba—Patatha dzaka mazana atatu, onse Anefi ndi Alamani ndi oipa—Amaroni abisa zolemba zopatulika. Mdzaka za pafupifupi Yesu atabadwa 35–321.

1 Ndipo zidachitika kuti chaka cha makumi atatu ndi chachinayi chidapita, komanso cha makumi atatu ndi zisanu, ndipo taonani ophunzira a Yesu adali atapanga mpingo wa Khristu m’mayiko onse ozungulira. Ndipo onse amene adadza kwa iwo; ndipo adalapa moonadi machimo awo, adabatizidwa m’dzina la Yesu; ndipo adalandiranso Mzimu Woyera.

2 Ndipo zidachitika mu chaka cha makumi atatu ndi chachisanu ndi chimodzi, anthu onse adatembenukira kwa Ambuye, pa nkhope yonse ya dziko, onse Anefi ndi Alamani, ndipo padalibe mikangano ndi mapokoso pakati pawo, ndipo munthu aliyense adachitirana chilungamo wina ndi mnzake.

3 Ndipo adali nazo zonse zofanana mwa iwo; kotero padalibe olemera ndi osauka, akapolo ndi afulu, koma onse adapangidwa afulu, ndi ogawana nawo a mphatso yakumwamba.

4 Ndipo zidachitika kuti chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi ziwiri chidapitanso, ndipo kudapitilirabe kukhala mtendere mu dzikolo.

5 Ndipo padali ntchito zazikulu ndi zodabwitsa zidachitidwa ndi ophunzira a Yesu, kotero kuti adachiritsa odwala, ndi kuwukitsa akufa, ndi kupangitsa olumala miyendo kuyenda, ndi akhungu kulandiranso kupenya kwawo, ndi ogontha kumva; ndipo mitundu yonse ya zozizwitsa adachita pakati pa ana a anthu; ndipo sadachite chozizwa chilichonse kupatula mudali mudzina la Yesu.

6 Ndipo motero chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi zitatu chidapita, ndiponso china cha makumi atatu ndi zisanu ndi zinayi, ndi cha makumi anayi ndi choyamba, ndi cha makumi anayi ndi chachiwiri, inde, ngakhale mpaka dzaka makumi anayi ndi zisanu ndi zinayi zidapita, ndiponso cha makumi asanu ndi chimodzi, ndi cha makumi asanu ndi chachiwiri; inde, ndipo ngakhale mpaka dzaka makumi asanu ndi zisanu ndi zinayi zidapita.

7 Ndipo Ambuye adawachititsa bwino kwambiri m’dzikomo; inde, kufikira kuti adamanganso mizinda kumene kudali mizinda itawotchedwa.

8 Inde, ngakhale mzinda waukulu uwo Zarahemula adapangitsa kuti umangidwe kachiwiri.

9 Koma padali mizinda yambiri imene idamira, ndipo madzi adakwera m’malo mwake; kotero mizinda iyi sikadatheka kukonzedwanso mwatsopano.

10 Ndipo tsopano, taonani, zidachitika kuti anthu a Nefi adakula mumphamvu, ndipo adachuluka mofulumira kwambiri, ndipo adakhala anthu okongola ndi osangalatsa kwambiri.

11 Ndipo iwo adakwatira, ndi kuperekedwa ku ukwati, ndipo adadalitsidwa molingana ndi unyinji wa malonjezano amene Ambuye adapanga kwa iwo.

12 Ndipo sadatsatenso machitidwe ndi m’miyambo ya chilamulo cha Mose; koma adatsata malamulo amene adalandira kwa Ambuye wawo ndi Mulungu wawo, kupitiriza kusala kudya ndi kupemphera, ndi kusonkhana pamodzi kawiri kawiri kupemphera ndi kumva mawu a Ambuye.

13 Ndipo zidachitika kuti padalibe kukangana mwa anthu onse, m’dziko lonse; koma padali zozizwitsa zamphamvu zidachitidwa pakati pa ophunzira a Yesu.

14 Ndipo zidachitika kuti chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu imodzi chidapita, ndiponso chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu ziwiri, inde, ndipo pomaliza, mpaka chaka cha makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi zinayi chidatha; inde, ngakhale dzaka zana zidali zitapita, ndipo ophunzira a Yesu, amene iye adawasankha, onse adapita ku paradiso wa Mulungu, kupatula atatu okhawo amene adayenera kutsala; ndipo padali ophunzira ena oikidwa m’malo mwawo; ndiponso ambiri a m’badwo umenewo adali atapita.

15 Ndipo zidachitika kuti mudalibe mkangano m’dzikomo, chifukwa cha chikondi cha Mulungu chimene chidakhala m’mitima ya anthu.

16 Ndipo kudalibe nsanje, kapena ndewu, kapena zipolowe, kapena zadama, kapena mabodza, kapena kuphana, kapena khalidwe lonyansa; ndipo ndithu sipadakhalepo anthu osangalala kwambiri pakati pa anthu onse amene adalengedwa ndi dzanja la Mulungu.

17 Kudalibe achifwamba, kapena akupha, kapena padalibe Alamani, kapena mtundu uli wonse wa anthu; koma adali mwa umodzi, ana a Khristu, ndi acholowa cha Ufumu wa Mulungu.

18 Ndipo adadalitsidwa motani nanga! Pakuti Ambuye adawadalitsa iwo m’zochita zawo zonse; inde, ngakhale iwo adadalitsidwa ndi kuchititsidwa bwino kufikira zitapita dzaka zana limodzi ndi khumi; ndipo m’badwo woyamba kuchokera kwa Khristu udali utapita, ndipo padalibe mkangano m’dziko lonselo.

19 Ndipo zidachitika kuti Nefi, iye amene adasunga zolemba zomalizazi, (ndipo iye adazisunga izo pa mapale a Nefi) adafa, ndipo mwana wake Amosi adazisunga izo m’malo mwake; ndipo iye adazisunganso pa mapale a Nefi.

20 Ndipo adazisunga dzaka makumi asanu ndi atatu mphambu zinayi, ndipo m’dziko mudali mtenderebe, kupatulapo padali gawo laling’ono la anthu limene lidagalukira mpingo ndipo lidatenga pa iwo dzina la Alamani; kotero kudayamba kukhala Alamaninso m’dzikomo.

21 Ndipo zidachitika kuti Amosi adamwaliranso, (ndipo zidali dzaka zana limodzi ndi makumi asanu ndi anayi kudza mphambu zinayi kuchokera pa kubwera kwa Khristu) ndipo mwana wake Amosi adasunga zolemba m’malo mwake; ndipo iye nayenso adazisunga izo pa mapale a Nefi; ndipo zidalembedwanso m’buku la Nefi, limene liri buku ili.

22 Ndipo zidachitika kuti dzaka mazana awiri zidali zitapita; ndipo m’badwo wachiwiri wonse udali utapita kupatula ochepa okha.

23 Ndipo tsopano ine, Mormoni, ndikufuna kuti mudziwe kuti anthu adali atachuluka, kotero kuti adafalikira pa nkhope yonse ya dzikolo, ndipo adali atalemera kwambiri, chifukwa cha kuchita bwino kwawo mwa Khristu.

24 Ndipo tsopano, m’chaka chimenechi cha mazana awiri ndi chimodzi kudayamba kukhala pakati pawo amene adakwezedwa m’kunyada, monga ngati kuvala zobvala za mtengo wapatali, ndi mtundu uliwonse wa ngale zabwino, ndi zinthu zabwino za dziko.

25 Ndipo kuyambira nthawi imeneyo katundu wawo ndi chuma chawo sichidalinso chofanana pakati pawo.

26 Ndipo adayamba kugawikana m’magulu; ndipo adayamba kumanga mipingo kwa iwo okha kuti apeze phindu, ndipo adayamba kukana mpingo woona wa Khristu.

27 Ndipo zidachitika kuti pamene dzaka mazana awiri ndi khumi zidali zitapita padali mipingo yambiri mu dziko; inde, padali mipingo yambiri yomwe imadzinenera kuti imadziwa Khristu, ndipo koma iwo adakana mbali zambiri za uthenga wake wabwino, kotero kuti iwo adalandira mitundu yonse ya zoipa, ndipo adapereka icho chimene chidali chopatulika kwa iye amene chidaletsedwa chifukwa cha kusayenera.

28 Ndipo mpingo uwu udachuluka mopitilira chifukwa cha kusaweruzika, ndi chifukwa cha mphamvu ya Satana yemwe adagwira pa mitima yawo.

29 Ndiponso, padali mpingo wina umene udakana Khristu; ndipo adazunza mpingo woona wa Khristu, chifukwa cha kudzichepetsa kwawo ndi chikhulupiliro chawo mwa Khristu; ndipo adawanyoza iwo chifukwa cha zozizwitsa zambiri zomwe zidachitidwa pakati pawo.

30 Kotero iwo adagwiritsa ntchito mphamvu ndi ulamuliro pa ophunzira a Yesu amene adakhala nawo limodzi, ndipo adawaponya iwo mu ndende; koma ndi mphamvu ya mawu a Mulungu amene adali mwa iwo, ndende zidang’ambika pakati, ndipo adatuluka nachita zozizwa zamphamvu pakati pawo.

31 Komabe, pakusatengera za zozizwitsa zonsezi, anthu adaumitsa mitima yawo, ndipo adafuna kuwapha, ngakhale ngati Ayuda ku Yerusalemu adafuna kupha Yesu, molingana ndi mawu ake.

32 Ndipo iwo adawaponya m’ng’anjo zamoto, ndipo adatuluka osavulala.

33 Ndipo iwo adawaponya m’mayenje a zilombo; ndipo adasewera ndi zilombozo ngati mwana ndi mwana wa nkhosa; ndipo adatuluka mwa iwo, osavulala.

34 Komabe, anthu adaumitsa mitima yawo, pakuti iwo adatsogozedwa ndi ansembe ambiri ndi aneneri onyenga kuti amange mipingo yambiri, ndi kuchita mitundu yonse ya kusaweruzika. Ndipo iwo adakantha anthu a Yesu; koma anthu a Yesu sadawakanthenso. Ndipo kotero iwo ankacheperachepera mu kusakhulupilira ndi kuipa, kuyambira chaka ndi chaka, ngakhale mpaka dzaka mazana awiri ndi makumi atatu zitapita.

35 Ndipo tsopano zidachitika m’chaka chimenechi, inde, m’chaka cha mazana awiri ndi makumi atatu ndi chimodzi, padali kugawanika kwakukulu pakati pa anthu.

36 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chimenechi kudauka anthu amene ankatchedwa Anefi, ndipo iwo adali okhulupilira owona mwa Khristu; ndipo pakati pa iwo padali iwo amene adatchedwa Alamani—Ayakobe, ndi Ayosefe, ndi Azoramu;

37 Chotero okhulupilira owona mwa Khristu, ndi olambira owona a Khristu, (pakati pawo padali ophunzira atatu a Yesu amene adatsala) ankatchedwa Anefi, ndi A Yakobo, ndi Ayosefe, ndi Azoramu.

38 Ndipo zidachitika kuti iwo amene adakana uthenga wabwino ankatchedwa Alamani, ndi Alemueli, ndi Aismayeli; ndipo iwo sadacheperechepere m’kusakhulupilira, koma adapandukira mwadala Uthenga Wabwino wa Khristu; ndipo iwo adaphunzitsa ana awo kuti asakhulupilire, ngakhale monga makolo awo, kuyambira pachiyambi, adacheperachepera.

39 Ndipo zidali chifukwa cha kuipa ndi kunyansa kwa makolo awo, ngakhale monga momwe zidaliri pachiyambi. Ndipo adaphunzitsidwa kudana ndi ana a Mulungu; ngakhale monga Alamani adaphunzitsidwa kudana ndi ana a Nefi kuyambira pachiyambi.

40 Ndipo zidachitika kuti dzaka mazana awiri mphambu makumi anayi kudza zinayi zidali zitapita, ndipo motero ndimomwe zidaliri zochitika za anthu. Ndipo gawo loipa kwambiri la anthu lidakula mumphamvu, ndipo lidakhala lochuluka kwambiri kuposa momwe adaliri anthu a Mulungu.

41 Ndipo iwo adapitirizabe kudzimangira mipingo kwa iwo eni, ndi kuikongoletsa ndi mitundu yonse ya zinthu zamtengo wapatali. Ndipo motero zidapita dzaka mazana awiri mphambu makumi asanu, ndiponso dzaka mazana awiri mphambu makumi asanu ndi limodzi.

42 Ndipo zidachitika kuti gawo loipa la anthu lidayambanso kumanga malumbiro achinsinsi ndi magulu a Gadiyantoni.

43 Ndiponso anthu omwe ankatchedwa anthu a Nefi adayamba kunyada m’mitima yawo, chifukwa cha chuma chawo chochuluka, ndipo adakhala opanda pake monga kwa abale awo, Alamani.

44 Ndipo kuchokera panthawi imeneyi ophunzira adayamba kumva chisoni chifukwa cha machimo adziko lapansi.

45 Ndipo zidachitika kuti pamene dzaka mazana atatu zidali zitapita, onse anthu a Nefi ndi Alamani adali ataipa kwambiri wina monga kwa wina.

46 Ndipo zidachitika kuti achifwamba a Gadiantoni adafalikira pa nkhope yonse ya dziko; ndipo padalibe amene adali olungama kupatula ophunzira a Yesu. Ndipo golide ndi siliva iwo adazisunga mowunjika, ndipo adagulitsa malonda amitundumitundu.

47 Ndipo zidachitika kuti zitapita dzaka mazana atatu ndi zisanu, (ndipo anthu adatsalirabe mu zoipa) Amosi adamwalira; ndipo m’bale wake, Amaroni, adasunga zolemba m’malo mwake.

48 Ndipo zidachitika kuti pamene dzaka mazana atatu ndi makumi awiri zidali zitapita, Amaroni, pokakamizidwa ndi Mzimu Woyera, adabisa zolemba zomwe zidali zopatulika—inde, ngakhale zolemba zopatulika zonse zimene zidaperekedwa kuchokera ku m’badwo kupita ku m’badwo, zimene zidali zopatulika—ngakhale mpaka chaka cha mazana atatu ndi makumi awiri kuchokera pa kubwera kwa Khristu.

49 Ndipo iye adazibisa izo kwa Ambuye, kuti izo zikathe kubweranso kwa otsalira a nyumba ya Yakobo, molingana ndi maulosi ndi malonjezano a Ambuye. Ndipo motero awa ndi mapeto a zolemba za Amaroni.

Print