Malembo Oyera
Alima 8


Mutu 8

Alima alalikira ndi kubatiza ku Meleki—Iye akanidwa ku Amoniha ndipo achokako—Mngelo amulamula iye kuti abwelere ndi kufuura kulapa kwa anthu—Iye alandilidwa ndi Amuleki, ndipo awiriwa alalika ku Amoniha. Mdzaka dza pafupifupi 82 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti Alima atabwelera kuchokera ku dziko la Gideoni, atamaliza kuphunzitsa anthu a Gideoni zinthu zambiri zimene sizingalembedwe, atakhazikitsa dongosolo la mpingo, molingana ndi m’mene adachitira ku dziko la Zarahemula, inde, adabwelera ku nyumba kwake ku Zarahemula kukapumula ku ntchito zomwe iye adagwira.

2 Ndipo kotero chidatha chaka cha chisanu ndi zinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.

3 Ndipo zidachitika kuti kumayambiliro kwa chaka chakhumi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, kuti Alima adanyamuka kuchoka kumeneko ndi kutenga ulendo wake kupita ku dziko la Meleki, cha kumadzulo kwa mtsinje wa Sidoni, chakumadzulo kufupi ndi malire a chipululu.

4 Ndipo adayamba kuphunzitsa anthu mu dziko la Meleki molingana ndi dongosolo loyera la Mulungu, limene iye adaitanidwira; ndipo adayamba kuphunzitsa anthu m’dziko lonse la Meleki.

5 Ndipo zidachitika kuti anthu adabwera kwa iye m’malire onse a dziko limene lidali m’mbali mwa chipululu. Ndipo iwo adabatizidwa m’dziko lonselo;

6 Kotero kuti pamene iye adamaliza ntchito yake ku Meleki adachokako, ndi kuyenda ulendo wa masiku atatu ku mpoto kwa dziko la Meleki; ndipo adafika ku mzinda umene umatchedwa Amoniha.

7 Tsopano chidali chikhalidwe cha anthu a Nefi kutchula maiko awo, ndi midzi yawo, inde, ngakhale midzi yawo yonse ing’onoing’ono, potsatira dzina la iye amene adayamba kukhalako; ndipo motero ndim’mene zidalili ndi dziko la Amoniha.

8 Ndipo zidachitika kuti pamene Alima adafika ku mzinda wa Amoniha adayamba kulalikira mawu a Mulungu kwa iwo.

9 Tsopano Satana adali atagwiritsitsa mitima ya anthu a mzinda wa Amoniha; kotero sadamvera mawu a Alima.

10 Komabe Alima adagwira ntchito kwambiri mu mzimu, kulimbana ndi Mulungu mu pemphero la mphamvu, kuti atsanulire Mzimu wake pa anthu amene adali mu mzindawo; kuti amulorenso kuti awabatize anthuwo kuti alape.

11 Komabe, iwo adaumitsa mitima yawo, nati kwa iye: Taona, Ife tikudziwa kuti iwe ndi Alima; ndipo tikudziwa kuti ndiwe mkulu wansembe kwa mpingo umene iwe udakhazikitsa m’madera ambiri a dziko, monga mwa chikhalidwe chako; ndipo ife sitili a mpingo wako, ndipo sitimakhulupilira mu zikhalidwe zopusazo.

12 Ndipo tsopano tikudziwa kuti chifukwa sitiri a mpingo wako tikudziwa kuti iwe ulibe mphamvu pa ife; ndipo iwe wapereka mpando wa chiweruzo kwa Nefiha; kotero iwe sindiwe mkulu wa oweruza pa ife.

13 Tsopano pemene anthu adayankhula izi, ndi kukana mawu ake onse, ndi kumunyoza iye, ndi kumulavulira iye, ndipo adachititsa kuti atulutsidwe kunja kwa mzinda wawo, iye adachoka kumeneko ndi kutenga ulendo wake kuyandikira ku mzinda umene umatchedwa Aroni.

14 Ndipo zidachitika kuti pamene iye adali kuyenda kumeneko, okhala olemedwa ndi chisoni, akudutsa m’masautso aakulu, ndi kuwawa kwa moyo, chifukwa cha kuipa kwa anthu amene adali mu mzinda wa Amoniha, zidachitika kuti pamene Alima adali olemedwa motere ndi chisoni, taonani mngelo wa Ambuye adaonekera kwa iye nati:

15 Odala ndi iwe, Alima; kotero, kweza mutu wako ndi kukondwera, pakuti iwe uli nacho chifukwa chachikulu chokondwera; pakuti iwe wakhala okhulupirika m’kusunga malamulo a Mulungu kuyambira nthawi imene iwe udalandira uthenga wako oyamba kwa iye. Taona, ine ndine amene ndidaupereka kwa iwe.

16 Ndipo taona, ndatumidwa kuti ndikulamule iwe kuti ubwelere ku mzinda wa Amoniha, ndi kulalikanso kwa anthu a mzindawo; inde, kalalikire kwa iwo. Inde, ukati kwa iwo, kupatula iwo alape Ambuye Mulungu adzawawononga iwo.

17 Pakuti taona, iwo akuphunzira pa nthawi ino kuti awononge ufulu wa anthu ako, (pakuti atero Ambuye) zimene ziri zosemphana ndi malamulo olembedwa, ndi ziweruzo, ndi malamulo amene iye wapereka kwa anthu ake.

18 Tsopano zidachitika kuti Alima atalandira uthenga wake kuchokera kwa mngelo wa Ambuye adabwelera mofulumira ku dziko la Amoniha. Ndipo adalowa mzindawo kudzera njira ina, inde, m’njira imene ili kum’mwera kwa mzinda wa Amoniha.

19 Ndipo pamene adalowa m’mzindawo adamva njala, ndipo adati kwa munthu wina: Mungamupatse mdzakadzi wodzichepetsa wa Mulungu kanthu koti adye?

20 Ndipo munthuyo adati kwa iye: Ndine Mnefi, ndipo ndikudziwa kuti iwe ndi mneneri oyera wa Mulungu, pakuti ndiwe munthu amene mngelo adanena m’masomphenya: Udzamulandira. Kotero, pita ndi ine kunyumba kwanga ndipo ndidzakupatsa iwe chakudya changa; ndipo ndikudziwa kuti iwe udzakhala mdalitso kwa ine ndi nyumba yanga.

21 Ndipo zidachitika kuti munthuyo adamulandira iye ku nyumba kwake; ndipo munthuyo adali wotchedwa Amuleki; ndipo adabweretsa mkate ndi nyama ndikuika pamaso pa Alima.

22 Ndipo zidachitika kuti Alima adadya mkatewo ndipo adakhuta; ndipo adadalitsa Amuleki ndi nyumba yake, ndipo adapereka mayamiko kwa Mulungu.

23 Ndipo atatha kudya ndi kukhuta adati kwa Amuleki: ine ndine Alima, ndipo ndine mkulu wansembe wa mpingo wa Mulungu m’dziko lonseli.

24 Ndipo taona, ndaitanidwa kuti ndilalikire mawu a Mulungu pakati pa anthu awa, monga mwa mzimu wa chibvumbulutso ndi uneneri; ndipo ndidali mu dziko lino ndipo sadandilandire, koma adanditulutsa ndipo ndidali pafupi kuika nsana wanga ku dziko lino kwamuyaya.

25 Koma taona, ndalamulidwa kuti nditembenukenso ndi kunenera kwa anthu awa, inde, ndi kuchitira umboni mowatsutsa zokhudzana ndi mphulupulu zawo.

26 Ndipo tsopano, Amuleki, chifukwa iwe wandidyetsa ine ndi kundilandira, ndiwe odala; chifukwa ndidali ndi njala, pakuti ndasala chakudya masiku ambiri.

27 Ndipo Alima adakhala masiku ambiri ndi Amuleki asadayambe kulalikira kwa anthu.

28 Ndipo zidachitika kuti anthuwo adakula kwambiri mu zoipa ndi mphulupulu zawo.

29 Ndipo mawu adafika kwa Alima, nati: Pita, ndiponso ukati kwa mdzakadzi wanga Amuleki, pita uko ndipo ukanenere kwa anthu awa, nati—Lapani inu, pakuti atero Ambuye, pokhapokha mutalapa ndidzayendera anthu awa ndi mkwiyo wanga; inde, sindidzabweza mkwiyo wanga oopsa.

30 Ndipo Alima adapita ndiponso Amuleki, pakati pa anthu, kukalalikira mawu a Mulungu kwa iwo; ndipo adadzadzidwa ndi Mzimu Oyera.

31 Ndipo adali ndi mphamvu yopatsidwa kwa iwo, kotero kuti sakadatha kuponyedwa mu ndende; kapena sikudali kotheka kuti munthu aliyense akadatha kuwapha; komabe iwo sadaonetse mphamvu zawo kufikira atamangidwa ndi zingwe ndi kuponyedwa mu ndende. Tsopano, izi zidachitika kuti Ambuye athe kuwonetsa mphamvu yake mwa iwo.

32 Ndipo zidachitika kuti adapita ndi kuyamba kulalikira ndi kunenera kwa athu, molingana ndi mzimu ndi mphamvu imene Ambuye adawapatsa iwo.

Print