Malembo Oyera
Omuni 1


Buku la Omuni

Mutu 1

Omuni, Amaroni, Kemisi, Abinadomu, ndi Amaleki, onse motsatana, asunga zolemba—Mosiya apeza anthu a Zarahemula, amene adachokera ku Yerusalemu m’masiku a Zedekiya—Mosiya apangidwa mfumu pa iwo—Mbumba ya Muleki ku Zarahemula idapeza Koriyantumuri, omaliza wa Ayaredi—Mfumu Benjamini alowa m’malo mwa Mosiya—Anthu akuyenera kupereka miyoyo yawo ngati nsembe kwa Khristu. Mdzaka dza pafupifupi 323–130 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, zidachitika kuti ine, Omuni, nditalamulidwa ndi atate anga, Yaromu, kuti ndikuyenera kulemba zinazake pa mapale, kuti tisunge m’badwo wathu—

2 Kotero, m’masiku anga, ndikufuna kuti mudziwe kuti ndidamenya nkhondo kwambiri ndi lupanga kuti ndisunge anthu anga, Anefi, kuti asagwe m’manja mwa adani awo, Alamani. Koma taonani, ine mwandekha ndine munthu oipa, ndipo sindidasunge malemba ndi malamulo a Ambuye monga ndidayenera kuchitira.

3 Ndipo zidachitika kuti dzaka mazana awiri ndi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi zidali zitapita, ndipo ife tidali ndi nyengo zambiri za mtendere; ndipo tidali ndi nyengo zambiri za nkhondo yoopsa ndi kukhetsa mwazi. Inde, ndipo mu zonse, dzaka mazana awiri mphambu makumi asanu ndi atatu mphambu ziwiri zidali zitapita, ndipo ndidasunga mapale awa molingana ndi malamulo a makolo anga; ndipo ndidapereka kwa mwana wanga Amaroni. Ndipo ndikutsiliza.

4 Ndipo tsopano ine, Amaroni, ndikulemba zinthu zirizonse zomwe ndikulemba, zomwe ziri zochepa, mu buku la atate anga.

5 Taonani, zidachitika kuti dzaka mazana atatu ndi makumi awiri zidali zitapita, ndipo gawo la Anefi loipa kwambiri lidawonongedwa.

6 Chifukwa Ambuye sakadalora, atawatsogolera ku dziko la Yerusalemu ndi kuwasunga ndi kuwasamala iwo kuti asagwe m’manja mwa adani awo, inde, sakadalora kuti mawu ake asatsimikiziridwe, amene iye adayankhula kwa makolo athu, kunena kuti: Ngati inu simudzasunga malamulo anga, simudzachita bwino m’dziko.

7 Kotero, Ambuye adawayendera iwo mu chiweruzo chachikulu, komabe, iye adawasiya olungama kuti asawonongedwe, koma adawapulumutsa iwo m’manja mwa adani awo.

8 Ndipo zidachitika kuti ine ndidapereka mapale kwa m’bale wanga Kemisi.

9 Tsopano ine, Kemisi, ndikulemba zimene ndi zinthu zochepa ndalemba, mu buku lomweli ndi m’bale wanga; pakuti taonani, ndidaona zomaliza zimene iye adalemba, kuti iye adalemba izi ndi dzanja lake la iye mwini; ndipo adalemba izi mu tsiku limene iye adapereka izo kwa ine. Ndipo moteremu ife timasunga zolemba, chifukwa ziri molingana ndi malamulo a makolo athu. Ndipo ine ndikutsiriza.

10 Taonani, ine, Abinadomu, ndine mwana wa Kemisi. Taonani, zidachitika kuti ndidaona nkhondo zochuluka ndi mikangano pakati pa anthu anga, Anefi, ndi Alamani; ndipo ine, ndi lupanga langa, ndachotsa miyoyo ya Alamani ochuluka m’chitetezo cha abale anga.

11 Ndipo taonani, mbiri ya anthu awa yazokotodwa pa mapale amane adali ndi mafumu, molingana ndi mibadwo; ndipo sindikudziwa za mavumbulutso kupatula iwo amene alembedwa, kapena mauneneri; kotero, zokhazo zimene ndizokwanira zalembedwa. Ndipo ine ndikutsiriza.

12 Taonani, ine ndi Amaleki, mwana wa Abinadomu. Taonani, ndidzayankhula kwa inu pang’ono zokhudzana ndi Mosiya, amene adapangidwa kukhala mfumu pa dziko la Zalahemula; pakuti taonani, iye pochenjezedwa ndi Ambuye kuti athawe kuchokera mu dziko la Nefi, ndipo ambiri omwe adzamvetsera kwa mawu Ambuye akuyeneranso kunyamuka kuchoka mu dzikolo limodzi ndi iye, kupita m’chipululu—

13 Ndipo zidachitika kuti iye adachita molingana ndi momwe ambuye adamulamulira. Ndipo adaturuka kuchoka m’dzikolo kupita m’chipululu, onse amene adatha kumvera mawu a Ambuye; ndipo adatsogoleredwa ndi maulaliki ndi mauneneri ochuluka. Ndipo adalangizidwa mosalekeza ndi mawu a Mulungu; ndipo adatsogoleredwa ndi mphamvu ya mkono wake, kudzera mchipululu mpaka adatsikira ku dzilo limene ndilotchedwa dziko la Zarahemula.

14 Ndipo adapezako anthu, amene amatchedwa anthu a Zarahemula. Tsopano, kudali chikondwelero pakati pa anthu a Zarahemula; ndiponso Zarahemula adakondwera kwambiri, chifukwa Ambuye adatumiza anthu a Mosiya ndi mapale a mkuwa amene adali ndi mbiri ya Ayuda.

15 Taonani, zidachitika kuti Mosiya adapeza kuti anthu a Zarahemula adachokera ku Yerusalemu pa nthawi yomwe Zedekiya, mfumu ya Yuda, adatengedwa ku ukapolo ku Babulo.

16 Ndipo adayenda ulendo m’chipululu, ndipo adabweretsedwa ndi dzanja la Ambuye kuwoloka madzi aakulu, kulowa mu dziko limene Mosiya adawapeza iwo; ndipo adakhala kumeneko kuchokera panthawiyo kufika mtsogolo.

17 Ndipo pa nthawi imene Mosiya adawapeza iwo, adali atachulukana kwambiri. Komabe, iwo adali ndi nkhondo zambiri ndi mikangano yoopsa, ndipo adagwa ndi lupanga kwa nthawi ndi nthawi; ndipo chinenero chawo chidaipitsidwa, ndipo sadabwere nazo zolemba ndi iwo; ndipo adakana kukhala kwa Mlengi wawo; ndipo Mosiya, kapena anthu a Mosiya, sadathe kuwamva iwo.

18 Koma zidachitika kuti Mosiya adachititsa kuti iwo akuyenera kuphunzitsidwa mchinenero chake. Ndipo zidachitika kuti atatha kuwaphunzitsa mu chinenero cha Mosiya, Zarahemula adapereka mbiri ya makolo ake, molingana ndi kukumbukira kwake; ndipo zalembedwa, koma osati mu mapale awa.

19 Ndipo zidachitika kuti anthu a Zarahemula, ndi a Mosiya, adagwirizana pamodzi; ndipo Mosiya adasankhidwa kukhala mfumu yawo.

20 Ndipo zidachitika m’masiku a Mosiya, kudabweretsedwa mwala waukulu kwa iye wokhala ndi zozokotedwa pa iwo, ndipo iye adamasulira zozokotedwazo mwa mphatso ndi mphamvu ya Mulungu.

21 Ndipo iwo udapereka mbiri ya m’modzi Koriyantumuri, ndi kuphedwa kwa anthu ake. Ndipo Koriyantumuri adapezedwa ndi anthu a Zarahemula; ndipo adakhala nawo kwa nthawi ya miyezi isanu ndi inayi.

22 Ndipo idayankhulanso mawu ochepa okhudzana ndi makolo ake. Ndipo makolo ake oyamba adaturuka kuchokera ku nsanja, pa nthawi imene Ambuye adasokoneza chinenero cha anthu; ndipo mkwiyo wa ambuye udagwera pa iwo molingana ndi ziweruzo zake, zimene ndi zolungama; ndipo mafupa awo adabalalika mu dziko la kumpoto.

23 Taonani, ine, Amaleki, ndidabadwa mu masiku a Mosiya; ndipo ndakhala ndi moyo kuti ndione imfa yake; ndipo Benjamini, mwana wake, adalowa ufumu m’malo mwake.

24 Ndipo taonani, ine ndaona, m’masiku a mfumu Benjamini, nkhondo yoopsa ndi kukhetsedwa mwazi kochuluka pakati pa Anefi ndi Alamani. Koma taonani, Anefi adapeza mwayi wambiri kuposa iwo; inde mwakuti mfumu Benjamini adawathamangitsa iwo kunja kuchoka m’dziko la Zarahemula.

25 Ndipo zidachitika uti, ndidayamba kukalamba; ndipo, pokhala wopanda mbewu, ndipo kuti mfumu Benjamini adali munthu olungama pamaso pa Ambuye, kotero, ndidzapereka mapale awa kwa iye, kulangiza anthu anthu onse kuti abwere kwa Mulungu, Woyera wa Israeli, ndi kukhulupilira mu uneneri, ndi mavumbulutso, ndi mu utumiki wa angelo, ndi mu mphatso ya kuyankhula malilime, ndi mphatso yakuthanthauzira zinenero, ndi mu zinthu zonse zimene ziri zabwino; pakuti palibe chirichonse chomwe chiri chabwino pokhapokha chiri chochokera kwa Ambuye: ndipo chimene chiri choipa chimachokera kwa mdyerekezi.

26 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, ndikufuna kuti mubwere kwa Khristu, amene ali Woyera wa Israeli, ndi kulandira chipulumutso chake, ndi mphamvu ya chiwombolo chake. Inde, bwerani kwa iye, ndi kupereka miyoyo yanu yonse kwa iye, ndi kupitiriza mu kusala kudya ndi kupemphera, ndi kulimbikira kufikira chimaliziro, ndipo pamene Ambuye ali wamoyo, inu mudzapulumutsidwa.

27 Ndipo tsopano ndidzayankhula zinazake zokhudzana ndi anthu ena amene adapita ku chipululu kuti abwelere ku dziko la Nefi; pakuti adalipo ambiri amene ankakhumbira kutenga dziko la cholowa chawo.

28 Kotero, adapita m’chipululu. Ndipo mtsogoleri wawo okhala wa mphamvu ndi dzitho, ndi munthu osamvara, kotero, adapangitsa mkangano pakati pawo; ndipo onse adaphedwa, kupatula makumi asanu, m’chipululu, ndipo adabweleranso ku dziko la Zarahemula.

29 Ndipo zidachitika kuti adatenganso ena, kagulu ndithu, ndi kuyamba ulendo wina kupita m’chipululu.

30 Ndipo ine, Amaleki, ndidali ndi m’bale, amene adapita nawo; ndipo sindidadziwenso chichokere iwo chirichonse chokhudza iwo. Ndipo ndatsala pang’no kutsikira kumanda anga, ndipo mapale awa adzadza. Ndipo tsopano ndikumaliza zoyankhula zanga.