Nkhani ya anthu a Nefi, ndi nkhondo ndi kusagwirizana kwawo mu masiku a Helamani, molingana ndi zolemba za Helamani, zimene adasunga m’masiku ake.
Yophatikiza mitu 45 mpaka 62.
Mutu 45
Helamani akhulupilira mawu a Alima—Alima anenera za chiwonongeko cha Anefi—Iye adalitsa ndi kutembelera dzikolo—Alima akhonza kukhala kuti adatengedwa ndi Mzimu, monga ngati Mose—Kusagwirizana kukula mu Mpingo. Mdzaka dza pafupifupi 73 Yesu asadabadwe.
1 Taonani tsopano zidachitika kuti anthu a Nefi adakondwa kwambiri, chifukwa Ambuye adawawomboranso kuchokera m’manja mwa adani awo; kotero iwo adapereka chiyamiko kwa Ambuye Mulungu wawo; inde, ndipo adasala kudya kwambiri ndi kupemphera kwambiri, ndipo adapembedza Mulungu ndi chisangalalo chachikulu kwambiri.
2 Ndipo zidachitika mu chaka cha khumi ndi chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, kuti Alima adabwera kwa mwana wake Helamani ndipo adati kwa iye: Kodi ukukhulupilira mawu amene ine ndidayankhula kwa iwe okhudzana ndi zolemba zimene zakhala zikusungidwa?
3 Ndipo Helamani adati kwa iye: Inde, ndikukhulupilira.
4 Ndipo Alima adatinso: Kodi iwe ukukhulupilira mwa Yesu Khristu, amene atadzabwere?
5 Ndipo iye adati: Inde, ndikukhulupilira mawu onse amene inu mwayankhula.
6 Ndipo Alima adatinso kwa iye: Kodi iwe udzasunga malamulo anga?
7 Ndipo iye adati: Inde, ndidzasunga malamulo anu ndi mtima wanga onse.
8 Ndiye Alima adati kwa iye: Odala ndi iwe; ndipo Ambuye adzakuchititsa bwino mu dzikoli.
9 Koma taona, ndiri ndi zinazake zoti ndinenere kwa iwe; koma zimene ndikunenera kwa iwe, iwe usadzaziulure; inde, zimene ndikunenera kwa iwe zisazadziwike, ngakhale kufikira uneneriwu utakwaniritsidwa; kotero ulembe mawu amene ine nditanene.
10 Ndipo awa ndiwo mawuwo: Taona, ndikuona kuti anthu awa omwewa, Anefi, malingana ndi mzimu wa chibvumbulutso umene uli mwa ine, mu zaka mazana anayi kuchokera pa nthawi imene Yesu Khristu adzadzionetsera yekha kwa iwo, adzacheperachepera m’kusakhulupilira.
11 Inde, ndipo kenako iwo adzaona nkhondo ndi miliri, inde, zilala ndi kukhetsa mwazi, ngakhale kufikira anthu a Nefi adzatha psiti—
12 Inde, ndipo izi chifukwa cha kucheperachepera m’kusakhulupira ndi kugwa mu ntchito za mdima, ndipo kutayilira, ndi zoipa zamitundu yonse; inde, ndikunena kwa iwe, kuti chifukwa iwo adzachimwira motsutsana ndi kuwala kwakukulu ndi chidziwitso, inde, ndikunena kwa iwe, kuti kuchokera pa tsikulo, mpakana m’badwo wa chinayi siudzatha pasadafike kuipa kwakukuluku.
13 Ndipo pamene tsiku lalikululo lidzafika, taona, nthawi ifika posachedwa imene iwo amene tsopano, kapena mbewu ya iwo amene tsopano awerengedwa pakati pa anthu a Nefi, sadzawerengedwanso pakati pa anthu a Nefi.
14 Koma aliyense amene atsalira, ndipo sadawonongedwe mu tsiku ilo lalikulu ndi loopsya, adzawerengedwa pakati pa Alamani, ndipo adzakhala ngati iwo, onse, kupatula iwo ochepa amene adzatchedwe ophunzira a Ambuye; ndipo awo Alamani adzawalondola kufikira atatheratu. Ndipo tsopano, chifukwa cha kusaweruzika, ulosi uwu udzakwaniritsidwa.
15 Ndipo zidachitika kuti Alima atamaliza kuyankhula zinthu izi kwa Helamani, adamudalitsa iye, ndiponso ana ake ena aamuna; ndiponso iye adadalitsa dziko lapansi kwa ubwino wa olungama.
16 Ndipo iye adati: Akutero Ambuye Mulungu—Lotembeleredwa lidzakhala dzikoli, inde, dziko ili, kwa dziko lililonse, mtundu, chinenero, ndi anthu, ku chiwonongeko, amene amachita zoipa, pamene iwo adzakhwimitsitsa; ndipo monga ndanena chomwecho zidzakhala; pakuti ili ndi thembelero ndi mdalitso wa Mulungu pa dzikoli, pakuti Ambuye sangathe kuyang’ana patchimo ndi mlingo ngakhale wochepa wa chilolezo.
17 Ndipo tsopano, pamene Alima adanena mawu awa adadalitsa mpingo, inde, onse amene adzaima olimbika mu chikhulupiliro kuchokera panthawiyi kupita kutsogolo.
18 Ndipo pamene Alima adachita izi iye adachoka ku dziko la Zarahemula, ngati kuti akupita ku dziko la Meleki. Ndipo zidachitika kuti sadamvekenso; monga pa za imfa yake kapena kuikidwa ife sitikudziwa za izo.
19 Taonani, ichi tikudziwa, kuti iye adali munthu olungama; ndipo mawu adabuka mu mpingo kuti iye adatengedwa ndi Mzimu, kapena kuikidwa ndi dzanja la Ambuye, monga ngati Mose. Koma taonani, malembo oyera amati Ambuye adatenga Mose kwa iye mwini; ndipo ife tikuganiza kuti iye walandiranso Alima mu mzimu, kwa iye mwini; kotero, pachifukwa ichi ife sitikudziwa kanthu kokhudzana ndi imfa ndi kuikidwa kwake.
20 Ndipo tsopano zidachitika kumayambiliro a chaka cha khumi ndi chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, kuti Helamani adapita pakati pa anthu kukalalikira mawu kwa iwo.
21 Pakuti taonani, chifukwa cha nkhondo zawo ndi Alamani ndi kuchuluka timikangano ndi chisokonezo chimene chidali pakati pa anthuwo, kudakhala kofunikira kwambiri kuti mawu a Mulungu alalikidwe pakati pawo, inde, ndipo kuti lamulo liperekedwe mu mpingo wonse.
22 Kotero Helamani ndi abale ake adapita kukakhazikitsanso mpingo mu dziko lonselo, inde, mu mzinda uliwonse kuzungulira dziko lonselo limene lidatengedwa ndi anthu a Nefi. Ndipo zidachitika kuti iwo adasankha ansembe ndi aphunzitsi kuzungulira dziko lonselo, pa mipingo yonse.
23 Ndipo tsopano zidachitika kuti Helamani ndi abale ake atatha kusankha ansembe ndi aphunzitsi pa mipingoyo kuti padauka kusagwirizana pakati pawo, ndipo iwo sadamvetsere mawu a Helamani ndi abale ake;
24 Koma iwo adakula m’kunyada, ndikudzikweza mu mitima yawo, chifukwa cha chuma chawo chochuluka kwambiri; kotero iwo adalemera m’maso mwawo, ndipo sakadamvetsera ku mawu awo, kuti ayende mowongoka pamaso pa Mulungu.