Malembo Oyera
Moroni 10


Mutu 10

Umboni wa Buku la Mormoni umabwera ndi mphamvu ya Mzimu Woyera—Mphatso za Mzimu zimaperekedwa kwa okhulupilira—Mphatso zauzimu nthawi zonse zimabwera ndi chikhulupiliro—Mawu a Moroni ayankhula kuchokera ku fumbi—Bwerani kwa Khristu, khalani angwiro mwa Iye, ndipo yeretsani miyoyo yanu. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 421.

1 Tsopano ine, Moroni, ndikulemba zinazake monga zowoneka zabwino kwa ine; ndipo ine ndikulemba kwa abale anga, Alamani; ndipo ndikufuna kuti adziwe kuti zaka zoposa mazana anayi ndi makumi awiri zapita chiyambire pamene chizindikiro chidaperekedwa cha kudza kwa Khristu.

2 Ndipo ine ndikusindikiza zolemba izi, nditatha kuyankhula mawu ochepa mwa njira ya chilimbikitso kwa inu.

3 Taonani, ndikufuna ndikulimbikitseni kuti pamene mudzawerenga zinthu izi, ngati ili nzeru mwa Mulungu kuti mudzawerenga izo, kuti mudzakumbukire momwe Ambuye adakhalira wachifundo kwa ana a anthu, kuchokera ku chilengedwe cha Adamu ngakhale mpaka nthawi imene inu mudzalandire zinthu izi, ndi kuzilingalira mu mitima yanu.

4 Ndipo pamene mudzalandira zinthu izi; ndikufuna ndikulimbikitseni inu kuti mudzafunse kwa Mulungu, Atate Wamuyaya, mu dzina la Khristu, ngati zinthu izi siziri zoona; ndipo ngati mudzafunsa ndi mtima woona, ndi cholinga chenicheni, pokhala ndi chikhulupiliro mwa Khristu, iye adzawonetsera choonadi cha izo kwa inu, ndi mphamvu ya Mzimu Woyera.

5 Ndipo mwa mphamvu ya Mzimu Woyera inu mutha kudziwa choonadi cha zinthu zonse.

6 Ndipo chilichonse chabwino chili cholungama ndi choona; kotero, palibe chomwe chili chabwino chimakana Khristu, koma chimavomereza kuti iye ali.

7 Ndipo inu mutha kudziwa kuti iye ali, mwa mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero ine ndikufuna ndikulimbikitseni inu kuti musakane mphamvu ya Mulungu; chifukwa amagwira ntchito ndi mphamvu; monga mwa chikhulupiliro cha ana a anthu, chimodzimodzi lero ndi mawa, ndi ku nthawi zosatha.

8 Ndiponso ndikukulimbikitsani, abale anga, kuti musakane mphatso za Mulungu, pakuti ndizochuluka; ndipo izo zimachokera kwa Mulungu yemweyo. Ndipo pali njira zosiyanasiyana zomwe mphatso izi zimagwiritsidwira ntchito; koma Mulungu yemweyo ndiye wakuchita zonse mwa onse; ndipo zimaperekedwa ndi maonetseredwe a Mzimu wa Mulungu kwa anthu, kuti apindule nazo.

9 Pakuti taonani, kwa m’modzi kwapatsidwa mwa Mzimu wa Mulungu, kuti akaphunzitse mawu a nzeru;

10 Ndi kwa wina, kuti akaphunzitse mawu a chidziwitso mwa Mzimu womwewo;

11 Ndi kwa wina, chikhulupiliro chachikulu kwambiri; ndi kwa wina mphatso za machiritso, mwa Mzimu womwewo;

12 Ndiponso, kwa wina, kuti akachite zozizwitsa zamphamvu;

13 Ndiponso, kwa wina, kuti athe kunenera zokhudzana ndi zinthu zonse;

14 Ndiponso, kwa wina, kuona kwa angelo ndi mizimu yotumikira;

15 Ndiponso, kwa wina, mitundu yonse ya malilime;

16 Ndiponso, kwa wina, kumasulira kwa ziyankhulo ndi mitundu yosiyanasiyana ya malilime.

17 Ndipo mphatso zonse izi zimadza mwa Mzimu wa Khristu; ndipo zimadza kwa munthu aliyense payekhapayekha, molingana ndi momwe afunire.

18 Ndipo ndikukulimbikitsani, abale anga okondedwa, kuti mukumbukire kuti mphatso yabwino iliyonse imachokera kwa Khristu.

19 Ndipo ndikukulimbikitsani inu, abale anga okondedwa, kuti mukumbukire kuti ali yemweyo dzulo, lero, ndi kunthawi zosatha, ndi kuti mphatso zonsezi zomwe ndayankhula, zomwe ndi zauzimu, sizidzathetsedwa, ngakhale konse pamene dziko lidzayima, pokhapokha molingana ndi kusakhulupilira kwa ana a anthu.

20 Kotero, pakuyenera kukhala chikhulupiliro; ndipo ngati pakuyenera kukhala chikhulupiliro pakuyeneranso kukhala chiyembekezo; ndipo ngati pali chiyembekezo pakuyeneranso kukhala chikondi.

21 Ndipo pokhapokha muli ndi chikondi inu simungathe mwanjira iliyonse kupulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu; ngakhale inu simungathe kupulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu ngati inu mulibe chikhulupiliro; ngakhale simungathe ngati mulibe chiyembekezo.

22 Ndipo ngati mulibe chiyembekezo mukuyenera kukhala otaya mtima; ndipo kutaya mtima kumabwera chifukwa cha kusaweruzika.

23 Ndipo Khristu adanenadi kwa makolo athu: Ngati muli ndi chikhulupiliro mukhonza kuchita zinthu zonse zomwe zili zoyenera kwa ine.

24 Ndipo tsopano ndikuyankhula ku malekezero onse a dziko lapansi—kuti ngati tsiku lidzafika kuti mphamvu ndi mphatso za Mulungu zidzachotsedwa pakati panu, chidzakhala chifukwa cha kusakhulupilira.

25 Ndipo tsoka lidzakhala kwa ana a anthu ngati izi zili choncho; pakuti sipadzakhala wina wakuchita zabwino mwa inu, sadzakhalapo ngakhale m’modzi. Pakuti ngati pali m’modzi mwa inu amene achita zabwino, iye adzagwira ntchito ndi mphamvu ndi mphatso za Mulungu.

26 Ndipo tsoka kwa iwo amene adzachita zinthu izi ndi kufa, pakuti adzafa m’machimo awo, ndipo sangathe kupulumutsidwa mu ufumu wa Mulungu; ndipo ndikunena molingana ndi mawu a Khristu; ndipo sindikunama.

27 Ndipo ndikukulimbikitsani kuti mukumbukire zinthu izi; pakuti nthawi ilinkudza mwansanga imene inu mudzadziwa kuti sindikunama, pakuti mudzandiona ku bwalo la Mulungu; ndipo Ambuye Mulungu adzanena kwa inu: Kodi ine sindidanene mawu anga kwa inu, amene adalembedwa ndi munthu ameneyu, monga ngati wofuula kuchokera kwa akufa, inde, ngakhale monga woyankhula kuchokera m’fumbi?

28 Ndikulengeza zinthu izi ku kukwaniritsidwa kwa mauneneri. Ndipo taonani, zidzatuluka kuchokera mkamwa mwa Mulungu wosatha; ndipo mawu ake adzapita ndi mphamvu kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo.

29 Ndipo Mulungu adzaonetsa kwa inu, kuti zimene ndalemba ndi zoona.

30 Ndiponso ndikufuna ndikulimbikitseni inu kuti mudze kwa Khristu, ndipo gwirani pa mphatso yabwino iliyonse, ndipo musakhudze mphatso yoipa, kapena chinthu chodetsedwa.

31 Ndipo galamuka, ndikudzuka ku fumbi, O Yerusalemu; inde, ndipo vala zovala zako zokongola, O mwana wamkazi wa Ziyoni; ndi kulimbikitsa zikhomo zako ndi kukulitsa malire ako kwamuyaya, kuti iwe usadzasokonezedwenso, kuti mapangano a Atate Wamuyaya amene adapanga kwa iwe, O nyumba ya Israeli, akathe kukwaniritsidwa.

32 Inde, bwerani kwa Khristu, ndi kukhala angwiro mwa iye, ndi kudzikana nokha ku kupanda umulungu konse; ndipo ngati mudzadzikana inu eni pa kupanda umulungu konse, ndi kukonda Mulungu ndi mphamvu zanu zonse, malingaliro ndi mphamvu zanu zonse, pamenepo chisomo chake chili chokwanira kwa inu, kuti mwa chisomo chake mutha kukhala angwiro mwa Khristu; ndipo ngati ndi chisomo cha Mulungu muli angwiro mwa Khristu, simungathe mwanjira iliyonse kukana mphamvu ya Mulungu.

33 Ndiponso, ngati inu mwa chisomo cha Mulungu muli angwiro mwa Khristu, ndi kusakana mphamvu yake, pamenepo inu mwayeretsedwa mwa Khristu mwa chisomo cha Mulungu, kudzera mu kukhetsa kwa mwazi wa Khristu, umene uli mu pangano la Atate ku chikhululukiro cha machimo anu, kuti inu mukhale oyera, opanda banga.

34 Ndipo tsopano ndikutsanzika kwa nonse, tsalani bwino. Posachedwapa ndipita kukapumula mu paradiso wa Mulungu, mpaka mzimu wanga ndi thupi langa zidzalumikizanenso, ndipo ndidzabweretsedwa mwachipambano mumlengalenga, kudzakumana nanu pamaso pa bwalo lokondweretsa la Yehova wamkulu, Woweruza Wamuyaya wa amoyo ndi akufa. Ameni.

Print