Malembo Oyera
Alima 9


Mawu a Alima, ndiponso mawu a Amuleki, amene adapelekedwa kwa anthu amene adali mu dziko la Amoniha. Ndiponso aponyedwa mu ndende, ndi kuwomboledwa mwa mphamvu yozwizwitsa ya Mulungu imene idali mwa iwo, molingana ndi zolemba za Alima.

Yophatikiza mitu 9 mpaka 14.

Mutu 9

Alima alamula anthu a Amoniha kuti alape—Ambuye adzachitira chifundo Alamani m’masiku omaliza—Ngati Anefi asiya kuwala, adzawonongedwa ndi Alamani—Mwana wa Mulungu adzabwera posachedwa—Iye adzawombola iwo amene alapa, abatizidwa, ndi kukhala ndi chikhulupiliro mu dzina lake. Mdzaka dza pafupifupi 82 Yesu asadabadwe.

1 Ndiponso, ine, Alima, nditalamulidwa ndi Mulungu kuti ndimutenge Amuleki ndipo tipite ndi kukalalikiranso kwa anthu awa, kapena anthu amene adali mu mzinda wa Amoniha, zidachitika pamene ine ndidayamba kulalika kwa iwo, adayamba kulimbana nane, nati:

2 Kodi iwe ndi ndani? Ukuganiza kuti ife tingakhulupilire umboni wa munthu m’modzi, ngakhale atalalika kwa ife kuti dziko lapansi lidzatha?

3 Tsopano iwo sadamvetse mawu amene amayankhula; pakuti sadadziwe kuti dziko lapansi lidzatha.

4 Ndipo iwo adatinso: Ife sitidzakhulupilira mawu ako ngati iwe utanenere kuti mzinda waukulu uno udzawonongedwa mu tsiku limodzi.

5 Tsopano iwo sadadziwe kuti Mulungu akhonza kuchita ntchito zodabwitsa zoterozo, pakuti iwo adali anthu a mitima-yolimba ndi osamvera.

6 Ndipo iwo adati: Mulungu ndi ndani, kuti satumiza ulamuliro winanso woposa munthu m’modzi pakati pa anthu awa, kuti alalikire kwa iwo choonadi cha zinthu zazikulu ndi zodabwitsa zoterozo?

7 Ndipo adaimilira kuti aike manja awo pa ine; koma taonani, iwo sadatero. Ndipo ndidaima molimba mtima kuti ndilalike kwa iwo, inde, ndidachitira umboni molimba mtima kwa iwo, nati:

8 Taonani, O inu oipa ndi m’badwo wopotoka mwaiwala bwanji miyambo ya makolo anu; inde, mwaiwala mwachangu bwanji malamulo a Mulungu?

9 Kodi inu simukukumbukira kuti atate athu, Lehi, adabweretsedwa kuchokera ku Yerusalemu ndi dzanja la Mulungu? Kodi inu simukukumbukira kuti iwo wonse adatsogoleledwa ndi iye kudutsa m’chipululu?

10 Ndipo kodi inu mwaiwala posachedwapa kuti ndi nthawi zingati iye adawombola makolo athu m’manja mwa adani awo, ndi kuwasunga iwo kuti asawonongedwe, ngakhale ndi manja a abale awo omwe?

11 Inde, ndipo ngati kukadapanda kukhala mphamvu yake yosayerekezeka, ndi chifundo chake, ndi kuleza mtima kwake kwa ife, tikadadulidwa mosapeweka kuchoka pankhope yadziko lapansi tisadafike m’nyengo ya nthawi ino, ndipo mwina tikadakhazikidwa mu mkhalidwe wa chisoni ndi tsoka losatha.

12 Taonani, tsopano ndinena kwa inu kuti iye wakulamulani inu kuti mulape, ndipo pokhapokha mulape, inu simungathe kulandira ufumu wa Mulungu. Koma taonani, izi sizokhazi—iye wakulamulani inu kuti mulape, kapena adzakuwonongani kotheratu kuchoka pankhope ya dziko lapansi, inde, adzakuyenderani mu mkwiyo wake, ndipo mumkwiyo wake oopsya sadzayang’ana kumbali.

13 Taonani, kodi inu simukukumbukira mawu amene adayankhula kwa Lehi, kunena kuti: Pamene inu mudzasunga malamulo anga, mudzachita bwino m’dziko? Ndiponso kwanenedwa kuti: Pamene simudzasunga malamulo anga mudzadulidwa kuchoka pamaso pa Ambuye.

14 Tsopano ndikufuna kuti mukumbukire, kuti motero ngati Alamani sadasunge malamulo a Mulungu, iwo adulidwa kuchoka pamaso pa Ambuye. Tsopano tikuwona kuti mawu a Ambuye adatsimikizika mu chinthu ichi, ndipo Alamani adadulidwa kuchoka pamaso pake, kuyambira pa chiyambi cha zolakwitsfa zawo m’dzikomo.

15 Komabe ndikunena kwa inu, kuti chidzakhala chopilirika kwa iwo pa tsiku la chiweruzo kuposa kwa inu, ngati mukhalabe mu machimo anu, inde, ndipo ngakhale chopilirika kwambiri kwa iwo mu moyo uno kuposa kwa inu pokhapokha mutalapa.

16 Pakuti malonjezano alipo ambiri amene aperekedwa kwa Alamani; pakuti ndi chifukwa cha miyambo ya makolo awo imene idawachititsa iwo kukhala mu kusadziwa; kotero Ambuye adzawachitira chifundo kwa iwo ndi kutalikitsa kukhala kwawo m’dziko.

17 Ndipo pa nyengo ina ya nthawi adzafikitsidwa kuti kukhulupilira mu mawu ake, ndi kudziwa za kusalondola kwa miyambo ya makolo awo; ndipo ambiri mwa iwo adzapulumutsidwa, pakuti Ambuye adzachitira chifundo kwa onse amene ayitanira pa dzina lake.

18 Koma taonani, ndikunena kwa inu kuti ngati mulimbikira m’kuipa kwanu kuti masiku anu sadzatalikitsidwa mu dzikolo, pakuti Alamani adzatumizidwa pa inu; ndipo ngati inu simulapa iwo adzabwera mu nthawi yomwe simukudziwa, ndipo inu mudzayenderedwa ndi chiwonongeko chotheratu; ndipo zidzakhala molingana ndi mkwiyo woopsya wa Ambuye.

19 Pakuti iye sadzalora inu kuti mukhalebe m’kusaweruzika kwanu, kuti muwononge anthu ake. Ndinena kwa inu, Ayi: iye angathe kulolera kuti Alamani athe kuwononga anthu ake wonse amene amatchedwa anthu a Nefi, ngati kukadakhala kotheka kuti adzagwe mu machimo ndi zolakwitsa, atatha kukhala ndi kuwala kwakukulu ndi kupatsidwa chidziwitso chachikulu kuchokera kwa Ambuye Mulungu wawo.

20 Inde, atatha kukhala anthu okonderedwa kwambiri a Ambuye; inde, atatha kukhala anthu okonderedwa kuposa dziko lirilonse, mafuko, manenedwe kapena anthu; atatha kukhala ndi zinthu zonse kudziwitsidwa kwa iwo molingana ndi zokhumba zawo, ndi chikhulupiliro chawo, ndi mapemphero, a izo zimene zidali, ndi zimene zili, ndi zimene ziri nkudza;

21 Atayenderedwa ndi Mzimu wa Mulungu; atayankhulana ndi angelo, ndipo atayankhuliwa kwa iwo ndi mawu a Ambuye; ndi kukhala ndi mzimu wa uneneri, ndi mzimu wa chibvumbulutso, ndiponso mphatso zambiri, mphatso ya kuyankhula ndi malilime, ndi mphatso ya kulalikira, ndi mphatso ya Mzimu Woyera, ndi mphatso ya kumasulira;

22 Inde, atapulumutsidwa ndi Mulungu kuchokera m’dziko la Yerusalemu, ndi dzanja la Ambuye; atapulumutsidwa ku chilala, ndi ku matenda, ndi mitundu yonse ya matenda a mtundu uliwonse; ndi kukula mu mphamvu ya nkhondo, kuti asawonongedwe; atatulutsidwa mu ukapolo ku nthawi ndi nthawi, ndipo atasungidwa ndi kutetezedwa kufikira tsopano; ndipo iwo achita bwino kufikira ali olemera mu zinthu za mitundu yonse—

23 Ndipo tsopano taonani ndikunena kwa inu, kuti ngati anthu awa, amene alandira madalitso ochuluka chotere kuchokera m’dzanja la Ambuye, angalakwitse mosemphana ndi kuwala ndi chidziwitso chimene iwo ali nacho, ine ndikunena kwa inu kuti ngati izi zili choncho, kuti ngati atagwe mu kulakwitsa, chidzakhala chopilirika kwambiri kwa Alamani kuposera kwa iwo.

24 Pakuti taonani, malonjezano a Ambuye aperekedwa kwa Alamani, koma sali kwa inu ngati inu mulakwa; pakuti kodi Ambuye sadalonjeze momveka bwino ndi kulamula mwamphamvu, kuti ngati inu mudzaukira iye kuti mudzawonongedwa kotheratu kuchoka pankhope ya dziko lapansi?

25 Ndipo tsopano pachifukwa ichi, kuti inu musawonongedwe, Ambuye atumiza mngelo wake kuti ayendere ambiri a anthu ake, kulengeza kwa iwo kuti akuyenera kupita ndi kulilira mwamphamvu kwa anthu awa, nati: Lapani inu, pakuti ufumu wa kumwamba wayandikira.

26 Ndipo si masiku ambiri kuchokera pano Mwana wa Mulungu adzabwera mu ulemelero wake; ndipo ulemelero wake udzakhala ulemelero wa Wobadwa Yekhayo wa Atate, wodzadza ndi chisomo, chilungamo, ndi choonadi, wodzadza ndi chipiliro, chifundo, ndi kuleza mtima, wachangu kumvera kulira kwa anthu ake ndi kuyankha mapemphero awo.

27 Ndipo taonani, akubwera kudzawombola amene adzabatizidwe m’kulapa, kudzera m’chikhulupiliro pa dzina lake.

28 Kotero, konzani inu njira ya Ambuye, pakuti nthawi ili pafupi kuti anthu wonse adzakolole mphotho ya ntchito zawo, molingana ndi ichi chimene akhala—ngati iwo akhala olungama adzakolola chipulumutso cha miyoyo yawo, molingana ndi mphamvu ndi chiwombolo cha Yesu Khristu; ndipo ngati akhala oipa adzakolola chiwonongeko cha moyo wawo, molingana ndi mphamvu ndi ukapolo wa mdyerekezi.

29 Tsopano taonani, awa ndi mawu a mngelo, kulilira kwa anthu.

30 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, pakuti inu ndi abale anga, ndipo mukuyenera kukondedwa, ndipo inu mukuyenera kubweretsa ntchito zimene ziri zoyenerana ndi kulapa, poona kuti mitima yanu yalimbitsitsa monyansa motsutsana ndi mawu a Mulungu, ndi kuona kuti ndinu anthu osochera ndi akugwa.

31 Ndipo zidachitika kuti pamene ine, Alima, ndidayankhula mawu awa, taonani, anthu adakwiya nane chifukwa ndidanena kwa iwo kuti adali anthu olimba mitima ndi osamvera.

32 Ndiponso chifukwa ndidanena kwa iwo kuti adali osochera ndi anthu akugwa adakwiya nane, ndipo adafuna kuti aike manja awo pa ine, kuti andiponye ine mundende.

33 Koma zidachitika kuti Ambuye sadalore iwo kuti anditenge ine pa nthawi imeneyi ndikundiponya ine mundende.

34 Ndipo zidachitika kuti Amuleki adapita ndi kuima patsogolo, ndipo adayamba kulalikanso kwa iwo. Ndipo tsopano mawu a Amuleki sadalembedwe onse, komabe gawo lina la mawu ake lalembedwa mu buku ili.