Malembo Oyera
Moroni 7


Mutu 7

Kuyitanidwa kwaperekedwa kuti alowe mu mpumulo wa Ambuye—Pempherani ndi cholinga chenicheni—Mzimu wa Khristu umapangitsa anthu kudziwa zabwino ndi zoipa—Satana amakopa anthu kuti akane Khristu ndi kuchita zoipa—Aneneri amaonetsa kudza kwa Khristu—Mwa chikhulupiliro, zozizwa zimachitidwa ndipo angelo amatumikira—Anthu akuyenera kuyembekezera moyo wosatha ndi kukangamira ku chikondi. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401–421.

1 Ndipo tsopano ine, Moroni, ndilemba mawu wochepa a atate anga Mormoni, omwe adayankhula zokhudzana ndi chikhulupiliro, chiyembekezo, ndi chikondi; pakuti motere adayankhula ndi anthu, pamene adawaphunzitsa musunagoge imene adamanga kuti ndi malo opembedzeramo.

2 Ndipo tsopano ine, Mormoni, ndikuyankhula kwa inu, abale anga okondedwa; ndipo ndi mwa chisomo cha Mulungu Atate, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chifuniro chake choyera, chifukwa cha mphatso ya mayitanidwe ake kwa ine, kuti ndaloredwa kuyankhula ndi inu pa nthawi ino.

3 Kotero, ndikuyankhula kwa inu amene muli a mpingo, omwe muli otsatira amtendere a Khristu, ndipo amene mwapeza chiyembekezo chokwanira chomwe mungalowere mu mpumulo wa Ambuye, kuyambira nthawi ino mpaka mudzapumule naye kumwamba.

4 Ndipo tsopano abale anga, ine ndikuweruza zinthu izi za inu chifukwa cha kuyenda kwanu kwamtendere ndi ana a anthu.

5 Pakuti ine ndikukumbukira mawu a Mulungu amene amati ndi ntchito zawo inu mudzawadziwa iwo; pakuti ngati ntchito zawo zili zabwino, ndiyekuti iwonso ali abwino.

6 Pakuti taonani, Mulungu adati munthu pokhala woipa sangachite icho chimene chili chabwino; pakuti ngati apereka mphatso, kapena apemphera kwa Mulungu, pokhapokha iye adzachita icho ndi cholinga chenicheni sizimupindulira kalikonse.

7 Pakuti taonani, sizikuwerengedwa kwa iye ku chilungamo.

8 Pakuti taonani, ngati munthu wokhala woipa apereka mphatso, amachita monyinyirika; kotero chimawerengedwa kwa iye chimodzimodzi monga ngati adasunga mphatsoyo; kotero amatengedwa woipa pamaso pa Mulungu.

9 Ndipo momwemonso kumayesedwa koipa kwa munthu, ngati angapemphere osati ndi cholinga chenicheni cha mtima; inde, ndipo sizimupindulira kalikonse, pakuti Mulungu salandira otere.

10 Kotero, munthu pokhala woipa sangachite icho chomwe chili chabwino; kapena kupereka mphatso yabwino.

11 Pakuti taonani, kasupe owawa satulutsa madzi abwino; ngakhale kasupe wabwino sadzatulutsa madzi owawa; kotero, munthu pokhala kapolo wa mdyerekezi sangathe kutsatira Khristu; ndipo ngati atsatira Khristu sangakhale kapolo wa mdyerekezi.

12 Kotero, zinthu zonse zomwe zili zabwino zimachokera kwa Mulungu; ndipo icho choipa chimachokera kwa mdyerekezi; pakuti mdyerekezi ali m’dani kwa Mulungu, ndipo amenyana ndi iye mosalekeza, ndipo amaitanira ndi kukopera ku uchimo, ndi kuchita icho chimene chili choipa kosalekeza.

13 Koma taonani, chimene chili cha Mulungu chimayitana ndi kukopa kuchita zabwino mosalekeza; kotero, chilichonse chomwe chimayitanira ndi kukopa kuchita zabwino, ndi kukonda Mulungu, ndi kumutumikira iye, ndi chowuziridwa ndi Mulungu.

14 Kotero, chenjerani, abale anga okondedwa, kuti musaweruze icho chimene chili choipa kukhala cha Mulungu, kapena icho chimene chili chabwino ndi cha Mulungu kukhala cha mdyerekezi.

15 Pakuti taonani, abale anga, kwapatsidwa kwa inu kuti muweruze, kuti mudziwe zabwino ndi zoipa; ndipo njira ya kuweruza ili yomveka, kuti inu mudziwe ndi chidziwitso chonse, monga kuwala kwa usana kuli kuchokera ku usiku wamdima.

16 Pakuti, taonani, Mzimu wa Khristu wapatsidwa kwa munthu aliyense, kuti inu mudziwe zabwino kuchoka ku zoipa; kotero, ndikuonetsa kwa inu njira yoweruzira; pakuti chinthu chilichonse choyitanira kuchita zabwino, ndi kukopa kuti akhulupilire mwa Khristu, chimatumizidwa ndi mphamvu ndi mphatso ya Khristu; kotero mungathe kudziwa ndi chidziwitso chonse kuti ndi cha Mulungu.

17 Koma chilichonse chokopa anthu kuti achite zoipa, ndi kusakhulupilira Khristu, ndi kumkana, ndi kusatumikira Mulungu, pamenepo inu mudzadziwa ndi chidziwitso chonse kuti chili cha mdyerekezi; pakuti mdyerekezi achita motero, pakuti sakopa munthu aliyense kuchita chabwino, inde, ngakhale m’modzi; ngakhalenso angelo ake; ngakhalenso iwo odziyika okha pansi pa iye.

18 Ndipo tsopano, abale anga, poona kuti mwadziwa kuwala kumene mungaweruzire, kuwala kumene kuli kuwala kwa Khristu, onani kuti musaweruze molakwika; pakuti ndi chiweruzo chomwe muweruza nacho inunso mudzaweruzidwira.

19 Kotero, ndikukupemphani inu, abale, kuti mufunitsitse mwakhama mu kuwala kwa Khristu, kuti muthe kudziwa zabwino ndi zoipa; ndipo ngati inu mugwira pa chinthu chabwino chilichonse, ndikusachitsutsa icho, inu ndithudi mudzakhala mwana wa Khristu.

20 Ndipo tsopano, abale anga, zingatheke bwanji kuti mugwire chinthu chabwino chilichonse?

21 Ndipo tsopano ine ndabwera ku chikhulupiliro chimenecho, chimene ine ndidati ndidzayankhula; ndipo ndidzakuuzani njira imene mungathe kugwilira zabwino zonse.

22 Pakuti taonani, Mulungu podziwa zinthu zonse, pokhala wochokera ku nthawi yosatha mpaka kunthawi yosatha, taonani, adatumiza angelo kukatumikira kwa ana a anthu, kuti awonetsere zokhudzana ndi kudza kwa Khristu; ndipo mwa Khristu mukuyenera kubwera zabwino zonse.

23 Ndipo Mulungu adalengezanso kwa aneneri, ndi pakamwa pake, kuti Khristu adzabwera.

24 Ndipo taonani, kudali njira zosiyanasiyana zimene adasonyezera zinthu kwa ana a anthu, zimene zidali zabwino; ndipo zinthu zonse zabwino zimachokera kwa Khristu; apo ayi anthu adali okugwa, ndipo padalibe kanthu kabwino kakadabwera kwa iwo.

25 Kotero, kudzera mu kutumikira kwa angelo, ndi mawu aliwonse amene adatuluka kuchokera mkamwa mwa Mulungu, anthu adayamba kusonyeza chikhulupiliro mwa Khristu; ndipo choncho mwa chikhulupiliro, iwo adagwira pa chinthu chabwino chilichonse; ndipo izo zidali motero mpaka kudza kwa Khristu.

26 Ndipo atabwera anthunso adapulumutsidwa mwa chikhulupiliro m’dzina lake; ndipo mwa chikhulupiliro, iwo amakhala ana a Mulungu. Ndipo inde monga m’mene Khristu alili wa moyo adayankhula mawu awa kwa makolo athu, nati: Chilichonse chimene inu mudzapempha Atate m’dzina langa, chimene chili chabwino, m’chikhulupiliro kukhulupilira kuti mudzalandira, taonani, chidzachitidwa kwa inu.

27 Kotero, abale anga okondedwa, kodi zozizwitsa zatha chifukwa Khristu adakwera kumwamba, ndipo wakhala pansi pa dzanja lamanja la Mulungu, kuti atenge kwa Atate ma ufulu ake a chifundo chimene iye alinacho pa ana a anthu?

28 Pakuti iye wayankha malekezero a chilamulo, ndipo akuwatenga iwo onse amene ali ndi chikhulupiliro mwa iye; ndipo iwo amene ali ndi chikhulupiliro mwa iye adzakangamira ku chinthu chilichonse chabwino; kotero amaimilira njira ya ana a anthu; ndipo iye amakhala kumwamba kwamuyaya.

29 Ndipo chifukwa chakuti wachita ichi, abale anga okondedwa, kodi zozizwitsa zatha? Taonani ndinena kwa inu, ayi; ngakhale angelo sadaleke kutumikira kwa ana a anthu.

30 Pakuti taonani, iwo ali pansi pa iye, kutumikira monga mwa mawu a lamulo lake, kudzionetsera okha kwa iwo a chikhulupiliro cholimba ndi malingaliro okhazikika mu mtundu uliwonse wa umulungu.

31 Ndipo udindo wa utumiki wawo ndi kuyitanira anthu ku kulapa, ndi kukwaniritsa ndi kuchita ntchito ya mapangano a Atate, amene adawapanga kwa ana a anthu, kukonza njira pakati pa ana a anthu; pa kulalikira mawu a Khristu kwa zotengera zosankhika za Ambuye, kuti zikathe kupereka umboni wa iye.

32 Ndipo pakuchita izi, Ambuye Mulungu amakonza njira kuti otsala a anthu akakhale ndi chikhulupiliro mwa Khristu, kuti Mzimu Woyera ukathe kukhala ndi malo m’mitima yawo, molingana ndi mphamvu yake; ndipo monga momwemu adzakwaniritsa Atate, mapangano amene adawapanga kwa ana a anthu.

33 Ndipo Khristu adati: Ngati mudzakhala ndi chikhulupiliro mwa ine mudzakhala ndi mphamvu yakuchita chinthu chilichonse chili choyenera mwa ine.

34 Ndipo iye adati: Lapani malekezero onse a dziko lapansi, ndipo idzani kwa ine, ndipo batizidwani m’dzina langa, ndipo khalani ndi chikhulupiliro mwa ine, kuti inu muthe kupulumutsidwa.

35 Ndipo tsopano, Abale anga okondedwa, ngati izi zili choncho kuti zinthu izi zili zoona zimene ine ndayankhula kwa inu, ndipo Mulungu adzaonetsa kwa inu, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu pa tsiku lomaliza, kuti zili zoona, ndipo ngati zili zoona kodi tsiku la zozizwitsa lidatha?

36 Kapena angelo adaleka kuonekera kwa ana a anthu? Kapena wakaniza mphamvu ya Mzimu Woyera kwa iwo? Kapena iye adzatero, mpaka m’mene nthawi idzakhalire, kapena dziko lapansi lidzayima, kapena padzakhala munthu m’modzi pa nkhope yake kuti apulumutsidwe?

37 Taonani ndinena kwa inu, Ayi; pakuti ndi mwa chikhulupiliro kuti zozizwitsa zimachitidwa; ndipo ndi mwa chikhulupiliro kuti angelo amaonekera ndi kutumikira kwa anthu; kotero ngati zinthu izi zaleka tsoka kwa ana a anthu, pakuti ndi chifukwa cha kusakhulupilira, ndipo zonse zili chabe.

38 Pakuti palibe munthu angapulumutsidwe, molingana ndi mawu a Khristu, pokhapokha iwo adzakhale ndi chikhulupiliro mu dzina lake; kotero, ngati zinthu izi zidalekeka, pamenepo chikhulupiliro chidalekeka; ndipo woopsa ndi mkhalidwe wa munthu, pakuti ali ngati kuti padalibe chiwombolo chomwe chidapangidwa.

39 Koma taonani, Abale anga okondedwa, ndiweruza zinthu zabwino za inu, pakuti ndikuweruza kuti muli ndi chikhulupiliro mwa Khristu chifukwa cha kufatsa kwanu; pakuti ngati simuli ndi chikhulupiliro mwa iye ndiye kuti simukuyenera kuwerengeredwa pakati pa anthu a mpingo wake.

40 Ndiponso, abale anga okondedwa, ndikufuna kuyankhula kwa inu zokhudzana ndi chiyembekezo. Ndimotani momwe inu mungathe kufika ku chikhulupiliro, pokhapokha inu mutakhala nacho chiyembekezo?

41 Ndipo ndi chiyani chimene mudzayembekezera ? Taonani ndikunena kwa inu kuti mudzakhala nacho chiyembekezo mwa chitetezero cha Khristu ndi mphamvu ya chiukitso chake, kuukitsidwa ku moyo wosatha, ndipo izi chifukwa cha chikhulupiliro chanu mwa iye molingana ndi lonjezano.

42 Kotero, ngati munthu ali ndi chikhulupiliro akuyenera kukhala ndi chiyembekezo; pakuti popanda chikhulupiliro sipangakhale chiyembekezo chilichonse.

43 Ndiponso, taonani ndikunena kwa inu kuti iye sangakhale ndi chikhulupiliro ndi chiyembekezo, pokhapokha iye atakhala wofatsa, ndi wodzichepetsa mu mtima.

44 Ngati ndi choncho, chikhulupiliro chake ndi chiyembekezo chake n’chachabe, pakuti palibe amene alandiridwa pamaso pa Mulungu, kupatula wofatsa ndi wodzichepetsa mu mtima; ndipo ngati munthu ali wofatsa ndi wodzichepetsa mu mtima, ndi kuvomereza mwa mphamvu ya Mzimu Woyera kuti Yesu ndi Khristu, iye akuyenera kukhala ndi chikondi; pakuti ngati alibe chikondi ali chabe; kotero akuyenera kukhala nacho chikondi.

45 Ndipo chikondi chimaleza mtima, ndipo ndichokoma mtima, ndipo sichichita nsanje, ndipo sichidzikuza, sichitsata zake, sichikwiya msanga, sichiganizira zoipa, ndipo sichikondwera ndi kusaweruzika, koma chimakondwera muchoonadi, chimalolera zinthu zonse, chimakhulupilira zinthu zonse, chimayembekezera zinthu zonse, chimapilira zinthu zonse.

46 Kotero, abale anga okondedwa, ngati mulibe chikondi, muli chabe, pakuti chikondi sichilephera. Kotero, kangamirani ku chikondi, chomwe chili chachikulu mwa zonse, pakuti zinthu zonse zikuyenera kulephera—

47 Koma chifundo ndicho chikondi chenicheni cha Khristu, ndipo chimapilira ku nthawi zosatha; ndipo amene adzapezeke ali nacho tsiku lomaliza, zidzakhala bwino kwa iye.

48 Kotero, abale anga okondedwa, pempherani kwa Atate ndi mphamvu zonse za mtima, kuti mudzadzidwe ndi chikondi ichi, chimene iye apereka pa onse amene ali otsatira owona a Mwana wake, Yesu Khristu; kuti mukathe kukhala ana a Mulungu; kuti pamene adzaonekera tidzakhala monga iye, pakuti tidzamuona iye monga alili; kuti tikhale nacho chiyembekezo ichi; kuti tithe kuyeretsedwa, monga iye ali woyera. Ameni.

Print