Malembo Oyera
Alima 5


Mawu amene Alima, Mkulu Wansembe molingana ndi dongosolo loyera la Mulungu, operekedwa kwa anthu m’mizinda ndi m’midzi mwawo m’dziko lonselo.

Kuyambira ndi mutu 5.

Mutu 5

Kuti apulumuke, anthu akuyenera kulapa ndi kusunga malamulo, kubadwanso mwatsopano, kuyeretsa zovala zawo mu mwazi wa Khristu, kudzichipetsa ndi kudzivula okha kunyada ndi kaduka, ndi kuchita ntchito zolungama—M’busa wabwino aitana anthu ake—Iwo amene amachita ntchito zoipa ndi ana a mdyerekezi—Alima achitira umboni za choonadi cha chiphunzitso chake ndipo alamula anthu kuti alape—Maina a olungama adzalembedwa mu buku la moyo. Mdzaka dza pafupifupi 83 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidachitika kuti Alima adayamba kugawa mawu a Mulungu kwa anthu, koyamba mdziko la Zarahemula, ndipo kuchokera kumeneko kuzungulira dziko lonselo.

2 Ndipo awa ndi mawu amene iye adayankhula kwa anthu a mu mpingo umene udakhazikitsidwa mu mzinda wa Zarahemula molingana ndi zolemba zake zomwe nati:

3 Ine, Alima, nditapatulidwa ndi atate anga, Alima, kuti ndikhale mkulu wansembe pa mpingo wa Mulungu, iwo okhala ndi mphamvu ndi ulamuliro ochokera kwa Mulungu kuti achite zinthu izi, taonani, ndikunena kwa inu kuti iwo adayamba kukhazikitsa mpingo mu dziko limene lidali m’malire ndi Nefi; inde, dziko limene linkatchedwa dziko la Mormoni; inde, ndipo iwo adabatiza abale awo m’madzi a Mormoni.

4 Ndipo taonani, ndikunena kwa inu, iwo adapulumutsidwa kuchoka m’manja mwa anthu a mfumu Nowa, mwa chifundo ndi mphamvu ya Mulungu.

5 Ndipo taonani, atatha izo, adabweretsedwa mu ukapolo m’manja mwa Alamani m’chipululu; inde, ndikunena kwa inu, iwo adabweretsedwa mu ukapolo, ndipo kachiwiri Ambuye adawawombola iwo kuchokera mu ukapolo mwa mphamvu ya mawu ake; ndipo ife tidabweretsedwa mu dziko lino, ndipo kuno tidayamba kukhazikitsa mpingo wa Mulungu kuzungulira m’dziko munonso.

6 ndipo tsopano taonani, ndikunena kwa inu, abale anga, inu amene muli mu mpingo uwu, kodi mwasunga mokwanira m’kukumbukira ukapolo wa makolo anu? Inde, ndipo kodi inu mwasunga mokwanira m’kukumbukira chifundo chake ndi chipiliro chake kwa iwo? Ndipo kuonjezera apo, kodi inu mwasunga mokwanira m’kukumbukira kuti iye wapulumutsa miyoyo yawo kuchokera ku gahena?

7 Taonani, iye adasintha mitima yawo; inde, iye adawadzutsa iwo ku tulo tozama, ndipo adadzuka kwa Mulungu. Taonani, iwo adali pakati pa mdima, komabe, miyoyo yawo idali yolumikizana ndi kuunika kwa mawu wosatha; inde, iwo adazungulilidwa ndi nsinga za imfa, ndi maunyolo a gahena, ndipo chiwonongeko chosatha chinkawayembekezera iwo.

8 Ndipo tsopano ndikukufunsani inu, abale anga, kodi adawonongedwa? Taonani, ndinena kwa inu, Ayi, sadawonongedwe.

9 Ndipo kachiwiri ndikufunsa, kodi nsinga za imfa zidadulidwa, ndi maunyolo a gahena amene adawazinga iwo mozungulira, kodi adamasulidwa? Ndikunena ndi inu, Inde, iwo adamasulidwa, ndipo miyoyo yawo idakula, ndipo adayimba nyimbo ya chikondi cha kuwombola. Ndipo ndikunena kwa inu kuti iwo apulumutsidwa.

10 Ndipo tsopano ndikufunsani inu kodi ndi pa ndondomeko zotani zomwe iwo adapulumutsidwira? Inde, ndi pa gwero lanji adali nalo kukhala ndi chiyembekezo cha chipulumutso? Kodi n’chiyani chomwe chili chochititsa cha iwo kuti amasulidwe ku nsinga za imfa, inde, ndiponso ku maunyolo a gahena?

11 Taonani, ine ndikhoza kukuuzani inu—kodi atate anga Alima sadakhulupilire mu mawu amene adaperekedwa ndi pakamwa pa Abinadi? Ndipo kodi iye sadali mneneri oyera? Kodi iye sadayankhule mawu a Mulungu, ndipo atate anga Alima adawakhulupilira iwo?

12 Ndipo molingana ndi chikhulupiliro chawo kudali kusintha kwakukulu kudachitika mu mtima mwawo. Taonani ndikunena kwa inu kuti izi zonsezi ndi zoona.

13 Ndipo taonani, iwo adalalikira mawu kwa makolo anu, ndipo kusintha kwakukulu kudachitikanso m’mitima yawo, ndipo adadzichepetsa ndi kuika chikhulupiliro chawo mwa Mulungu woona ndi wamoyo. Ndipo taonani, adali okhulupirika kufikira kumapeto, kotero adapulumutsidwa.

14 Ndipo tsopano taonani, Ndikufunsani kwa inu, abale anga a mumpingo, kodi mudabadwa muuzimu mwa Mulungu? Kodi mwalandira chifaniziro chake m’maonekedwe anu? Kodi mudakumanako ndi kusintha kwakukulu kumeneku m’mitima mwanu?

15 Kodi mumaika chikhulupiliro mu chiwombolo cha iye amene adakulengani inu? Kodi mukuyang’ana chitsogolo ndi diso la chikhulupiliro, ndi kuona thupi la chivundili likuukitsidwa ku moyo wosafa, ndi chivundi ichi chikuukitsidwa m’kusavunda, kudzaima pamaso pa Mulungu kuweruzidwa malingana ndi ntchito zimene lachita thupi la chivundi?

16 Ndikunena kwa inu, mungadziganizire kwa inu nokha kuti mukumva mawu a Ambuye, akunena kwa inu mutsikulo: Bwerani kwa ine inu odala, pakuti taonani, ntchito zanu zakhala ntchito zolungama pa nkhope ya dziko lapansi?

17 Kapena kodi mukudziganizira kwa inu nokha kuti munganame kwa Ambuye mutsikulo, ndi kunena—Ambuye, ntchito zathu zakhala ntchito zolungama pa nkhope yadziko lapansi—ndipo kuti iye adzakupulumutsani inu?

18 Kapena mwinamwake, kodi mungadziganizire nokha kubweretsedwa pa bwalo lamilandu la Mulungu ndi miyoyo yanu yodzadzidwa ndi kulakwa ndi chisoni, kukhala ndi chikumbutso cha zolakwa zanu zonse, inde, kukumbukira kwa mngwiro kuipa kwanu konse, inde, kukumbukira kuti inu mwanyoza malamulo a Mulungu?

19 Ndikunena kwa inu, kodi mungayang’ane kwa Mulungu pa tsiku limenelo ndi mtima oyera ndi manja oyera? Ndikunena kwa inu, kodi mungayang’ane m’mwamba, n’kukhala ndi chifanizo cha Mulungu chozokotedwa pa maonekedwe anu?

20 Ndikunena kwa inu, kodi mungaganize zopulumutsidwa pamene mwadzipereka nokha kukhala otsatira a mdyerekezi?

21 Ndinena kwa inu, mudzadziwa pa tsikulo kuti inu simungapulumutsidwe; pakuti palibe munthu aliyense angathe kupulumutsidwa pokhapokha zovala zake zayeretsedwa; inde zovala zake zikuyenera kuyeretsedwa kufikira zitayeretsedwa ku litsiro lirilonse, kudzera mu mwazi wa iye amene adayankhulidwa ndi makolo athu, amene adzabwere kudzawombola anthu ake ku machimo awo.

22 Ndipo tsopano ine ndikufunsa kwa inu, abale anga, kodi aliyense wa inu adzamva bwanji, ngati mudzaima pamaso pa bwalo lamilandu la Mulungu, muli ndi zovala zanu zodetsedwa ndi mwazi ndi zonyansa zamitundu yonse? Taonani, kodi zinthu izi zidzachitira umboni wanji kwa inu?

23 Taonani kodi sizidzachitira umboni kuti inu ndi akupha, inde, ndiponso kuti ndinu olakwa pa zoipa zamitundu yonse?

24 Taonani, abale anga, kodi mukuganiza kuti munthu otereyo akhonza kudzakhala ndi malo okhala pansi mu ufumu wa Mulungu, ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, ndiponso aneneri oyera onse, amene zovala zawo zayeretsedwa ndi zopanda banga, angwiro ndi oyera?

25 Ndikunena kwa inu, Ayi; pokhapokha mutamupanga Mlengi wathu kukhala wabodza kuyambira pachiyambi, kapena kuganiza kuti iye ndi wabodza kuyambira pa chiyambi, inu simungaganize kuti oterewo akhonza kukhala ndi malo mu ufumu wa kumwamba; koma iwo adzaponyedwa kunja chifukwa iwo ndi ana a ufumu wa mdyerekezi.

26 Ndipo tsopano taonani, ndikunena kwa inu, abale anga, ngati mwamva kusintha kwa mtima, ndipo ngati mudamva kuti muyimbe nyimbo ya chikondi chowombola, ndingakufunseni, kodi mungamve choncho tsopano?

27 Kodi mudayenda, modzisunga nokha osalakwa pamaso pa Mulungu? Kodi mukhonza kunena, ngati mwaitanidwa kuti mufe pa nthawi ino, mwa inu nokha, kuti inu mwadzichepetsa kwathunthu? Kuti zovala zanu zayeretsedwa ndi kupangidwa zoyera kudzera mu mwazi wa Khristu, amene adzabwere kudzawombola anthu ake kumachimo awo?

28 Taonani, kodi mwavula kunyada? Ndikunena kwa inu, ngati simudatero, simuli okonzeka kukumana ndi Mulungu. Taonani mukuyenera kukonzekera mwamsanga; pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira, ndipo otereyu alibe moyo wamuyaya.

29 Taonani, ndikuti, alipo wina mwa inu amene sadavulidwe nsanje? Ndikunena kwa inu kuti otereyo sadakonzeke; ndipo ndikadakonda kuti akonzekere mwamsanga, chifukwa ora iri pafupi, ndipo iye sakudziwa pamene nthawiyo idzafike; pakuti otere sadzapezeka osalakwa.

30 Ndipo kachiwiri ndinena kwa inu, kodi alipo wina pakati pa inu amene amatonza m’bale wake, kapena kumuwunjikira mazunzo?

31 Tsoka kwa m’modzi otereyo, chifukwa iye sadakonzekere, ndipo nthawi yayandikira yoti alape kapena iye sangapulumutsidwe.

32 Inde, ngakhale tsoka kwa inu nonse ochita mphulupulu; lapani, lapani, pakuti Ambuye Mulungu wayankhula ichi!

33 Taonani, iye watumiza uthenga kwa anthu onse, pakuti mikono ya chifundo yatambasulidwa kwa iwo, ndipo iye wati: Lapani, ndipo ine ndidzakulandirani inu.

34 Inde, iye wati: Bwerani kwa ine ndipo mudzadye chipatso cha mtengo wa moyo; inde, mudzadye ndi kumwa za mkate ndi madzi a moyo kwaulele.

35 Inde, bwerani kwa ine ndipo bweretsani ntchito zolungama, ndipo inu simudzadulidwa ndi kuponyedwa m’moto—

36 Pakuti taonani, nthawi yayandikira yakuti aliyense amene wosabala zipatso zabwino, kapena aliyense amene sachita ntchito zolungama, yemweyo ali ndi chifukwa cholilira ndi chisoni.

37 O ogwira ntchito zamphulupulu; inu amene muli odzikuza mu zinthu zachabechabe za dziko lapansi, inu amene mudadzinenera kuti mumadziwa njira zolungama koma mudasochera, ngati nkhosa zopanda m’busa, pakusaona kuti m’busa wakuitanani inu ndipo akuitanabe kwa inu, koma inu simumvera mawu ake!

38 Taonani, ndikunena ndi inu, kuti m’busa wabwino akukuitanani inu; inde, ndipo mu dzina lake lomwe iye wakuitanani inu, limene ndi dzina la Khristu; ndipo ngati inu simudzamvera kwa mawu a m’busa wabwino, ku dzina limene inu mwaitanidwira, taonani, inu simuli nkhosa za m’busa wabwino.

39 Ndipo tsopano ngati simuli nkhosa za m’busa wabwino, kodi muli a khola lanji? Taonani, ndikunena kwa inu, kuti mdyerekezi ndiye m’busa wanu, ndipo inu muli a khola lake; ndipo tsopano, angakane izi ndani? Taonani, ndikunena kwa inu, aliyense amene akana izi ndi wabodza ndipo ndi mwana wa mdyerekezi.

40 Pakuti ndikunena kwa inu kuti chilichonse chili chabwino chimachokera kwa Mulungu, ndipo chilichonse choipa chimachokera kwa mdyerekezi.

41 Kotero, ngati munthu abweretsa ntchito zabwino iye amamvera kwa mawu a m’busa wabwino, ndipo iye amatsatira iye; koma aliyense amene amabweretsa ntchito zoipa, yemweyonso amakhala mwana wa mdyerekezi, chifukwa amamvera mawu ake, ndipo amamutsatira iye.

42 Ndipo aliyense amene achita izi akuyenera kulandira mphotho yake kwa iye; kotero, mphotho yake iye amalandira imfa, monga mwa zinthu zokhudzana ndi kulungama, kukhala okufa ku ntchito zonse zabwino.

43 Ndipo tsopano, abale anga, ndikufuna kuti mundimve, chifukwa ndikuyankhula mu mphamvu za moyo wanga; pakuti taonani, ndayankhula kwa inu momveka kuti simungalakwitse, kapena ndayankhula molingana ndi malamulo a Mulungu.

44 Pakuti ndaitanidwa kuti ndiyankhule monga momwemu, molingana ndi dongosolo loyera la Mulungu, limene liri mwa Khristu Yesu; inde, ndalamulidwa kuti ndiime ndi kuchitira umboni kwa anthu awa za zinthu zimene zidayankhulidwa ndi makolo athu zokhudzana ndi zinthu zomwe ziri nkudza.

45 Ndipo izi si zonse. Kodi simukuganiza kuti ine ndikudziwa zinthu izi ndekha? Taonani, ndikuchitira umboni kwa inu kuti ndikudziwa kuti zinthu izi zimene ine ndayankhula ndi zoona. Ndipo kodi mukuganiza kuti ndikudziwa bwanji za chitsimikizo chake?

46 Taonani, ndikunena kwa inu kuti zazindikiritsidwa kwa ine mwa Mzimu Oyera wa Mulungu. Taonani, ndasala kudya ndi kupemphera masiku ambiri kuti ndidziwe zinthu izi mwa ndekha. Ndipo tsopano ndikudziwa kwa ine ndekha kuti ndi zoona; pakuti Ambuye Mulungu waziwonetsera izo kwa ine mwa Mzimu wake Woyera; ndipo uwu ndi mzimu wa chibvumbulutso umene uli mwa ine.

47 Ndipo moonjezera, ndikunena kwa inu kuti motero zabvumbulitsidwa kwa ine, kuti mawu amene adayankhulidwa ndi makolo athu ndi oona, ngakhale motero molingana ndi mzimu wa uneneri umene uli mwa ine, umene ulinso mwa kuwonetseredwa kwa Mzimu wa Mulungu.

48 Ndikunena kwa inu, kuti ndikudziwa mwa ndekha kuti chilichonse chomwe ndidzanena kwa inu, chokhudzana ndi zomwe zirinkudza, ndi zoona; ndipo ndikunena kwa inu, kuti ndikudziwa kuti Yesu Khristu adzabwera, inde, Mwana, Wobadwa yekha wa Atate, odzadza ndi chisomo ndi chifundo ndi chilungamo. Ndipo taonani, ndi iye amene abwera kudzachotsa machimo a dziko lapansi, inde, machimo a munthu aliyense amene akhulupilira mokhazikika mu dzina lake.

49 Ndipo tsopano ndikunena kwa inu kuti ili ndilo dongosolo limene ine ndayitanidwira, inde, kuti ndilalikire kwa abale anga okondedwa, inde, ndi kwa aliyense amene akukhala mu dzikoli; inde kulalikira kwa onse, okalamba ndi achichepere omwe, akapolo ndi aufulu omwe; inde, ndikunena ndi inu achikulire, ndi aunsinkhu wapakati, ndi m’badwo wa achinyamata; inde, kufuula kwa iwo akuyenera kuti alape ndi kubadwanso mwatsopano.

50 Inde, atero Mzimu; Lapani, nonse a kumalekezero a dziko lapansi, chifukwa ufumu wa Kumwamba wayandikira, inde, Mwana wa Mulungu akubwera mu ulemelero wake, mu dzitho zake, mu ukulu wake, mphamvu ndi ulamuliro. Inde, abale anga okondedwa, ndinena kwa inu, kuti Mzimu ukuti: Taonani ulemelero wa Mfumu ya dziko lonse lapansi; ndiponso Mfumu ya kumwamba posachedwa idzawala pakati pa ana onse a anthu.

51 Ndiponso Mzimu wati kwa ine, inde, kufuula kwa ine ndi mawu amphamvu, nati: Pita nati kwa anthu awa—Lapani, pakuti pokhapokha inu mutalapa simungalandire ufumu wa kumwamba.

52 Ndipo kachiwiri ndikunena kwa inu, Mzimu wati: Taonani, nkhwangwa yaikidwa pa mtsitsi wa mtengo; kotero mtengo uliwonse osabala chipatso chabwino udzadulidwa ndi kuponyedwa m’moto, inde, moto umene sungathe kuthetsedwa, ngakhale moto osazimitsika. Taonani, ndipo kumbukirani, Oyerayo wayankhula ichi.

53 Ndipo tsopano abale anga okondedwa, ndinena kwa inu, kodi mungatsutsane ndi zonena izi; inde, kodi mungaziyike pambali zinthu izi, ndi kupondereza Oyerayo pansi pa mapazi anu; inde, kodi mungadzikweze m’kunyada kwa mitima yanu; inde, kodi mudzapitirizabe kuvala zovala zamtengo wapatali ndi kuika mitima yanu pa zinthu zachabe za dziko lapansi, pa chuma chanu?

54 Inde, kodi mudzapitiriza kuganiza kuti ndinu abwino kuposa wina; inde, kodi mudzapitiriza kuzunza abale anu, amene adzichepetsa okha ndi kuyenda motsata dongosolo loyera la Mulungu, limene iwo abweretsedwa nalo mu mpingo, atayeretsedwa ndi Mzimu Woyera, ndi kubweretsa ntchito zabwino zimene ndizofunikira polapa—

55 Inde, ndipo kodi mudzapitiriza kutembenuzira misana yanu anthu osauka, ndi osowa, ndi kuwamana chuma chanu?

56 Ndipo pomaliza, inu nonse amene mudzapitiriza m’zoipa zanu, ndikunena kwa inu kuti awa ndi iwo amene adzadulidwe ndi kuponyedwa m’moto pokhapokha atalapa mofulumira.

57 Ndipo tsopano ndikunena kwa inu, nonse amene mukufuna kutsata mawu a m’busa wabwino, tulukani kwa oipayo, ndipo patukani, ndipo musagwire zinthu zawo zodetsedwa; ndipo taonani, maina awo adzafufutidwa, kuti maina a oipa sadzawerengedwa pamodzi ndi maina a olungama, kuti mawu a Mulungu akwanilitsidwe, amene amati: Maina a oipa sadzasakanizidwa ndi maina a anthu anga.

58 Pakuti maina a olungama adzalembedwa mu buku la moyo, ndipo kwa iwo ndidzawapatsa cholowa pa dzanja langa lamanja. Ndipo tsopano, abale anga, munenapo chiyani motsutsana ndi izi? Ndinena kwa inu, ngati muyankhula motsutsana ndi izi, zilibe kanthu, pakuti mawu a Mulungu akuyenera kukwaniritsidwa.

59 Pakuti ndi m’busa wanji ali pakati panu okhala ndi nkhosa zambiri koma osaziyang’anira, kuti nkhandwe zisalowe ndi kuwononga nkhosa zake? Ndipo taonani, ngati nkhandwe ilowa mu nkhosa zake kodi iye sadzayithamangitsa? Inde, ndipo pamapeto pake, ngati angathe, adzaiwononga.

60 Ndipo tsopano ndikunena kwa inu kuti m’busa wabwino akukuitanani inu; ndipo ngati inu mudzamvera mawu ake iye adzakubweretsani inu mu khola lake, ndipo inu ndinu nkhosa zake; ndipo akukulamulani inu kuti musalore nkhandwe yolusa kuti ilowe pakati panu, kuti musawonongedwe.

61 Ndipo tsopano, ine, Alima, ndikukulamulani inu muchiyankhulo cha iye amene wandilamula ine, kuti musamale kuchita mawu amene ine ndiyankhula kwa inu.

62 Ndikuyankhula mwa njira ya lamulo kwa inu amene muli a mpingo; ndi kwa aliyense amene sali mu mpingo mwa kukuitanani, nati: Bwerani ndi kudzabatizidwa mwa kulapa, kuti inunso mukakhale okudya chipatso cha mtengo wa moyo.

Print