Malembo Oyera
Alima 51


Mutu 51

Anthu a mfumu afuna kusintha lamulo ndi kukhazikitsa mfumu—Pahorani ndi anthu omasuka athandizidwa ndi mawu a anthu—Moroni akakamiza anthu a mfumu kuti ateteze dziko lawo kapena kuphedwa—Amalikiya ndi Alamani alanda mizinda yotetezedwa yambiri—Teyankumu abweza upandu wa Alamani, ndi kupha Amalikiya mu hema wake. Mdzaka za pafupifupi 67–66 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kumayambiliro a chaka cha makumi awiri ndi chisanu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, iwo atakhazikitsa mtendere pakati pa anthu a Lehi ndi athu a Moriyantoni wokhudzana ndi maiko awo, ndipo atayamba chaka cha makumi awiri ndi chisanu mumtendere.

2 Komabe, iwo sadasunge kwa nthawi yaitali mtendere wathunthu mu dzikolo, pakuti kudayamba kukhala mkangano pakati pa anthu okhudza mkulu wa oweruza Pahorani; pakuti taonani, padali gawo la anthu amene ankafuna kuti mfundo zingapo za lamulo zisinthidwe.

3 Koma taonani, Pahorani sadasinthe kapena kulora lamulo kuti lisinthidwe; kotero, iye sadamvetsere iwo amene adatumiza mawu awo ndi zopempha zawo zokhudzana ndi kusintha kwa lamulo.

4 Kotero, iwo amene ankakhumba kuti lamulo lisinthidwe adakwiya naye, ndipo adafuna kuti iye asakhalenso mkulu wa oweruza pa dzikolo; kotero padabuka mkangano wotentha wokhudzana ndi nkhaniyi, koma osati mpaka kukhetsa mwazi.

5 Ndipo zidachitika kuti iwo amene ankafuna kuti Pahorani achotsedwe pa mpando wa chiweruzo ankatchedwa anthu a mfumu, pakuti ankakhumbira kuti lamulo lisinthidwe munjira yochotsa boma laufulu ndi kukhazikitsa mfumu pa dzikolo.

6 Ndipo iwo amene ankakhumbira kuti Pahorani akhalebe mkulu wa oweruza pa dzikolo adadzitengera pawokha dzina la anthu aufulu; ndipo motero padali kugawanika pakati pawo, pakuti anthu aufuluwo adalumbira kapena kupangana kusunga maufulu awo ndi mwayi wa chipembedzo chawo mwa boma la ufulu.

7 Ndipo zidachitika kuti nkhani iyi ya mkangano wawo idathetsedwa ndi mawu a anthu. Ndipo zidachitika kuti mawu a anthu adafika mokomera anthu aufulu, ndipo Pahorani adapitiriza pa mpando wa chiweruzo, zimene zidachititsa chimwemwe chachikulu pakati pa abale a Pahorani ndiponso ambiri mwa anthu a ufulu, amenenso adakhazika anthu amfumu chete, kuti iwo sadayerekeze kutsutsa koma kukakamizika kusunga cholinga cha ufulu.

8 Tsopano iwo amene ankafuna mafumu adali obadwira pabwino, ndipo ankafuna kukhala mafumu; ndipo ankathandizidwa ndi iwo amene ankafuna mphamvu ndi ulamuliro pa anthuwo.

9 Koma taonani, iyi idali nthawi yovuta kuti mikangano yotere ikhale pakati pa anthu a Nefi; pakuti taonani, Amalikiya adali atautsanso mitima ya anthu Achilamani motsutsana ndi anthu Achinefi, ndipo iye adasonkhanitsa pamodzi ankhondo kuchokera ku mbali zonse za dzikolo, ndipo adawapatsa zida, ndi kuwakonzekeretsa ku nkhondo ndi kulimbika konse; pakuti iye adalumbira kumwa mwazi wa Moroni.

10 Koma taonani, tidzaona kuti lonjezo lake limene iye adapanga lidali lopanda pake; komabe, iye adakonzekera yekha ndi ankhondo ake kubwera kunkhondo kudzamenyana ndi Anefi.

11 Tsopano ankhondo ake sadali ambiri monga m’mene adalili kale, chifukwa cha zikwi zambiri zimene zidaphedwa m’manja mwa Anefi; koma posatengera za kutaika kwawo kwakukulu, Amalikiya adasonkhanitsa pamodzi ankhondo aakulu modabwitsa, kotero kuti iye sadaope kubwera kudziko la Zarahemula.

12 Inde, ngakhale Amalikiya mwini adabweranso, patsogolo pa Alamani. Ndipo mudali mu chaka cha makumi awiri ndi chisanu cha ulamuliro wa oweruza; ndipo idali nthawi yomweyi yomwe iwo adayamba kuthetsa zochitika za mikangano yokhudza mkulu wa oweruza, Pahorani.

13 Ndipo zidachitika kuti pamene amunawo amene ankatchedwa anthu a mfumu adamva kuti Alamani adali kubwera kudzamenyana nawo, iwo adakondwera m’mitima mwawo; ndipo adakana kutenga zida, pakuti adali wokwiya ndi mkulu wa oweruza, ndiponso ndi anthu aufulu, kuti iwo sangatenge zida kuti ateteze dziko lawo.

14 Ndipo zidachitika kuti pamene Moroni adaona izi, ndiponso kuona kuti Alamani adali kubwera kumalire adzikolo, iye adali okwiya kwambiri chifukwa cha makani a anthu amenewo amene iye adagwira ntchito molimbikira kwambiri kuti awapulumutse; inde, iye adali okwiya kwambiri; moyo wake udadzadza ndi mkwiyo motsutsana nawo.

15 Ndipo zidachitika kuti adatumiza pempho, ndi mawu a anthu, kwa kazembe wa dzikolo, kufuna kuti iye aliwerenge, ndi kum’patsa iye (Moroni) mphamvu yokakamiza ogalukirawo kuti ateteze dziko lawo kapena kuti aphedwe.

16 Pakuti chidali chosamala chake choyamba kuti athetse mikangano yotero ndi kusagwirizana pakati pa anthu; pakuti taonani, ichi chidali panthawiyo chochititsa chiwonongeko chawo chonse. Ndipo zidachitika kuti chidaperekedwa molingana ndi mawu a anthu.

17 Ndipo zidachitika kuti Moroni adalamula kuti ankhondo ake apite kukamenyana ndi anthu a mfumuwo, kukachotsa kunyada kwawo ndi kulemekezeka kwawo ndi kuwagoneka pansi, kapena atenge zida ndi kuthandizira ntchito ya ufulu.

18 Ndipo zidachitika kuti ankhondo adaguba kupita kukamenyana nawo; ndipo adachotsa kunyada kwawo ndi kulemekezeka kwawo, kotero kuti pamene iwo adakweza zida zawo zankhondo kuti amenyane ndi anthu a Moroni iwo adagwetsedwa ndi kugonekedwa pansi.

19 Ndipo zidachitika kuti adalipo zikwi zinayi a iwo ogalukira amene adagwetsedwa pansi ndi lupanga; ndipo ena a atsogoleri awo amene sadaphedwa adatengedwa ndi kuponyedwa mu ndende, pakuti kudalibe nthawi kuti azengedwe munyengo imeneyi.

20 Ndipo otsalira mwa ogalukirawo, m’malo mokanthidwa pansi ndi lupanga, adagonjera ku mbendera ya ufulu, ndipo adakakamizidwa kunyamula mbendera ya ufuluyo pa msanja zawo, ndi mizinda yawo, ndi kunyamula zida potetezera dziko lawo.

21 Ndipo motero Moroni adathetsa anthu a mfumuwo, kuti padalibepo amene ankadziwika ndi kutchulidwa kuti anthu a mfumu; ndipo motero iye adathetsa makani ndi kunyada kwa anthuwo amene ankati ndi a magazi achifumu; koma iwo adatsitsidwa pansi kuti adzichepetse okha ngati abale awo, ndi kumenyera molimba mtima ufulu wawo kuchoka kuukapolo.

22 Taonani, zidachitika kuti pamene Moroni adali akuthetsa nkhondo ndi mikangano pakati pa anthu ake, ndi kuwaika iwo mu mtendere ndi chitukuko, ndi kupanga malamulo owakonzekeretsa kunkhondo motsutsana ndi Alamani, taonani Alamani adafika ku dziko la Moroni, limene lidali m’malire ndi gombe la nyanja.

23 Ndipo zidachitika kuti Anefi sadali amphamvu zokwanira mu mzinda wa Moroni; kotero Amalikiya adawathamangitsa, ndi kupha ambiri. Ndipo zidachitika kuti Amalikiya adalanda mzindawo, inde, kulanda malinga awo onse.

24 Ndipo iwo amene adathawira kunja kwa mzinda wa Moroni adabwera ku mzinda wa Nefiha; ndiponso anthu a mzinda wa Lehi adadzisonkhanitsa pamodzi, ndipo adapanga zokonzekera komanso adali okhonzeka kuwalandira Alamani kunkhondo.

25 Koma zidachitika kuti Amalikiya sadalore kuti Alamani apite kukhondo motsutsana ndi mzinda wa Nefiha kukamenyana, koma adawasunga iwo pa gombe la nyanja, kusiya amuna mumzinda uliwonse kuti ausunge ndi kuutetezera.

26 Ndipo motero iye adapitilira, kulanda mizinda yambiri, mzinda wa Nefiha, ndi mzinda wa Lehi, ndi mzinda wa Moriyantoni, ndi mzinda wa Omineri, ndi mzinda wa Gidi, ndi mzinda wa Muleki, ndi yonse imene idali ku malire akum’mawa kwa gombe la nyanja.

27 Ndipo motero Alamani adatenga, mwa kuchenjera kwa Amalikiya, mizinda yambiri, kudzera mwa makamu awo osawerengeka, yonseyo imene idalimbitsidwa mwamphamvu potsatira malinga a Moroni; onse amene adapereka malinga kwa Alamani.

28 Ndipo zidachitika kuti iwo adayamba kugubira kumalire a dziko la Chuluka, akuthamangitsa Anefi patsogolo pawo ndi kupha ambiri.

29 Koma zidachitika kuti iwo adakumanizana ndi Teyankumu, amene adapha Moriyantoni ndipo adatsogolera anthu ake pakuthawa kwake.

30 Ndipo zidachitika kuti iye adatsogoleranso Amalikiya, pamene iye ankaguba ndi ankhondo ake ochuluka kuti akalande dziko la Chuluka, komanso dziko la kumpoto kwake.

31 Koma taonani iye adakumana ndi chokhumudwitsa pobwezedwa ndi Teyankumu ndi anthu ake, pakuti iwo adali ankhondo aakulu; pakuti munthu aliyense wa Teyankumu adaposera Alamani mu mphamvu zawo ndi mu luso lawo la nkhondo, kufikira kuti iwo adapeza mwayi pa Alamani.

32 Ndipo zidachitika kuti iwo adawatsutsa iwo, kotero kuti adawapha iwo mpaka kunada. Ndipo zidachitika kuti Teyankumu ndi anthu ake adakhoma mahema awo ku malire a dziko la Chuluka, ndipo Amalikiya adakhoma mahema awo kumalire a gombe la nyanja, ndipo potsatira njira imeneyi iwo adathamangitsidwa.

33 Ndipo zidachitika kuti pamene usiku udafika, Teyankumu ndi antchito ake adazemba ndi kupita pa usiku, ndipo adapita ku msasa wa Amalikiya; ndipo taonani, tulo tidawagonjetsa iwo chifukwa cha kutopa kwambiri, kumene kudachitika chifukwa cha ntchito ndi kutentha kwa tsikulo.

34 Ndipo zidachitika kuti Teyankumu adazemba mwamseri kupita ku hema la mfumu, ndipo abaya ndi nthungo pamtima pake; ndipo adapangitsa imfa yamfumuyo nthawi yomweyo kuti sadadzutse antchito ake.

35 Ndipo iye adabweleranso mwanseri ku msasa wake, ndipo taonani, anthu ake adali atagona, ndipo iye adawadzutsa iwo ndi kuwauza zinthu zonse zimene iye adachita.

36 Ndipo iye adachititsa kuti ankhondo ake akhale okonzeka, kuopa Alamani angadzuke ndi kubwera kwa iwo.

37 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi awiri ndi zisanu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi; ndipo choncho adatha masiku a Amalikiya.

Print