Kalata yachiwiri ya Mormoni kwa mwana wake Moroni.
Yophatikizidwa Mutu 9.
Mutu 9
Onse Anefi ndi Alamani ndi woipitsidwa ndi kuchepetsedwa—Iwo azunzana ndi kuphana wina ndi mnzake—Mormoni apemphera kuti chisomo ndi ubwino zikhale pa Moroni kwamuyaya. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401.
1 Mwana wanga wokondedwa, ndakulemberanso kuti udziwe kuti ndikadali wamoyo; Koma ine ndalemba zinazake zomwe zili zokhumudwitsa.
2 Pakuti taona, ndidakhala ndi nkhondo yowawa ndi Alamani, imene ife sitidagonjetse; ndipo Akentu wagwa ndi lupanga, ndiponso Luramu ndi Emironi; inde, ndipo tataya anthu ambiri osankhika athu.
3 Ndipo tsopano taona, mwana wanga, ine ndikuopa kuti mwina Alamani adzawononga anthu awa; pakuti sakulapa; ndipo Satana amautsa iwo kosalekeza kuti akwiyirane wina ndi mzake.
4 Taona, ndikugwira nawo ntchito kosalekeza; ndipo pamene ndikuyankhula mawu a Mulungu mwamphamvu iwo amanjenjemera ndi kukwiya motsutsana nane; Ndipo ndikapanda kudzudzula mwamphamvu amaumitsa mitima yawo pa izo; kotero, ndikuopa kuti kapena Mzimu wa Ambuye waleka kulimbana nawo.
5 Pakuti kwambiri iwo akwiya mpaka akundiwonekera kuti alibe mantha ndi imfa; ndipo iwo ataya chikondi chawo, wina ndi mzake; ndipo akumva ludzu la mwazi, ndi kubwenzera chilango kosalekeza.
6 Ndipo tsopano, mwana wanga okondedwa, posatengera za kuuma kwawo, tiye ife tigwire ntchito molimbika; pakuti ngati tileka kugwira ntchito, tidzatsutsidwa; pakuti tili ndi ntchito yoti tichite pamene tili m’chihema ichi cha dongo, kuti tikathe kugonjetsa mdani wa chilungamo chonse, ndi kupumula miyoyo yathu mu ufumu wa Mulungu.
7 Ndipo tsopano ndikulemba zinazake zokhudzana ndi mazunzo a anthu awa. Pakuti molingana ndi chidziwitso chomwe ndalandira kuchokera kwa Amoroni, taona, Alamani ali ndi akaidi ambiri, amene adawatenga pa nsanja ya Sheriza; ndipo padali amuna, akazi, ndi ana.
8 Ndipo amuna ndi abambo a akazi amenewo ndi ana amenewo adawapha; ndipo amadyetsa akazi ndi mnofu wa amuna awo, ndi ana ndi matupi a makolo awo; ndipo popanda madzi, koma pang’ono; amawapatsa.
9 Ndipo posatengera chonyansa chachikulu ichi cha Alamani, sichikupitilira icho cha anthu athu mu Moriyantumu. Pakuti, taona, ambiri a ana aakazi a Alamani awatenga akaidi; ndipo atawalanda iwo chimene chidali chokondedwa kwambiri ndi chamtengo wapatali koposa zinthu zonse, chimene chili kudzisunga ndi ungwiro—
10 Ndipo atatha kuchita ichi, iwo adawapha iwo m’njira yankhanza kwambiri, kuzunza matupi awo ngakhale mpaka ku imfa; ndipo atatha kuchita izi, amadya nyama yawo ngati zilombo zakuthengo, chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo; ndipo amazichita ngati chizindikiro cha kulimba mtima.
11 O mwana wanga okondedwa, angatani anthu ngati awa, amene ali opanda chitukuko?
12 (Ndipo zaka zochepa zapita, ndipo adali anthu akhalidwe labwino ndi okondweretsa).
13 Koma O mwana wanga, angatani anthu onga awa, amene chikondwelero chawo chili chonyansa kwambiri motere?
14 Kodi tingayembekezere bwanji kuti Mulungu angatsekereze dzanja lake ku chiweruzo motsutsana nafe?
15 Taona, mtima wanga ulira: Tsoka kwa anthu awa. Tulukani mu chiweruzo, O Mulungu, ndipo bisani machimo awo, ndi kuipa, ndi zonyansa kuchokera pamaso panu!
16 Ndiponso, mwana wanga, kuli akazi amasiye ambiri ndi ana awo aakazi amene atsalira mu Sheriza; ndipo gawo limenelo la chakudya chimene Alamani sadachitenge, taona, gulu lankhondo la Zenefi lawatengera kutali, ndipo lidawasiya iwo kuti aziyendayenda kulikonse kumene angathe chifukwa cha chakudya; ndipo amayi achikulire ambiri akomoka panjira, ndikumwalira.
17 Ndipo ankhondo amene ali ndi ine afooka; ndipo magulu ankhondo a Alamani ali pakati pa Sheriza ndi ine; ndipo onse amene athawira ku gulu lankhondo la Aroni akhala ogwidwa ku nkhanza zawo zoopsa.
18 O, kuipa kwa anthu anga! Iwo ali opanda dongosolo ndi opanda chifundo. Taona, ine ndine munthu, ndipo ndili ndi mphamvu za munthu, ndipo sindingathenso kugwiritsa ntchito malamulo anga.
19 Ndipo akhala amphamvu m’kusochera kwawo; ndipo afanana munkhanza, osasiya aliyense, achikulire kapena achichepere; ndipo amakondwera ndi chilichonse kupatula icho chimene chili chabwino; ndipo mazunzo a akazi athu ndi ana athu pa nkhope yonse ya dziko lino aposa chilichonse; inde lilime silingathe kunena, kapena kutheka kuzilemba.
20 Ndipo tsopano, mwana wanga, sindikhalanso pa chochitika choipa ichi. Taona, iwe ukudziwa kuipa kwa anthu awa; iwe ukudziwa kuti iwo ali opanda chikhalidwe, ndipo adutsa pa kumvelera kulikonse; ndipo kuipa kwawo kwapambana uko kwa Alamani.
21 Taona, mwana wanga, sindingathe kuwavomereza iwo kwa Mulungu kuopa kuti angandikanthe.
22 Koma taona, mwana wanga, ndikukuvomereza iwe kwa Mulungu, ndipo ndikhulupilira mwa Khristu kuti udzapulumutsidwa; ndipo ndikupemphera kwa Mulungu kuti asunge moyo wako, kuti ukachitire umboni kubwelera kwa anthu ake kwa iye, kapena chiwonongeko chawo chotheratu; pakuti ndikudziwa kuti akuyenera kuwonongeka pokhapokha atalapa ndi kubwelera kwa iye.
23 Ndipo ngati adzawonongeka zidzakhala ngati kwa Ayeredi, chifukwa cha kufuna kwa mitima yawo, kufunafuna mwazi ndi kubwenzera choipa.
24 Ndipo ngati zitadzakhale kuti iwo awonongeka, tikudziwa kuti ambiri a abale athu apita kwa Alamani, ndipo ochulukanso adzapita kwa iwo; kotero, udzalembe zinthu zingapo pang’ono, ngati udzapulumuke ndipo ine ndidzawonongedwa ndipo sindidzakuona iwe; koma ndikukhulupilira kuti ndidzakuona posachedwa; pakuti ine ndili nazo zolemba zopatulika zomwe ndikufuna kupereka kwa iwe.
25 Mwana wanga, khala okhulupirika mwa Khristu; ndipo zisakukhumudwitse zimene ndalemba, kuti zikulemetse iwe kufikira imfa; koma Khristu akukweze pamwamba, ndipo zowawa zake ndi imfa, ndi kuzionetsa kwa thupi lake kwa makolo athu, ndi chifundo chake ndi kuleza mtima kwake, ndi chiyembekezo cha ulemelero wake ndi cha moyo wosatha, zikhale mu malingaliro ako kwamuyaya.
26 Ndipo chisomo cha Mulungu Atate, amene mpando wachifumu wake uli m’mwamba mwamba, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, amene wakhala pa dzanja lamanja la mphamvu yake, mpaka zinthu zonse zidzakhala pansi pa iye, chikhale, ndi kukhala ndi iwe kwamuyaya. Ameni.