Mutu 18
Mfumu Lamoni iganiza kuti Amoni ndi Mzimu Waukulu—Amoni aphunzitsa mfumu za chilengedwe, Ntchito za Mulungu ndi anthu, ndi chiwombolo chimene chimabwera kudzera mwa Khristu—Lamoni akhulupilira ndipo agwa pansi ngati wamwalira. Mdzaka dza pafupifupi 90 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo zidachitika kuti mfumu Lamoni idapangitsa kuti adzakazi ake aime patsogolo ndikuchitira umboni wa zinthu zonse zimene iwo adaona zokhudzana ndi nkhaniyi.
2 Ndipo pamene wonse adachitira umboni ku zinthu zimene iwo adaona, ndipo iye adadziwa za kukhulupilika kwa Amoni pa kusunga ziweto zake, ndiponso za mphamvu zake zazikulu pakulimbana ndi iwo amene adafuna kumupha, adadabwa kwambiri, ndipo adati: Indedi, uyu simunthu wamba. Taonani, kodi ameneyu si Mzimu Waukulu umene umatumiza chilango chachikulu chotere kwa anthu awa, chifukwa cha kupha kwawo?
3 Ndipo iwo adayankha mfumuyo, ndipo adati: Kaya ndi Mzimu Waukulu kapena munthu, ife sitikudziwa; koma zambiri izi zokha ife tidziwa, kuti iye sangaphedwe ndi adani a mfumu; ngakhale iwo sangathe kubalalitsa ziweto za mfumu pamene iye ali ndi ife, chifukwa cha ukatswiri wake ndi mphamvu zake zazikulu; kotero, ife tikudziwa kuti iye ndi bwenzi wa mfumu. Ndipo tsopano, O mfumu, ife sitikukhulupilira kuti munthu ali ndi mphamvu zotere, pakuti tikudziwa kuti iye sangaphedwe.
4 Ndipo tsopano, pamene mfumu idamva mawu awa, iyo idati kwa iwo: Tsopano ndikudziwa kuti ndi Mzimu Waukulu; ndipo iye wabwera pansi nthawi ino kudzateteza miyoyo yanu, kuti ine ndisakupheni inu monga ndidachitira abale anu. Tsopano uwu ndi Mzimu Waukulu umene makolo athu adakamba.
5 Tsopano ichi chidali chikhalidwe cha Lamoni, chimene iye adalandira kuchokera kwa atate ake, kuti kudali Mzimu Waukulu. Ngakhale iwo ankakhulupilira za Mzimu Waukulu, ankaganiza kuti chilichonse ankachita chidali cholondola: komabe, Lamoni adayamba kuchita mantha kwambiri, ndi kuopa kuti iye adachita zolakwa pa kupha adzakazi ake.
6 Pakuti iye adapha ambiri a iwo chifukwa abale awo adabalalitsa ziweto zawo kumadzi; ndipo choncho, chifukwa iwo adabalalitsidwira ziweto zawo adaphedwa.
7 Tsopano adali machitidwe a Alamaniwa kuima pa madzi a Sebusi kuti abalalitse ziweto za anthu, kuti kotero azitha kuthamangitsa zambiri zimene zabalalika kuti zithawire ku dziko lawo, awa adali machitidwe a kuba pakati pawo.
8 Ndipo zidachitika kuti mfumu Lamoni adafunsa adzakazi ake, kuti: Alikuti munthu ameneyu amene ali ndi mphamvu zazikulu zotere?
9 Ndipo iwo adati kwa iye: Taonani, akudyetsa akavalo anu. Tsopano mfumu idalamula adzakazi ake, isadafike nthawi yomwetsera ziweto zawo, kuti akonzekeretse akavalo ake ndi magaleta, ndipo amupititse iye ku dziko la Nefi; pakuti kumeneko kudakonzedwa phwando lalikulu lokhazikitsidwa pa dziko la Nefi, ndi atate ake a Lamoni, amene adali mfumu ya dziko lonse.
10 Tsopano pamene mfumu Lamoni adamva kuti Amoni adali kukonzekeretsa akavalo ake ndi magaleta ake anadabwa kwambiri, chifukwa cha kukhulupirika kwa Amoni, nati: Indedi sipadakhale m’dzakazi aliyense pakati pa adzakazi anga onse amene wakhala okhulupilika ngati munthu uyu; pakuti ngakhale iye amakumbukira malamulo anga onse kuwachita.
11 Tsopano ndikudziwa ndithu kuti ameneyu ndi Mzimu Waukulu, ndipo ndikadakhumbira kuti iye abwere kwa ine, koma ine sinditero.
12 Ndipo zidachitika kuti pamene Amoni adakonzekeretsa akavalo ndi magaleta a mfumu ndi adzakazi ake, adapita kwa mfumu, ndipo adaona kuti maonekedwe a mfumu adasinthika; kotero adali pafupi kubwelera kuchoka pamaso pake.
13 Ndipo m’modzi mwa adzakazi amfumu adati kwa iye, Rabana, amene ali, kutanthauzira kwake, wamphamvu kapena mfumu yaikulu, poganizira mafumu awo kukhala amphamvu; ndipo choncho iye adati kwa iye: Rabana, amfumu akufuna inu kuti mukhale.
14 Kotero Amoni adatembenukira kwa mfumu, ndipo adati kwa iye: Kodi mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani, O mfumu? Ndipo mfumu siidamuyankhe iye kwa nthawi ya ora limodzi, molingana ndi nthawi yawo, pakuti sadadziwe choti anene kwa iye.
15 Ndipo zidachitika kuti Amoni adatinso kwa iye: Kodi inu mukukhumba chiyani kwa ine? Koma mfumuyo siidamuyankhe.
16 Ndipo zidachitika kuti Amoni, podzadzidwa ndi Mzimu wa Mulungu, kotero, adadziwa maganizo a mfumuyo. Ndipo iye adati kwa iyo; Kodi ndichifukwa choti mwamva zokuti ndidateteza adzakazi anu ndi ziweto zanu, ndi kupha abale awo asanu ndi awiri ndi legeni ndi lupanga ndi kudula mikono ya ena, kuti nditeteze ziweto zanu ndi adzakazi anu; taonani, kodi ndizimenezi zimene zachititsa kudabwa kwanu?
17 Ine ndikunena kwa inu, ndi chiyani, kuti kudabwitsika kwanu n’kwakukulu? Taonani, ine ndi munthu, ndipo ndine m’dzakazi wanu; kotero, chilichonse chimene inu mukukhumba chimene chiri choyenera, chimenecho ine ndidzachita.
18 Tsopano pamene mfumu idamva mawu awa, idadabwanso, pakuti idaona kuti Amoni ankazindikira malingaliro ake; koma posatengera izi, mfumu Lamoni idatsegula pakamwa pake, ndipo idati kwa iye: Ndiwe ndani? Kodi ndiwe Mzimu Waukulu uja, umene umadziwa zinthu zonse?
19 Amoni adayankha nati kwa iye: Sindine.
20 Ndipo Mfumu idati: Kodi ukudziwa bwanji maganizo a mtima mwanga? Uyankhule mopanda mantha, ndipo undiuze zokhudza zinthu izi; ndiponso undiuze ndi mphamvu yanji imene udaphera ndi kudula mikono ya abale anga amene adabalalitsa dziweto dzanga—
21 Ndipo tsopano, ngati iwe utandiuze ine zokhudza zinthu izi, chirichonse chimene iwe ukhumba ine ndidzakupatsa kwa iwe; ndipo ngati n’kofunika, ndidzakulondera iwe ndi ankhondo anga; koma ndikudziwa kuti iwe ndi wamphamvu kwambiri kuposa iwo onse; komabe, chirichonse chimene iwe ukhumba kwa ine ndidzapereka icho kwa iwe.
22 Tsopano Amoni pokhala wanzeru, koma osaopsya, adati kwa Lamoni: Kodi mudzamvera mawu anga, ngati nditakuuzeni inu ndi mphamvu yanji yomwe ndimachitira zinthu izi? Ndipo ichi ndi chinthu chomwe ine ndikhumba kwa inu.
23 Ndipo mfumu idamuyankha iye, nati: inde, ndidzakhulupilira mawu ako onse. Ndipo kotero iye adagwidwa ndi chinyengo.
24 Ndipo Amoni adayamba kuyankhula kwa iye molimba mtima, nati kwa iye: Kodi mukukhulupilira kuti kuli Mulungu?
25 Ndipo iye adayankha, nati kwa iye: Sindikudziwa chimene izi zikutanthauza.
26 Ndipo kenako Amoni adati: Kodi mukukhulupilira kuti kuli Mzimu Waukulu?
27 Ndipo adati, Inde.
28 Ndipo Amoni adati: Ameneyu ndi Mulungu. Ndipo Amoni adatinso kwa iye: Kodi mukukhulupilira kuti Mzimu Waukulu umenewu, umene ndi Mulungu, udalenga zinthu zonse zimene ziri kumwamba ndi mu dziko lapansi?
29 Ndipo iye adati: Inde, ndikukhulupilira kuti iye adalenga zinthu zonse zimene ziri mu dziko lapansi; koma sindikudziwa za kumwamba.
30 Ndipo Amoni adati kwa iye: Kumwamba ndi malo amene Mulungu amakhala ndi angelo oyera ake onse.
31 Ndipo mfumu Lamoni idati: Kodi ndi pamwamba pa dziko lapansi?
32 Ndipo Amoni adati: Inde, ndipo amayang’anira pansi pa ana a anthu onse; ndipo amadziwa maganizo onse ndi zolinga za mitima; pakuti ndi dzanja lake onse adalengedwa kuchokera pa chiyambi.
33 Ndipo mfumu Lamoni idati: Ndikukhulupilira zinthu zonsezi zimene iwe wayankhula. Kodi iwe watumidwa kuchokera kwa Mulungu?
34 Amoni adati kwa iye: Ndine munthu; ndipo munthu kuchokera pachiyambi adalengedwa m’chifaniziro cha Mulungu, ndipo ine ndidaitanidwa ndi Mzimu Wake Woyera kuti ndiphunzitse zinthu izi kwa anthu awa, kuti abweretsedwe ku chidziwitso cha zimene zili zolungama ndi zoona.
35 Ndipo gawo la Mzimu umenewo umakhala mwa ine, umene umandipatsa chidziwitso, ndiponso mphamvu molingana ndi chikhulupiliro changa ndi zokhumba zimene ziri mwa Mulungu.
36 Tsopano pamene Amoni adanena mawu awa, adayambira pa chilengedwe cha dziko lapansi, ndiponso chilengedwe cha Adamu, ndipo adamuuza iye zinthu zonse zokhudzana ndi kugwa kwa munthu, ndipo adabwerezanso ndi kuyala pamaso pake zolemba ndi malembo woyera a anthu, amene adayankhulidwa ndi aneneri, ngakhale mpaka nthawi yomwe kholo lawo, Lehi, adachoka ku Yerusalemu.
37 Ndiponso adabwereza kwa iwo (pakuti zidali kwa mfumuyo ndi adzakazi ake) za maulendo a makolo awo m’chipululu, ndi mazunzo awo onse ndi njala ndi ludzu, ndi kuvutika kwawo, ndi zina zotero.
38 Ndipo adabwerezanso kwa iwo zokhudzana kupandukira kwa Lamani ndi Lemueli, ndi ana a Ismaeli, inde, zopandukira zawo zonse iye adauza iwo; ndipo iye adatanthauzira kwa iwo zonse zolemba ndi malembo oyera kuchokera ku nthawi imene Lehi adachoka ku Yerusalemu kutsikira ku nthawi ino.
39 Koma izi sizokhazo: pakuti adatanthauzira kwa iwo dongosolo la chiwombolo, chimene chidakonzedwa kuchokera pa maziko a dziko lapansi; ndiponso adawadziwitsa iwo zokhudzana ndi kubwera kwa Khristu, ndi ntchito zonse za Ambuye iye adawadziwitsa iwo.
40 Ndipo zidachitika kuti atatha kunena zinthu zonsezi, ndi kuzitanthauzira kwa mfumu, kuti mfumu idakhulupilira mawu ake onse.
41 Ndipo idayamba kufuula kwa Ambuye, nati: O Ambuye, chitireni chifundo; molingana ndi zifundo zanu zochuluka zimene mwakhala nazo pa anthu a Nefi; zikhale pa ine, ndi anthu anga.
42 Ndipo tsopano, pamene adanena izi, adagwa pansi, ngati kuti wamwalira.
43 Ndipo zidachitika kuti adzakazi ake adamutenga ndi kumunyamulira kwa mkazi wake, ndi kumugoneka pa kama lake; ndipo adagona ngati kuti wamwalira kwa nthawi ya usana uwiri ndi usiku uwiri; ndipo mkazi wake, ndi ana ake aamuna, ndi ana ake aakazi adalira pa iye, motsatira chikhalidwe cha Alamani, kudandaula kwambiri za kufa kwake.