Malembo Oyera
Moroni 8


Mutu 8

Ubatizo wa ana ang’onoang’ono ndi chonyansa choipa—Ana ang’onoang’ono ali ndi moyo mwa Khristu chifukwa cha Chitetezero—Chikhulupiliro, kulapa, kufatsa ndi kudzichepetsa kwa mtima, kulandira Mzimu Woyera, ndi kupilira mpaka ku mapeto kumatsogolera ku chipulumutso. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401–421.

1 Kalata ya atate anga Mormoni, yolembedwa kwa ine, Moroni; ndipo idalembedwa kwa ine posakhalitsa pambuyo pa mayitanidwe anga ku utumiki. Ndipo motere adandilembera ine, nati:

2 Mwana wanga okondedwa, Moroni, ndikondwera kwambiri kuti Ambuye wako Yesu Khristu amakukumbukira, ndipo wakuyitana ku utumiki wake, ndi ku ntchito yake yopatulika.

3 Ndimakukumbukira nthawi zonse m’mapemphero anga, ndikupemphera mosalekeza kwa Mulungu Atate m’dzina la Mwana wake Woyera, Yesu, kuti iye, kudzera mu ubwino wake wopanda malire ndi chisomo chake, akusunge kudzera pa chipiliro cha chikhulupiliro pa dzina lake mpaka kumapeto.

4 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikuyankhula kwa iwe zokhudzana ndi izo zimene zikundikhumudwitsa ine kwakukulu; pakuti zikundikhumudwitsa ine kuti pakubuka mikangano pakati panu.

5 Pakuti, ngati ndamva choonadi, pakhala mikangano pakati panu pa zokhudzana ndi ubatizo wa ana anu aang’ono.

6 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikufuna kuti ugwire ntchito mwakhama, kuti kulakwa kwakukulu kumeneku kuchotsedwe mwa inu; pakuti, pa chifukwa cha ichi ndalemba kalata imeneyi.

7 Pakuti nthawi yomweyo nditangomva zinthu zimenezi kwa iwe ndidafunsa Ambuye zokhudzana ndi nkhaniyi. Ndipo mawu a Ambuye adadza kwa ine ndi mphamvu ya Mzimu Woyera, nati:

8 Mvetsera ku mawu a Khristu, Muwomboli wako, Ambuye wako ndi Mulungu wako. Taona, sindidadze m’dziko kudzayitana olungama koma ochimwa ku kulapa; alunga safuna dokotala, koma amene akudwala; kotero, ana aang’ono ndi alunga, pakuti iwo samatha kuchita tchimo; kotero, thembelero la Adamu lachotsedwa mwa iwo mwa ine, kuti lilibe mphamvu pa iwo; ndipo lamulo la mdulidwe latha mwa ine.

9 Ndipo monga momwemu Mzimu Woyera udawonetsera mawu a Mulungu kwa ine; kotero, mwana wanga wokondedwa, ndikudziwa kuti ndi chipongwe pamaso pa Mulungu, kuti mubatize ana aang’ono.

10 Taona ndikunena kwa iwe kuti chinthu ichi udzaphunzitsa—kulapa ndi ubatizo kwa iwo amene ali ozindikira kuyankha ndi okhala ndi kuthekera kochita tchimo; inde, phunzitsani makolo kuti akuyenera kulapa ndi kubatizidwa, ndi kudzichepetsa okha monga ana awo aang’ono, ndipo iwo onse adzapulumutsidwa ndi ana awo aang’ono.

11 Ndipo ana awo aang’ono samafunikira kulapa, ngakhale ubatizo. Taona, ubatizo uli wa kulapa kwa kukwaniritsa malamulo ku chikhululukiro cha machimo.

12 Koma ana aang’ono ali moyo mwa Khristu, ngakhale kuchokera ku maziko a dziko; ngati sichoncho, Mulungu ali Mulungu wa tsankho, ndiponso Mulungu wosinthika, ndi wokondera anthu ena; pakuti ndi ana angati amene adamwalira asadabatizidwe!

13 Kotero, ngati ana aang’ono sakadatha kupulumutsidwa popanda ubatizo, awa akadayenera kupita ku gehena yosatha.

14 Taona ndinena ndi iwe, kuti amene amaganiza kuti ana aang’ono akufunika ubatizo ali mu ndulu ya kuwawa ndi m’nsinga za uchimo; pakuti alibe ngakhale chikhulupiliro, chiyembekezo, kapena chikondi; kotero, ngati iye afa pamene ali mu lingaliroli, iye akuyenera kupita pansi ku gehena.

15 Pakuti koopsa ndi kuipa koganiza kuti Mulungu amapulumutsa mwana mmodzi chifukwa cha ubatizo, ndipo winayo akuyenera kuwonongeka chifukwa alibe ubatizo.

16 Tsoka kwa iwo amene adzapotoza njira za Ambuye pambuyo pa chikhalidwe ichi, pakuti adzawonongeka pokhapokha atalapa. Taonani, ndikuyankhula molimba mtima, pokhala nawo ulamuliro wa kwa Mulungu; ndipo sindimaopa chimene munthu angachite; pakuti chikondi changwiro chimachotsa mantha onse.

17 Ndipo ndadzadzidwa ndi chikondi, chimene chili chikondi chosatha; kotero, ana onse ali ofanana kwa ine; kotero, ndimakonda ana ang’ono ndi chikondi changwiro; ndipo onse ali ofanana ndi olandira nawo chipulumutso.

18 Pakuti ndikudziwa kuti Mulungu sali Mulungu watsankho, kapena munthu wosinthika; koma iye ndi wosasinthika kuchokera muyaya mpaka muyaya.

19 Ana aang’ono sangathe kulapa; kotero, ndi kuipa koopsa kukana chifundo choyera cha Mulungu kwa iwo, pakuti onse ali ndi moyo mwa iye chifukwa cha chifundo chake.

20 Ndipo iye amene amanena kuti ana aang’ono akufunika ubatizo amakana chifundo cha Khristu, ndipo amaika pachabe chitetezero cha iye ndi mphamvu ya chiwombolo chake.

21 Tsoka kwa otere, chifukwa ali pachiwopsezo cha imfa, gahena, ndi mazunzo osatha. Ndikuyankhula izi molimba mtima; Mulungu wandilamulira. Mvetsera kwa izo ndi kumvera, kapena zidzayima motsutsana nawe pampando wachiweruzo wa Khristu.

22 Pakuti taona kuti ana aang’ono onse ali ndi moyo mwa Khristu, ndiponso onse amene ali opanda lamulo. Pakuti mphamvu ya chiwombolo imafika pa onse amene alibe lamulo; kotero, iye amene satsutsidwa, kapena iye amene sali pansi pa kutsutsidwa, sangathe kulapa; ndipo kwa wotere ubatizo suthandiza kanthu—

23 Koma ndi mnyozo pamaso pa Mulungu, kukana chifundo cha Khristu, ndi mphamvu ya Mzimu wake Woyera, ndi kudalira ntchito zakufa.

24 Taona, mwana wanga, chinthu ichi sichikuyenera kukhala; pakuti kulapa kuli kwa awo omwe ali pansi pa kutsutsika ndi pansi pa thembelero la chilamulo chosweka.

25 Ndipo zipatso zoyamba za kulapa ndi ubatizo; ndipo ubatizo umadza mwa chikhulupiliro m’kukwaniritsa malamulo; ndipo kukwaniritsa malamulo kumabweretsa chikhululukiro cha machimo;

26 Ndipo chikhululukiro cha machimo chimabweretsa kufatsa, ndi kudzichepetsa kwa mtima; ndipo chifukwa cha kufatsa ndi kudzichepetsa kwa mtima kudza kuyenderedwa kwa Mzimu Woyera, amene Mtonthonzi amadzadza ndi chiyembekezo ndi chikondi changwiro, chikondi chimene chimapilira mwa khama ku pemphero, mpaka mapeto adzafika, pamene oyera onse adzakhala ndi Mulungu.

27 Taona, mwana wanga, ndidzakulemberanso ngati sindipita posachedwapa motsutsana ndi Alamani. Taona, kunyada kwa mtundu uwu, kapena anthu a Anefi, kwatsimikizira chiwonongeko chawo pokhapokha iwo atalapa.

28 Apemphelere iwo, mwana wanga, kuti kulapa kubwere kwa iwo. Koma taona, ine ndikuwopa kuti kapena Mzimu udasiya kulimbana ndi iwo; ndi ku mbali iyi ya dziko iwonso akufunafuna kutaya mphamvu zonse ndi ulamuliro umene umachokera kwa Mulungu; ndipo iwo akukana Mzimu Woyera.

29 Ndipo atakana chidziwitso chachikulu chotere, mwana wanga, akuyenera kuwonongeka posachedwa, mpaka kukwaniritsidwa kwa mauneneri amene adanenedwa ndi aneneri, komanso mawu a Mpulumutsi wathu iye mwini.

30 Tsala bwino, mwana wanga, mpaka ine ndidzakulembera iwe, kapena ndidzakumana nawenso. Ameni.