Malembo Oyera
Alima 25


Mutu 25

Ziwawa za Alamani zifalikira—Mbewu ya ansembe a Nowa iwonongeka momwe adanenera Abinadi—Alamani ambiri atembenuka ndi kuphatikizana ndi anthu a Anti-Nefi-Lehi—Akhulupilira mwa Khristu ndi kusunga chilamulo cha Mose. Mdzaka dza pafupifupi 90–77 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo taonani, tsopano zidachitika kuti Alamaniwo adali wokwiya kwambiri chifukwa adapha abale awo, kotero adalumbira kubwenzera kwa Anefi; ndipo iwo sadafunenso kupha anthu Aanti-Nefi-Lehi panthawiyo.

2 Koma adatenga ankhondo awo ndikupita ku malire a dziko la Zarahemula, ndipo adagwera kwa anthu amene adali ku dziko la Amoniha ndi kuwawononga iwo.

3 Ndipo atatha pamenepo, adakhala ndi nkhondo zambiri ndi Anefi, kumene iwo adathamangitsidwa ndi kuphedwa.

4 Ndipo pakati pa Alamani amene adaphedwa padali pafupifupi wonse a mbewu ya Amuloni ndi abale ake, amene adali ansembe a Nowa, ndipo adaphedwa ndi manja a Anefi.

5 Ndipo otsalawo, atathawira ku chipululu chakum’mawa, ndipo atalanda mphamvu ndi ulamuliro pa Alamani, adachititsa kuti ambiri mwa Alamani awonongedwe ndi moto chifukwa cha chikhulupiliro chawo—

6 Pakuti ambiri mwa iwo, atatha kutaya zambiri ndi masautso ochuluka, adayamba kusonkhezeredwa m’kukumbukira mawu amene Aroni ndi abale ake adalalikira kwa iwo mu dziko lawo; kotero adayamba kusakhulupilira miyambo ya makolo awo, ndipo adayamba kukhulupilira mwa Ambuye, ndipo kuti iye adapereka mphamvu zazikulu kwa Anefi; ndipo motero adalipo ambiri amene adatembenuka m’chipululu.

7 Ndipo zidachitika kuti olamulira amene adali otsalira a ana a Amuloni adachititsa kuti aphedwe, inde, wonse amene adakhulupilira mu zinthu zimenezi.

8 Tsopano kuphedwa uku kudachititsa kuti ambiri mwa abale awo atakasike mu mkwiyo; ndipo kudayambika mkangano m’chipululumo; ndipo Alamani adayamba kusaka mbewu za Amuloni ndi abale ake ndi kuyamba kuwapha; ndipo iwo adathawira ku chipululu cha kum’mawa.

9 Ndipo taonani iwo akusakidwabe kufikira tsiku lino ndi Alamani. Choncho mawu a Abinadi adakwaniritsidwa, amene iye adanena zokhudzana ndi mbewu ya ansembe amene adachititsa kuti iye azunzike imfa ya moto.

10 Pakuti iye adati kwa iwo: Zimene inu mudzachite kwa ine zidzakhala chifaniziro cha zinthu zomwe ziri nkudza.

11 Ndipo tsopano Abinadi adali oyambilira kuphedwa ndi moto chifukwa cha chikhulupiliro chake mwa Mulungu; tsopano izi ndi zomwe iye adatanthauza, kuti ambiri adzazunzika imfa ya moto, molingana ndi m’mene iye adazunzikira.

12 Ndipo iye adati kwa ansembe a Nowa kuti mbewu yawo idzachititsa ambiri kuti aphedwe, mu njira yofanana ndi m’mene iye adachitira, ndipo adzabalalitsidwira kutali ndi kuphedwa, monga ngati nkhosa zopanda m’busa zimathamangitsidwa ndi kuphedwa ndi zilombo za kutchire; ndipo tsopano taonani, mawu awa adakwaniritsidwa, pakuti iwo adathamangitsidwa ndi Alamani, ndipo iwo ankasakidwa, ndipo adakanthidwa.

13 Ndipo zidachitika kuti pamene Alamani adaona kuti sakadatha kuwagonjetsa Anefi adabweleranso ku dziko lawo; ndipo ambiri mwa iwo adabwera kudzakhala mu dziko la Ismaeli ndi ku dziko la Nefi, ndipo adadziphatikiza wokha kwa anthu a Mulungu, amene adali anthu a Anti-Nefi-Lehi.

14 Ndipo nawonso adakwilira zida zawo zankhondo, molingana ndi momwe abale awo adachitira, ndipo adayamba kukhala anthu wolungama; ndipo adayenda mu njira za Ambuye, ndi kutsatira kusunga malamulo ndi malemba ake.

15 Inde, ndipo iwo adasunga lamulo la Mose; pakuti kudali kofunikira kuti iwo adzisungabe lamulo la Mose, pakuti lidali lisadakwanitsidwe. Koma posatengera lamulo la Mose, iwo ankayang’anira kubwera kwa Khristu, poganizira kuti lamulo la Mose lidali chifaniziro cha kubwera kwake, ndipo pokhulipilira kuti akuyenera kuchita ntchito zakunjazo kufikira pa nthawi imene iye adzawululidwa kwa iwo.

16 Tsopano iwo sadayese kuti chipulumutso chimabwera mwa lamulo la Mose; koma lamulo la Moselo lidali kuti lilimbikitse chikhulupiliro chawo mwa Khristu; ndipo motero iwo adakhalabe ndi chiyembekezo kudzera mu chikhulupiliro, ku chipulumutso chosatha, kudalira pa mzimu wa uneneri, umene unkayankhula za zinthu zomwe ziri nkudza.

17 Ndipo tsopano taonani, Amoni ndi Aroni, ndi Omineri, ndi Himuni, ndi abale awo adakondwera kwambiri, pa chipambano chomwe iwo adali nacho pakati pa Alamani, poona kuti Ambuye adapereka kwa iwo molingana ndi mapemphero awo, ndi kuti adatsimikiziranso mawu ake kwa iwo mwapadeladela.