Malembo Oyera
Alima 4


Mutu 4

Alima abatiza zikwizikwi za otembenuka—Kusaweruzika kulowa mu mpingo, ndipo kupita patsogolo kwa mpingo kusokonezedwa—Nefiha asankhidwa kukhala wamkulu wa oweruza—Alima, monga mkulu wansembe, adzipereka yekha ku utumiki. Mdzaka dza pafupifupi 86–83 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidachitika m’chaka cha chisanu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, mudalibe mikangano kapena nkhondo mu dziko la Zarahemula.

2 Koma anthu adali wosautsika, inde, wosautsika kwambiri chifukwa cha kutaika kwa abale awo, ndiponso chifukwa cha kutaika kwa nkhosa zawo ndi ng’ombe zawo, ndiponso kutaika kwa minda yawo ya mbewu, imene idapondedwa pansi ndi kuwonongedwa ndi Alamani.

3 Ndipo aakulu adali masautso awo kuti munthu aliyense adali ndi chifukwa cholilira; ndipo adakhulupilira kuti zidali ziweruzo za Mulungu zotumizidwa pa iwo chifukwa cha kuipa kwawo ndi zonyasa zawo, kotero adadzutsidwa kuti akumbukire udindo wawo.

4 Ndipo adayamba kukhazikitsa mpingo mokwanira; inde, ambiri adabatizidwa m’madzi a Sidoni ndipo adaphatikizidwa mu mpingo wa Mulungu; inde, adabatizidwa ndi dzanja la Alima, amene adapatulidwa kukhala mkulu wansembe pa anthu amumpingo, ndi dzanja la atate ake Alima.

5 Ndipo zidachitika kuti mu chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ulamuliro wa oweruza kudali miyoyo pafupifupi mazana a zikwi zitatu ndi mazana asanu amene adadzigwirizanitsa wokha ku mpingo wa Mulungu ndipo adabatizidwa. Ndipo choncho chidatha chaka cha chisanu ndi ziwiri cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, ndipo padali mtendere wachikhalire mu nthawi yonseyi.

6 Ndipo zidachitika mu chaka cha chisanu ndi zitatu cha ulamuliro wa oweruza, kuti anthu a mu mpingo adayamba kukula m’kunyada, chifukwa cha chuma chawo chambiri, silika zawo zabwino kwambiri, ndi nsalu zawo zopota bwino, ndipo chifukwa cha nkhosa zawo zochuluka ndi ng’ombe, ndi golide wawo ndi siliva wawo, ndi mitundu yonse ya zinthu zamtengo wapali, zimene iwo adazipeza mwa malonda awo; ndipo mu zinthu zonsezi iwo adakuzidwa m’kunyada kwa maso awo, pakuti adayamba kuvala zovala za mtengo wapatali.

7 Tsopano ichi chidali chiyambi cha kusautsika kwakukulu kwa Alima, inde, ndi kwa anthu ambiri amene Alima adawapatura kukhala aphunzitsi, ndi ansembe, ndi akulu pa mpingo; inde, ambiri mwa iwo adali ndi chisoni kwambiri chifukwa cha zoipa zimene adaziona kuti zayamba kuchitika pakati pa anthu awo.

8 Pakuti iwo adayang’ana ndi kuona ndi chisoni chachikulu kuti anthu amumpingo adayamba kudzikuza m’kunyada kwa maso awo, ndi kuyika mitima yawo pa chuma ndi zithu zachabechabe za dziko lapansi, kuti iwo adayamba kunyozana, wina ndi mzake, ndipo adayamba kuzunza iwo amene sadakhulupilire monga mwa kufuna kwawo ndi kusangalatsidwa kwawo.

9 Ndipo kotero, mu chaka chimenechi cha chisanu ndi zitatu cha ulamuliro wa oweruza, kudayamba kukhala mikangano yaikulu pakati pa anthu a mumpingo; inde, kudali kaduka, ndewu, ndi dumbo, ndi mazunzo, ndi kunyada, ngakhale kuposera kunyada kwa iwo amene sadali a mumpingo wa Mulungu.

10 Ndipo kotero chidatha chaka cha chisanu ndi chitatu cha ulamuliro wa oweruza; ndipo kuipa kwa mu mpingo kudakhala chophunthwitsa chachikulu kwa iwo amene sadali mu mpingo; ndipo motero mpingo udayamba kulephera kupita chitsogolo kwake.

11 Ndipo zidachitika kuti kumayambiliro kwa chaka cha chisanu ndi chinayi, Alima adaona kuipa kwa mpingo, ndipo adaonanso kuti chitsanzo cha mpingo chidayamba kutsogolera iwo amene adali osakhulupilira kuchoka ku gawo limodzi la mphulupulu kupita ku lina, motero kubweretsa patsogolo chiwonongeko kwa anthu.

12 Inde, iye adaona kusiyana kwakukulu pakati pa anthu, ena akudzikuza okha m’kunyada kwawo, kunyoza ena, kutembenuzira misana yawo pa osowa ndi amaliseche ndi iwo amene adali anjala, ndi iwo amene adali a ludzu, ndi iwo amene adali odwala ndi osautsika.

13 Tsopano ichi chidali chifukwa chachikulu cha maliro pakati pa anthu, pamene ena adali kudzichepetsa okha, kuthandiza iwo amene adali kusowa chithandizo chawo, monga kugawana chuma chawo kwa osauka ndi osowa, kudyetsa anjala, ndi kuvutika mitundu yonse ya masautso, chifukwa cha Khristu, amene akuyenera kubwera molingana ndi mzimu wa uneneri.

14 Kuyang’anira kufikira ku tsiku limeneri, motero kusunga chikhulukiro cha machimo awo; atadzadzidwa ndi chisangalalo chachikulu chifukwa cha chiukitso cha akufa, monga mwa chifuniro ndi mphamvu ndi chipulumutso cha Yesu Khristu ku zingwe za imfa.

15 Ndipo tsopano zidachitika kuti Alima, ataona masautso a otsatira odzichepetsa a Mulungu, ndi mazunzo amene adaunjikidwa pa iwo ndi otsalira a anthu ake, kuona kusiyana kwawo konse, adayamba kumva chisoni chachikulu, komabe Mzimu wa Ambuye sudamusiye iye.

16 Ndipo iye adasankha munthu wanzeru amene adali pakati pa akulu a mpingo, ndipo adampatsa iye mphamvu molingana ndi mawu a anthu, kuti iye akhale ndi mphamvu yakukhazikitsa malamulo molingana ndi malamulo amene adaperekedwa, ndi kuwaika iwo mwa mphamvu molingana ndi zoipa ndi milandu ya anthu.

17 Tsopano munthu ameneyu dzina lake lidali Nefiha, ndipo adasankhidwa kukhala mkulu wa oweruza; ndipo adakhala pa mpando wa chiweruzo kuti aweruze ndi kutsogolera anthu.

18 Tsopano Alima sadapereke kwa iye udindo wokhala mkulu wansembe pa mpingo, koma adasunga udindo wa wamkulu wansembe kwa iye mwini; koma adapereka mpando wa chiweruzo kwa Nefiha.

19 Ndipo izi adachita kuti iye mwini apite kwa anthu ake, kapena pakati pa anthu a Nefi, kuti akalalilikire mawu a Mulungu kwa iwo, kuwachangamutsa iwo kukumbukira udindo wawo, ndi kuti agwetse, ndi mawu a Mulungu, kunyada konse ndi chinyengo chonse ndi mikangano yonse imene idali pakati pa anthu ake, poona palibe njira yoti angawalanditse iwo kupatula pochitira umboni oyera motsutsana nawo.

20 Ndipo motero kumayambiliro kwa chaka cha chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, Alima adapereka mpando wa chiweruzo kwa Nefiha, ndi kudzipanikiza yekha ku unsembe waukulu wa dongosolo loyera la Mulungu, ku umboni wa mawu, molingana ndi mzimu wa chibvumbulutso ndi uneneri.

Print