Malembo Oyera
Alima 2


Mutu 2

Amiliki afuna kukhala mfumu ndipo akanidwa ndi mawu a anthu—Otsatira ake amupanga iye mfumu—Aamiliki apanga nkhondo pa Anefi ndipo agonjetsedwa—Alamani ndi Aamiliki agwirizana magulu ankhondo ndipo agonjetsedwa—Alima apha Amiliki. Mdzaka dza pafupifupi 87 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti kumayambiliro a chaka cha chisanu cha ulamuliro wawo kudayamba kukhala mkangano pakati pa anthu; pakuti munthu wina, wotchedwa Amiliki, iye wokhala munthu ochenjeretsa, inde, munthu wanzeru monga mwa nzeru za padziko, iye amene adali wotsatira dongosolo la munthu amene adapha Gideoni ndi lupanga, amene adaphedwa molingana ndi chilamulo—

2 Tsopano Amiliki uyu, mwa kuchenjera kwake, adakokera anthu ambiri kumtsatira pambuyo pake; ngakhale kotero kuti iwo adayamba kukhala amphamvu kwambiri; ndipo adayamba kuyesetsa kukhazikitsa Amiliki kuti akhale mfumu pa anthuwo.

3 Tsopano ichi chidali choopsa kwa anthu a mpingo, ndiponso kwa onse amene sadakokedwepo pambuyo pa kukopa kwa Amiliki; pakuti iwo adadziwa kuti molingana ndi chilamulo chawo kuti zinthu zotere izi zikuyenera kukhazikitsidwa ndi mawu a anthu.

4 Kotero, kukadakhala kotheka kuti Amiliki apeze mawu a anthu, iye, okhala munthu oipa, akadawachotsera iwo maufulu awo ndi mwayi wa mpingo; pakuti chidali cholinga chake kuti awononge mpingo wa Mulungu.

5 Ndipo zidachitika kuti anthu adasonkhana okha pamodzi mudziko lonse, munthu aliyense molingana ndi nzeru zake, kaya adali wa kapena otsutsana ndi Amiliki, mu magulu osiyana, kukhala osemphana kwambiri ndi mikangano yodabwitsa wina ndi mzake.

6 Ndipo motero adasonkhana okha pamodzi kuti aponye mawu awo ponena zokhudzana ndi nkhaniyo; ndipo adayikidwa pamaso pa oweruza.

7 Ndipo zidachitika kuti mawu a anthu adabwera motsutsana ndi Amiliki, kuti iye sadapangidwe mfumu pa anthuwo.

8 Ndipo izi zidachititsa chisangalalo chachikulu m’mitima mwa iwo amene adali otsutsana naye; koma Amiliki adautsa mkwiyo wa iwo amene adali ku mbali yake kukwiira omwe sadali kumbali yake.

9 Ndipo zidachitika kuti iwo adasonkhana okha pamodzi, ndipo adapatura Amiliki kuti akhale mfumu yawo.

10 Tsopano pamene Amiliki adapangidwa mfumu pa iwo adawalamulira iwo kuti atenge zida kumenyana ndi abale awo; ndipo ichi adachita kuti athe kuwaika iwo mu ulamuliro wake.

11 Tsopano anthu a Amiliki adasiyanitsidwa ndi dzina la Amiliki, kutchedwa Aamiliki; ndipo otsalirawo ankatchedwa Anefi, kapena anthu a Mulungu.

12 Kotero anthu a Anefi adali ozindikira cholinga cha Aamiliki, ndipo kotero iwo adakonzekera kukumana nawo; inde, adazikonzekeretsa okha ndi malupanga, ndi zikwanje, ndi mauta, ndi mivi, ndi miyala, ndi malegeni, ndi zida zankhondo zamitundu yonse, zosiyanasiyana.

13 Ndipo choncho iwo adali okonzeka kukumana ndi Aamiliki pa nthawi yakubwera kwawo. Ndipo padali atsogoleri ankhondo osankhidwa, ndi apamwamba pa atsogoleri ankhondo, ndi akulu ankhondo, monga mwa kuchuluka kwawo.

14 Ndipo zidachitika kuti Amiliki adakonzekeretsa anthu ake ndi zida zankhondo za mitundu yonse zosiyanasiyana; ndipo adasankhanso olamulira ndi atsogoleri pa anthu ake, kuti atsogolere iwo ku nkhondo kokamenyana ndi abale awo.

15 Ndipo zidachitika kuti Aamiliki adafika pa phiri la Amunihu, limene lidali ku m’mawa kwa mtsinje wa Sidoni, umene udadutsa pafupi ndi dziko la Zarahemula, ndipo kumeneko adayamba kumenya nkhondo ndi Anefi.

16 Tsopano Alima, pokhala mkulu wa oweruza ndi kazembe wa anthu a Nefi, potero adapita ndi anthu ake, inde, ndi atsogoleri ankhondo ake, ndi apamwamba a atsogoleri ankhondo, inde ndi akulu ankhondo, kukamenyana ndi Aamiliki ku nkhondo.

17 Ndipo adayamba kupha Aamiliki pa phiri la kum’mawa kwa Sidoni. Ndipo Aamiliki adalimbana ndi Anefi ndi mphamvu zazikulu, kufikira kuti Anefi ambiri adagwa pamaso pa Aamiliki.

18 Komabe Ambuye adalimbitsa dzanja la Anefi, kuti adapha Aamiliki ndi kuwagonjetsa kwakukulu, kufikira iwo ayamba kuthawa pamaso pawo.

19 Ndipo zidachitika kuti Anefi adawathamangitsa a Aamiliki tsiku lonse, ndipo adawapha ndi kupha kwakukulu, kufikira kuti idaphedwa miyoyo ya Aamiliki zikwi khumi ndi ziwiri mphambu zisanu ndi makumi atatu ndi miyoyo iwiri; ndipo idaphedwa miyoyo ya Anefi zikwi zisanu ndi chimodzi ndi mphambu mazana asanu ndi makumi asanu ndi chimodzi ndi mphambu ziwiri.

20 Ndipo zidachitika kuti pamene Alima sakadathanso kulondora Aamiliki adapangitsa anthu ake kuti akhome ma hema awo mu chigwa cha Gideoni, chigwacho chidatchedwa motsatira Gideoni amene adaphedwa ndi dzanja la Neho ndi lupanga; ndipo mu chigwa chimenechi Anefi adakhoma ma hema awo usikuwo.

21 Ndipo Alima adatumiza akazitape kuti atsatire otsalira a Aamiliki, kuti iye adziwe zolinga zawo ndi ziwembu zawo, kotero kuti iye adzitchinjirize kwa iwo, kuti iye asunge anthu ake kuti asawonongedwe.

22 Tsopano iwo amene adawatumiza kukasuzumira ku msasa wa Aamiliki adali otchedwa Zeramu ndi Amunori, ndi Manti, ndi Limheri; awa adali iwo amene adapita ndi anthu awo kukasuzumira ku msasa wa Aamiliki.

23 Ndipo zidachitika kuti m’mawa mwake adabwelera mu msasa wa Anefi mwa changu, ali odabwa kwambiri, ndipo adagwidwa ndi mantha aakulu, nati:

24 Taonani, tidatsatira msasa wa Aamiliki, ndipo mozizwa kwakukulu kwa ife, mu dziko la Minoni, pamwamba pa dziko la Zarahemula, m’njira ya dziko la Nefi, tidaona chikhamu cha Alamani; ndipo taonani, Aamiliki agwirizana nawo.

25 Ndipo iwo ali pa abale athu m’dzikomo; ndipo akuthawa pamaso pawo ndi ziweto zawo, ndi akazi awo, ndi ana awo, kuyandikira ku mzinda wathu; ndipo pokhapokha titachita changu alanda mzinda wathu, ndipo makolo athu ndi akazi athu, ndi ana athu aphedwa.

26 Ndipo zidachitika kuti anthu a Nefi adatenga mahema awo, ndikunyamuka kuchoka m’chigwa cha Gideoni kupita ku mzinda wawo, umene udali mzinda wa Zarahemula.

27 Ndipo taonani, pamene iwo adali kuoloka mtsinje wa Sidoni, Alamani ndi Aamiliki, okhala ochuluka pafupifupi, ngati mchenga wa ku nyanja, adabwera kwa iwo kuti awawononge.

28 Komabe, Anefi atalimbitsidwa ndi dzanja la Ambuye, atapemphera mwamphamvu kwa iye kuti awawombole kuchokera m’manja mwa adani awo, choncho Ambuye adamva kulira kwawo, ndipo adawalimbitsa iwo, ndipo Alamani ndi Aamiliki adagwa pamaso pawo.

29 Ndipo zidachitika kuti Alima adamenyana ndi Amiliki ndi lupanga, maso ndi maso; ndipo adalimbana mwamphamvu, wina ndi mzake.

30 Ndipo zidachitika kuti Alima, okhala munthu wa Mulungu, okhala ndi chikhulupiliro chachikulu, adafuula, nati: O Ambuye, mundichitire chifundo ndi kupulumutsa moyo wanga, kuti ndikhale chida m’manja mwanu kupulumutsa ndi kusunga anthu awa.

31 Tsopano pamene Alima adanena mawu awa adamenyananso ndi Amiliki; ndipo adalimbitsidwa kufikira kuti adapha Amiliki ndi lupanga.

32 Ndipo adalimbananso ndi mfumu ya Alamani; koma mfumu ya Alamani idathawa pamaso pa Alima ndipo idatuma achitetezo ake kuti akamenyane ndi Alima.

33 Koma Alima, ndi achitetezo ake, adalimbana ndi achitetezo a mfumu ya Alamani mpakana adawapha ndi kuwathamangitsa iwo kubwelera.

34 Ndipo choncho iye adalambula bwalo, kapena mphepete mwa mtsinje, umene udali kumadzulo kwa mtsinje wa Sidoni, kuponya matupi a Alamani amene adaphedwa m’madzi a Sidoni, kuti mwa kutero anthu ake akakhale ndi malo oti awolokere ndi kulimbana ndi Alamani ndi Aamiliki ku madzulo kwa mtsinje wa Sidoni.

35 Ndipo zidachitika kuti pamene onse adawoloka mtsinje wa Sidoni kuti Alamani ndi Aamiliki adayamba kuthawa pamaso pawo, ngakhale kuti adali ochuluka kwambiri kuti sakadatha kuwerengeka.

36 Ndipo adathawa pamaso pa Anefi kuyandikira m’chipululu chimene chidali kumadzulo ndi kumpoto, kutali kupitilira malire a dziko; ndipo Anefi adawathamangitsa ndi mphamvu zawo ndipo adawapha.

37 Inde, adakumanizidwa paliponse, ndi kuphedwa ndi kuthamangitsidwa, kufikira adabalalitsidwa ku madzulo, ndi kumpoto, kufikira adafika ku chipululu, chimene chimatchedwa Herimonti; ndipo lidali gawo limeneli la chipululu limene lidali lodzala ndi zilombo zakuthengo ndi zolusa.

38 Ndipo zidachitika kuti ambiri adafa m’chipululu chifukwa cha mabala awo, ndipo adadyedwa ndi zilombozo ndiponso miimba ya mlengalenga; ndipo mafupa awo adapezeka ndi kuwunjikidwa pa mthaka.