Malembo Oyera
Moroni 6


Mutu 6

Anthu olapa abatizidwa ndi kutumikiridwa—Mamembala a mpingo amene amalapa amakhululukidwa—Misonkhano imayendetsedwa ndi mphamvu ya Mzimu Woyera. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401–421.

1 Ndipo tsopano ine ndikuyankhula zokhudzana ndi ubatizo. Taonani, akulu, ansembe, ndi aphunzitsi adabatizidwa; ndipo iwo sadabatizidwe kupatula iwo adabweretsa zipatso zoyenera kuti iwo adali oyenera izo.

2 Ngakhale sadalandire aliyense munthu ku ubatizo kupatula iwo adabwera ndi mtima wosweka ndi mzimu wolapa, ndi kuchitira umboni kwa mpingo kuti iwo adalapa mowonadi machimo awo onse.

3 Ndipo palibe amene adalandiridwa ku ubatizo kupatula iwo adatenga pa iwo dzina la Khristu, kukhala ndi kutsimikiza kwa mtima kumtumikira iye mpaka mapeto.

4 Ndipo atalandiridwa ku ubatizo, ndi kupangitsidwa ndi kuyeretsedwa ndi mphamvu ya Mzimu Woyera; adawerengedwa pakati pa anthu a mpingo wa Khristu; ndipo maina awo adatengedwa, kuti akakumbukiridwe ndi kudyetsedwa ndi mawu abwino a Mulungu, kuwasunga iwo m’njira yolondola, kuwasunga iwo moyang’anisitsa kosalekeza ku pemphero, kudalira pa ubwino wokha wa Khristu, amene adali woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiliro chawo.

5 Ndipo mpingo unkakumana pamodzi kawirikawiri, kusala kudya ndi kupemphera, ndi kuyankhulana wina ndi mzake zokhudzana ndi ubwino wa miyoyo yawo.

6 Ndipo iwo ankakumana pamodzi kawiri kawiri kuti adye mkate ndi vinyo, pokumbukira Ambuye Yesu.

7 Ndipo adali otsatira mosamalitsa kuti pasakhale mphulupulu pakati pawo; ndipo amene adapezedwa kuti akuchita mphulupulu, mboni zitatu za mpingo zidawaweruza iwo patsogolo pa akulu, ndipo ngati sadalape, ndi kusavomereza, maina awo adachotsedwa, ndipo iwo sadawerengedwe pakati pa anthu a Khristu.

8 Koma kawirikawiri pamene adalapa ndi kupempha chikhululukiro, ndi cholinga chenicheni, ankakhululukidwa.

9 Ndipo misonkhano yawo inkayendetsedwa ndi mpingo motsatira machitidwe a ntchito za Mzimu, ndi mphamvu ya Mzimu Woyera; pakuti monga mphamvu ya Mzimu Woyera idawatsogolera iwo kulalikira, kapena kulimbikitsa, kapena kupemphera, kapena kupembedzera, kapena kuyimba, ngakhale momwemo zidachitidwa.

Print