Malembo Oyera
Alima 11


Mutu 11

Ndondomeko ya ndalama za Anefi zikhazikitsidwa—Amuleki alimbana ndi Zeziromu—Khristu sadzapulumutsa anthu m’machimo mwawo—Okhawo amene adzalandire ufumu wa kumwamba adzapulumuka—Anthu onse adzauka m’chisavundi—Palibenso imfa patatha chiukitso. Mdzaka dza pafupifupi 82 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidali mu lamulo la Mosiya kuti munthu aliyense amene adali oweruza wa chilamulo, kapena iwo amene adasankhidwa kukhala oweruza, akuyenera kulandira malipiro molingana ndi nthawi yomwe agwira kuti aweruze iwo omwe adabweretsedwa pamaso pawo kuti aweruzidwe.

2 Tsopano ngati munthu adali ndi ngongole kwa wina, ndipo sadabwenze izo zimene adangongola, amakasumilidwa kwa oweruza; ndipo oweruzayo ankachita ulamuliro, ndi kutumiza akapitawo kuti munthuyo abweretsedwe pamaso pake; ndipo iye amaweruza munthuyo molingana ndi lamulo ndi umboni umene udabweretsedwa motsutsana naye, ndipo choncho munthuyo amakakamizika kupereka zimene iye adangongola, kapena amalandidwa, kapena kutulutsidwa pakati pa anthu ngati wakuba ndi wambanda.

3 Ndipo oweruza ankalandira malipiro ake molingana ndi nthawi yake—senine wa golide pa tsiku, kapena senumu wa siliva, yomwe idali mulingo umodzi ndi senine wa golide; ndipo izi molingana ndi lamulo limene lidaperekedwa.

4 Tsopano awa ndiwo mayina a zidutswa zosiyanasiyana za golide wawo, ndi za siliva wawo, molingana ndi mulingo wawo. Ndipo mainawa aperekedwa ndi Anefi, pakuti iwo sadawerenge potsatira machitidwe a Ayuda amene adali ku Yerusalemu; ngakhale kuyeza mulingo potsatira machitidwe a Ayuda; koma iwo adasintha kawerengedwe kawo ndi kayezedwe kawo molingana ndi kaganizidwe ndi zochitika za anthu, mu m’badwo uliwonse, kufikira ulamuliro wa oweruza, iwo atakhazikitsidwa ndi mfumu Mosiya.

5 Tsopano kawerengedweko kali motere—senine wa golide, seyoni wa golide, shumu wa golide ndi limuna wa golide.

6 Senumu wa siliva, amunori wa siliva, eziromu wa siliva ndi onti wa siliva.

7 Senumu wa siliva adali olingana ndi senine wa golide, ndipo onse adali mulingo wa bale, ndiponso mulingo wa mbewu zamtundu uliwonse.

8 Tsopano kuchuluka kwa seyoni ya golide kudali kawiri ku mtengo wa senine.

9 Ndipo shumu ya golide idali kuphatikiza kawiri mtengo wa seyoni

10 Ndipo limuna ya golide idali yophatikiza mtengo wa zonsezi.

11 Ndipo amunori ya siliva idali yaikulu ngati ma senumu awiri.

12 Ndipo eziromu ya siliva idali yaikulu ngati ma senumu anayi.

13 Ndipo onti adali wamkulu ngati zonsezi.

14 Tsopano uwu ndiwo mtengo wa mawerengero ochepa a kawerengedwe kawo—

15 Shibuloni ndi theka la senumu; kotero shibuloni kwa theka la muyezo wa bale.

16 Ndipo shibulumu ndi theka la shibuloni.

17 Ndipo leya ndi theka la shibulumu.

18 Tsopano awa ndiwo mawerengedwe awo, molingana ndi kuwerengera kwawo.

19 Tsopano antiyoni wa golide ndi olingana ndi ma shibuloni atatu.

20 Tsopano, chidali cholinga chimodzi kuti apeze phindu, chifukwa ankalandira malipiro awo molingana ndi ntchito yawo, kotero, amautsa anthu ku zipolowe, ndi mitundu yonse ya zipolowe ndi zoipa, kuti iwo akhale ndi ntchito zambiri, kuti apeze ndalama molingana ndi milandu yomwe yabwera pamaso pawo; kotero adautsa anthu kutsutsana ndi Alima ndi Amuleki.

21 Ndipo Zeziromu ameneyu adayamba kufunsa Amuleki, nati: Kodi uyankha mafunso ochepa amene ine nditakufunse? Tsopano Zeziromu adali munthu amene adali katswiri mu njira za mdyerekezi, kuti akhonze kuwononga izo zimene zidali zabwino; kotero; adati kwa Amuleki: Kodi uyankha mafunso amene nditawaike pa iwe?

22 Ndipo Amuleki adati kwa iye: Inde, ngati zili molingana ndi Mzimu wa Ambuye, umene uli mwa ine; pakuti sindidzanena kanthu kamene kali kosemphana ndi Mzimu wa Ambuye. Ndipo Zeziromu adati kwa iye: Taona, apa pali ma onti a siliva asanu ndi m’modzi, ndipo onsewa ndidzakupatsa iwe ngati utakane za kukhalapo kwa Munthu Wamkulu.

23 Tsopano Amuleki adati: O iwe mwana wa gahena, undiyeseranji ine? Kodi sukudziwa kuti olungama samagwa m’mayesero oterewa?

24 Kodi umakhulupilira kuti kulibe Mulungu? Ndinena kwa iwe, Ayi, iwe ukudziwa kuti kuli Mulungu, koma iwe umakonda ndalama koposa iye.

25 Ndipo tsopano iwe wanama pamaso pa Mulungu kwa ine. Iwe wati kwa ine—Taona ma onti asanu ndi m’modzi awa, amene ndi a mtengo wapatali, ndidzapereka kwa iwe—pamene muntima mwako ukuganiza zowatenganso kwa ine; ndipo chidali chikhumbo chako chokha kuti ine ndikane Mulungu woonadi ndi wamoyo, kuti iwe ukathe kukhala ndi chifukwa chondiwonongera ine. Ndipo tsopano taona, chifukwa cha choipa chachikulu chimenechi iwe udzalandira mphotho yako.

26 Ndipo Zeziromu adati kwa iye: Kodi iwe ukunena kuti kuli Mulungu oona ndi wamoyo?

27 Ndipo Amuleki adati: Inde, kuli Mulungu oona ndi wamoyo.

28 Tsopano Zeziromu adati: Kodi alipo Mulungu oposa m’modzi?

29 Ndipo iye adayankha, Ayi.

30 Tsopano Zeziromu adanenanso kwa iye: Kodi iwe ukudziwa bwanji zinthu izi?

31 Ndipo iye adati: Mngelo wandidziwitsa izo kwa ine.

32 Ndipo Zeziromu adatinso: Kodi iye ndi ndani amene atadzabwere? Kodi ndi Mwana wa Mulungu?

33 Ndipo adati kwa iye, Inde.

34 Ndipo Zeziromu adatinso: Kodi iye adzapulumutsa anthu m’machimo awo? Ndipo Amuleki adayankha ndi kunena kwa iye: Ndikunena kwa iwe iye sadzatero, pakuti ndikosatheka kwa iye kukana mawu ake.

35 Tsopano Zeziromu adati kwa anthu: Muone kuti mukukumbukira zinthu izi; pakuti iye wati alipo koma Mulungu m’modzi; komabe iye akuti Mwana wa Mulungu adzabwera, koma sadzapulumutsa anthu ake—monga ngati ali ndi ulamuliro olamula Mulungu.

36 Tsopano Amuleki adatinso kwa iye: Taona iwe wanama, pakuti ukuti ine ndayankhula ngati kuti ndidali ndi ulamuliro wakulamula Mulungu chifukwa ndanena kuti iye sadzapulumutsa anthu m’machimo awo.

37 Ndipo ndikunena kwa iwe kachiwiri kuti iye sangapulumutse iwo m’machimo awo; pakuti ine sindingakane mawu ake, ndipo iye adati kuti palibe chinthu chodetsedwa chingalandire ufumu wa kumwamba; kotero, kodi ungapulumutsidwe bwanji, pokhapokha utalandira ufumu wakumwamba? Kotero, iwe sungapulumutsidwe m’machimo ako.

38 Tsopano Zeziromu adatinso kwa iye: Kodi Mwana wa Mulungu ndiye Atate wa Muyaya?

39 Ndipo Amuleki adati kwa iye: Inde, iye ndiye Atate wa Muyaya wakumwamba ndi dziko lapansi yemweyo, ndi zinthu zonse zimene ziri m’menemo; iye ndi chiyambi ndi chimaliziro, woyamba ndi wotsiliza.

40 Ndipo adzabwera ku dziko lapansi kudzawombola anthu ake; ndipo adzatenga pa iye zolakwitsa za iwo amene akhulupilira mu dzina lake; ndipo awa ndiwo amene adzakhale ndi moyo wamuyaya, ndipo chipulumutso sichidza kwa wina aliyense.

41 Kotero oipa adzakhalabe ngati kuti chiwombolo sichidachitidwe, kupatula kutakhala kumasulidwa kwa zingwe za imfa; pakuti taonani, tsiku likudza limene onse adzauka kwa akufa ndi kuima pamaso pa Mulungu, ndi kuweruzidwa molingana ndi ntchito zawo.

42 Tsopano, kuli imfa yomwe imatchedwa imfa ya kuthupi; ndipo imfa ya Khristu idzamasula nsinga za imfa ya kuthupi, kuti onse adzaukitsidwe kuchokera ku imfa ya kuthupi.

43 Mzimu ndi thupi zidzalumikizananso mu ungwiro wake; zonse ziwalo ndi zolumikizira zake zidzabwenzeretsedwa m’chimake, ngakhale monga m’mene tiliri nthawi ino; ndipo tidzabweretsedwa kuima pamaso pa Mulungu, kudziwa ngati m’mene tikudziwira tsopano, ndipo kukhala ndi kukumbukira kowala cha zolakwa zathu zonse.

44 Tsopano, kubwenzeretsa kumeneku kudzabwera kwa wonse, wonse aakulu ndi ana omwe, wonse womangidwa ndi afulu womwe, wonse amuna ndi akazi womwe, oipa ndi wolungama womwe; ndipo ngakhale sipadzakhala tsitsi lotaika pamutu pawo; koma chirichonse chidzabwezeretsedwa mchimake chaungwiro, monga ziliri pano, kapena mu thupi, ndipo adzabweretsedwa ndi kuiyimitsidwa pa bwalo lamilandu la Khristu Mwanayo, ndi Mulungu Atate, ndi Mzimu Woyera, amene ali Mulungu wa Muyaya m’modzi, kuti aweruzidwe monga mwa ntchito zawo, ngakhale ziri zabwino kapena ngakhale ziri zoipa.

45 Tsopano, taonani, ndayankhula kwa inu zokhudzana ndi imfa ya thupi la chivundi, ndiponso zokhudzana ndi chiukitso cha thupi lachivundi. Ndikunena kwa inu kuti thupi lachivundili lidzaukitsidwa ku thupi lachisavundi, zimene ndi kuchokera ku imfa, ngakhale kuchokera ku imfa yoyamba kupita ku moyo, kuti sadzafanso; mizimu yawo ikulumikizana ndi matupi awo, osagawanika konse; motero thupi lonse kukhala lauzimu ndi lachisavundi, kuti asadzaonenso kuola.

46 Tsopano, pamene Amuleki adamaliza mawu awa anthu adayamba kuzizwa, ndiponso Zeziromu adayamba kunjenjemera. Ndipo motero adathera mawu a Amuleki, kapena izi ndi zonse zimene ndazilemba.

Print