Malembo Oyera
Alima 23


Mutu 23

Ufulu wachipembedzo ulengezedwa—Alamani mu maiko ndi mizinda isanu ndi iwiri atembenuka—Adzitcha okha a Anti-Nefi-Lehi ndipo amasulidwa ku thembelero—Aamaleki ndi Aamuloni akana choonadi. Mdzaka dza pafupifupi 90–77 Yesu asadabadwe.

1 Taonani, tsopano zidachitika kuti mfumu ya Alamani idatumiza chilengezo pakati pa anthu ake wonse, kuti iwo asaike manja awo pa Amoni, kapena Aroni, kapena Omineri, kapena Himuni, kapena aliyense wa abale awo amene adzapite kukalalikira mawu a Mulungu, m’malo ena aliwonse amene iwo adzakhalamo mu gawo lirilonse la dziko lawo.

2 Inde, iye adatumiza chilamulo pakati pawo, kuti asaike manja awo pa iwo kuti awamange, kapena kuwaponya mu ndende; ngakhale kuwalavulira iwo, kepana kuwakantha iwo, kapena kuwatulutsa iwo m’ma sunagoge awo, kapena kuwakwapula, ngakhale kuwagenda miyala, koma kuti iwo akhale ndi ufulu olowa m’nyumba zawo, ndiponso m’makachisi awo, ndi m’malo awo opatulika.

3 Ndipo motero iwo adzitha kupita ndi kulalikira mawu molingana ndi zokhumba zawo, pakuti mfumuyo idali itatembenukira kwa Ambuye, ndi banja lake lonse; n’chifukwa chake idatumiza chilengezocho m’dziko lonselo kwa anthu ake, kuti mawu a Mulungu asakhale ndi chotchinga, koma kuti afalikire m’dziko lonselo, kuti anthu ake akathe kutsimikizika zokhudzana ndi miyambo yoipa ya makolo awo, ndipo kuti akathe kutsimikizika kuti wonse adali pachibale, ndipo kuti iwo sakuyenera kupha, kapena kulandana, kapena kubelana, kapena kuchita chigololo, kapena kuchita mtundu uliwonse wa zoipa.

4 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene mfumuyo idatumiza chilengezochi, kuti Aroni ndi abale ake adayenda kuchokera mzinda ndi mzinda, ndipo kuchokera nyumba yopembedzera imodzi kupita ku inzake, akukhazikitsa mipingo, ndi kupatula ansembe ndi aphunzitsi m’dziko lonselo la Alamani, kuti akalalikire ndi kuphunzitsa mawu a Mulungu pakati pawo; ndipo motero adayamba kukhala ndi chipambano chachikulu.

5 Ndipo zikwizikwi zidabweretsedwa ku chidziwitso cha Ambuye, inde, zikwizikwi zidabweretsedwa m’kukhulupilira mu miyambo ya Anefi; ndipo adaphunzitsidwa zolemba ndi ma uneneri amene adaperekedwa ngakhale kufikira ku nthawi yatsopano.

6 Ndipo motsimikizikika monga Ambuye ali wamoyo, ndimotsimikizikadi monga ambiri amene anakhulupilira, kapena monga ambiri adabweretsedwa ku chidziwitso cha choonadi, kudzera mu ulaliki wa Amoni ndi abale ake, molingana ndi mzimu wa chibvumbulutso ndi uneneri, ndi mphamvu ya Mulungu akuchita zodabwitsa mwa iwo—inde, ndikunena ndi inu, monga Ambuye ali wa moyo, monga ambiri a Alamani adakhulipilira mu ulaliki wawo, ndipo adatembenukira kwa Ambuye, sadagwenso.

7 Pakuti iwo adakhala anthu wolungama; iwo adatula pansi zida za kuwukira kwawo, kuti sadamenyanenso ndi Mulungu, kapena kumenyana ndi aliyense wa abale awo.

8 Tsopano, awa ndiwo amene adatembenukira kwa Ambuye:

9 Anthu achilamani amene adali mu dziko la Ismaeli;

10 Ndiponso anthu achilamani amene adali mu dziko la Midoni.

11 Ndiponso anthu achilamani amene adali mu mzinda wa Nefi.

12 Ndiponso anthu Achilamani amene adali mu dziko la Shilomu, ndipo amene adali mu dziko la Shemuloni, ndi mu mzinda wa Lemueli, ndi mu mzinda wa Shimunilomu.

13 Ndipo awa ndiwo maina a mizinda ya Alamani amene adatembenukira kwa Ambuye; ndipo awa ndiwo amene adatula pansi zida zawo za kuwukira, inde, zida zawo zonse zankhondo; ndipo wonse adali Alamani.

14 Ndipo Aamaleki sadatembenuke, kupatula m’modzi yekha; ngakhale padalibe m’modzi mwa Aamuloni; koma iwo adaumitsa mitima yawo, ndiponso mitima ya Alamani a m’magawo aliwonse amene iwo amakhalamo, inde, ndi midzi yawo yonse, ndi mizinda yawo yonse.

15 Kotero, tatchula maina a mizinda yonse ya Alamani mumene iwo adalapa ndi kubwera ku chidziwitso cha choonadi, ndipo adatembenuka.

16 Ndipo tsopano zidachitika kuti mfumu ndi iwo amene adatembenuka adakhumba kuti akhale ndi dzina, kuti motero adzilekanitsidwa kwa abale awo, kotero mfumu idakambirana ndi Aroni ndi ambiri mwa ansembe awo, zokhudzana ndi dzina lakuti iwo atengere pa iwo, kuti iwo adzizindikirika.

17 Ndipo zidachitika kuti adadzitcha maina awo Aanti-Nefi-Lehi; ndipo ankatchulidwa dzina limeneli ndipo sadatchulidwenso Alamani.

18 Ndipo adayamba kukhala anthu akhama kwambiri; inde, ndipo adali anthu amsangala ndi Anefi; kotero, adatsegulira ubale ndi iwo, ndipo thembelero la Mulungu silidawatsatilenso.