Malembo Oyera
Alima 20


Mutu 20

Ambuye atumiza Amoni ku Midoni kukapulumutsa abale ake am’ndende—Amoni ndi Lamoni akumana ndi atate ake a Lamoni, amene ali mfumu pa dziko lonse—Amoni akakamiza mfumu yokalambayo kuti itulutse abale ake. Mdzaka dza pafupifupi 90 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adakhazikitsa mpingo mu dzikolo, kuti mfumu Lamoni adakhumbira kuti Amoni apite naye limodzi ku dziko la Nefi, kuti akamuonetse iye kwa atate ake.

2 Ndipo mawu a Ambuye adadza kwa Amoni, nati: Usapite ku dziko la Nefi, pakuti taona, mfumuyo ikafuna moyo wako; koma iwe udzapite ku dziko la Midoni, pakuti taona, m’bale wako Aroni, ndiponso Muloki ndi Ama ali mu ndende.

3 Tsopano zidachitika kuti pamene Amoni adamva izi, adati kwa Lamoni: Taona, mchimwene ndi abale anga ali mu ndende ku Midoni, ndipo ine ndikupita kuti ndikawapulumutse iwo.

4 Tsopano Lamoni adati kwa Amoni: Ndikudziwa, mu mphamvu ya Ambuye iwe ukhonza kuchita zinthu zonse. Koma taona, ndidzapita nawe ku dziko la Midoni; pakuti mfumu ya dziko la Midoni, amene dzina lake ndi Antiyomuno, ndi bwenzi kwa ine, kotero ndipita ku dziko la Midoni, kuti ndikanyengelere mfumu ya dzikolo, ndipo adzawatulutsa abale ako mu ndendemo. Tsopano Lamoni adati kwa iye: Wakuuza ndi ndani kuti abale ako ali mu ndende?

5 Ndipo Amoni adati kwa iye: Palibe amene wandiuza, kupatula Mulungu; ndipo iye wati kwa ine—Pita ndi kukapulumutsa abale ako, pakuti ali mu ndende mu dziko la Midoni.

6 Tsopano pamene Lamoni adamva izi adachititsa kuti antchito ake akhonzekeretse akavalo ake ndi magaleta ake.

7 Ndipo adati kwa Amoni: Bwera, ndidzapita nawe ku dziko la Midoni, ndipo kumeneko ndidzachondelera kwa mfumu kuti adzatulutse abale ako mu ndende.

8 Ndipo zidachitika kuti pamene Amoni ndi Lamoni adali kupita kumeneko, adakumana ndi atate ake a Lamoni, amene adali mfumu ya dziko lonse.

9 Ndipo taonani, atate ake a Lamoni adati kwa iye: Bwanji siudabwere ku phwando pa tsiku lalikulu pamene ine ndidapanga phwando kwa ana anga aamuna, ndi kwa anthu anga?

10 Ndiponso iye adati: Ukupita kuti ndi M’nefiyu, amene ali m’modzi wa ana a wabodza?

11 Ndipo zidachitika kuti Lamoni adalongosola kwa iwo kumene iye adali kupita, pakuti adaopa kuwakhumudwitsa iwo.

12 Ndipo adamuuzanso iye zonse zidachititsa iye kukhalabe m’dziko lake, kuti iye sadapite ku phwando la atate ake limene iwo adakonza.

13 Ndipo tsopano pamene Lamoni adalongosola kwa atate ake zinthu zonsezi, taonani, m’kudabwitsika kwake, atate ake adakwiya naye, ndipo adati: Lamoni, ukupita kukapulumutsa Anefi awa, amene ali ana a wabodza. Taonani, iwo adabera makolo athu; ndipo tsopano ana akenso abwera pakati pathu kuti athe, mwa chinyengo chawo ndi bodza lawo, kutinamiza ife, kuti atiberenso ife chuma chathu.

14 Tsopano atate ake a Lamoni adamulamula iye kuti amuphe Amoni ndi lupanga. Ndipo adalamulanso iye kuti asapite ku dziko la Midoni, koma kuti abwelere ndi iye ku dziko la Ismaeli.

15 Koma Lamoni adati kwa iyo: Sindidzamupha Amoni, kapena kubwelera ku dziko la Ismaeli, koma ndidzapita ku dziko la Midoni kuti ndikawatulutse abale ake a Amoni, pakuti ndikudziwa kuti iwo ndi anthu olungama ndi aneneri oyera a Mulungu oona.

16 Tsopano pamene atate ake adamva mawu awa, adakwiya naye, ndipo adasolora lupanga lawo kuti amukhapire iye pansi.

17 Koma Amoni adaimilira patsogolo ndi kunena kwa iyo: Taonani, musamuphe mwana wanu; komabe, kukadakhala kwabwino kuti iye agwe kuposa inu, pakuti taonani, iye walapa machimo ake; koma ngati inu mutagwe pa nthawi ino, mu mkwiyo wanu, moyo wanu sudzapulumutsidwa.

18 Ndiponso, ndikofunikira kuti inu musatero; pakuti ngati mutaphe mwana wanu, iye okhala munthu osalakwa, mwazi wake udzafuula kuchokera ku nthaka kwa Ambuye Mulungu wake, kuti kubwenzera kudzafike pa inu; ndipo mwina inu mudzataya moyo wanu.

19 Tsopano pamene Amoni adanena mawu awa kwa iye, iye adamuyankha, nati: Ndikudziwa kuti ngati ndingaphe mwana wanga, kuti ndidzakhetsa mwazi osalakwa; pakuti ndi iweyo amene wafuna kuti uwononge iye.

20 Ndipo adatambasula dzanja lake kuti amuphe Amoni. Koma Amoni adazinda nkhonya zake, ndiponso adakantha nkono wake kuti iye sakadathanso kuugwiritsa ntchito.

21 Tsopano pamene mfumuyo idaona kuti Amoni akadatha kuipha, idayamba kuchondelera kwa Amoni kuti ayisiyile moyo wake.

22 Koma Amoni adakweza lupanga lake, ndi kunena kwa iye: Taonani, ndidzakukanthani inu pokhapokha mupereke kwa ine kuti abale anga atulutsidwe m’ndende.

23 Tsopano mfumuyo, poopa kuti ingathe kutaya moyo wake, idati: Ngati iwe undisiya ine ndidzakupatsa iwe chilichonse chomwe udzapempha, ngakhale kwa theka la ufumuwo.

24 Tsopano pamene Amoni adaona kuti adachitira mfumu yokalambayo monga mwa chokhumba chake, iye adati kwa iyo: Ngati mudzapereke kuti abale anga atulutsidwe m’ndende, ndiponso kuti Lamoni akhalebe ndi ufumu wake, ndipo kuti inu simudzakhumudwa naye, koma kumulora kuti iye achite molingana ndi zokhumba zake mu china chilichonse iye achiganize, pamenepo ine ndidzakusiyani inu; kupanda apo ndidzakukanthirani inu pansi.

25 Tsopano, pamene Amoni adanena mawu awa, mfumuyo idayamba kukondwera chifukwa cha moyo wake.

26 Ndipo pamene idaona kuti Amoni adalibe chikhumbo choiwononga iyo, ndipo pamene iyonso idaona chikondi chachikulu chomwe adali nacho kwa mwana wake Lamoni, idadabwa kwambiri, ndipo idati: Chifukwa izi ndi zonse zomwe iwe wakhumba, kuti ine nditulutse abale ako, ndi kulora mwana wanga Lamoni kuti akhalebe ndi ufumu wake, taonani, ndipereka kwa iwe kuti mwana wanga akhalebe ndi ufumu wake kuyambira nthawi ino ndi kunthawi zosatha; ndipo ine sindidzamulamuliranso iye—

27 Ndipo ndidzakupatsa kwa iwe kuti abale ako atulutsidwe mu ndende, ndipo iwe ndi azibale ako muthe kubwera kwa ine, mu ufumu wanga; pakuti ndidzafunitsitsa kuti ndikuoneni. Pakuti mfumuyo idazizwa kwambiri pa mawu amene adayankhulidwa, ndiponso pa mawu amene adayankhulidwa ndi mwana wake Lamoni, kotero idakhumbira kuti awaphunzire.

28 Ndipo zidachitika kuti Amoni ndi Lamoni adapitiriza ulendo wawo molunjika ku dziko la Midoni. Ndipo Lamoni adapeza chisomo m’maso mwa mfumu ya dzikolo; kotero abale a Amoni adatulutsidwa m’ndende.

29 Ndipo pamene Amoni adakumana nawo adali ndi chisoni chachikulu kwambiri, pakuti taonani adali amaliseche, ndipo khungu lawo lidasupuka kwambiri chifukwa cha kumangidwa ndi zingwe zamphamvu. Ndipo iwonso adazunzika ndi njala, ludzu, ndi mazunzo amitundu yonse; komabe adali woleza mtima mu masautso awo onse.

30 Ndipo, monga zidachitikira, lidali gawo lawo lidagwera m’manja mwa anthu oipa kwambiri ndi osamva; kotero sadamvere mawu awo, ndipo adawathamangitsa iwo ndi kuwakantha, ndi kuwathamangitsa kuchokera kunyumba ndi nyumba, ndi kuchokera malo kupita kumalo, ngakhale mpaka pamene adafika ku dziko la Midoni; ndipo kumeneko adatengedwa ndi kuponyedwa mu ndende, ndipo adamangidwa ndi dzingwe zamphamvu, ndipo adasungidwa m’ndende kwa masiku ambiri, ndipo adapulumutsidwa ndi Lamoni ndi Amoni.

Print