Malembo Oyera
Moroni 5


Mutu 5

Njira yoperekera vinyo wa mgonero ikhazikitsidwa. Mdzaka dza pafupifupi Yesu atabadwa 401–421.

1 Mchitidwe operekera vinyo—Taonani, adatenga chikho, nati:

2 O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani, m’dzina la Mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndi kuyeretsa vinyo uyu ku miyoyo ya onse amene amamwamo, kuti athe kuchita ichi pokumbukira mwazi wa Mwana wanu, umene udakhetsedwa chifukwa cha iwo; kuti akathe kuchitira umboni kwa inu, O Mulungu; Atate Wamuyaya, kuti amukumbukire iye nthawi zonse, kuti akathe kukhala ndi Mzimu wake nthawi zonse kukhala nawo. Ameni.