Malembo Oyera
Alima 1


Buku la Alima
mwana wa Alima

Nkhani ya Alima, amene adali mwana wa Alima, oweruza oyamba ndi wamkulu pa anthu a Nefi, ndiponso mkulu wansembe pa mpingo. Nkhani ya ulamuliro wa oweruza, ndi nkhondo ndi mikangano pakati pa anthu. Ndiponso nkhani ya nkhondo pakati pa Anefi ndi Alamani, molingana ndi zolemba za Alima, oweruza oyamba ndi wamkulu.

Mutu 1

Neho aphunzitsa ziphunzitso zabodza, akhazikitsa mpingo, ayambitsa zaunsembe zachinyengo, ndi kupha Gideoni—Neho aphedwa chifukwa cha milandu yake—Zaunsembe zachinyengo ndi mazunzo zifalikira pakati pa anthu—Ansembe adzithandiza okha, anthu asamalira osauka, ndipo mpingo uchita bwino. Mdzaka dza pafupifupi 91–88 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidachitika kuti m’chaka choyamba cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, kuyambira panthawiyi kupita kutsogolo, mfumu Mosiya atapita m’njira ya dziko lonse, atamenya nkhondo yabwino, atayenda mowongoka pamaso pa Mulungu, sadasiye wina olamulira m’malo mwake; komabe iye adali atakhazikitsa malamulo, ndipo iwo adavomelezedwa ndi anthu; kotero iwo adali okakamizika kutsata malamulo amene iye adawapanga.

2 Ndipo zidachitika kuti mu chaka choyamba cha ulamuliro wa Alima mu mpando wa chiweruzo, padali munthu amene adabweretsedwa pamaso pake kuti aweruzidwe, munthu amene adali wojintcha, ndipo amadziwika ndi mphamvu zake zochuluka.

3 Ndipo iye adayendayenda pakati pa anthu, kulalikira kwa iwo chimene iye amachitcha mawu a Mulungu, kutsutsana ndi mpingo; kulalikira kwa anthu kuti wansembe aliyense ndi mphunzitsi akuyenera kukhala wotchuka; ndipo iwo sakuyenera kugwira ntchito ndi manja awo, koma kuti akuyenera kumathandizidwa ndi anthu.

4 Ndipo iyenso adachitira umboni kwa anthuwo kuti anthu onse akuyenera kupulumutsidwa patsiku lomaliza, ndipo kuti iwo sakuyenera kuchita mantha kapena kunjenjemera, koma kuti iwo akakweze mitu yawo ndi kukondwera; pakuti Ambuye adalenga anthu onse, ndipo adali atawombolanso anthu onse; ndipo, pamapeto pake, anthu onse akuyenera kudzakhala nawo moyo wamuyaya.

5 Ndipo zidachitika kuti iye adaphunzitsa zinthu zimenezi kwambiri moti anthu ambiri adakhulupilira mawu akewo, mpaka kuti ambiri adayamba kumuthandiza iye ndikumupatsa ndalama.

6 Ndipo adayamba kudzikuza m’kunyada kwa mtima wake, ndi kuvala zovala zokwera mtengo kwambiri, inde, ndipo ngakhale adayamba kukhazikitsa mpingo motsatira ndondomeko ya malalikidwe ake.

7 Ndipo zidachitika pamene iye adali kupita, kukalalikira kwa iwo amene adakhulupilira mawu ake, iye adakumana ndi munthu amene adali wa mpingo wa Mulungu, inde, ngakhale m’modzi wa aphunzitsi awo; ndipo iye adayamba kulimbana nawo mwamphamvu, kuti awasocheletse anthu a mpingowo; koma munthuyo adamugonjetsa iye, nkumuchenjeza iye ndi mawu a Mulungu.

8 Tsopano dzina la munthuyo lidali Gideoni; ndipo adali iye amene adali chida m’manja mwa Mulungu pakupulumutsa anthu a Limuhi kuchoka mu ukapolo.

9 Tsopano, chifukwa Gideoni adamugonjetsa iye ndi mawu a Mulungu adali wokwiya ndi Gideoni, ndipo adasolora lupanga ndi kuyamba kumukantha iye. Tsopano Gideoni pokhala ndi dzaka zambiri, kotero sakadatha kuima ndi makhomo ake, kotero adaphedwa ndi lupangalo.

10 Ndipo munthu amene adamupha iye adatengedwa ndi anthu a mpingo, ndipo adabweretsedwa pamaso pa Alima, kuti aweruzidwe molingana ndi milandu imene iye adapalamula.

11 Ndipo zidachitika kuti iye adayima pamaso pa Alima ndi kudzichondelera yekha ndi kulimba mtima kwakukulu.

12 Koma Alima adati kwa iye: Taona, iyi ndi nthawi yoyamba kuti zaunsembe zachinyengo ziyambitsidwe pakati pa anthu awa. Ndipo taona, iwe suli olakwa pa zaunsembe zachinyengo zokha, koma wayesetsa kuzikakamiza ndi lupanga; ndipo ngati zaunsembe zachinyengo zikadakakamizidwa pakati pa anthu awa, zikadatsimikizira chiwonongeko chawo chonse.

13 Ndipo iwe wakhetsa mwazi wa munthu wolungama, inde, munthu amene wachita zinthu zabwino kwambiri pakati pa anthu awa; ndipo ife tikakusiya iwe, mwazi wake ukhoza kufikira pa ife pa kubwenzera chilango.

14 Kotero iwe wagamulidwa kuti ufe, molingana ndi lamulo limene lidapatsidwa kwa ife ndi Mosiya, mfumu yathu yomaliza; ndipo izi zimavomelezedwa ndi anthu awa; kotero anthu awa ayenera kukhala mwa lamulolo.

15 Ndipo zidachitika kuti adamutenga iye; ndipo dzina lake lidali Neho; ndipo adamutengera iye pa mwamba pa phiri la Manti, ndipo pamenepo iye adapangidwa, kapena kuti adavomeleza, pakati pa kumwamba ndi dziko lapansi, kuti iye ankaphunzitsa kwa anthu mosemphana ndi mawu a Mulungu; ndipo pamenepo adafa ndi imfa yochititsa manyazi.

16 Komabe, izi sizidathetse kufalikira kwa zaunsembe zachinyengo m’dzikomo; pakuti adalipo ambiri amene ankakonda zinthu zachabechabe za dziko la pansi, ndipo adapitiriza kulalikira ziphunzitso zabodza; ndipo izi ankachita chifukwa chofuna chuma ndi ulemu.

17 Komabe, iwo sadayerekeze kunama, ngati zingadziwike, chifukwa chakuopa lamulo, pakuti abodza ankalangidwa; kotero iwo ankanamizira kulalika molingana ndi chikhulupiliro chawo; ndipo tsopano lamulo silikadakhala ndi mphamvu pa munthu aliyense pa chikhulupiliro chake.

18 Ndipo iwo samayerekeza kuba, chifukwa cha kuopa lamulo, pakuti otere ankalangidwa; ngakhale sankalanda, kapena kupha, chifukwa iye wokupha ankalangidwa pa kuphedwa.

19 Koma zidachitika kuti aliyense amene sadali wa mpingo wa Mulungu adayamba kuzunza iwo amene adali mu mpingo wa Mulungu, ndipo adatenga pa iwo dzina la Khristu.

20 Inde, iwo adawazunza iwo, ndi kuwasautsa iwo ndi mawu a mtundu onse, ndipo izi chifukwa cha kudzichepetsa kwawo; chifukwa iwo sadali onyada m’maso mwawo, ndipo chifukwa iwo ankagawana mawu a Mulungu, wina ndi mzake, opanda ndalama ndi opanda mtengo.

21 Tsopano padali lamulo lokhwima pakati pa anthu a mpingo, kuti pasakhale munthu aliyense okhala mu mpingo, angadzuke ndi kuzunza amene sadali a mu mpingo, ndipo kuti pasakhale kuzunzana pakati pawo.

22 komabe, padali ambiri pakati pawo amene adayamba kunyada, ndipo adayamba kulimbana ndi adani awo mwamphamvu, ngakhale ku ndewu; inde, iwo ankamenyana wina ndi mzake ndi zibakera zawo.

23 Tsopano izi zidali mchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Alima, ndipo chidali chifukwa cha masautso aakulu ku mpingo; inde, chidali chifukwa cha mayesero ambiri ndi mpingo.

24 Pakuti mitima ya ambiri idalimbitsidwa, ndipo mayina awo adachotsedwa kuti sadakumbukiridwenso pakati pa anthu a Mulungu. Ndipo ambiri adadzipatutsa pakati pawo.

25 Tsopano ili lidali yesero lalikulu kwa iwo amene adaimabe mokhazikika mchikhulupiliro; komabe, iwo adali okhazikika ndi osasunthika pa kusunga malamulo a Mulungu, ndipo adapilira ndi mazunzo amene adaunjikidwa pa iwo.

26 Ndipo pamene ansembe adasiya ntchito yawo kuti agawe mawu a Mulungu kwa anthu, anthu nawonso adasiya ntchito zawo kuti amvere mawu a Mulungu. Ndipo pamene wansembe adagawa kwa anthu mawu a Mulungu onse adabweleranso mwakhama ku ntchito zawo; ndipo wansembe, osadziyesa yekha wapamwamba kuposa omumvera, pakuti olalikira sadali woposa omumvera, kapena mphunzitsi sadali wabwino koposa ophunzira; ndipo potere onse adali ofanana, ndipo onse adagwira ntchito, aliyense molingana ndi mphamvu zake.

27 Ndipo iwo ankagawana chuma chawo, aliyense molingana ndi zomwe adali nazo, kwa osauka, ndi kwa osowa, ndi kwa odwala, ndi kwa osautsika; ndipo sankavala zovala zamtengo wapatali, koma zidali zaukhondo ndi zokongola.

28 Ndipo choncho adakhazikitsa zochitika za mpingo; ndipo choncho adayambanso kukhala ndi mtendere wosalekeza, posaona mazunzo awo onse.

29 Ndipo tsopano, chifukwa cha kukhazikika kwa mpingo adayamba kukhala olemera mopambanitsa, kukhala ndi kuchuluka kwa zinthu zambiri zomwe iwo ankafunikira—Nkhosa ndi ng’ombe, ndi ziweto zosiyanasiya zambiri, ndiponso mbewu zambiri, ndi golide, ndi siliva, ndi zinthu zamtengo wapatali, ndi ulusi wambiri, ndi nsalu zopota bwino, ndi mitundu yonse ya nsalu zabwino zapakhomo.

30 Ndipo choncho, mu nyengo yakuchita bwino kwawo, sadathamangitse aliyense amene adali wamaliseche, kapena amene adali wanjala, kapena amene adali waludzu, kapena amene adali odwala, kapena onyentchera; ndipo iwo sadayike mitima yawo pa chuma; kotero adali anthu omasuka kwa onse, akulu ndi ana omwe, omangidwa ndi amfulu omwe, amuna ndi akazi omwe, kaya a kunja kwa mpingo kapena a mu mpingo, opanda tsankho kwa munthu monga kwa iwo amene adali osowa.

31 Ndipo choncho iwo adachita bwino ndikukhala anthu achuma chambiri kuposa iwo amene sadali mu mpingo wawo.

32 Pakuti iwo amene sadali mu mpingo wawo adali kudzilowetsa mu zamatsenga, ndi mu kupembedza mafano, ndi mu ulesi, ndi mu zobwebweta, ndi kaduka, ndi ndewu; kuvala zovala zamtengo wapali; odzikuza m’kunyada m’maso mwawo; kuzunza, kunama, kuba, kufwamba, kuchita zachigololo, ndi kupha, ndi zoipa za mtundu uliwonse; komabe, lamulo lidakhwimitsidwa kwa onse amene adalakwira ilo, m’mene zikadathekera.

33 Ndipo zidachitika kuti mwa choncho pokwaniritsa lamulo pa iwo, munthu aliyense wozunzika molingana ndi momwe adachitira, adakhala okhazikika, ndipo sankayesa kuchita choipa chilichonse ngati chili chodziwika; potero, kudali mtendere wochuluka pakati pa anthu a Nefi kufikira mchaka cha chisanu cha ulamuliro wa oweruza.

Print