Zidziwike kwa maiko onse, mafuko, zinenero, ndi anthu, kwa amene ntchito iyi idzafika: kuti ife, kupyolera mu chisomo cha Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, taona mapale amene ali ndi mbiri iyi, yomwe ili mabuku a anthu a Nefi, ndiponso Alamani, abale awo, ndiponso a anthu a Yaredi, omwe adachokera kunsanja yomwe yalankhulidwa. Ndipo ife tikudziwanso kuti iwo adamasuliridwa ndi mphatso ndi mphamvu ya Mulungu, pakuti mawu ake adalengezedwa kwa ife; kotero tikudziwa motsimikiza kuti ntchitoyi ndi yowona. Ndipo ife tikuchitiranso umboni kuti tawona zozokotedwa zomwe ziri pa mapale; ndipo izo zasonyezedwa kwa ife ndi mphamvu ya Mulungu, ndipo osati ya munthu. Ndipo ife tikulengeza ndi mawu osamalitsa, kuti mngelo wa Mulungu adatsika kuchokera kumwamba, ndipo adabweretsa ndi kuika patsogolo pa maso athu, kuti tidapenya ndi kuona mapale; ndi zolemba zake; ndipo tidziwa kuti ndi chisomo cha Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti tidapenya ndi kuchitira umboni kuti zinthu izi ziri zoona. Ndipo nzodabwitsa m’maso mwathu. Komabe, mawu a Ambuye adatilamulira ife kuti tiyenera kuchitira umboni za izo; kotero, pakumvera malamulo a Mulungu, tikuchitira umboni za zinthu zimenezi. Ndipo tikudziwa kuti ngati tili okhulupilika mwa Khristu, tidzachotsa mu zovala zathu mwazi wa anthu onse, ndipo tidzapezedwa opanda banga pamaso pa mpando wa chiweruzo wa Khristu, ndipo tidzakhala ndi iye kwamuyaya kumwamba. Ndipo ulemu ukhale kwa Atate, ndi kwa Mwana, ndi kwa Mzimu Woyera, amene ali Mulungu mmodzi. Ameni.