Malembo Oyera
Alima 13


Mutu 13

Amuna amayitanidwa ngati akulu ansembe chifukwa cha chikhulupiliro chawo chachikulu ndi ntchito zabwino—Iwo akuyenera kuphunzitsa malamulo—Kudzera m’chilungamo iwo ayeretsedwa ndipo alowa mu mpumulo wa Ambuye—Melikizedeki adali m’modzi wa amenewa—Angelo akulalika uthenga wabwino kuzungulira dziko lonse—Adzalalika kubwera kwenikweni kwa Khristu. Mdzaka dza pafupifupi 82 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo kachiwiri, abale anga, ndikufuna kukumbutsa maganizo anu chitsogolo ku nthawi imene Ambuye Mulungu adapereka malamulo awa kwa ana ake; ndipo ndikufuna kuti mukumbukire kuti Ambuye Mulungu adadzodza ansembe, potsatira dongosolo lake lopatulika, limene lidali dongosolo la Mwana wake, kuti aphunzitse zinthu izi kwa anthu.

2 Ndipo ansembe amenewo adadzodzedwa potsatira dongosolo la Mwana wake, mu machitidwe akuti anthu adziwe mu njira yanji yoti ayan’ganire Mwana wake ku chiwombolo.

3 Ndipo umu ndi momwe iwo adadzodzedwera—ataitanidwa ndi kukonzekeretsedwa kuyambira ku maziko a dziko lapansi molingana ndi kudziwiratu kwa Mulungu, pa chifukwa cha chikhulupiliro chawo chachikulu ndi ntchito zabwino; pachiyambi adasiyidwa kusankha chabwino kapena choipa; kotero iwo atasankha chabwino, ndi kuonetsa chikhulupiliro chachikulu kwambiri, ayitanidwa ndi mayitanidwe opatulika, inde, ndi maitanidwe oyera amene adakonzekera, ndipo molingana ndi chiwombolo chokonzekera cha otero.

4 Ndipo choncho iwo ayitanidwa ku mayitanidwe oyerawa chifukwa cha chikhulupiliro chawo, pamene ena adakana Mzimu wa Mulungu chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo ndi khungu la m’maganizo mwawo, pamene, kukadapanda zimenezi akadakhala ndi mwayi waukulu ngati abale awo.

5 Kapena mwachidule, pachiyambi adali mu mbali imodzi ndi abale awo; choncho mayitanidwe awa oyerawa adakonzedwa kuchokera ku maziko a dziko lapansi kwa iwo ngati sadzalimbitsa mitima yawo, pokhala mwa ndi kudzera mu chitetezero cha Mwana Wobadwa Yekha, amene adakonzedwa—

6 Ndipo choncho poyitanidwa ndi mayitanidwe oyerawa, ndi kudzodzedwa ku unsembe waukulu wa dongosolo loyera la Mulungu, kuti aphunzitse malamulo ake kwa ana a anthu, kuti nawonso alowe mu mpumulo wake—

7 Unsembe waukuluwu otsatira dongosolo la Mwana wake, umene dongosolo lake lidachokera pa maziko a dziko lapansi; kapena m’mawu ena, okhala opanda chiyambi cha masiku kapena mathero a dzaka, kukhala okonzekeredwa kuchokera ku nthawi za nthawi zonse, molingana ndi chidziwitso chake cha zinthu zonse.

8 Tsopano iwo adadzodzedwa motere—poitanidwa ndi mayitanidwe oyera, ndi kudzodzedwa mwa mwambo oyera, ndi kutengera pa iwo unsembe waukulu wa dongosolo lopatulika, limene mayitanidwe ake, ndi mwambo, ndi unsembe waukuluwo, ulibe chiyambi kapena mathero—

9 Choncho iwo amakhala akulu ansembe kwa muyaya, potsatira dongosola la Mwana, Wobadwa Yekha wa Atate, amene alibe chiyambi cha masiku kapena mapeto adzaka, amene ndi odzadza ndi chisomo, chilungamo ndi choonadi. Ndipo zili choncho. Ameni.

10 Tsopano, monga ndanena zokhudzana ndi dongosolo lopatulika, kapena unsembe waukuluwu, adalipo ambiri amene adadzodzedwa ndi kukhala akulu ansembe a Mulungu; ndipo chidali chifukwa cha chikhulupiliro chawo chopambana ndi kulapa, ndi kulungama kwawo pamaso pa Mulungu, iwo atasankha kulapa ndi kuchita chilungamo m’malo mwa kuwonongeka;

11 Kotero iwo adayitanidwa potsatira dongosolo lopatulikali, ndipo ayeretsedwa, ndipo zovala zawo zidachapidwa moyera kudzera mu mwazi wa mwana wa Nkhosa.

12 Tsopano iwo, atayeretsedwa ndi Mzimu Woyera, zovala zawo zitayeretsedwa, pokhala oyera ndi opanda banga pamaso pa Mulungu, sakadayang’ananso pa tchimo kupatura mo nyansidwa nalo; ndipo adalipo ambiri, ambiri kwambiri, amene adapangidwa kukhala oyera ndipo adalowa mu mpumulo wa Ambuye Mulungu wawo.

13 Ndipo tsopano, abale anga, ndikufuna kuti mudzichepetse pamaso pa Mulungu, ndi kubweretsa zipatso zoyenera ku kulapa, kuti inunso mukalowe mu mpumulo umenewo.

14 Inde, dzichepetseni inu eni ngakhale ngati anthu a m’masiku a Melikizedeki, amenenso adali mkulu wansembe potsatira dongosolo lomweli limene ndanena, amenenso adatengera pa iye unsembe waukulu kwamuyaya.

15 Ndipo adali Melikizedeki yemweyu kwa amene Abrahamu ankapereka chakhumi; inde, ngakhale atate athu Abrahamu ankapereka limodzi mwa magawo khumi a zonse iye adali nazo.

16 Tsopano miyambo imeneyi inkaperekedwa motere, kuti potero anthu adzitha kuyang’ana patsogolo pa Mwana wa Mulungu, iwo kukhala chitsanzo cha dongosolo lake, kapena iwo kukhala dongosolo la iye, ndipo izi kuti iwo akathe kuyang’ana patsogolo kwa iye ku chikhululukiro cha machimo awo, kuti adzathe kulowa mu mpumulo wa Ambuye.

17 Tsopano Melikizedeki ameneyu adali mfumu ya dziko la Salemu; ndipo anthu ake adali atakula mphamvu mu kusaweruzika ndi zonyasa; inde, iwo onse adasochera; iwo adali odzadza ndi zoipa zamitundu yonse;

18 Koma Melikizedeki pokhala ndi chikhulupiliro champhamvu, ndi kulandira udindo wa wansembe waukulu molingana ndi dongosolo lopatulika la Mulungu, adalalikira kulapa kwa anthu ake. Ndipo taonani, iwo adalapa; ndipo Melikizedeki adakhazikitsa mtendere mu dzikolo m’masiku ake; kotero iye ankatchedwa kalonga wa mtendere, popeza adali mfumu ya Salemu, ndipo adalamulira pansi pa atate ake.

19 Tsopano, adalipo ambiri m’mbuyo mwake, komanso adalipo ambiri patsogolo pake, koma padalibe amene adali opambana; kotero, za iye iwo azitchulapo mwapadera.

20 Tsopano sindikufunika kubwerenza nkhaniyi; zomwe ndanena zingakwanire. Taonani, malembo oyera ali pafupi ndi inu, ngati mulimbana nawo adzakhala kwa inu chiwonongeko chanu chomwe.

21 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Alima adayankhula mawu awa kwa iwo, adatambasulira dzanja lake kwa iwo ndipo adafuula ndi mawu amphamvu, nati: Tsopano ndi nthawi ya kulapa, pakuti tsiku la chipulumutso likudza chifupi.

22 Inde, ndipo mawu a Ambuye, mwa pakamwa pa mngelo, akulalika ichi kwa maiko onse; inde, akulalika ichi, kuti iwo akhale ndi uthenga wabwino wa chisangalalo chachikulu; inde, ndipo iye akulengeza uthenga wabwino umenewu pakati pa anthu ake onse, inde, ngakhale kwa iwo amene adabalalitsidwa pankhope ya dziko lapansi; kotero iwo adabwera kwa ife.

23 Ndipo adziwitsidwa kwa ife momveka bwino, kuti tiwamvetsetse, kuti tisalakwitse, ndipo izi chifukwa cha kukhala kwathu oyendeyenda m’dziko lachilendo; kotero, ife tiri okonderedwa kwambiri, pakuti ife tiri ndi uthenga wabwino umenewu kulalikidwa kwa ife m’mbali zonse za munda wathu wampesa.

24 Pakuti taonani, angelo akulalikira ichi kwa ambiri pa nthawi ino mu dziko lathu; ndipo izi ndi cholinga chokonzekeretsa mitima ya ana a anthu kuti alandire mawu ake pa nthawi ya kubwera kwake mu ulemelero wake.

25 Ndipo tsopano ife tikungoyembekezera kuti timve uthenga wachisangalalo kulalikidwa kwa ife kudzera pakamwa pa angelo, wa kubwera kwake; pakuti nthawi ikubwera, sitikudziwa changu chake. Ndikadakonda kwa Mulungu kuti zidzakhale m’masiku anga; koma zikhala posachedwa kapena mtsogolomu, m’menemo ndidzakondwera.

26 Ndipo zidzadziwika kwa olungama ndi anthu oyera, kudzera pakamwa pa angelo, pa nthawi ya kubwera kwake, kuti mawu amakolo athu akwaniritsidwe, molingana mwa izo zimene iwo adayankhula zokhudza iye, zimene zidali molingana ndi mzimu wa uneneri umene udali mwa iwo.

27 Ndipo tsopano, abale anga, ndikulakalaka kuchokera mkati mwa mtima wanga, inde, ndi kudera nkhawa kwakukulu ngakhale mpaka ululu, kuti inu mukamvere mawu anga, ndi kusiya machimo anu, ndipo musazengereze tsiku lakulapa kwanu.

28 Koma kuti inu mudzichepetse pamaso pa Ambuye, ndi kuitanira pa dzina lake loyera, ndi kuyang’anira ndi kupemphera mosalekeza, kuti musayesedwe koposa zimene inu mungathe kukwanitsa, ndipo motero kutsogoleredwa ndi Mzimu Woyera, kukhala odzichepetsa, wofatsa, womvera, wopilira, wodzala ndi chikondi ndi woleza mtima;

29 Kukhala ndi chikhulupiliro pa Ambuye; kukhala nacho chiyembekezo kuti mudzalandira moyo wamuyaya; kukhala ndi chikondi cha Mulungu nthawi zonse m’mitima mwanu, kuti muthe kudzakwezedwa pa tsiku lomaliza ndi kulowa mu mpumulo wake.

30 Ndipo ambuye apereke kwa inu kulapa, kuti musagwetse mkwiyo pa inu, kuti musamangidwe pansi ndi maunyolo a gahena, kuti musazunzike imfa yachiwiri.

31 Ndipo Alima adayankhula mawu enanso ambiri kwa anthuwo, amene sadalembedwe mu buku ili.

Print