Malembo Oyera
Alima 61


Mutu 61

Pahorani auza Moroni za kuwukira ndi kupanduka kotsutsana ndi boma—Anthu amfumu atenga Zarahemula ndipo agwirizana ndi Alamani—pahorani apempha chithandizo cha nkhondo motsutsana ndi opandukira. Mdzaka dza pafupifupi 62 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, tsopano zidachitika kuti posakhalitsa Moroni atatumiza kalata yake kwa kazembe wamkulu, iye adalandira kalata kuchoka kwa Pahorani, kazembe wamkulu. Ndipo mawu amene iye adalandira ndi awa:

2 Ine, Pahorani, amene ndine kazembe wamkulu wa dziko lino, ndikutumiza mawu awa kwa Moroni, mkulu wa nkhondo pa ankhondo. Taona, ndikunena kwa iwe, Moroni, kuti sindili osangalala mu masautso ako aakulu, inde, zikumvetsa chisoni moyo wanga.

3 Koma taona, kuli iwo amene akusangalala mu masautso ako, inde, kotero kuti iwo awukira mu upandu motsutsana nane, ndiponso iwo ena mwa anthu anga amene ali aufulu, inde, ndi iwo amene awukira ndi ochuluka kwambiri.

4 Ndipo ndi iwo amene akufuna kutenga mpando wachiweruziro kwa ine amene akhala akuchititsa mphulupulu zazikulu zimenezi; pakuti agwiritsa ntchito kusyasyalika kwakukulu, ndipo asocheletsa mitima ya anthu ambiri, zimene zidzachititse masautso aakulu pakati pathu; iwo akaniza zokudya zathu, ndipo awopsyeza anthu omasulidwa kuti asabwere kwa iwe.

5 Ndipo taona, iwo andithamangitsa ine pamaso pawo, ndipo ndathawira ku dziko la Gideoni, ndi anthu ochuluka monga kudaliri kotheka kuti ndiwatenge.

6 Ndipo taona, ndatumiza chilengezo kuzungulira chigawo chino cha dziko; ndipo taona, akubwera kwa ife tsiku lililonse, ku zida zawo, potetezera dziko lawo ndi ufulu wawo, ndi kubwenzera zolakwika zathu.

7 Ndipo iwo abwera kwa ife, kotero kuti iwo amene awukira mu upandu motsutsana nafe ayamba kukhala wosamvera, inde, kufikira kuti iwo akutiopa ife ndipo sakuyerekeza kubwera kudzamenyana nafe ku nkhondo.

8 Iwo adalanda dziko, kapena mzinda, wa Zarahemula; asankha mfumu pa iwo, ndipo iye walembera kwa mfumu ya Alamani, mumene iye waphatikizana mum’gwirizano ndi iye; mumene m’gwirizano wake iye wavomeleza kusunga mzinda wa Zarahemula, umene kusungidwa kwake iye akuganiza kuti kudzathandizira Alamani kugonjetsa dziko lotsaliralo, ndipo iye adzaikidwa mfumu pa anthu awa pamene iwo adzagonjetsa pansi pa Alamani.

9 Ndipo tsopano, mu kalata yako iwe wandidzudzula ine, koma zilibe kanthu; sindidakwiye, koma ndikukondwera mu kukula kwa mtima wako. Ine, Pahorani, sindikufuna mphamvu, kupatula kungobwelera pa mpando wachiweruziro kuti nditeteze ma ufulu a anthu anga. Moyo wanga waima nji mu ufulu umene Mulungu watimasula ife.

10 Ndipo tsopano taona, ife tidzakaniza zoipa ngakhale mpaka kukhetsa mwazi. Sitidzakhetsa mwazi wa Alamani ngati iwo adzakhala mu dziko lawo.

11 Sitidzakhetsa mwazi wa abale athu ngati iwo sadzawukira mu upandu ndi kutenga lupanga motsutsana nafe.

12 Tidzadzipereka tokha ku goli la ukapolo ngati kuli kofunikira ndi chilungamo cha Mulungu, kapena ngati iye adzatilamula ife kutero.

13 Koma taona iye sakutilamula ife kuti tidzipereke tokha kwa adani athu, koma kuti tiike chikhulupiliro chathu mwa iye, ndipo iye adzatiwombola ife.

14 Kotero, m’bale wanga okondedwa, Moroni, tiye tikane zoipa, ndipo chilichonse choipa chimene sitingathe kuchikana ndi mawu athu, inde, monga upandu ndi mpatuko, tiye tizikane ndi malupanga athu, kuti tibwenzeretse ufulu wathu, kuti tithe kukondwera mu mwayi waukulu wa mpingo wathu, ndi mu chifukwa cha Muwomboli wathu ndi Mulungu wathu.

15 Kotero, ubwere kwa ine mwachangu ndi anthu ako ochepa, ndi kusiya otsalawo mu ulamuliro wa Lehi ndi Teyankumu; uwapatse iwo mphamvu zoyendetsa nkhondo mu chigawo chimenecho cha dziko, molingana ndi Mzimu wa Mulungu, umene ulinso mzimu wa ufulu omwe uli mwa iwo.

16 Taona ndatumiza zakudya zochepa kwa iwo, kuti iwo asawonongeke kufikira iwe utabwera kwa ine.

17 Sonkhanitsa pamodzi ankhondo aliwonse womwe ungathe pogubira kuno, ndipo tidzapita mwachangu motsutsana ndi iwo ogalukirawo, mu mphamvu ya Mulungu wathu molingana ndi chikhulupiliro chimene chili mwa ife.

18 Ndipo tidzatenga mzinda wa Zarahemula, kuti tikhale ndi chakudya chambiri chotumiza kwa Lehi ndi Teyankumu; inde, tidzapita kolimbana nawo mu mphamvu ya Ambuye, ndipo tidzathetsa zoipa zazikulu zimenezi.

19 Ndipo tsopano, Moroni, ndili osangalala pakulandira kalata yako, pakuti ndidali penapake odandaula zokhudzana ndi zomwe tingachite, ngati zingakhale zolondora kwa ife kupita kolimbana ndi abale athu.

20 Koma iwe wati, pokhapokha iwo alape Ambuye akulamula iwe kuti upite motsutsana nawo.

21 Ona kuti umulimbikitse Lehi ndi Teyankumu mwa Ambuye; uwauze kuti asaope, pakuti Mulungu adzawapulumutsa, inde, ndiponso onse amene adzaima nji pa ufulu umene Mulungu waamasula nawo. Ndipo tsopano ndikutseka kalata yanga kwa m’bale wanga okondedwa, Moroni.

Print