Malembo Oyera
Alima 24


Mutu 24

Alamani abwera kudzatsutsana ndi anthu a Mulungu—Aanti-Nefi-Lehi akondwera mwa Khristu ndipo ayenderedwa ndi angelo—Iwo asankha kuzunzika imfa kuposa kudziteteza wokha—Alamani ambiri atembenuka. Mdzaka dza pafupifupi 90–77 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti Aamaleki ndi Aamuloni ndi Alamani amene adali mu dziko la Amuloni, ndiponso mu dziko la Helamu, ndi amene adali mu dziko la Yerusalemu, ndipo kungoti, m’maiko wonse wozungulira, amene sadatembenuke ndipo sadadzitengele pa iwo dzina la Anti-Nefi-Lehi, adasonkhezeredwa ndi Aamaleki ndi Aamuloni kuti akwiye ndi abale awo.

2 Ndipo chidani chawo chidakula kwambiri kwa iwo, mpaka kufikira kuti adayamba kupandukira mfumu yawo, kufikira kuti iwo sadafunenso kuti akhale mfumu yawo; kotero, adanyamula zida kumenyana ndi anthu Aanti-Nefi-Lehi.

3 Tsopano mfumuyo idapereka ufumu kwa mwana wake wamwamuna, ndipo adamutcha dzina lake Anti-Nefi-Lehi.

4 Ndipo mfumuyo idamwalira mu chaka chomwecho chimene Alamani adayamba kukonzekera nkhondo motsutsana ndi anthu a Mulungu.

5 Tsopano pamene Amoni ndi abale ake ndi wonse amene adabwera limodzi naye adaona kukonzekera kwa Alamani kuti awononge abale awo, iwo adabwera ku dziko la Midiani, ndipo kumeneko Amoni adakumana ndi abale ake wonse; ndipo kuchokera pamenepo adabwera ku dziko la Ismaeli kuti akhale ndi zokambirana ndi Lamoni ndiponso m’bale wake Anti-Nefi-Lehi, zimene angachite kuti adzitetezere wokha kwa Alamani.

6 Tsopano kudalibiletu munthu m’modzi pakati pa anthu wonse amene adatembenukira kwa Ambuye amene akadatenga zida motsutsana ndi abale awo; ayi, iwo sadapange ngakhale zokonzekera zankhondo; inde, ndiponso mfumu yawo idalamula iwo kuti asatero.

7 Tsopano, awa ndiwo mawu amene iyo idanena kwa anthu zokhudzana ndi nkhaniyi: Ndikuthokoza Mulungu wanga, anthu anga okondedwa, kuti Mulungu wathu wamkulu mu ubwino wake adatumiza abale athu awa, Anefi, kwa ife kudzatilalikira, ndi kutitsimikizira ife za zikhalidwe zoipa za makolo athu.

8 Ndipo taonani, ndikuthokoza Mulungu wanga wamkulu kuti watipatsa ife gawo la Mzimu wake kufewetsa mitima yathu, kuti ife tatsegulira ubale ndi azibale athuwa, Anefi.

9 Ndipo taonani, ndikuthokozanso Mulungu wanga, kuti pakutsegulira ubalewu ife tatsimikiziridwa za machimo athu, ndi kupha kochuluka komwe ife tachita.

10 Ndipo ndikuthokozanso Mulungu wanga, inde, Mulungu wanga wamkulu, kuti iye adapereka kwa ife kuti tikhonza kulapa pa zinthu izi, ndiponso iye watikhululukira ife machimo athu wochulukawo ndi kupha kumene ife tidachita, ndipo wachotsa kulakwa kwathu m’mitima yathu, kudzera mwa kuyenerera kwa Mwana wake.

11 Ndipo tsopano, abale anga, popeza zakhala zonse zomwe ife tikadachita (monga tidali anthu otaika mwa anthu onse) ku kulapa machimo athu onse, ndi kupha kochuluka kumene ife tachita, ndi kumpangitsa Mulungu kuchotsa izo m’mitima yathu, pakuti zidali zonse zomwe ife tikadatha kuchita kuti tilape mokwanira pamaso pa Mulungu kuti iye achotse banga lathu.

12 Tsopano, abale anga okondwedwa apamtima, popeza kuti Mulungu wachotsa mabanga athu, ndipo malupanga athu ayeretsedwa, ndiye tiyeni tisadetsenso malupanga athu ndi mwazi wa abale athu

13 Taonani, ndinena kwa inu, Ayi, tiyeni tisunge malupanga athu kuti asadetsedwe ndi mwazi wa abale athu, pakuti mwina, ngati tingadetse malupanga athu kachiwiri sangayeretsedwenso mowala kudzera mwa mwazi wa Mwana wa Mulungu wathu wamkulu, umene udzakhetsedwe chifukwa cha chitetezero cha machimo athu.

14 Ndipo Mulungu wamkulu watichitira chifundo, ndipo adadziwitsa zinthu izi kwa ife kuti ife tisawonongeke; inde, ndipo iye watidziwitsiratu zinthu izi, chifukwa iye amakonda moyo wathu chimodzimodzi m’mene amakondera ana athu; kotero, mu chifundo chake iye amatiyendera ife ndi angelo ake, kuti dongosolo la chipulumutso likhale lodziwika kwa ife chimodzimodzi ndi mibadwo ilinkudza.

15 O, ndi wachifundo chotani Mulungu wathu! Ndipo tsopano, taonani, popeza zakhala monga momwe ife tikadathera kuchotsa mabanga athu kwa ife, ndipo malupanga athu anyezimira, tiyeni tiwabise kuti akakhale owala, akhale mboni kwa Mulungu wathu tsiku lomaliza, kapena pa tsiku limene ife tidzabweretsedwa kuyima pamaso pake kuti tiweruzidwe, kuti sitinadetse malupanga athu m’mwazi wa abale athu chiyambire pamene iye adapereka mawu ake kwa ife ndipo adatiyeretsa ife mwa kutero

16 Ndipo tsopano, abale anga, ngati abale athu akufuna kutiwononga ife, ife tidzabisa malupanga athu, inde, ngakhale tidzawakwilira pansi panthaka, kuti akathe kukhala owala, ngati umboni kuti ife sitidawagwiritse ntchito, patsiku lomaliza; ndipo ngati abale athu adzatiwononga ife, taonani, tidzapita kwa Mulungu wathu ndipo tidzapulumutsidwa.

17 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene mfumuyo idamaliza kuyankhula izi, ndipo anthu wonse adasonkhana pamodzi, adatenga malupanga awo, ndi zida zonse zimene zinkagwiritsidwa ntchito pokhetsera mwazi wa munthu, ndipo adazikwilira pansi panthaka.

18 Ndipo izi adazichita, izo kukhala m’maonedwe awo umboni kwa Mulungu, ndiponso kwa anthu, kuti iwo sadzagwiritsanso ntchito zida kuti akhetse mwazi wa munthu, ndipo izi adazichita, kutsimikizira ndi kupangana ndi Mulungu, kuti koposa kukhetsa mwazi wa azibale awo iwo adzapereka miyoyo yawo yomwe; ndipo m’malo molanda kwa m’bale iwo adzapereka kwa iye, ndipo m’malo mokhala m’masiku awo mwa ulesi iwo adzagwira ntchito ndi manja awo mochuluka.

19 Ndipo choncho tikuona kuti, pamene Alamani awa adabweretsedwa kuti akhulupilire ndi kudziwa choonadi, adali ochilimika, ndipo akadazunzika ngakhale ku imfa koposa kuchita tchimo; ndipo choncho tikuona kuti iwo adakwilira zida zawo za mtendere, kapena adakwilira zida zawo za nkhondo, chifukwa cha mtendere.

20 Ndipo zidachitika kuti abale awo, Alamani, adakonzekera nkhondo, ndipo adabwera ku dziko la Nefi pa cholinga chowononga mfumu, ndi kuikapo wina m’malo mwake, ndiponso kowononga anthu a Anti-Nefi-Lehi kuchoka m’dzikomo.

21 Tsopano pamene anthu adaona kuti akubwera kudzamenyana nawo, adatuluka kukakumana nawo, ndipo adagwada pansi pamaso pawo, ndi kuyamba kuitanira pa dzina la Ambuye; ndipo choncho iwo adali mu mchitidwe uwu pamene Alamani adayamba kugwa pa iwo, ndipo adayamba kuwapha iwo ndi malupanga.

22 Ndipo motero popanda kulimbana kulikonse, adapha chikwi chimodzi ndi asanu a iwo, ndipo tikudziwa kuti adali odalitsidwa, pakuti iwo apita kukakhala ndi Mulungu wawo.

23 Tsopano pamene Alamani adaona kuti abale awo sakadathawa lupanga, ngakhale kutembenukira kudzanja lamanja kapena kumanzere, koma kuti iwo adagona pansi ndi kuwonongedwa, ndipo adatamanda Mulungu ngakhale pamene adali kuwonongedwa pansi pa lupanga—

24 Tsopano pamene Alamani adaona izi iwo adaleka kuwapha; ndipo adalipo ambiri amene mitima yawo idakhudzika mkati mwawo chifukwa cha abale awo amene adagwa pansi pa lupanga, pakuti adalapa pa zinthu zomwe iwo adachita.

25 Ndipo zidachitika kuti iwo adaponya pansi zida zawo zankhondo, ndipo sadazitengenso, pakuti iwo adawawidwa ndi kupha kumene iwo adachita; ndipo adabwera monga ngati abale awo, kudalira pa zifundo za iwo amene manja awo adakwezedwa kuti awaphe.

26 Ndipo zidachitika kuti anthu a Mulungu adaphatikizidwa tsiku limenero ndi ambiri kuposa amene adaphedwa; ndipo iwo amene adaphedwa adali anthu wolungama, kotero tilibe chifukwa chokaikira koma kuti iwo adapulumutsidwa.

27 Ndipo padalibe munthu oipa amene adaphedwa pakati pawo; koma adalipo oposera chikwi chimodzi womwe adabweretsedwa ku chidziwitso cha choonadi; choncho tikuona kuti Ambuye amagwira nchito njira zambiri ku chipulumutso cha anthu ake.

28 Tsopano chiwerengero chachikulu cha iwo amene Alamani adapha ambiri mwa abale awo adali Aamaleki ndi Aamuloni, chiwerengero chachikulu cha iwo amene adali a dongosolo la Neho.

29 Tsopano pakati pa iwo amene adalowa mwa anthu a Ambuye, padalibepo amene adali Aamaleki kapena Aamuloni, kapena iwo amene adali a dongosolola Neho, koma adali zidzukulu zenizeni za Lamani ndi Lemueli.

30 Ndipo choncho tikhonza kuona poyera, kuti potsatira kuunikiridwa kwa anthu ndi Mzimu wa Mulungu, ndi kukhala ndi chidziwitso chachikulu cha zinthu zokhudzana ndi chilungamo, ndipo kenako akagwa mu uchimo ndi kulakwitsa, iwo amakhala oumitsitsa, ndipo choncho kukhala kwawo kumakhala koipitsitsa kuposa ngati kuti sadazidziwe zinthu izi.