Malembo Oyera
Alima 54


Mutu 54

Amoroni ndi Moroni akambirana za kusinthanitsa kwa akaidi—Moroni afuna kuti Alamani achoke ndi kusiya kuukira kwawo kwakupha—Amoroni afuna kuti Anefi atule pansi zida zawo ndi kukhala m’manja mwa Alamani. Mdzaka dza pafupifupi 63 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika chakumayambiliro kwa chaka cha makumi awiri ndi zisanu n’chinayi cha ulamuliro wa oweruza, kuti Amoroni adatumiza kwa Moroni kufuna kuti iye asinthanitse akaidi.

2 Ndipo zidachitika kuti Moroni adamva chisangalalo chachikulu pa pempho limeneli, chifukwa iye ankafuna zinthu zomwe zinkapatsidwa kuti zithandizire akaidi Achilamani kuti zithandizire anthu ake; ndiponso iye ankafuna kuti anthu ake alimbitse ankhondo ake.

3 Tsopano Alamani adatenga azimayi ndi ana ambiri, ndipo padalibe mzimayi kapena mwana pakati pa akaidi onse a Moroni, kapena akaidi amene Moroni adatenga; kotero Moroni adapanga njira yoti apezere akaidi ambiri a Anefi kuchokera kwa Alamani ngati kudali kotheka.

4 Kotero iye adalemba kalata, ndipo adaitumiza kudzera kwa wantchito wa Amoroni, yemweyo amene adabweretsa kalata kwa Moroni. Tsopano awa ndiwo mawu amene iye adalemba kwa Amoroni, nati:

5 Taona, Amoroni, ine ndalemba kwa iwe pang’ono zokhudzana ndi nkhondoyi imene iwe waipalamula motsutsana ndi anthu anga, kapena kuti imene m’bale wako waipalamula motsutsana nawo, ndipo imene iwe udakali otsimikizika kuipitiriza iye atamwalira.

6 Taona, ndikuuza pang’ono zokhudzana ndi chilungamo cha Mulungu, ndi lupanga lake la mkwiyo wamphamvu zonse, limene likwezedwa pa iwe pokhapokha iwe utalapa ndi kuchotsa ankhondo ako kupita kumaiko anu, kapena kudziko la cholowa chanu, limene liri dziko la Nefi.

7 Inde, ndikadakuuza iwe zinthu izi ngati udali ndikuthekera komvera izo; inde, ndikadakuuza iwe zokhudzana ndi gahena oopsya amene akudikira kulandira akupha otero ngati iwe ndi m’bale wako mwakhalira, pokhapokha iwe utalapa ndi kuchotsa zolinga zako zakupha, ndi kubwelera ndi ankhondo ako kumaiko anu.

8 Koma monga udakanapo zinthu izi, ndi kumenyana motsutsana ndi anthu a Ambuye, ngakhale zili choncho ndikuyembekeza kuti udzachitanso kawiri.

9 Ndipo tsopano taona, ife tili okonzekera kukulandira iwe; inde, ndipo pokhapokha utachotsa zolinga zako, taona, udzachotsa mkwiyo wa Mulungu amene iwe wakhala ukumukana, ngakhale kuchiwonongeko chako chotheratu.

10 Koma, monga Ambuye ali wamoyo, ankhondo athu adzabwera pa inu pokhapokha mutachoka, ndipo posachedwa mudzayenderedwa ndi imfa. pakuti ife tidzatenganso mizinda yathu ndi maiko athu; inde, ndipo tidzasungabe chipembedzo chathu ndi cholinga cha Mulungu wathu.

11 Koma taona, ndikuyerekeza kuti ndiyankhula nawe zokhudzana ndi zinthu izi pachabe; kapena ndikuyerekeza kuti iwe ndi mwana wa gahena; kotero nditseka kalata yanga pakukuuza iwe kuti sindidzasinthanitsa akaidi, pokhapokha zikhale pa ndondomeko yoti iwe udzapereka munthu ndi mkazi wake ndi ana ake, pa mkaidi m’modzi; ngati izi ndi zomwe iwe udzachite, ine ndidzasinthanitsa.

12 Ndipo taona, ngati suchita izi, ndidzabwera motsutsana nawe ndi ankhondo anga; inde, ngakhale ndidzaveka azimayi anga ndi ana anga, ndipo ndidzabwera motsutsana nawe, ndipo ndidzakutsata iwe ngakhale kudziko lako, limenel liri dziko la cholowa chathu choyamba; inde, ndipo kudzakhala mwazi ku mwazi, inde, moyo ku moyo; ndipo ndidzakupatsa iwe nkhondo ngakhale kufikira iwe utawonongedwa kuchoka pa nkhope ya dziko lapansi.

13 Taona, ndili mu mkwiyo wanga, ndiponso anthu anga; iwe wafunafuna kutipha ife, ndipo ife timangofuna kudziteteza tokha. Koma taona, ngati iwe ufunabe kutiwononga ifenso tidzafuna kukuwononga; inde, ndipo tidzafuna dziko lathu, ndi dziko la cholowa chathu choyamba.

14 Tsopano ndikutseka kalata yanga. Ndine Moroni, ndine mtsogoleri wa anthu achinefi.

15 Tsopano zidachitika kuti Amoroni, pamene iye adalandira kalata imeneyi, adakwiya; ndipo iye adalemba kalata ina kwa Moroni, ndipo awa ndiwo mawu amene iye adalemba, nati:

16 Ine ndi Amoroni, mfumu ya Alamani; ndine m’bale wa Amalikiya amene iwe udamupha. Taona, ndidzabwenzera mwazi wake pa iwe, inde, ndipo ndidzabwera pa iwe ndi ankhondo anga pakuti sindikuopa kuopseza kwako.

17 Pakuti taona, makolo ako adalakwira abale awo, kufikira kuti adawabera iwo ufulu wawo waulamuliro pamene udali owayenera iwowo.

18 Ndipo tsopano taona, ngati inu mutatule pansi zida zanu, ndi kudzipereka nokha kulamulidwa ndi iwo amene ulamuliro ukuyenera kukhala wawo, kenako ine ndidzachititsa kuti anthu anga adzatule pansi zida zawo ndipo sadzakhalanso pa nkhondo.

19 Taona, iwe watulutsa ziopsyezo zambiri motsutsa ine ndi anthu anga, koma taona, ife sitikuopa ziopsyezo zako.

20 Komabe, ndidzalora kusinthanitsa akaidi molingana ndi pempho lako, mokondwa, kuti ine ndisunge chakudya cha anthu anga ankhondo; ndipo tidzapanga nkhondo imene idzakhala yamuyaya, kaya kuwaika Anefi ku ulamuliro wathu kapena kuwawonongeratu kwamuyaya.

21 Ndipo monga zokhudzana ndi Mulungu amene iwe ukunena ife tamukana, taona, ife sitimudziwa munthu ameneyo; ngakhale iwenso; koma ngati zili choncho kuti alipo munthu oteroyo, ife sitikudziwa koma kuti iye watipanga ife chimodzimodzi ndi inu.

22 Ndipo ngati zilichoncho kuti kuli mdyerekezi ndi gahena, taona, kodi iye sadzakutumiza iwe kumeneko kukakhala ndi m’bale wanga amene iwe udamupha, amene iwe wanena kuti iye wapita kumalo oterowo? Koma taona zinthu izi zilibe kanthu.

23 Ine ndi Amoroni, ndipo mwana wa Zoramu, makolo ako adam’kakamiza ndi kum’bweretsa kuchokera ku Yerusalemu.

24 Ndipo taona tsopano, ine ndi Mlamani olimba mtima; taona, nkhondo iyi yamemedwa kubwenzera zolakwa zawo, ndi kusunga ndi kutenga maufulu awo aulamuliro; ndipo ndikutseka kalata yanga kwa Moroni.