Mutu 2
Yesu adapereka kwa ophunzira khumi ndi awiri Achinefi mphamvu yopereka mphatso ya Mzimu Woyera. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401–421.
1 Mawu a Khristu, amene adayankhula kwa ophunzira ake, khumi ndi awiri amene iye adawasankha, pamene adasanjika manja ake pa iwo—
2 Ndipo adawayitana powatchula dzina, nati: Inu mudzayitana pa Atate m’dzina langa, m’pemphero lamphamvu; ndipo mukadzatha kuchita izi mudzakhala ndi mphamvu kuti kwa iye amene inu mudzasanjika manja anu, mudzapereka Mzimu Woyera; ndipo m’dzina langa mudzaupereka, pakuti atumwi anga amachita motero.
3 Tsopano Khristu adayankhula mawu awa kwa iwo pa nthawi ya kuwonekera kwake koyamba; ndipo khamulo silidamve, koma ophunzira adamva; ndipo pa onse amene adasanjika manja awo, udagwa Mzimu Woyera.