Malembo Oyera
Alima 15


Mutu 15

Alima ndi Amuleki apita ku Sidomu ndipo akhazikitsa mpingo—Alima achiritsa Zeziromu, amene walowa mu Mpingo—Ambiri abatizidwa, ndipo Mpingo uchita bwino—Alima ndi Amuleki apita ku Zarahemula. Mdzaka dza pafupifupi 81 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti Alima ndi Amuleki adalamulidwa kuti achoke mu mzinda umenewo; ndipo iwo adachoka, ndi kutuluka ngakhale mu mzinda wa Sidomu; ndipo taonani, kumeneko adapeza anthu onse amene adachoka kutuluka mu mzinda wa Amoniha, amene adathamangitsidwa ndi kugendedwa, chifukwa iwo adakhulupiIira mu mawu a Alima.

2 Ndipo iwo adakamba kwa iwo zonse zimene zidachitika kwa akazi ndi ana awo, ndiponso zokhudzana ndi iwo eni, ndi za mphamvu yawo ya chipulumutso.

3 Ndiponso Zeziromu adagona akudwala ku Sidomu, ndi kutentha thupi, kumene kudachitika chifukwa cha masautso aakulu m’maganizo mwake pa nkhani ya kusaweruzika kwake, pakuti iye adaganiza kuti Alima ndi Amuleki adamwalira; ndipo iye adaganiza kuti adaphedwa chifukwa cha mphulupulu zake. Ndipo tchimo lalikulu ili, ndi machimo ake ena ambiri, adamukhumudwitsa m’maganizo ake mpaka adakhala owawa kwambiri, opanda chipulumutso; kotero iye adayamba kuwotchedwa ndi kutentha kwakukulu.

4 Tsopano, pamene adamva kuti Alima ndi Amuleki adali mu dziko la Sidomu, mtima wake udayamba kukhala olimbitsika; ndipo pomwepo iye adatumiza uthenga kwa iwo, kufuna kuti iwo abwere kwa iye.

5 Ndipo zidachitika kuti iwo adapita nthawi yomweyo, kumvera uthenga umene iye adatumiza kwa iwo, ndipo adalowa m’nyumba ya Zeziromu; ndipo adam’peza iye ali pa kama lake, akudwala, atalefuka ndi kutentha thupi; ndipo maganizo ake adali owawidwa chifukwa cha zoipa zake, ndipo pamene iye adawaona iwo adatambasula dzanja lake, ndi kuwapempha iwo kuti amuchiritse.

6 Ndipo zidachitika kuti Alima adati kwa iye, kumugwira iye pa dzanja; Kodi ukukhulupilira mu mphamvu ya Khristu ku chipulumutso?

7 Ndipo iye adayankha nati: Inde, ndikukhulupilira mawu onse amene inu mwaphunzitsa.

8 Ndipo Alima adati: Ngati iwe ukukhulupilira mu chiwombolo cha Khristu ukhonza kuchiritsidwa.

9 Ndipo iye adati: Inde, ndikukhulupilira monga mwa mawu anu.

10 Ndipo kenako Alima adafuula kwa Ambuye, nati: O Ambuye Mulungu wathu, chitirani chifundo kwa munthu uyu, ndipo muchiritseni monga mwa chikhulupiliro chake chimene chiri mwa Khristu.

11 Ndipo pemene Alima adanena mawu awa, Zeziromu adalumpha pa mapazi ake, ndipo adayamba kuyenda; ndipo izi zidachitika modabwitsa kwambiri anthu onse; ndipo chidziwitso cha izi chidafikira konse mu dziko lonse la Sidomu.

12 Ndipo Alima adabatiza Zeziromu kwa Ambuye; ndipo adayamba kuyambira nthawi imeneyo kulalikira kwa anthu.

13 Ndipo Alima adakhazikitsa mpingo mu dziko la Sidomu, ndipo adapatula ansembe ndi aphunzitsi m’dzikolo, kuti abatize kwa Ambuye aliyense amene adali ndi chikhumbo choti abatizidwe.

14 Ndipo zidachitika kuti iwo adalipo ambiri; pakuti adakhamukira kuchokera mu madera onse ozungulira Sidomu, ndipo adabatizidwa.

15 Koma ponena za anthu amene adali mu dziko la Amoniha, iwo adakhalabe anthu owuma‑mtima ndi anthu osamvera; ndipo sadalape machimo awo, kupereka mphamvu za Alima ndi Amuleki kwa mdyerekezi; pakuti adali achipembedzo cha Neho, ndipo sadakhulupilire mu zakulapa kwa machimo awo.

16 Ndipo zidachitika kuti Alima ndi Amuleki, Amuleki atasiya golide wake yense, ndi siliva, ndi zinthu zake zonse zamtengo wapatali, zimene zidali mu dziko la Amoniha, chifukwa cha mawu a Mulungu, iye atakanidwa ndi iwo amene poyamba adali anzake ndiponso ndi atate ake ndi abale ake;

17 Kotero, Alima atatha kukhazikitsa mpingo ku Sidomu, poona kukonza kwakukulu, inde, poona kuti anthu adakonzedwa mokhudzana ndi kunyada kwa mitima yawo, ndi kuyamba kudzichepetsa okha pamaso pa Mulungu, ndipo adayamba kusonkhana pamodzi m’malo awo opatulika kuti apembedze Mulungu pa guwa, kuyang’anira ndi kupemphera mosalekeza, kuti apulumutsidwe kwa Satana, ndi ku imfa, ndi kuchiwonongeko—

18 Tsopano monga ndanenera, Alima ataona zinthu zonsezi, kotero adatenga Amuleki ndi kubwera ku dziko la Zarahemula, ndi kumutenga iye kunyumba kwake, ndipo adamtumikira iye mu masautso ake, ndi kumulimbikitsa iye mwa Ambuye.

19 Ndipo motero chidatha chaka cha khumi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.