Malembo Oyera
Alima 31


Mutu 31

Alima atsogolera ntchito yobwenzeretsa Azoramu opatuka—Azoramu akana Khristu, akhulupilira mfundo zabodza za chisankho, ndipo apembedza motsata mapemphero woikidwiratu—Amishonale adzadzidwa ndi Mzimu Woyera—Masautso awo amezedwa mu chimwemwe cha Khristu. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidachitika kuti potsatira mathero a Koriho, Alima atalandira uthenga wakuti Azoramu adali kupotoza njira za Ambuye, ndipo kuti Zoramu, amene adali mtsogoleri wawo, adali kutsogolera mitima ya anthu kugwadira mafano wosayankhula, mtima wake udayambanso kudwala chifukwa cha kusaweruzika kwa anthuwo.

2 Pakuti chidali chochititsa chisoni chachikulu kwa Alima kudziwa za kusaweruzika pakati pa anthu ake; kotero mtima wake udali wachisoni kwambiri chifukwa cha kulekana kwa Azoramu ndi Anefi.

3 Tsopano Azoramu adadzisonkhanitsa pamodzi mu dziko limene limatchedwa Antionamu, limene lidali kum’mawa kwa dziko la Zarahemula, limene lidayandikira malire a gombe lanyanja, limene lidali kum’mwera kwa dziko la Yeresoni, limene lidachitanso malire ndi chipululu cha kum’mwera, chimene chipululucho chidali chodzadza ndi Alamani.

4 Tsopano Anefi adachita mantha kwambiri kuti Azoramu angadzalowe mu mgwirizano ndi Alamani, ndipo kuti ingadzakhale njira yakutaika kwa gawo la Anefi.

5 Ndipo tsopano, pamene kulalikira kwa mawu kudali ndi chizoloŵezi chachikulu cha kutsogolera anthu kuchita chimene chidali cholungama—inde, kudali ndi chikoka champhamvu kwambiri pa maganizo a anthu kuposa lupanga, kapena chinthu chilichonse, chimene chidachitika pa iwo—kotero Alima adaganiza kuti kudali koyenera kuti iwo ayesere mphamvu za mawu a Mulungu.

6 Kotero iye adatenga Amoni, ndi Aroni, ndi Omineri; ndipo Himuni adamusiya mu mpingo ku Zarahemula; koma atatu woyambilirawo iye adawatenga ndi iye ndiponso Amuleki ndi Zeziromu, amene adali ku Meleki; ndipo iye adatenganso ana ake aamuna awiri.

7 Tsopano wamkulu wa ana ake iye sadamutenge, ndipo dzina lake lidali Helamani; koma maina a amene iye adawatenga adali Shibuloni ndi Koriyantoni; ndipo awa adali maina a iwo amene adapita naye pakati pa Azoramu, kuti akalalikire kwa iwo mawu.

8 Tsopano Azoramu adali wotsutsa kuchokera kwa Anefi; kotero adakhalapo ndi mawu a Mulungu kulalikidwa kwa iwo.

9 Koma iwo adagwa mu zolakwika zazikulu, pakuti iwo sankatsata kusunga malamulo a Mulungu, ndi malembo ake, monga mwa lamulo la Mose.

10 Ngakhalenso iwo samatsata zochitika zamumpingo, kuti apitirizebe m’mapemphero ndi mapembedzero kwa Mulungu tsiku lirilonse, kuti iwo asalowe m’mayesero.

11 Inde, mwachidule, iwo ankapotoza njira za Ambuye mu nthawi zambiri; kotero, pachifukwa ichi, Alima ndi abale ake adapita ku dzikolo kukalalika mawu kwa iwo.

12 Tsopano, pamene iwo adafika ku dzikolo, taonani, m’kudabwitsika kwawo adapeza kuti Azoramu adamanga masunagoge, ndipo kuti iwo ankasonkhana pamodzi pa tsiku limodzi mu sabata, limene tsikulo ankalitcha tsiku la Ambuye; ndipo ankapembedza potsatira njira imene Alima ndi abale ake sadaonepo;

13 Pakuti iwo adali ndi malo omangidwa chapakati pa sunagoge wawo, pa malo oimirapo, amene adali pamwamba pa mutu; ndipo pamwamba pakepo amalora munthu m’modzi basi.

14 Kotero, aliyense amene amakhumba kupembedza amayenera kupita ndi kuima pamwambapo, ndi kutambasulila manja ake kumwamba, ndipo amafuula ndi mawu aakulu, nati:

15 Oyera, oyera Mulungu, ife tikukhulupilira kuti inu ndi Mulungu, ndipo ife tikukhulupilira kuti inu ndi oyera, ndipo kuti inu mudali mzimu, ndipo kuti inu ndi mzimu, ndipo kuti inu mudzakhalabe mzimu kwa muyaya.

16 Mulungu Oyera, tikukhulupilira kuti inu mudatisiyanitsa ife kwa abale athu; ndipo ife sitikhulupilira mu miyambo ya abale athu, imene idaperekedwa kwa iwo mwa ubwana wa makolo awo; koma ife tikukhulupilira kuti inu mwasankha ife kukhala ana anu oyera; ndiponso inu mwadziwitsa kwa ife kuti sikudzakhala Khristu.

17 Koma inu muli yemweyo dzulo, lero ndi kunthawi zonse; ndipo inu mwatisankha ife kuti tidzapulumuka, pamene onse ozungulira ife asankhidwa kuti adzatayidwa ndi mkwiyo wanu kupita ku gahena; pa chiyero chimenechi, O Mulungu, tikukuthokozani; ndipo ifenso tikuthokoza inu kuti mwatisankha ife, kuti tisasocheretsedwe potsata miyambo yopusa ya abale athu, imene imawamanga iwo m’kukhulupilira kuti Khristu, amene amatsogolera mitima yawo kufikira kutali ndi inu, Mulungu wathu.

18 Ndipo kachiwiri tikukuthozani inu, O Mulungu, kuti ife ndife anthu osankhidwa ndi oyera. Ameni.

19 Ndipo zidachitika kuti atamaliza Alima ndi abale ake ndi ana ake kumva mapemphero amenewa, anadabwa koposa mulingo onse.

20 Pakuti taonani, munthu wina aliyense adapitapo ndi kupereka mapemphero omwewa.

21 Tsopano malowa ankatchedwa ndi iwo kuti Ramemputomu, amene kutanthauzira kwake ndi nsanja yoyera.

22 Tsopano, kuchokera ku nsanja imeneyi iwo ankapereka, munthu aliyense, pemphero limodzimodzi lomwelo kwa Mulungu, kuthokoza Mulungu wawo kuti iwo adasankhidwa ndi iye, ndipo kuti iye sadawasocholetse potsatira miyambo ya abale awo, ndipo kuti mitima yawo siidapusitsike m’kukhulupilira mwa zinthu ziri nkudza, zimene iwo sankadziwapo kanthu kake.

23 Tsopano, anthuwa atatha kupereka mathokozo awo mu njira imeneyi, adabwelera ku nyumba zawo osayankhulanso zokhudza Mulungu wawo kufikira iwo adzasonkhanenso pamodzi ku nsanja yoyera, kukapereka mathokozo monga mwa njira yawo.

24 Tsopano pamene Alima adaona izi mtima wake udamva chisoni; pakuti iye adaona kuti iwo adali oipa ndi anthu wopotoka; inde, iye adaona kuti mitima yawo idali pa golide, ndi pa siliva, ndi pa mitundu yonse ya zinthu zabwino.

25 Inde, ndipo iye adaona kuti mitima yawo idali yodzikweza m’kudzitamandira kwakukulu, mu kunyada kwawo.

26 Ndipo iye adakweza mawu ake kumwamba ndipo adafuula nati: O, kwa nthawi yaitali bwanji, O Ambuye, mudzalora kuti adzakazi anu adzakhale pano pansi mu thupi, kuonelera zoipa zonyansa pakati pa ana a anthu?

27 Taonani, O Mulungu, akufuula kwa inu, ndipo chonsecho mitima yawo yamezedwa m’kudzikweza kwawo. Taonani, O Mulungu, iwo akufuula kwa inu ndi pakamwa pawo, koma iwo ndiwodzikweza, ngakhale kwakukulu, ndi zinthu zachabechabe za dziko lapansi.

28 Taonani, O Mulungu wanga, zovala zawo zamtengo wapali, ndi mphete zawo, ndi zibangili zawo, ndi zokongoletsera zawo za golide, ndi zonse zamtengo wapatali zimene amazikongoletsera; ndipo taonani, mitima yawo ili pa izo, ndipo komabe akufuula kwa inu nati—Tikuthokozani inu, O Mulungu, pakuti ndife anthu wosankhidwa kwa inu, pamene enawo adzawonongeka.

29 Inde, ndipo iwo akunena kuti inu mwawadziwitsa iwo kuti sikudzakhala Khristu.

30 O Ambuye Mulungu, inu mudzalora kwa nthawi yaitali bwanji kuipa ndi kusakhulupilika kotere kukhala pakati pa anthu awa? O Ambuye, kodi mudzandipatsa ine mphamvu, kuti ndipilire mzofooka zanga. Pakuti ndine ofooka, ndipo kuipa kotere pakati pa anthu awa kukundiwawitsa moyo wanga.

31 O Ambuye, mtima wanga uli ndi chisoni chachikulu; kodi inu mudzatonthoza moyo wanga mwa Khristu. O Ambuye, kodi mudzapereka kwa ine kuti ndikhale ndi mphamvu, kuti ndizunzike moleza mtima mazunzo awa amene adzabwera kwa ine, chifukwa cha zoipa za anthu awa.

32 O Ambuye, kodi mudzatonthoza moyo wanga, ndi kundipatsa ine chipambano, ndiponso antchito anzanga amene ali nane—inde, Amoni, ndi Aroni, ndi Omineri, ndiponso Amuleki ndi Zeziromu, ndiponso ana anga aamuna—inde, ngakhale onsewa kodi mudzawatonthoza, O Ambuye. Inde, kodi mudzatonthoza miyoyo yawo mwa Khristu.

33 Kodi mudzawapatsa iwo kuti akhale ndi mphamvu, kuti adzapilire mazunzo awo amene adzabwera kwa iwo chifukwa cha zoipa za anthu awa.

34 O Ambuye, kodi mudzapereka kwa ife kuti tipambane pobweretsanso iwo kwa inu mwa Khristu.

35 Taonani, O Ambuye, miyoyo yawo ndi yamtengo wapatali, ndipo ambiri mwa iwo ndi abale athu; kotero, mutipatse ife, O ambuye, mphamvu ndi nzeru kuti ife tibweretse awa, abale athu, kachiwiri kwa inu.

36 Ndipo zidachitika kuti pamene Alima adanena mawu awa, kuti iye adawombera m’manja pa onse amene adali ndi iye. Ndipo taonani, pamene iye adawombera m’manja pa iwo, iwo adadzadzidwa ndi Mzimu Woyera.

37 Ndipo pambuyo pake iwo adadzilekanitsa wina ndi mzake, osadziganizira iwo wokha zimene angadye, kapena zimene iwo angamwe, kapena zimene iwo angavale.

38 Ndipo Ambuye adawasamalira iwo kuti iwo asamve njala, ngakhale kumva ludzu, inde, ndipo adawapatsanso iwo mphamvu, kuti asamve masautso aliwonse, kupatula amezedwe m’chimwemwe cha Khristu. Tsopano izi zidali molingana ndi pemphero la Alima; ndipo izi ndi chifukwa iye adapemphera mwachikhulupiliro.

Print