Malembo Oyera
Alima 42


Mutu 42

Chibvundi ndi nthawi yoyesedwera kumthandiza munthu kuti alape ndi kutumikira Mulungu—Kugwa kudabweretsa imfa yakuthupi ndi ya uzimu pa anthu onse—Chiwombolo chimabwera kudzera mu kulapa—Mulungu mwini adatetezera ku machimo a dziko lapansi—Chifundo ndi cha okhawo olapa—Ena onse ndiwoyenera chilungamo cha Mulungu—Chifundo chimabwera chifukwa cha Chitetezero—Okhawo olapa moona ndi amene adzapulumuke. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikuona kuti pali zina zochuluka zimene zikudandaulitsa malingaliro ako, zimene iwe sungathe kuzimvetsa—zimene ndi zokhudzana ndi chilungamo cha Mulungu mu chilango cha wochimwa, pakuti iwe ukuyesera kuganiza kuti ndi kusalungama kuti wochimwa atumizidwe ku mkhalidwe wa chisoni.

2 Tsopano taona, mwana wanga, ine ndilongosola chinthu ichi kwa iwe. Pakuti taona, Ambuye Mulungu atatha kuthamangitsa makolo athu oyamba m’munda wa Edeni, kukalima m’nthaka, imene iwo adachokera—taona, iye adatulutsa munthu, ndipo iye adaika kumapeto chakum’mawa kwa munda wa Edeni, kerubi, ndi lupanga lamoto limene limatembenuka mbali zonse, kusunga mtengo wa moyo—

3 Tsopano, tikuona kuti munthu adakhala monga Mulungu, kudziwa chabwino ndi choipa; ndipo poopa kuti angaike dzanja lake, ndikuthyolanso cha mtengo wa moyo, ndi kudya ndi kukhala moyo kwamuyaya, Ambuye Mulungu adaika kerubi ndi lupanga la moto, kuti iye asadye chipatsocho—

4 Ndipo motero tikuona, kuti kudali nthawi yopatsidwa kwa munthu kuti alape, inde, nthawi yoyesedwa, nthawi yakulapa ndi kutumikira Mulungu.

5 Pakuti taona, ngati Adamu akadatambasula dzanja lake mwachangu, ndi kudya mwa mtengo wa Moyo, akadakhala moyo kwa muyaya, molingana ndi mawu a Mulungu, opanda mpata wolapa; inde, ndiponso mawu a Mulungu akadakhala opanda ntchito, ndipo dongosolo lalikulu la chipulumutso likadasokonekera.

6 Koma taona, kudaikika kwa munthu kuti afe—kotero, monga iwo adadulidwa kuchokera ku mtengo wa moyo akuyenera kudulidwa pa nkhope ya dziko lapansi—ndipo munthu adakhala wotaika kwa muyaya, inde, adakhala munthu wakugwa.

7 Ndipo tsopano, ukuona mwa ichi kuti makolo athu oyamba adadulidwa ku zonse kuthupi ndi uzimu kuchoka pamaso pa Ambuye; ndipo choncho tikuona iwo adakhala odalira kutsata chifuniro chawo.

8 Tsopano taona, sikudali kofunikira kuti munthu alanditsidwe ku imfa yakuthupiyi, pakuti izo zikadawononga dongosolo lalikulu la chisangalalo.

9 Kotero, monga mzimu sukadatha kufa, ndipo kugwa kudabweretsa pa anthu onse imfa yauzimu chimodzimodzi yakuthupi, ndiye kuti, iwo adadulidwa kuchoka pamaso pa Ambuye, kudali kofunika kuti munthu alanditsidwe kuchokera ku imfa ya uzimu.

10 Kotero, monga iwo adakhala achithupithupi, adama, ndi ausatana, mwa chilengedwe, mkhalidwe woyesedwawu udakhala mkhalidwe wa iwo kuti akonzekere; udakhala mkhalidwe wokonzekera.

11 Ndipo tsopano kumbukira, mwana wanga, pakadapanda dongosolo la chiwombolo, (kusiya pa mbali) posakhalitsa iwo atangofa mizimu yawo idali yachisoni, podulidwa kuchoka pamaso pa Ambuye.

12 Ndipo tsopano, kudalibe njira ina yolanditsa anthu mu khalidwe lakugwa kumeneku, kumene munthu adadzibweretsera yekha chifukwa cha kusamvera kwake;

13 Kotero, molingana ndi chilungamo, dongosolo la chiwombolo silikadabweretsedwa, kupatula pa mfundo za kulapa kwa anthu mu mkhalidwe wakuyesedwawu, inde, mkhalidwe wokonzekerawu; pakuti pokhapokha pali mfundo zimenezi, chifundo sichikadakhala ndi zotsatira pokhapokha chitawononga ntchito ya chilungamo. Tsopano ntchito ya chilungamo siingawonongedwe; ngati ndi choncho, Mulungu akadasiya kukhala Mulungu.

14 Ndipo choncho tikuona kuti anthu onse adagwa, ndipo adagwidwa ndi chilungamo; inde, chilungamo cha Mulungu, chimene chidaika iwo kwa muyaya kukhala odulidwa pamaso pake.

15 Ndipo tsopano, dongosolo la chifundo silikadabweretsedwa pokhapokha chitetezero chichitidwe; kotero Mulungu mwini atetezera ku machimo a dziko lapansi, kubweretsa dongosolo la chifundo, kuziziritsa zofuna za chilungamo, kuti Mulungu akhale wangwiro, Mulungu wolungama, ndiponso Mulungu wachifundo.

16 Tsopano, kulapa sikukadabwera kwa anthu pokhapokha padali chilango, chimenenso chidali chamuyaya monga moyo wa mzimu ukhalira, poikidwa motsutsana ndi dongosolo la chisangalalo, chimenenso chidali chamuyaya monga moyo wa mzimu.

17 Tsopano, munthu akadalapa bwanji pokhapokha atachimwa? Nanga akadachimwa bwanji ngati padalibe lamulo? Nanga pakadakhala bwanji lamulo ngati padalibe chilango?

18 Tsopano, padali chilango choikidwa, ndipo lamulo lachilungamo lidaperekedwa, limene lidabweretsa chisoni cha chikumbumtima kwa munthu.

19 Tsopano, ngati sipadaperekedwe lamulo—ngati munthu wapha iye akuyenera afe—kodi akadaopa kuti afa ngati iye ataphe?

20 Ndiponso, ngati sipadaperekedwe lamulo lotsutsana ndi tchimo anthu sakadaopa kuchita tchimo.

21 Ndipo ngati pakadapanda kuperekedwa lamulo, ngati anthu achimwa kodi chilungamo chikadachita chiyani, kapena ngakhale chifundo, pakuti sizikadakhala ndi chonena pa cholengedwacho?

22 Koma pali lamulo lopekedwa, ndi chilango choikidwa, ndipo kulapa kwapatsidwa; kulapa kumene, chifundo chili ndi chonena; kupanda apo, chilungamo chikhala ndi chonena cholengedwa ndi kutsata lamulo, ndipo lamulo limapereka chilango; ngati sichoncho, ntchito za chilungamo zikadawonongeka, ndipo Mulungu akadasiya kukhala Mulungu.

23 Koma Mulungu sangasiye kukhala Mulungu, ndipo chifundo chimafuna wolapa, ndipo chifundo chimabwera chifukwa cha chitetezero; ndipo chitetezero chimabweretsa chiukitso cha akufa; ndipo chiukitso cha akufa chimabweretsa anthu pamaso pa Mulungu; ndipo choncho iwo amabwenzeretsedwa pamaso pake, kuti aweruzidwe molingana ndi ntchito zawo, molingana ndi lamulo ndi chilungamo.

24 Pakuti taona, chilungamo chimachita zofuna zake zonse, ndiponso chifundo chimakhala ndi chonena zonse zimene zili zake; ndipo choncho, palibe amene amapulumutsidwa koma wolapadi amapulumutsidwa.

25 Chiyani, kodi ukuganiza kuti chifundo chingabere chilungamo? Ndikunena kwa iwe, Ayi; n’kosatheka olo pang’ono. Ngati ndi choncho, Mulungu akadasiya kukhala Mulungu.

26 Ndipo choncho Mulungu amabweretsa zolinga zake zazikulu ndi zamuyaya, zimene zidakonzedwa kuchokera pa maziko a dziko lapansi. Ndipo choncho kudzabwera chipulumutso ndi chiwombolo cha anthu, ndiponso chiwonongeko chawo ndi chisoni.

27 Kotero, O mwana wanga, aliyense amene afuna kubwera abwere ndi kudzamwa madzi a moyo kwaulele; ndipo aliyense amene safuna kubwera yemweyonso sakukakamizidwa kubwera; koma pa tsiku lomaliza chidzabwenzeretsedwa kwa iye molingana ndi ntchito zake.

28 Ngati iye akhumba kuchita zoipa, ndipo sadalape mu masiku ake, taona, choipa chidzachitidwa kwa iye, molingana ndi chibwenzeretso cha Mulungu.

29 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikufuna kuti iwe usalore zinthu izi zikuvutitsenso, ndipo ulore machimo ako okha akuvutitse iwe, ndi kuvutitsa kumene kudzakugwetsa iwe pansi mkulapa.

30 O mwana wanga, ndikufuna kuti usakanenso chilungamo cha Mulungu. Usayesetsenso kudzilungamitsa wekha ngakhale pang’ono chifukwa cha machimo ako, pokana chilungamo cha Mulungu; koma lora chilungamo cha Mulungu, ndi chifundo chake, ndi chipiliro chake zikhale ndi mphamvu zonse mumtima mwako; ndipo uzilore zikubweretse iwe pansi pa fumbi mkudzichepetsa.

31 Ndipo tsopano, O mwana wanga, iwe waitanidwa ndi Mulungu kukalalikira mawu kwa anthu awa. Ndipo tsopano, mwana wanga, pita njira yako, lalika mawu ndi choonadi ndi kudziletsa, kuti iwe ubweretse miyoyo m’kulapa, kuti dongosolo la chifundo likhale ndi chonena pa iwo. Ndipo Mulungu apereke kwa iwe ngakhale molingana ndi mawu anga. Ameni.

Print