Malembo Oyera
Alima 16


Mutu 16

Alamani awononga anthu a Amoniha—Zoramu atsogolera Anefi mu kupambana pa Alamani—Alima ndi Amuleki ndi ena ambiri alalika mawu—Iwo aphunzitsa kuti pambuyo pa Chiukitso Chake Khristu adzaonekera kwa Anefi. Mdzaka dza pafupifupi 81–77 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika mu chaka cha khumi ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, pa tsiku la chisanu la mwezi wachiwiri, pamene kudali mtendere waukulu mu dziko la Zarahemula, mopanda kukhala nkhondo kapena mikangano kwa dzaka zingapo, ngakhale kufikira tsiku la chisanu la mwezi wachiwiri mu chaka cha khumi ndi chimodzi, kudali mfuwu wa nkhondo udamveka m’dziko lonselo.

2 Pakuti taonani, ankhondo a Alamani adabwera kudzera mbali ya chipululu, kufika ku malire a dziko, ngakhale mu mzinda wa Amoniha, ndipo adayamba kupha anthu ndi kuwononga mzindawo.

3 Ndipo tsopano zidachitika, Anefi asadadzutse ankhondo okwanira kuti athamangitse iwo kunja kwa dzikolo, iwo adali atawononga anthu amene adali mu mzinda wa Amoniha, ndiponso ena ozungulira m’malire a Nowa, ndi kutenga ena ku ukapolo m’chipululu.

4 Tsopano zidachitika kuti Anefi adali ndi chikhumbo choti alanditse iwo amene adatengedwa ku ukapolo m’chipululu.

5 Kotero, iye adasankhidwa mkulu wa ankhondo pa ankhondo a Anefi, (ndipo dzina lake lidali Zoramu, ndipo adali ndi ana aamuna awiri, Lehi ndi Aha)—tsopano Zoramu ndi ana ake aamuna awiri, podziwa kuti Alima adali mkulu wansembe pa mpingo, ndipo atamva kuti adali ndi mzimu wa uneneri, kotero adapita kwa iye ndi kukhumba kwa iye kuti adziwe ngati Ambuye angalore kuti apite ku chipululu kukasaka abale awo, amene adatengedwa ukapolo ndi Alamani.

6 Ndipo zidachitika kuti Alima adafunsa kwa Ambuye zokhudzana ndi nkhaniyi. Ndipo Alima adabwelera ndi kunena kwa iwo: Taonani, Alamani adzawoloka mtsinje wa Sidoni kumadzulo kwa chipululu, kuchikweza cha malire a dziko la Manti. Ndipo taonani kumeneko mudzakumana nawo, cha ku m’mawa kwa mtsinje wa Sidoni, ndipo kumeneko Ambuye adzapereka kwa inu abale anu amene atengedwa ukapolo ndi Alamani.

7 Ndipo zidachitika kuti Zoramu ndi ana ake aamuna adawoloka mtsinje wa Sidoni, ndi ankhondo awo, ndipo adaguba kupitilira malire a Manti kupita ku chipululu chakumadzulo, chimene chidali ku mbali yakum’mawa kwa mtsinje wa Sidoni.

8 Ndipo adafika kwa ankhondo a Alamani, ndipo Alamani adabalalitsidwa ndi kuthamangitsidwira m’chipululu; ndipo adatenga abale awo amene adatengedwa ukapolo ndi Alamani, ndipo padalibe munthu m’modzi amene adaphedwa amene adatengedwa ukapolo. Ndipo adabweretsedwa ndi abale awo kuti adzatenge maiko awo.

9 Ndipo choncho chidatha chaka cha khumi ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza, Alamani atathamangitsidwa kutuluka mdzikolo, ndipo anthu a Amoniha adawonongedwa; inde, munthu aliyense wa a Amoniha adawonongedwa, ndiponso mzinda wawo waukulu, umene ankati Mulungu sangawuwononge, chifukwa cha kukula kwake.

10 Koma taonani, mu tsiku limodzi udasiyidwa kukhala bwinja; ndipo mitembo yawo idadyedwa ndi agalu ndi zilombo za m’chipululu.

11 Komabe, patatha masiku ambiri mitembo yawo idaunjikidwa pa nkhope ya dziko lapansi, ndipo idakwiliridwa m’manda osazama. Ndipo tsopano chachikulu chidali chifungo mokuti anthu sadapiteko kukatenga dziko la Amoniha kwa dzaka zambiri. Ndipo lidatchedwa Bwinja la Nehori; pakuti adali a chipembedzo cha Neho, amene adaphedwawo ndipo maiko awo adakhalabe mabwinja.

12 Ndipo Alamani sadabwerenso kudzamenyana ndi Anefi mpaka chaka cha khumi ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi. Ndipo motero kwa dzaka dzitatu anthu a Nefi adakhala mu mtendere wopitilira mu dziko lonse.

13 Ndipo Alima ndi Amuleki adapita kukalalikira kulapa kwa anthu mu makachisi awo, ndi m’malo opatulika awo, ndiponso m’ma sunagoge, amene adamangidwa potsatira machitidwe a Ayuda.

14 Ndipo monga ambiri adamva mawu awo, kwa iwo adapereka mawu a Mulungu, mopanda tsankho la munthu, mosalekeza.

15 Ndipo motero Alima ndi Amuleki adapita chitsogolo, ndi enanso ambiri amene adasankhidwa ku ntchitoyo, kukalalika mawu m’dziko lonselo. Ndipo kukhazikitsidwa kwa mpingo kudakhala chizolowezi m’dziko lonselo, m’chigawo chonse kuzungulira, pakati pa anthu onse a Anefi.

16 Ndipo padalibe kusiyana pakati pawo; Ambuye adatsanulira Mzimu wake pa nkhope yadziko lonse kukonzekeretsa maganizo a ana a anthu, kapena kukonzekeretsa mitima yawo kuti ilandire mawu amene akuyenera kudzaphunzitsidwa pakati pawo pa nthawi yakubwera kwake—

17 Kuti iwo asadzalimbitse mitima yawo motsutsana ndi mawu, kuti asadzakhale osakhulupilira, ndi kupita ku chiwonongeko, koma kuti adzalandire mawu ndi chisangalalo, ndipo monga nthambi ilumikizanitsidwa ku mpesa weniweni, kuti iwo adzalowe mu mpumulo wa Ambuye Mulungu wawo.

18 Tsopano ansembe aja amene adapita pakati pa anthu adalalikira motsutsana ndi mabodza onse, ndi chinyengo, ndi kaduka ndi mikangano, dumbo, ndi zachipongwe, ndi kuba, umbanda, kulanda, ndi kuphana, kuchita chigololo, ndi kutayilira kwa mtundu uliwonse, kulira kuti zinthu izi sizikuyenera kukhala choncho.

19 Kugwiritsa ku zinthu zimene zikudza posachedwa; inde, kugwiritsitsa ku kubwera kwa Mwana wa Mulungu, mazunzo ake, ndi imfa, ndinso kuuka kwa akufa.

20 Ndipo anthu ambiri adafunsa zokhudzana ndi malo amene Mwana wa Mulungu adzabwere; ndipo adaphunzitsidwa kuti iye adzaonekera kwa iwo pambuyo pa chiukitso chake; ndipo ichi anthu adachimva ndi chisangalalo chachikulu ndi kukondwera.

21 Ndipo tsopano mpingo utakhazikitsidwa m’dziko lonselo—atagonjetsa mdyerekezi, ndipo mawu a Mulungu atalalikidwa mu chiyero chake mu dziko lonse, ndipo Ambuye adatsanulira madalitso ake kwa anthu—motero chidatha chaka chakhumi ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

Print