Mutu 4
Momwe akulu ndi ansembe amaperekera mkate wa mgonero zifotokozedwa. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401–421.
1 Njira ya akulu ndi ansembe awo popereka thupi ndi mwazi wa Khristu ku mpingo; ndipo adazipereka molingana ndi malamulo a Khristu; kotero tikudziwa machitidwewo kukhala owona; ndipo mkulu kapena wansembe adatumikira izi;
2 Ndipo iwo adagwada pansi ndi mpingo, ndikupemphera kwa Atate m’dzina la Khristu, kuti:
3 O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani mu dzina la Mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndi kuyeretsa mwa uwu kwa miyoyo ya onse amene adye mkatewu; kuti adye pokumbukira thupi la Mwana wanu, ndi kuchitira umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya, kuti iwo ndiwofunitsitsa kutenga pa iwo dzina la Mwana wanu, ndi kumukumbukira iye nthawi zonse, ndikusunga malamulo ake amene iye wapereka kwa iwo, kuti akathe kukhala nawo Mzimu wake nthawi zonse. Ameni.