Malembo Oyera
Yaromu 1


Buku la Yaromu

Mutu 1

Anefi asunga lamulo la Mose, ayembekezera kubwera kwa Khristu, ndipo achita bwino m’dziko—Aneneri ambiri agwira ntchito kuti asunge anthu mnjira ya choonadi. Mdzaka dza pafupifupi 399–361 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano taonani, ine, Yaromu, ndikulemba mawu ochepa molingana ndi lamulo lochokera kwa atate anga, Enosi, kuti m’badwo wathu usungike.

2 Ndipo monga mapalewa ali aang’ono, ndipo monga zinthu izi zikulembedwa ndi cholinga cha ubwino wa abale athu Alamani, kotero, ndizofunika kuti ndilembe pang’ono; koma sindidzalemba zinthu za uneneri wanga, kapena za mavumbulutso anga. Pakuti n’chiyani chomwe ndingalembe kuposera zimene makolo anga adazilemba? Pakuti kodi iwo sadaulule dongosolo la chipulimutso? Ndinena kwa inu: Inde; ndipo ichi ndichokwanira kwa ine.

3 Taonani, ndikoyenera kuti zambiri zichitike pakati pa anthu awa, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yawo, ndi kugotha kwa makutu awo, ndi khungu la m’maganizo mwawo, ndi kuumitsa kwa makosi awo; komabe, Mulungu ndi wachifundo chachikulu kwa iwo, ndipo sadawasesebe kuwachotsa iwo pa nkhope ya dziko.

4 Ndipo alipo ambiri mwa ife amene ali ndi mavumbulutso ambiri, chifukwa si onse omwe ndi osamvera. Ndipo pamene ambiri sali osamvera ndikukhala ndi chikhulupiliro, ali ndi chiyanjano ndi Mzimu Woyera, umene umaonetseredwa kwa ana a anthu, molingana ndi chikhulupiliro chawo.

5 Ndipo tsopano, taonani, dzaka mazana awiri zidali zitapita, ndipo anthu a Nefi adakula mphamvu m’dzikomo. Iwo adaonetsetsa kusunga malamulo a Mose ndi kusunga tsiku la sabata loyera kwa Ambuye. Ndipo sadapeputse; kapena kunyoza. Ndipo malamulo a dzikolo adali okhwima kwambiri.

6 Ndipo adamwazikana kwambiri pa nkhope ya dziko, ndi Alamani nawonso. Ndipo iwo adali ochulukana kwambiri kuposera Anefi, ndipo ankakonda kupha, ndipo ankamwa mwazi wa zilombo.

7 Ndipo zidachitika kuti adabwera kudzamenyana nafe, Anefi, ku nkhondo. Koma mafumu athu ndi atsogoleri athu adali amuna amphamvu m’chikhulupiliro cha Ambuye, ndipo adaphunzitsa anthu njira za Ambuye; kotero, tidawagonjetsa Alamani ndi kuwasesa kuwathamangitsira kunja kwa dziko lathu, nayamba kulimbitsa mizinda yathu, kapena malo ena aliwonse acholowa chathu.

8 Ndipo tidachulukana kwambiri, ndi kumwazikana pa nkhope ya dziko, ndipo tidakhala olemera kwambiri ndi golide, ndi siliva, ndi zinthu zamtengo wapatali, ndi tchito zabwino za matabwa, pazomangamanga, ndi zamakina, ndiponso za zitsuro ndi kopa, ndi mkuwa ndi nsimbi, kupanga zida zonse zamitundumitundu kuti tilime mthaka, ndi zida zankhondo—inde, mivi yakunthwa, ndi a phodo, ndi a gweta, ndi nthungo, ndi zokonzekera zonse za nkhondo.

9 Ndipo kotero pokonzekera kukumana ndi Alamani, iwo sadapambane kutigonjetsa ife. Koma mawu a Ambuye adatsimikizidwa omwe adayankhula kwa makolo athu, kunena kuti: Ngati inu mudzasunga malamulo anga mudzachita bwino m’dziko.

10 Ndipo zidachitika kuti aneneri a Ambuye adaopseza anthu a Nefi, molingana ndi mawu a Mulungu, kuti ngati iwo sadzasunga malamulo, koma kugwa mu kulakwitsa, adzawonongedwa kuchoka pa nkhope ya dziko.

11 Kotero, aneneri, ndi ansembe, ndi aphunzitsi, adagwira ntchito mwakhama, ndikuwalimbikitsa anthu kupilira konse ku khama; kuphunzitsa chilamulo cha Mose, ndi cholinga chake chidapatsidwira; kuwakopa iwo kuti ayang’anire kwa Mesiya, ndi kukhulupilira mwa iye kuti adzabwera ngati kuti iye wabwera kale. Ndipo moteremu iwo adawaphunzitsa.

12 Ndipo zidachitika kuti pakuchita chonchi adawaleletsa iwo kuti asawonongedwe pa nkhope ya dziko; pakuti iwo adalasa mitima yawo ndi mawu, kupitiriza kuwautsa iwo m’kulapa.

13 Ndipo zidachitika kuti dzaka mazana awiri mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi zitatu zinali zitapita—potsatira njira za nkhondo, ndi mikangano, ndi kusagwirizana, kwa nthawi yaitali kwambiri.

14 Ndipo ine, Yaromu, sindilemba zambiri, chifukwa mapalewa ndi aang’ono. Koma taonani, abale anga, mukhonza kupita ku mapale ena a Nefi, pakuti taonani, pa iwo mbiri ya nkhondo zathu idazokotedwa, molingana ndi zolembedwa ndi mafumu, kapena amene adachititsa kuti zilembedwe.

15 Ndipo ndikupereka mapale awa m’dzanja la mwana wanga Omuni, kuti asungidwe molingana ndi malamulo a mokolo anga.