Malembo Oyera
Mawu a Mormoni 1


Mawu a Mormoni

Mutu 1

Mormoni afupikitsa mapale aakulu a Nefi—Aphatikiza mapale aang’ono ndi mapale ena—Mfumu Benjamini akhazikitsa mtendere m’dziko Mdzaka dza pafupifupi 385 Yesu atamwalira.

1 Ndipo tsopano ine, Mormoni, nditatsala pang’no kupereka zolemba zimene ndakhala ndikupanga m’manja mwa mwana wanga Moroni, taonani, ndachitira umboni pafupifupi chiwonongeko chonse cha anthu anga, Anefi.

2 Ndipo papita dzaka dzambiri Khristu atabwera, pamene ine ndikupereka zolemba izi m’manja mwa mwana wanga; ndipo ndikuganiza kuti iye adzachitira umboni chiwonongeko chonse cha anthu anga. Koma Mulungu ampatse iye kuti adzapulumuke kwa iwo, kuti adzalembe zinazake zokhudzana ndi iwo, ndi zinazake zokhudzana ndi Khristu, kuti mwina tsiku lina zidzawapindulire.

3 Ndipo tsopano ndikuyankhula zinazake zokhudzana ndi zimene ndazilemba; pakuti nditamaliza kufupikitsa kuchokera ku mapale a Nefi, kutsikira ku ulamuliro wa mfumu Benjamini, amane Amaleki adayankhula, ndidafufuza pakati pa zolemba zimene zidaperekedwa m’manja mwanga, ndipo ndidapeza mapale awa, amane mudali nkhani iyi yochepa ya aneneri, kuchokera kwa Yakobo kutsika kufikira ulamuliro wa iyi mfimu Benjamini, ndiponso mawu ambiri a Nefi.

4 Ndipo zinthu zimene ziri pa mapale awa n’zokondweretsa ine, chifukwa cha mauneneri akubwera kwa Khristu, ndipo makolo anga adadziwa kuti ambiri mwa iwo adakwaniritsidwa; inde, ndipo inenso ndikudziwa kuti monga zinthu zambiri zidaneneredwa zokhudzana ndi ife kufikira tsiku ili zakwaniritsidwa, ndipo monga ambiri amene akupita kutsogolo kwa tsiku ili adzachitika ndithu—

5 Kotero, ndasankha zinthu izi, kuti ndimalize zolemba zanga pa zimenezi, zimene zotsalira za zolemba zanga ndidzatenga kuchokera ku mapale a Nefi; ndipo sindingalembe gawo zana la zinthu za anthu anga.

6 Koma taonani, ndidzatenga mapale awa, amene ali ndi mauneneri ndi mavumbulutso, ndikuwaphatikiza ndi zotsala za zolemba zanga, pakuti ndi osankhika kwa ine; ndipo ndikudziwa adzakhala osankhika kwa abale anga.

7 Ndipo ndikuchita izi pa cholinga chofunikira; pakuti motere izi zanong’onezedwa kwa ine, molingana ndi ntchito za Mzimu wa Ambuye umene uli mwa ine. Ndipo tsopano, ine sindikudziwa zinthu zonse; koma Ambuye amadziwa zinthu zonse zimene zikubwera; kotero, iye amagwira ntchito mwa ine kuti ndichite molingana ndi chifuniro chake.

8 Ndipo pemphero langa kwa Mulungu ndilokhudzana ndi abale anga, kuti angathe kubweranso ku chidziwitso cha Mulungu, inde, chiwombolo cha Khristu; kuti angathe kukhalanso anthu osangalatsa.

9 Ndipo tsopano ine, Mormoni, ndikupitiriza kumaliza zolemba zanga, zimene ndikutenga ku mapale a Nefi; ndipo ndikuzipanga molingana ndi chidziwitso ndi kumvetsetsa kumene Mulungu wandipatsa ine.

10 Kotero, zidachitika kuti atamaliza Amaleki kupereka mapale awa m’dzanja la mfumu Benjamini, adawatenga ndi kuwaphatikiza ndi mapale ena, amene adali ndi mbiri imene idaperekedwa ndi mafumu, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo kufilira masiku a mfumu Benjamini.

11 Ndipo adaperekedwa kwa mfumu Benjamini, kuchokera ku m’badwo ndi m’badwo kufikira atagwera m’manja mwanga. Ndipo ine, Mormoni, ndikupemphera kwa Mulungu kuti athe kusungidwa kuchokera nthawi ino kupita kutsogolo. Ndipo ndikudziwa kuti adzasungidwa; pakuti pa iwo pali zinthu zazikulu zalembedwa pa iwo, kuchokera pamene anthu anga ndi abale awo adzaweruzidwa pa tsiku lalikulu ndi lomaliza, molingana ndi mawu a Mulungu amene alembedwa.

12 Ndipo tsopano, zokhudzana ndi mfumu Benjamini ameneyu—adali ndi zinazake zamikangano pakati pa anthu ake.

13 Ndipo zidachitikanso kuti magulu ankhondo a Alamani adabwera kuchokera ku dziko la Nefi, kudzamenyana ndi anthu ake. Koma taonani, mfumu Benjamini adasonkhanitsa pamodzi magulu ankhondo ake, ndipo adayima motsutsana nawo; ndipo adamenya ndi mphamvu ya mkono wake, ndi lupanga la Labani.

14 Ndipo mumphamvu ya Ambuye iwo adamenyana ndi adani awo, mpaka adapha zikwizikwi za Alamani. Ndipo zidachitika kuti iwo adamenyana ndi Alamani mpaka adawathamangitsa m’maiko onse a cholowa chawo.

15 Ndipo zidachitika kuti patatha ku dabwera a Khristu abodza, ndipo makamwa awo adatsekedwa, ndipo adalangidwa molingana ndi zolakwa zawo.

16 Ndipo patatha apo padabwera aneneri abodza, ndi alaliki abodza ndi aphunzitsi pakati pa anthu, ndipo onsewa atalangidwa molingana ndi zolakwa zawo; ndipo patatha kukhala mikangano yochuluka ndi kusagwirizana kwambiri kwa Alamani, taonani, zidachitika kuti mfumu Benjamini, ndi thandizo la aneneri oyera amene adali pakati pa anthu ake—

17 Pakuti taonani, mfumu Benjamini adali munthu woyera ndipo adalamulira pa anthu ake mu chilungamo; ndipo adalipo anthu woyera ambiri m’dzikolo, ndipo ankayankhula mawu a Mulungu ndi mphamvu ndi ulamuliro; ndipo adagwiritsa tchito mokuthwa kwambiri chifukwa cha kusamvera kwa anthu—

18 Kotero, ndi thandizo la awa, mfumu Benjamini, pakugwira ntchito ndi mphamvu za mnthupi mwake ndi mphamvu yonse ya moyo wake, ndiponso aneneri, adakhazikitsanso mtendere m’dzikolo.

Print