Mutu 63
Shibuloni ndipo kenako Helamani atenga zolemba zopatulika—Anefi ambiri apita ku dziko la kumpoto—Hagoti amanga ngalawa, zimene zimayenda mu nyanja yakumadzulo—Moroniha agonjetsa Alamani mu nkhondo. Mdzaka dza pafupifupi 56–52 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo zidachitika kuti kumayambiliro kwa chaka cha makumi atatu ndi chisanu n’chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, kuti Shibuloni adatenga zinthu zopatulika zija zimene zidaperekedwa kwa Helamani ndi Alima.
2 Ndipo iye adali munthu wolungama, ndipo iye adayenda mowongoka pamaso pa Mulungu; ndipo ankatsata kuchita zabwino mosalekeza, kusunga malamulo a Ambuye Mulungu wake; ndiponso m’bale wake ankachita momwemo.
3 Ndipo zidachitika kuti Moroni adamwaliranso. Ndipo motero chidatha chaka cha makumi atatu ndi chisanu n’chimodzi cha ulamuliro wa oweruza.
4 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha makumi atatu ndi chisanu ndi chiwiri cha ulamuliro wa oweruza, kudali gulu lalikulu la anthu, ngakhale anthu wokwanira zikwi zisanu ndi mazana anayi, ndi azikazi awo ndi ana awo, adachoka mu dziko la Zarahemula kupita ku dziko limene lidali chakumpoto.
5 Ndipo zidachitika kuti Hagoti, iye okhala munthu wachidwi kwambiri, kotero adapita ndi kumanga ngalawa yaikulu ndithu, ku malire a dziko la Chuluka, pafupi ndi dziko la Bwinja, ndipo adaikokera m’nyanja yakumadzulo, kudzera pa lowe lopapatiza limene limapititsa ku dziko la kumpoto.
6 Ndipo taonani, kudali ambiri mwa Anefi amene adalowa mkatimo ndipo adayenda nawo ndi chakudya chambiri, ndiponso azimayi ambiri ndi ana, ndipo adatenga njira yakumpoto. Ndipo kotero chidatha chaka cha makumi atatu ndi chisanu n’chiwiri.
7 Ndipo m’chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi zitatu, munthuyu adamanga ngalawa zina. Ndipo ngalawa yoyamba idabweleranso, ndipo anthu ambiri adalowamo; ndipo adatenga katundu wambiri, ndi kuyamba ulendo kupita ku dziko lakumpoto.
8 Ndipo zidachitika kuti sipadamvekenso konse za iwo. Ndipo tikuganiza kuti iwo adamira mkuya kwa nyanja. Ndipo zidachitika kuti ngalawa ina idayambanso ulendo; ndipo komwe idalowera sitidziwa.
9 Ndipo zidachitika kuti mu chaka chimenechi kudali anthu ambiri amene adapita ku dziko lakumpoto. Ndipo kotero chidatha chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi zitatu.
10 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi zinayi cha ulamuliro wa oweruza, Shibuloni adamwaliranso, ndipo Koriyantoni adali atapita ku dziko lakumpoto mu ngalawa, kutenga zakudya za anthu amene adapita ku dziko limenelo.
11 Kotero kudakhala kofunikira kwambiri kuti Shibuloni apereke zinthu zopatulikazo, asadamwalire, kwa mwana wa Helamani, amene ankatchedwa Helamani, potchulidwa potsata dzina la atate ake.
12 Tsopano taonani, zozokotedwa zonsezo zimene zidali ndi Helamani zidalembedwa ndi kutumizidwa pakati pa ana a anthu kuzungulira dziko lonselo, kupatula zigawo zimene zidalamulidwa ndi Alima kuti zisadapititsidwe.
13 Komabe, zinthu izi zidali zoti zisungidwe mopatulika, ndi kuperekedwa kuchokera ku m’badwo wina kupita ku wina; kotero, mu chaka chimenechi, zidaperekedwa kwa Helamani, asadamwalire Shibuloni.
14 Ndipo zidachitika kuti m’chaka chimenechi kudali ogalukira ena amene adapita kwa Alamani; ndipo adautsanso mkwiyo motsutsana ndi Anefi.
15 Ndiponso mu chaka chomwechi iwo adabwera ndi ankhondo ochuluka kudzamenyana ndi anthu a Moroniha, kapena kutsutsana ndi ankhondo a Moroniha, mumene iwo adamenyedwa ndi kuthamangitsidwanso ku maiko awo, atagonjetsedwa.
16 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi atatu ndi zisanu ndi zinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.
17 Ndipo motero idatha nkhani ya Alima, ndi Helamani mwana wake, ndiponso Shibuloni, amene adali mwana wake.