Malembo Oyera
Alima 21


Nkhani ya kulalika kwa Aroni, ndi Muloki, ndi abale awo, kwa Alamani.

Yophatikiza mitu 21 mpaka 25.

Mutu 21

Aroni aphunzitsa a Amaleki za Khristu ndi Chitetezero Chake—Aroni ndi abale ake amangidwa mu ndende ku Midoni—Atapulumutsidwa, iwo aphunzitsa mu masunagoge ndi kupangitsa ambiri kutembenuka—Lamoni apereka ufulu wachipembedzo kwa anthu a m’dziko la Ismaeli. Mdzaka dza pafupifupi 90–77 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano pamene Amoni ndi abale ake adadzilekanitsa wokha m’malire a dziko la Alamani, taonani Aroni adayamba ulendo wake kuyandikira dziko lomwe limatchedwa ndi Alamani kuti Yerusalemu, kulitcha ilo potsatira dziko lomwe makolo awo adachokera; ndipo lidali kutali kophatikizana ndi malire a Mormoni.

2 Tsopano Alamani ndi Aamaleki ndi anthu a Amuloni adamanga mzinda waukulu, umene adautcha Yerusalemu.

3 Tsopano Alamani mwa iwo wokha adali ouma mokwanira, koma Aamaleki ndi Aamuloni adali oumitsitsa; kotero iwo adachititsa Alamani kuti aumitse mitima yawo, kuti akule mu mphamvu m’kuipa ndi zonyansa.

4 Ndipo zidachitika kuti Aroni adabwera ku mzinda wa Yerusalemu, ndipo choyamba adayamba kulalikira kwa Aamaleki. Ndipo iye adayamba kulalikira kwa iwo mu masunagoge mwawo, pakuti iwo adamanga masunagoge potsatira dongosolo la Neho; pakuti ambiri mwa Aamaleki ndi Aamuloni adali a dongosolo la Neho.

5 Kotero, pamene Aroni adalowa mu imodzi mwa masunagoge awo kuti alalikire kwa anthu, ndipo pamene iye ankayankhula kwa iwo, taonani pamenepo padadzuka m’Amaleki m’modzi ndi kuyamba kulimbana naye, nati: Kodi ndi chiyani chomwe iwe wachitira umboni? Kodi udamuona mngelo? N’chifukwa chiyani angelo samaonekera kwa ife? Taona kodi anthu awa sali abwino monga anthu ako?

6 Iweyo watinso, pokhapokha ife tilape, ife tidzawonongedwa. Iwe ukudziwa bwanji maganizo ndi zolinga za mitima yathu? Iwe ukudziwa bwanji kuti ife tili ndi chifukwa cholapira? Iwe ukudziwa bwanji kuti ife sitili anthu olungama? Taona, ife tamanga malo opatulika, ndipo timasonkhana tonse pamodzi kulambira Mulungu. Ife timakhulipilira kuti Mulungu adzapulumutsa anthu wonse.

7 Tsopano Aroni adati kwa iye: Kodi ukukhulupilira kuti Mwana wa Mulungu adzabwera kudzawombola anthu ku machimo awo?

8 Ndipo munthuyo adati kwa iye: Ife sitikhulupilira kuti iwe ukudziwa chinthu choterocho. Ife sitikhulupilira mu miyambo yopusayi. Ife sitikukhulupilira kuti iwe umadziwa za zinthu ziri nkudza, kapena kukhulupilira kuti mokolo anu ndiponso makolo athu ankadziwa zokhudzana ndi zinthu zimene iwo adayankhula, za izo zimene ziri nkudza.

9 Tsopano Aroni adayamba kutsekula malembo oyera kwa iwo okhudzana ndi kubwera kwa Khristu, ndiponso okhudzana ndi chiukitso cha akufa, ndipo kuti kulibe chiwombolo kwa anthu pokhapokha kudzera mwa imfa ndi mazunzo a Khristu, ndi chitetezero cha mwazi wake.

10 Ndipo zidachitika kuti pamene iye adayamba kutanthauzira zinthu izi kwa iwo, adayamba kukwiya naye, ndi kuyamba kumunyoza iye; ndipo sadamvere mawu amene iye ankayankhula.

11 Kotero, pamene iye adaona kuti iwo sakumvera mawu ake, adawachokera mu sunagoge mwawo, ndipo adabwera ku mudzi wina umene unkatchedwa Ani-Anti, ndipo kumeneko iye adapeza Muloki akulalikira mawu kwa iwo; ndiponso Ama ndi abale ake. Ndipo iwo adakangana ndi ambiri pa mawuwo.

12 Ndipo zidachitika kuti iwo adaona kuti anthuwo aumitsa mitima yawo, kotero iwo adachoka ndi kubwera mu dziko la Midoni. Ndipo iwo adalalikira mawu kwa ambiri, ndipo ochepa adakhulupilira pa mawu amene iwo adaphunzitsa.

13 Komabe, Aroni ndi gulu lina la abale ake adatengedwa ndi kuponyedwa mu ndende, ndipo otsala mwa iwo adathawa kutuluka mu dziko la Midoni kupita ku zigawo zozungulira.

14 Ndipo iwo amene adaponyedwa mu ndende adazunzika zinthu zambiri, ndipo adapulumutsidwa ndi dzanja la Lamoni ndi Amoni, ndipo adadyetsedwa ndi kuvekedwa.

15 Ndipo adapitanso kukalalikira mawu, ndipo iwo adapulumutsidwa kwa nthawi yoyamba kutuluka kundende; ndipo moteremu iwo adazunzika.

16 Ndipo adapita kulikonse kumene adatsogozedwa ndi Mzimu wa Ambuye, kulalikira mawu a Mulungu mu sunagoge aliyense wa Aamaleki, kapena mu misonkhano iliyonse ya Alamani imene iwo akadaloledwa.

17 Ndipo zidachitika kuti Ambuye adayamba kuwadalitsa iwo, kotero kuti adabweretsa ambiri ku chidziwitso cha choonadi; inde, adatsimikizira ambiri za machimo awo, ndi za miyambo ya makolo awo, zimene zidali zosalondola.

18 Ndipo zidachitika kuti Amoni ndi Lamoni adabwelera kuchokera dziko la Midoni kupita ku dziko la Ismaeli, limene lidali dziko la cholowa chawo.

19 Ndipo mfumu Lamoni sadalole kuti Amoni amutumikire iye, kapena kuti akhale m’dzakazi wake.

20 Koma iye adachititsa kuti pakhale ma sunagoge omangidwa mu dziko la Ismaeli; ndipo iye adachititsa kuti anthu ake, kapena anthu amene adali pansi pa ulamuliro wake, asonkhane wonse pamodzi.

21 Ndipo iye adakondwera pa iwo, ndipo iye adawaphunzitsa zinthu zambiri. Ndipo iyenso adalengeza kwa iwo kuti adali anthu amene adali pansi pake, ndipo kuti adali anthu aufulu, kuti adali omasuka mu kuponderezedwa kwa mfumu, atate ake; pakuti atate ake adapereka kwa iye kuti alamulire pa anthu amene adali mu dziko la Ismaeli, ndi mu madera onse ozugulira

22 Ndiponso iye adalengeza kwa iwo kuti akakhale ndi ufulu wa kupembedza Ambuye Mulungu wawo molingana ndi zokhumba zawo, mu malo ena aliwonse iwo adalimo, ngati ali mu dziko limene liri pansi pa ulamuliro wa mfumu Lamoni.

23 Ndipo Amoni adalalikira kwa anthu a mfumu Lamoni; ndipo zidachitika kuti iye adawaphunzitsa iwo zinthu zonse zokhudzana ndi zinthu zokhudza chilungamo. Ndipo iye adawachenjeza iwo tsiku ndi tsiku, mwa khama lonse; ndipo iwo adamvetsera ku mawu ake, ndipo iwo adali achangu pakusunga malamulo a Mulungu.

Print