Malembo Oyera
Moroni 1


Buku la Moroni

Mutu 1

Moroni alemba kuti ziwapindulire wa Alamani—Anefi amene sadzakana Khristu aphedwa. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401–421.

1 Tsopano ine, Moroni, nditamaliza kufupikitsa nkhani ya anthu a Yaredi, sindidayenere kuti ndilembe zambiri, koma sindidawonongekebe; ndipo sindikuzidziwitsa ndekha kwa Alamani kuwopa kuti angandiwononge.

2 Pakuti taonani, nkhondo zawo ndi zowopsa kwambiri pakati pawo; ndipo chifukwa cha udani wawo iwo adapha Mnefi aliyense amene sadakane Khristu.

3 Ndipo ine, Moroni, sindikana Khristu; kotero, ndikumayendayenda kulikonse komwe ndingathe chifukwa cha chitetezo cha moyo wanga.

4 Kotero, ndikulemba zinthu zinanso zingapo, zosiyana ndi zomwe ndimaganiza; pakuti sindidayenere kulembanso; koma ndilemba zinthu zinanso zingapo, kuti mwina zingathe kukhala zofunikira kwa abale anga, Alamani, m’tsiku lina lamtsogolo, molingana ndi chifuniro cha Ambuye.

Print