Malembo Oyera
Alima 62


Mutu 62

Moroni aguba kukathandizira Pahorani mu dziko la Gideoni—Anthu amfumu amene akana kuteteza dziko lawo aphedwa—Pahorani ndi Moroni atenganso Nefiha—Ambiri mwa Alamani aphatikizana ndi anthu a Amoni—Teyankumu apha Amoroni ndipo kenako iye aphedwa—Alamani athamangitsidwa mu dzikolo, ndipo mtendere ukhazikitsidwa—Helamani abwelera ku utumiki ndi kumanga mpingo. Mdzaka dza pafupifupi 62–57 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Moroni adalandira kalata imeneyi mtima wake udalimbikitsika, ndipo adadzadzidwa ndi chisangalalo chachikulu kwambiri chifukwa cha kukhulupirika kwa Pahorani, kuti sadalinso wachiwembu ku ufulu ndi cholinga cha dziko lake.

2 Koma iye adaliranso kwambiri chifukwa cha kusaweruzika kwa iwo amene adathamangitsa Pahorani pa mpando wa chiweruziro, inde, makamaka chifukwa cha iwo amene adagalukira dziko lawo ndiponso Mulungu wawo.

3 Ndipo zidachitika kuti Moroni adatenga kagulu ka anthu, molingana ndi zokhumba za Pahorani, ndipo adapereka kwa Lehi ndi Teyankumu ulamuliro pa otsalira mwa ankhondo ake, ndi kuyamba kuguba kupita ku dziko la Gideoni.

4 Ndipo adaimika mbendera ya ufulu mu malo aliwonse amene iye adalowa, ndipo adapeza chithandizo china chirichonse chomwe akadatha m’kuguba kwake konse kopita ku dziko la Gideoni.

5 Ndipo zidachitika kuti zikwi zidatsatira mbendera yakeyo, ndi kutenga malupanga awo potetezera ufulu wawo, kuti asatengedwe mu ukapolo.

6 Ndipo motero, pamene Moroni adasonkhanitsa pamodzi anthu aliwonse amene akadatha m’kuguba kwake konse, iye adabwera ku dziko la Gideoni; ndipo pogwirizanitsa ankhondo ake ndi a Pahorani iwo adakhala amphamvu kwambiri, ngakhale amphamvu kuposa anthu a Pakusi, amene adali mfumu ya omwe adagalukira amene adathamangitsa anthu omasulidwa ku dziko la Zarahemula ndipo adatenga dzikolo.

7 Ndipo zidachitika kuti Moroni ndi Pahorani adapita ndi ankhondo awo ku dziko la Zarahemula, ndipo adapita kukalimbana ndi mzindawo, ndi kukumana ndi anthu a Pakusi, kufikira kuti adabwera kudzamenyana.

8 Ndipo taonani, Pakusi adaphedwa ndipo anthu ake adatengedwa ukaidi, ndipo Pahorani adabwenzeretsedwa ku mpando wake wachiweruziro.

9 Ndipo anthu a Pakusi adalandira mulandu, molingana ndi chilamulo, komanso iwo anthu amfumu amene adatengedwa ndi kuponyedwa mu ndende; ndipo adaphedwa molingana ndi chilamulo; inde, anthu a Pakusi ndi anthu amfumuwo, aliyense amene sadanyamule chida potetezera dziko lawo, koma kumenyana nalo, adaphedwa.

10 Ndipo motero kudakhala koyenera kuti chilamulo chimenechi chidzitsatidwa mosamalitsa chifukwa cha chitetezo cha dziko lawo; inde, ndipo aliyense amene adapezeka akukana ufulu wawo ankaphedwa mwachangu molingana ndi chilamulocho.

11 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi atatu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi; Moroni ndi Pahorani atabwenzeretsa mtendere ku dziko la Zarahemula, pakati pa anthu awo omwe, atapereka imfa kwa iwo onse amene sadali okhulupirika ku chifukwa cha ufulu.

12 Ndipo zidachitika kumayambiliro kwa chaka chamakumi atatu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, Moroni mwachangu adachititsa kuti zakudya zitumizidwe, ndiponso ankhondo okwana zikwi zisanu ndi chimodzi atumizidwe kwa Helamani, kukamuthandiza pakusunga chigawo chimenecho cha dziko.

13 Ndipo iye adachititsanso kuti ankhondo okwana zikwi zisanu ndi chimodzi, ndi zakudya zokwanira, zitumizidwe kwa ankhondo a Lehi ndi Teyankumu. Ndipo zidachitika kuti izi zidachitidwa kuti alimbitse dzikolo motsutsana ndi Alamani.

14 Ndipo zidachitika kuti Moroni ndi Pahorani, atasiya gulu lalikulu la anthu mu dziko la Zarahemula, adayamba kuguba ndi gulu lalikulu la anthu kupita ku dziko la Nefiha, potsimikizika kugwetsa Alamani mu mzinda umenewo.

15 Ndipo zidachitika kuti pamene adali kuguba kupita ku dzikolo, iwo adatenga gulu lalikulu la anthu Achilamani, ndi kupha ambiri mwa iwo, ndi kutenga chakudya chawo ndi zida zawo zankhondo.

16 Ndipo zidachitika kuti atamaliza kuwatenga iwo, adachititsa kuti alowe mu pangano kuti sadzatenganso zida zawo zankhondo motsutsana ndi Anefi.

17 Ndipo pamene iwo adalowa mu pangano limeneli adawatumiza kukakhala ndi anthu a Amoni, ndipo adalipo muchiwerengero pafupifupi zikwi zinayi amene sadaphedwe.

18 Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adawatumiza iwo adatsata kuguba kwawo kupita ku dziko la Nefiha. Ndipo zidachitika kuti pamene iwo adabwera ku mzinda wa Nefiha, iwo adakhoma mahema awo m’chigwa cha Nefiha, chimene chili pafupi ndi mzinda wa Nefiha.

19 Tsopano Moroni adali ndi chikhumbo choti Alamani abwere kudzamenyana nawo, pa zigwapo; koma Alamani, podziwa za kulimba mtima kwawo kwakukulu, ndi poona kukula kwa chiwerengero chawo, kotero sadafune kubwera kudzalimbana nawo; kotero sadabwere ku nkhondo tsiku limenelo.

20 Ndipo pamene usiku udafika, Moroni adapita mu m’dima wa usiku, ndi kukwera pamwamba pa khoma kuti asunzumire ndi mbali iti ya mzindawo imene Alamani adachita msasa ndi ankhondo awo.

21 Ndipo zidachitika kuti iwo adali chakum’mawa, cha polowera; ndipo onse adali atagona. Ndipo tsopano Moroni adabwelera kwa ankhondo ake, ndi kuchititsa kuti akonze mwachangu zingwe zolimba ndi makwelero, kuti aponyedwe kuchokera pamwamba pa khomalo kufika mbali ya mkati mwa khomalo.

22 Ndipo zidachitika kuti Moroni adachititsa kuti anthu ake agube ndi kubwera pamwamba pa khomalo, ndi kudzilowetsa okha ku mbali imeneyo ya mzinda, inde, ngakhale chakumadzulo, kumene Alamani sadamange msasa ndi ankhondo awo.

23 Ndipo zidachitika kuti onse adali atalowa mu mzindawo mkati mwa usiku, pogwiritsa zingwe zawo zolimba ndi makwelero; motero pamene m’mawa udafika iwo onse adali mkati mwa makoma a mzindawo.

24 Ndipo tsopano, pamene Alamani adadzuka ndi kuona kuti ankhondo a Moroni adali mkati mwa makomawo, adagwidwa ndi mantha kwambiri, kufikira kuti adathawa kutulukira pachipata.

25 Ndipo tsopano pamene Moroni adaona kuti iwo akuthawa pamaso pake, iye adachititsa kuti anthu ake agube kukalimbana nawo, ndi kupha ambiri, ndi kuzungulira ambiri enawo, ndi kuwatenga ukaidi; ndipo otsalawo adathawira ku dziko la Moroni, limene lidali ku malire ndi gombe lanyanja.

26 Motero Moroni ndi Pahorani adatenga umwini wa mzinda wa Nefiha opanda kutaya moyo wa munthu; ndipo kudali Alamani ambiri amene adaphedwa.

27 Tsopano zidachitika kuti ambiri mwa Alamani amene adali akaidi adali kukhumbira kuphatikizana ndi anthu a Amoni ndi kukhala anthu omasulidwa.

28 Ndipo zidachitika kuti monga ambiri omwe adali kukhumbira, kwa iwo chidapatsidwa molingana ndi kukhumba kwawo.

29 Kotero, akaidi onse Achilamani adaphatikizana ndi anthu a Amoni, ndipo adayamba kugwira ntchito kwambiri, kulima m’nthaka, kulima mitundu yonse ya mbewu, nkhosa ndi ziweto zamitundu yosiyanasiyana; ndipo motero Anefi adapepukidwa ku cholemetsa chachikulu, kufikira kuti adapeputsidwa kwa akaidi onse achilamani.

30 Tsopano zidachitika kuti Moroni, atamaliza kulanda mzinda wa Nefiha, atatenga akaidi ambiri, zimene zidachepetsa ankhondo Achilamani kwambiri, ndipo atatenganso ambiri mwa Anefi amene adatengedwa ukaidi, zimene zidalimbitsa ankhondo a Moroni kwambiri, kotero Moroni adachoka ku dziko la Nefiha kupita ku dziko la Lehi.

31 Ndipo zidachitika kuti pamene Alamani adaona kuti Moroni adali kubwera motsutsana nawo, adachitanso mantha ndi kuthawa pamaso pa ankhondo a Moroni.

32 Ndipo zidachitika kuti Moroni ndi ankhondo ake adawatsatira iwo kuchokera mzinda ndi mzinda, kufikira adakumana ndi Lehi ndi Teyankumu; ndipo Alamani adathawa kuchoka kwa Lehi ndi Teyankumu, ngakhale kupita ku malire ndi gombe lanyanja, mpakana iwo adabwera ku dziko la Moroni.

33 Ndipo ankhondo Achilamani adasonkhana onse pamodzi, kotero kuti adali onse mu gulu limodzi mu dziko la Moroni. Tsopano Amoroni, mfumu ya Alamani, idalinso ndi iwo.

34 Ndipo zidachitika kuti Moroni ndi Lehi and Teyankumu adamanga msasa ndi ankhondo awo mozungulira malire a dziko la Moroni, kotero kuti Alamani adazunguliridwa ku malire ndi chipululu cha kum’mwera, ndi kumalire a chipululu cha kum’mawa.

35 Ndipo motero iwo adamanga misasa kwa usikuwo. Pakuti taonani, Anefi ndi Alamaninso adali otopa chifukwa cha kuguba kwakukulu; kotero iwo sadakonze madongosolo aliwonse mu nthawi ya usiku, kupatula Teyankumu yekha; pakuti iye adali okwiya kwambiri ndi Amoroni, kufikira kuti iye adaganiza kuti Amoroni, ndi Amalikiya m’bale wake ndi amene adayambitsa nkhondo yaikulu imeneyi ndi yosatha pakati pa iwo ndi Alamani, zimene zidachititsa nkhondo yaikulu ndi kukhetsa mwazi, inde, komanso njala yochuluka kwambiri.

36 Ndipo zidachitika kuti Teyankumu mu mkwiyo wake adapita mu msasa wa Alamani, ndipo adalowa yekha podumpha makoma a mzindawo. Ndipo iye adapita ndi chingwe, kuchoka malo ndi malo, kotero kuti adaipeza mfumuyo; ndipo adaponya nthungo kwa iye, umene udalasa iye pafupi ndi mtima. Koma taonani, mfumuyo idadzutsa antchito ake isadafe, kotero kuti iwo adathamangitsa Teyankumu, ndi kumupha.

37 Tsopano zidachitika kuti pamene Lehi ndi Moroni adadziwa kuti Teyankumu wamwalira iwo adali ndi chisoni kwambiri, pakuti taonani, iye adali munthu amene adamenyera nkhondo dziko lake molimba mtima, inde, bwenzi lenileni la ufulu, ndipo iye adali atamva masautso ambiri ochuluka. Koma taonani, adamwalira, ndipo adapita njira yadziko lonse lapansi.

38 Tsopano zidachitika kuti Moroni adaguba mawa lake, ndi kubwera kwa Alamani, kufikira kuti adawapha iwo ndi kupha kwakukulu; ndipo adawathamangitsa iwo kunja kwa dzikolo; ndipo iwo adathawa, ngakhale kuti sadabwelere pa nthawiyo motsutsana ndi Anefi.

39 Ndipo motero chidatha chaka cha makumi atatu ndi chimodzi cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi; ndipo motero adakhala ndi nkhondo, kukhetsa mwazi, ndi chilala, ndi masautso kwa nthawi ya dzaka zambiri.

40 Ndipo kudali kuphana, ndi mikangano, ndi mipatuko, ndi zoipa zosiyanasiyana pakati pa anthu a Nefi; komabe chifukwa cha olungama, inde, chifukwa cha mapemphero a olungama, iwo adapulumutsidwa.

41 Koma taonani, chifukwa cha kutalika kwakukulu kwa nkhondo pakati pa Anefi ndi Alamani ambiri adakhala olimba, chifukwa cha kutalika kwakukulu kwa nkhondoyo; ndipo ambiri adafewetsedwa chifukwa cha masautso awo, kufikira kuti adadzichepetsa okha pamaso pa Mulungu, ngakhale m’kuya kwa kudzichepetsa.

42 Ndipo zidachitika kuti atamaliza Moroni kulimbitsa zigawo za dzikolo zimene zidali zophweka kwa Alamani, mpakana atakhala olimba mokwanira, iye adabwelera ku mzinda wa Zarahemula; ndiponso Helamani adabwelera ku malo a cholowa chake; ndipo kudakhalanso mtendere wokhazikika pakati pa anthu a Nefi.

43 Ndipo Moroni adapereka ulamuliro wa ankhondo ake m’manja mwa mwana wake amene dzina lake lidali Moroniha; ndipo iye adapumulira pa ntchito ku nyumba yake kuti athe kukhala masiku ake otsala mu mtendere.

44 Ndipo Pahorani adabwelera ku mpando wa chiweruziro; ndipo Helamani adayambiranso kulalikira kwa anthu mawu a Mulungu; pakuti chifukwa cha nkhondo zambiri ndi mikangano kudakhala kofunikira kwambiri kuti lamulo liyenera kupangidwanso mu mpingo.

45 Kotero, Helamani ndi abale ake adapita, ndi kulalikira mawu a Mulungu ndi mphamvu zambiri kuti atsimikizire anthu ambiri za kuipa kwawo, zimene zidawapangitsa iwo kulapa machimo awo ndi kubatizidwa kwa Ambuye Mulungu wawo.

46 Ndipo zidachitika kuti iwo adakhazikitsanso mpingo wa Mulungu, kuzungulira dziko lonselo.

47 Inde, ndipo malamulo adapangidwa okhudzana ndi chilamulo. Ndipo oweruza awo, ndi akulu a oweruza awo adasankhidwa

48 Ndipo anthu a Nefi adayamba kuchita bwinonso mu dzikolo, ndi kuyamba kuchulukana ndi kukula m’mphamvu kwambirinso mu dzikolo. Ndipo iwo adayamba kukula mu chuma chambiri.

49 Koma posatengera chuma chawo, kapena mphamvu zawo, kapena kuchita bwino kwawo, iwo sadadzikweze mkunyada m’maso mwawo; ngakhalenso sadachedwe kukumbukira Ambuye Mulungu wawo; koma iwo adadzichepetsa okha kwambiri pamaso pake.

50 Inde, iwo adakumbukira zinthu zazikulu zimene Ambuye adawachitira kwa iwo kuti iye adawapulumutsa iwo ku imfa, ndi ku maunyolo, ndi ku ndende, ndi zosautsa zosiyanasiyana, ndipo iye adawapulutsa iwo kuchokera m’manja mwa adani awo.

51 Ndipo iwo adapemphera kwa Ambuye Mulungu wawo mosalekeza, kotero kuti Ambuye adawadalitsa iwo, molingana ndi mawu ake, mpaka kuti adakula mphamvu ndi kuchita bwino m’dzikolo.

52 Ndipo zidachitika kuti zinthu zonsezi zidachitika. Ndipo Helamani adamwalira, mu chaka cha makumi atatu ndi chisanu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi.