Mutu 46
Amalikiya achita chiwembu kuti akhale mfumu—Moroni aimika mbendera ya ufulu—Iye amema anthu kuti ateteze chipembedzo chawo—Okhulupilira moona atchedwa Akhristu—Otsalira a Yosefe adzasungidwa—Amalikiya ndi ogalukira athawa mu dziko la Nefi—Iwo amene sadzathandizira ntchito ya ufulu aphedwa. Mdzaka dza pafupifupi 73–72 Yesu asadabadwe.
1 Ndipo zidachitika kuti pamene ambiri amene sadamvere mawu a Helamani ndi abale ake adasonkhana pamodzi motsutsana ndi abale awo.
2 Ndipo tsopano, iwo adakwiya kwambiri, kufikira kuti iwo adatsimikizika kuti awaphe.
3 Tsopano mtsogoleri wa iwo amene adali wokwiya motsutsana ndi abale awo adali munthu ojintcha ndi wamphamvu; ndipo dzina lake lidali Amalikiya.
4 Ndipo Amalikiya adakhumbira kukhala mfumu; ndipo anthu awo amene adali wokwiya adakhumbiranso kuti iye akhale mfumu yawo; ndipo adali gawo lalikulu la iwo oweruza a dzikolo ndipo iwo ankafuna mphamvu.
5 Ndipo adatsogozedwa ndi zinyengo za Amalikiya, kuti ngati iwo adzamuthandiza iye ndi kumukhazika iye kukhala mfumu yawo iye adzawapanga iwo olamulira pa anthuwo.
6 Motero iwo adasocheletsedwa ndi Amalikiya m’kusagwirizana, posatengera za ulaliki wa Helamani ndi abale ake, inde, posatengera za chisamaliro chawo chachikulu cha mpingo, pakuti iwo adali akulu ansembe pa mpingo.
7 Ndipo adalipo ambiri mu mpingo amene adakhulupilira mu mawu achinyengo a Amalikiya, kotero iwo adagalukira ngakhale kuchoka ku mpingo; ndipo motero zidali zochitika za anthu a Nefi zokayikitsa ndi zoopsya, posatengera za chipambano chawo chachikulu chimene iwo adali nacho pa Alamani, ndi chimwemwe chawo chachikulu chimene iwo adali nacho chifukwa cha chipulumutso chawo ndi dzanja la Ambuye.
8 Motero tikuona m’mene ana a anthu amafulumilira kuiwala Ambuye Mulungu wawo, inde, m’mene amafulumilira pakuchita zoipa, ndi kutsogoleredwa ndi woipayo.
9 Inde, ndiponso tikuonanso kuipa kwakukulu munthu m’modzi oipa angapangitse kuti kuchitike pakati pa ana a anthu.
10 Inde, tikuona kuti Amalikiya, chifukwa iye adali munthu wanjira zochenjera ndi munthu wa mawu achinyengo ambiri, kuti adasocheretsa mitima ya anthu ambiri kuchita zoipa; inde, ndipo kufuna kuwononga mpingo wa Mulungu, ndi kuwononga maziko a ufulu umene Mulungu adapereka kwa iwo, kapena madalitso amene Mulungu adatumiza pa nkhope ya dziko lapansi chifukwa cha olungama.
11 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Moroni, amene adali mkulu wa ankhondo a Anefi, adamva za kusagwirizanaku, iye adakwiya ndi Amalikiya.
12 Ndipo zidachitika kuti iye adang’amba chovala chake; ndi kutenga sanza yake, ndikulembapo—Pa kukumbukira Mulungu wathu, chipembedzo chathu, ufulu wathu, ndi mtendere wathu, akazi athu ndi ana athu—ndipo adamangilira pa nsonga ya mtengo.
13 Ndipo adamangilira chisoti chake chakumutu, ndi chapachifuwa chake, ndi chishango chake, ndi kumangira m’chiuno mwake lupanga lake, ndipo iye adatenga mtengo uja, umene kunsonga kwake kudali sanza ya chovala chake, (ndipo iye adaitcha mbendera ya ufulu) ndipo adadzigwaditsa pansi, ndipo adapemphera mwamphamvu kwa Mulungu wake kuti madalitso a ufulu akhale pa abale ake, kufikira pamene gulu la Akhristu lidzatsala ndi kutenga dzikolo.
14 Pakuti motero adali onse okhulupilira mwa Khristu, amene adali mu mpingo wa Mulungu, kutchedwa ndi iwo amene sadali ampingo.
15 Ndipo iwo amene adali a mpingo adali wokhulupirika; inde, onse amene adali wokhulupilira moonadi mwa Khristu adatenga pa iwo, mokondwera, dzina la Yesu, kapena Akhristu monga ankaitanidwira, chifukwa cha chikhulupiliro mwa Khristu amene akuyenera kudza.
16 Ndipo kotero, pa nthawi imeneyi, Moroni adapemphera kuti ntchito ya Akhristu, ndi ufulu wa dziko ukonderedwe.
17 Ndipo zidachitika kuti pamene iye adatsanulira moyo wake kwa Mulungu, adatchula dziko lonse limene lidali kum’mwera kwa dzikolo Bwinja, inde, ndipo pamapeto pake, dziko lonse, konse chakumpoto ndi chakum’mwera—Dziko losankhidwa, ndi dziko la ufulu.
18 Ndipo iye adati: Indedi Mulungu sadzalora kuti ife, amene tikunyozedwa chifukwa tatenga pa ife dzina la Khristu, tidzaponderezedwe ndi kuwonongedwa, kufikira titachibweretsa tokha ndi kulakwitsa kwathu komwe.
19 Ndipo pamene Moroni adanena mawu awa, iye adapita pakati pawo, akugwedeza mlengalenga nsaza ya chovala chong’ambidwacho, kuti onse aone zolembedwa zimene iye adalembapo, ndipo adafuula ndi mawu aakulu, nati:
20 Taonani, aliyense amene adzasunga mbendera iyi pa dzikoli, aloreni abwere mu mphamvu za Ambuye, ndi kulowa mu pangano kuti iwo adzasunga maufulu awo, ndi chipembedzo chawo, kuti Ambuye Mulungu awadalitse iwo.
21 Ndipo zidachitika kuti pamene Moroni adanena mawu awa, taonani, anthuwo adabwera akuthamanga limodzi ndi zida zawo zankhondo zitamangiliridwa m’chiuno mwawo, akung’amba zovala zawo m’chizindikiro, kapena ngati chipangano kuti iwo sadzamusiya Ambuye Mulungu wawo, kapena, mu mawu ena, ngati iwo adzalakwire malamulo a Mulungu, kapena kugwa mu kulakwitsa, ndi kuchita manyazi kutengera pa dzina la Khristu, Ambuye akuyenera kudzawang’amba monga ngati iwo adang’ambira chovala chawo.
22 Tsopano ichi chidali chipangano chimene iwo adapanga, ndipo iwo adaponya zovala zawo pamapazi a Moroni, nati: Ife tikupangana ndi Mulungu wathu, kuti ife tidzawonongedwe, monga ngati abale athu mu dziko lakumpoto, ngati ife tidzagwa mu kulakwitsa, inde, iye adzatiponye ife pamapazi a adani athu monga ngati ife taponyera zovala zathu pamapazi ako kuti zipondedwe pansi paphanzi, ngati ife tidzagwa mu kulakwitsa.
23 Moroni adati kwa iwo: Taonani, ife ndi otsalira a mbewu ya Yakobo, inde, ndife otsalira a mbewu ya Yosefe, amene chovala chake chidang’ambidwa ndi abale ake mdzidutswa zambiri, inde, ndipo tsopano taonani, tiyeni tikumbukire malamulo a Mulungu, kapena zovala zathu zidzang’ambidwa ndi abale athu, ndipo tidzaponyedwa mu ndende, kapena kugulitsidwa, kapena kuphedwa.
24 Inde, tiyeni titeteze ufulu wathu monga otsalira a Yosefe, inde, tiyeni tikumbukire mawu a Yakobo asadamwalire, pakuti taonani, iye adaona kuti gawo lotsalira la chovala cha Yosefe chidasungidwa ndipo sichidaole. Ndipo iye adati—Monga ngati chovala chotsalirachi mwana wanga wasungidwa, chomwechonso otsalira a mbewu ya mwana wanga adzasungidwa ndi dzanja la Mulungu, ndi kutengedwa kwa iye mwini, pamene otsalira a mbewu ya Yosefe adzawonongedwa, monga ngati chotsalira cha chovala chake.
25 Tsopano taonani, izi zikupatsa mzimu wanga chisoni, komabe, moyo wanga uli ndi chisangalalo mwa mwana wanga, chifukwa cha gawo lina la mbewu yake limene lidzatengedwe kwa Mulungu.
26 Tsopano taona, uku ndiko kudali kuyankhula kwa Yakobo.
27 Ndipo tsopano ndani adziwa koma chimene otsalira a mbewu ya Yosefe, amene adzawonongedwe monga chovala chake, ndi iwo amene asiyana ndi ife? Inde, ndipo monga zidzakhalira kwa ife tomwe ngati sitidzaima nji mu chikhulupiliro cha Khristu.
28 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamane Moroni adanena mawu awa, iye adapita, ndiponso adatumiza ku zigawo zonse za dziko limene kudali kusagwirizana, ndi kusonkhanitsa pamodzi anthu wonse amene adali ndi khumbo loteteza ufulu wawo, kuti aime motsutsana ndi Amalikiya ndi iwo amene adagalukira amene ankatchedwa Aamalikiya.
29 Ndipo zidachitika kuti pamene Amalikiya adaona kuti anthu a Moroni adali ochuluka kwambiri kuposera Aamalikiya—ndipo iye adaonanso kuti anthu ake ankakayikira zokhudzana ndi chilungamo cha cholinga chimene iwo adachita—kotero, poopa kuti sapindula kanthu, iye adatengana ndi iwo amene ankafuna ndi kunyamuka nawo kupita ku dziko la Nefi.
30 Tsopano Moroni adaganiza kuti sikudali koyenera kuti Alamani akhale ndi mphamvu zinanso; kotero iye adaganiza zowadula anthu a Amalikiya, kapena kuwatenga ndi kuwabweretsa iwo, ndi kupha Amalikiya; inde, pakuti iye adadziwa kuti iye adzawautsira ku mkwiyo Alamani kuwakwiyira iwo, ndi kuchititsa kuti abwere ku nkhondo motsutsana nawo; ndipo izi iye adadziwa kuti Amalikiya adzachita kuti apeze zolinga zake.
31 Kotero Moroni adaganiza kuti kudali koyenera kuti atenge ankhondo ake, amene adadzisonkhanitsa okha pamodzi, ndi zida zawo, ndi kulowa m’chipangano chosunga mtendere—ndipo zidachitika kuti iye adatenga ankhondo ake ndi kugubira ndi mahema awo kupita m’chipululu, kuti akadule njira ya Amalikiya m’chipululu.
32 Ndipo zidachitika kuti iye adachita molingana ndi zokhumba zake, ndipo adaguba kupita m’chipululu, ndipo adalondola ankhondo a Amalikiya.
33 Ndipo zidachitika kuti Amalikiya adathawa ndi chiwerengero chochepa cha anthu, ndipo otsalirawo adaperekedwa m’manja mwa Moroni ndipo adatengedwa kubwelera ku dziko la Zarahemula.
34 Tsopano, Moroni pokhala munthu amene adasankhidwa ndi mkulu wa oweruza ndi mawu a anthu, kotero iye adali ndi mphamvu molingana ndi chifuniro chake ndi ankhondo achinefi, kuti akhazikitse ndi kuonetsa ulamuliro pa iwo.
35 Ndipo zidachitika kuti aliyense wa Aamalikiya amene sadafune kulowa mu pangano kuthandizira ntchito ya ufulu, kuti akhalebe ndi ulamuliro waufulu, adachitititsa kuti aphedwe, ndipo adalipo koma ochepa amene adakana kulowa m’chipangano cha ufulu.
36 Ndipo zidachitikanso, kuti iye adachititsa kuti mbendera ya ufulu ipachikidwe pa nsanja imene idaikidwa mu dziko lonselo, limene mudali Anefi; ndipo motero Moroni adadzala mbendera ya ufulu pakati pa Anefi.
37 Ndipo iwo adayamba kukhalanso ndi mtendere mu dzikolo; ndipo motero adapitiliza kukhala ndi mtendere kufikira pafupifupi kumapeto kwa chaka cha khumi ndi chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa oweruza.
38 Ndipo Helamani ndi akulu ansembe adasunga dongosolo la mpingo; inde, mpakana kwa nthawi ya dzaka zinayi iwo adakhalabe ndi mtendere ndi chikondwelero mu mpingo.
39 Ndipo zidachitika kuti kudali ambiri amene adamwalira, kukhulupilira molimba kuti mizimu yawo idawomboledwa ndi Ambuye Yesu Khristu, motero iwo adachoka padziko lapansi okondwa.
40 Ndipo adalipo ena amene adamwalira ndi kuphwanya kwathupi, kumene mu nyengo zina za chakacho kudafala mu dzikolo—koma osati kwambiri ndi kuphwanya thupiko, chifukwa cha zitsamba ndi mitsitsi yabwino imene Mulungu adawakonzera kuti adzichotsera zoyambitsa matenda, amene anthu adali kutengera ndi kusintha kwa nyengo.
41 Koma kudali ambiri amene adamwalira ndi ukalamba; ndi ena amene adamwalira ndi chikhulupiliro cha Khristu ali okondwa mwa iye, monga momwe tikuyenera kuganizira.