Malembo Oyera
Alima 32


Mutu 32

Alima aphunzitsa osauka amene masautso awo adawapangitsa kudzichepetsa—Chikhulupiliro ndi chiyembekezo mu chimene sichioneka koma ndi choona—Alima achitira umboni kuti angelo amatumikira kwa amuna, akazi ndi ana—Alima afananiza mawu ndi mbewu—Ikuyenera kudzalidwa ndi kudyetsedwa—Kenako imakula kukhala mtengo umene chipatso chake cha moyo wamuyaya chimathyoledwa. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti adapita ndi kuyamba kulalikira mawu a Mulungu kwa anthuwo, kulowa m’masunagoge awo, ndi m’nyumba zawo; ndipo ngakhale adalalikira mawu m’misewu yawo.

2 Ndipo zidachitika kuti atatha kugwira ntchito yochuluka pakati pa iwo, adayamba kukhala ndi chipambano pakati pa gulu la osauka la anthu; pakuti taonani, iwo adatulutsidwa mu masunagoge chifukwa cha kukhakhala kwa zovala zawo—

3 Kotero iwo sankaloledwa kulowa m’masunagoge kuti apembedze Mulungu, poonedwa ngati onyansa; kotero iwo adali osauka; inde, ankaonedwa ndi abale awo ngati opanda pake; kotero adali osauka monga ku zinthu za padziko lapansi; ndiponso osauka mumtima.

4 Tsopano, pamene Alima adali kuphunzitsa ndi kuyankhula kwa anthu pa phiri la Onida, padabwera khamu lalikulu kwa iye, amene adali mwa iwo amene takhala tikunena, mwa limene lidali osauka mumtima, chifukwa cha umphawi wawo monga ku zinthu za padziko lapansi.

5 Ndipo adabwera kwa Alima; ndipo m’modzi amene adali patsogolo pawo adati kwa iye: Taonani, kodi achite chiyani abale angawa, pakuti iwo amanyozedwa ndi anthu onse chifukwa cha umphawi wawo, inde, ndipo makamaka ndi ansembe athu; pakuti iwo atithamangitsa ife kuchoka m’masunagoge athu amene ife tidagwira ntchito mwakhama kuwamanga ndi manja athu; ndipo iwo atithamangitsa ife chifukwa cha umphawi wathu waukulu; ndipo ife tilibe malo opembedzera Mulungu wathu; ndipo taonani, kodi tipange chiyani?

6 Ndipo tsopano pamene Alima adamva izi, iye adamutembenukira, nkhope yake kuyang’ana iye pomwepo, ndipo iye adayang’ana ndi chisangalalo chachikulu; pakuti iye adaona kuti masautso awo adawachepetsa iwo, ndipo kuti adali wokonzekera kumva mawu.

7 Kotero iye sadayankhulenso kanthu kwa khamu linalo; koma adatambasula dzanja lake, nafuula kwa iwo amene iye adawaona, amene adali olapa moonadi, nati kwa iwo:

8 Ndikuona kuti inu ndi odzichepetsa mtima, ndipo ngati ndi choncho, ndinu odala.

9 Taonani m’bale wanu wanena, Kodi tingapange chiyani?—pakuti ife tatulutsidwa m’masunagoge athu, kuti sitingapembedze Mulungu wathu.

10 Taonani, ndikunena kwa inu, kodi mukuganiza kuti simungapembedze Mulungu pokhapokha mukhale mu masunagoge anu wokha basi?

11 Ndipo moonjezera apo, ndikufunsani, kodi mukuganiza kuti mukuyenera kupembedza Mulungu kamodzi kokha pa sabata?

12 Ine ndikunena kwa inu, zilibwino kuti inu mwatulutsidwa m’masunagoge anu, kuti mukhale wodzichepetsa, ndipo kuti muphunzire nzeru; pakuti kuli koyenera kuti inu muphunzire nzeru; pakuti ndi chifukwa choti inu mwatulutsidwa, kuti inu mukunyozedwa ndi abale anu chifukwa cha umphawi wanu waukulu, kuti inu mwabweretsedwa m’kudzichepetsa kwa mtima; pakuti mudafunikira kubwera kuti mudzichepetse.

13 Ndipo tsopano, chifukwa inu mwakakamizika kuti mudzichepetse ndinu odala; pakuti munthu nthawi zina amakakamizika kukhala odzichepetsa, amafuna kulapa; ndipo tsopano ndithudi, aliyense amene walapa adzapeza chifundo, ndipo iye amene wapeza chifundo ndi kupilira kufikira chimaliziro yemweyo adzapulumutsidwa.

14 Ndipo tsopano, monga ndanena kwa inu, kuti chifukwa inu mwakakamizika kukhala wodzichepetsa, kodi simukuganiza kuti ndi odala kwambiri amene amadzichepetsadi wokha chifukwa cha mawu?

15 Inde, iye amene adzichepetsadi yekha, ndi kulapa machimo ake, ndi kupilira kufikira chimaliziro, yemweyo adzadalitsidwa—inde, kudalitsidwa kwambiri kuposa iwo amene akakamizidwa kukhala wodzichepetsa chifukwa cha umphawi wawo wochuluka.

16 Kotero, odala ndi iwo amene adzichepetsa okha popanda kukakamizidwa kukhala wodzichepetsa; kapena mwina, mu mawu ena, odala ndi iye amene akhulupilira mu mawu a Mulungu, ndi kubatizidwa popanda makani a mtima, inde, popanda kubweretsedwa kuti adziwe mawu, kapena ngakhale kukakamizidwa kudziwa, asadakhulupilire.

17 Inde, alipo ambiri amene amati: Ngati mungationetse ife chizindikiro chochokera kumwamba, pamenepo ife tidzadziwa ndithu, kenako tidzakhulupilira.

18 Tsopano ndikufunsa, kodi ichi ndi chikhulupiliro? Taonani, ndinena kwa inu, Ayi; pakuti ngati munthu adziwa chinthu alibe chifukwa chokhulupilira, pakuti iye akuchidziwa.

19 Ndipo tsopano, kodi ndiotembeleredwa mochuluka motani iye amene adziwa chifuniro cha Mulungu ndi kusachichita, kuposa iye amene angokhulupilira kokha, kapena ali ndi chifukwa chakukhulupira kokha, ndipo nkugwa mu zolakwitsa?

20 Tsopano za chinthu ichi inuyo mukuyenera muweruze. Taonani, ndikunena ndi inu, kuti ziri ku dzanja limodzi monga momwe ziliri ku linali; ndipo zidzakhala kwa munthu aliyense molingana ndi ntchito yake.

21 Ndipo tsopano monga ine ndanena zokhudzana ndi chikhulupiliro—chikhulupiliro sindicho kukhala ndi chidziwitso chonse cha zinthu; kotero ngati inu muli ndi chikhulupiliro mumayembekezera pa zinthu zimene inu simukuziona, zimene ziri zoona.

22 Ndipo tsopano, taonani, ndikunena ndi inu, ndipo ndikufuna kuti mukumbukire, kuti Mulungu ndi wachifundo kwa wonse amene akhulupilira mu dzina lake; kotero iye amakhumba, pachiyambi, kuti inu mukhulupilire, inde, ngakhale mawu ake.

23 Ndipo tsopano, iye amagawira mawu ake kudzera mwa angelo kwa amuna, inde, osati kwa amuna okha komanso kwa akazi. Tsopano izi sizokhazo; ana aang’ono amakhala ndi mawu opatsidwa kwa iwo nthawi zambiri, amene amasokoneza anzeru ndi ophunzira.

24 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, monga inu mwakhumbira kudziwa kuchokera kwa ine zimene mungachite chifukwa chakuti mukusautsidwa ndi kuponyedwa kunja—tsopano sindikufuna kuti inu muganize kuti ine ndikufuna kukuweruzani inu basi molingana ndi chimene chili choona—

25 Pakuti sindikutanthauza kuti inu nonse mwakakamizidwa kuti mudzichepetse; pakuti indetu ndikukhulupilira kuti alipo ena pakati panu amene angadzichepetse okha, angakhale mu zochitika zilizonse.

26 Tsopano, monga ine ndanena zokhudzana chikhulupiliro—kuti icho sichidziwitso chonse—ngakhale ziri ndi mawu anga. Simungathe kudziwa za chitsimikizo chake poyamba, mpaka ku ungwiro, chilichonse choposa chikhulupiliro ndi chidziwitso chonse.

27 Koma taonani, ngati inu mungadzuke ndi kudzutsa mphamvu zanu, ngakhale kuyesera pa mawu anga, ndi kuchita kachidutswa kakang’ono kachikhulupiliro, inde, ngakhale ngati simungakhumbenso kukhulupilira, lolani chikhumbo ichi chigwire ntchito mwa inu, mpakana kufikira mutakhulupilira mu njira imene inu mungapereke malo kwa gawo la mawu anga.

28 Tsopano, ife tidzafaniziritsa mawu ndi mbewu. Tsopano, ngati mungapereke malo, kuti mbewu idzalidwe mu mtima mwanu, taonani, ngati ili yoona, kapena ngati ili mbewu yabwino, ngati inu simuitaya chifukwa cha kusakhulupilira kwanu, kuti mukanize Mzimu wa Ambuye, Taonani idzayamba kufufuma mkati mwachifuwa chanu; ndipo pamene inu mumva kufufumaku, mudzayamba kunena mkati mwanu—zikuyenera kukhala kuti iyi ndi mbewu yabwino, kapena kuti mawuwa ndi abwino, pakuti ayamba kukulitsa moyo wanga; ayamba kuunikira kumvetsetsa kwanga, inde, ayamba kundikomera ine.

29 Tsopano taonani, kodi izi sizidzawonjezera chikhulupiliro chanu? Ine ndikunena kwa inu, Inde, komabe sichidakule kufika pa chidziwitso chonse.

30 Koma taonani pamene mbewu ifufuma, ndi kuphukira, ndi kuyamba kukula, kenako inu mumayenera kunena kuti mbewuyo ndi yabwino; pakuti yafufuma, ndi kuphukira ndipo yayamba kukula. Ndipo tsopano taonani, kodi izi sizidzalimbitsa chikhulupiliro chanu? Inde, zidzalimbitsa chikhulupiliro chanu; pakuti inu mudzati ndikudziwa kuti iyi ndi mbewu yabwino; pakuti yaphukira ndi kuyamba kukula.

31 Ndipo tsopano, taonani, kodi muli otsimikiza kuti iyi ndi mbewu yabwino? Ine ndikunena kwa inu, Inde, pakuti mbewu iliyonse imabeleka m’chifanizo chake.

32 Kotero, ngati mbewu yakula ndi yabwino, koma ngati mbewuyo siikula, taonani iyo siyabwino, kotero imatayidwa.

33 Ndipo tsopano, taonani, chifukwa inu mwayesera kuyesa, ndipo mwadzala mbewuyo, ndipo yafufuma, ndi kuphukira, ndipo kuyamba kukula, inu mukuyenera kudziwa kuti mbewuyo ndi yabwino.

34 Ndipo tsopano, taonani, kodi chidziwitso chanu ndi changwiro? Inde, chidziwitso chanu ndi changwiro mu chinthu chimenecho, ndipo chikhulupiliro chanu n’chosasuntha; ndipo izi chifukwa mukudziwa, pakuti mkudziwa kuti mawuwa afufumitsa miyoyo yanu, ndipo inu mukudziwa kuti iwo aphukira, kuti kumvetsetsa kwanu kudayamba kuunikiridwa, ndipo maganizo anu ayamba kukula.

35 O ndiye, kodi ichi sichoona? Ine ndikunena ndi inu, Inde, chifukwa ndi chowala, ndipo chilichonse chowala, ndi chabwino, chifukwa chimadziwika, kotero inu mukuyenera kudziwa kuti ndi chabwino, mutatha kulawa kuwalaku kodi chidziwitso chanu ndi changwiro?

36 Taonani, ndinena kwa inu, Ayi; ngakhale kuti inu simukuyenera kuika pambali chikhulupiliro chanu, pakuti inu mwangogwiritsa ntchito chikhulupiliro chanu podzala mbewu kuti muyesere kuyesa kuti mudziwe ngati mbewuyo ili yabwino.

37 Ndipo taonani, pamene mtengo ukuyamba kukula, inu mudzati: Tiyeni tiudyetse ndi chisamaliro chachikulu, kuti ungophuka mizu, kuti ukakule, ndi kubweretsa chipatso kwa ife. Ndipo tsopano taonani, ngati mungaudyetse ndi chisamaliro chachikulu udzaphuka mizu, ndi kukula, ndi kubeleka zipatso.

38 Koma ngati muulekelera mtengowo, ndi kusauganizira za chakudya chake, taonani siudzamera mizu; ndipo pamene kutentha kwa dzuwa kufika ndi kuuwotcha, chifukwa ulibe mizu iwo udzafota, ndipo inu mudzauzula ndi kuutaya.

39 Tsopano, izi siziri chifukwa mbewu sidali yabwino, ngakhalenso chifukwa chipatso chake sichikadakhala chokhumbirika; koma ndi chifukwa nthaka yanu ndiyoguga, ndipo inu simudaudyetsere mtengowo, kotero inu simungapezeko chipatso chake.

40 Ndipo motero, ngati inu simudzadyetsera mawu, kuyang’anira chitsogolo ndi diso la chikhulupiliro ku chipatso chakecho, simungathe kuthyola chipatso cha mtengo wa Moyo.

41 Koma ngati inu mudzadyetsera mawu, inde, kudyetsera mtengowo pamene wayamba kukula, mwa chikhulupiliro chanu ndi khama, ndi kuleza mtima, kuyang’ana kutsogolo kwa chipatso chakecho, udzamera mizu; ndipo taonani udzakhala mtengo ophukira ku moyo wosatha.

42 Ndipo chifukwa cha khama lanu ndi chikhulupiliro chanu ndi chipiliro chanu ndi mawu powadyetsera, kuti amere mizu mwa inu, taonani, pang’ono ndi pang’ono mudzathyola chipatso chake, chimene chili cha mtengo wapatali, chimene chili chotsekemera kuposa zonse zotsekemera, chimene chili choyera kuposa zonse zimene ziri zoyera, inde chowala kuposa chilichonse chimene chili chowala, ndipo mudzadyelera chipatso chimenechi ngakhale mpaka kukhuta, kuti simudzamvaso njala, ngakhale kumva ludzu.

43 Ndiye, abale anga, inu mudzakolola mphoto ya chikhulupiliro chanu ndi khama lanu, ndi kuleza mtima kwanu, ndi chipiliro chanu, kudikilira pa mtengowo kuti ubweretse zipatso kwa inu.

Print