Malembo Oyera
Alima 33


Mutu 33

Zenosi aphunzitsa kuti anthu adzipemphera ndi kupembedza m’malo aliwonse, ndipo ziweruzo zimabwezedwa chifukwa cha Mwana—Zenoki aphunzitsa kuti chifundo chapatsidwa chifukwa cha Mwanayo—Mose adakweza mu chipululu chifaniziro cha Mwana wa Mulungu. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano atamaliza Alima kuyankhula mawu awa, iwo adatumiza kwa iye kufuna kudziwa ngati iwo akuyenera kukhulupilira mwa Mulungu m’modzi, kuti iwo akalandire chipatso chimene iye adayankhula, kapena m’mene iwo angadzalire mbewuyo, kapena mawu amene iye adayankhula, amene iye adati akuyenera kudzalidwa m’mitima mwawo; kapena mu njira yanji imene iwo akuyenera kuwonetsera chikhulupiliro chawo.

2 Ndipo Alima adati kwa iwo: Taonani, inu mwati simukadatha kupembedza Mulungu chifukwa mwatulutsidwa kunja kwa masunagoge anu. Koma taonani, ine ndikunena ndi inu, ngati mukuganiza kuti simungapembedze Mulungu, mukulakwitsa kwakukulu ndipo mukuyenera kufufuza malembo oyera; ngati inu mukuganiza kuti iwo akuphunzitsani izi, simumawamvetsa.

3 Kodi mukukumbukira kuti mudawerenga zimene Zenosi, mneneri wakale, adanena zokhudzana ndi pemphero kapena kupembedza?

4 Pakuti iye adati: Inu ndinu wachifundo, O Mulungu, pakuti mwamva pemphero langa, ngakhale pamene ndidali m’chipululu; inde mudandichitira chifundo pamene ndidapemphera zokhudzana ndi iwo amene adali adani anga, ndipo inu mudawatembenuzira kwa ine.

5 Inde, O Mulungu, ndipo inu mudandichitira chifundo pemene ine ndidafuula kwa inu m’munda mwanga; pamene ine ndidafuula kwa inu mu pemphero langa, ndipo inu mudandimvera.

6 Ndiponso, O Mulungu, pamene ine ndidatembenukira kunyumba kwanga inu mudamva pemphero langa.

7 Ndipo pamene ine ndidatembenukira m’chipinda mwanga, O Ambuye, ndi kupemphera kwa inu, inu mudandimvera ine.

8 Inde, Inu ndi wachifundo kwa ana anga pamene iwo akufuula kwa inu, kuti amvedwe ndi inu, ndipo osati ndi anthu ndipo inu mudzawamvera iwo.

9 Inde, O Mulungu, mwandichitira ine chifundo, ndipo mwamva kulira kwanga pakati pa anthu anu.

10 Inde, ndipo inu mudandimvera ine pamene ndidathamangitsidwa ndi kunyozedwa ndi adani anga; inde, inu mudamva kulira kwanga, ndipo mudakwiya ndi adani anga, ndipo mudawayendera iwo mu mkwiyo wanu ndi kuwononga kwa msanga.

11 Ndipo inu mudandimvera ine chifukwa cha masautso anga ndi kuona mtima kwanga; ndipo ndi chifukwa cha Mwana kuti inu mwandichitira chifundo chotere, kotero ine ndidzafuula kwa inu m’masautso anga onse, pakuti mwa inu muli chimwemwe changa, pakuti inu mwachotsa chiweruzo chanu pa ine, chifukwa cha Mwana wanu.

12 Ndipo tsopano Alima adati kwa iwo: Kodi mukukhulupilira malembo oyera amenewo amene adalembedwa ndi iwo akale?

13 Taonani, ngati inu mutero, mukuyenera kukhulupilira zimene Zenosi adanena; pakuti, taonani iye adati: Inu mwabweza chiweruzo chanu chifukwa cha Mwana wanu.

14 Tsopano taonani, abale anga, ndikufunsani ngati inu mudaweranga malembo oyera? Ngati mudawerenga, bwanji inu simungakhulupilire mwa Mwana wa Mulungu?

15 Pakuti kodi sikudalembedwe kuti Zenosi yekha adayankhula zinthu izi, koma Zenoki adayankhulanso za zinthu izi—

16 Pakuti taonani, iye adati: Inu mwakwiya, O Ambuye, ndi anthu awa, chifukwa iwo sakumvetsa zifundo zanu zimene mwachita pa iwo chifukwa cha Mwana wanu.

17 Ndipo tsopano, abale anga, mukuona kuti mneneri wachiwiri wakale adachitira umboni za Mwana wa Mulungu, ndipo chifukwa anthu sadamvetse mawu ake iwo adamugenda miyala mpaka kufa.

18 Koma taonani, izi sizokhazo; awa siokhawo amene adanena zokhudzana ndi Mwana wa Mulungu.

19 Taonani, iye adakambidwapo ndi Mose; inde, ndipo taonani chifanizo chidakwezedwa m’chipululu, kuti wina aliyense amene angayang’ane pa icho akhale ndi moyo. Ndipo ambiri adayang’ana ndi kukhala ndi moyo.

20 Koma ochepa adamvetsa tanthauzo la zinthu zimenezo, ndipo izi chifukwa cha kulimba kwa mitima yawo. Koma adalipo ambiri amene adali olimba kuti sadafune kuyang’ana, kotero adawonongeka. Tsopano chifukwa chomwe iwo sadafune kuyang’ana ndi choti iwo sadakhulupilire kuti chikadatha kuwachiritsa.

21 O abale anga, ngati mukadachiritsidwa pakuyang’ana pakuponya maso anu okha kuti muchiritsidwe, simukadayang’ana mwachangu kodi, kapena mungalimbitse mitima yanu mu kusakhulupilira, ndi kuchedwa, kuti musaponye maso anu, kuti mungawonongedwe?

22 Ngati n’choncho, tsoka libwere pa inu; koma ngati sichoncho, ndiye ponyani maso anu ndi kuyamba kukhulupilira mwa Mwana wa Mulungu, kuti iye adzabwera ndi kuwombola anthu ake, ndipo kuti iye adzazunzika ndi kufa kutetezera machimo awo; ndipo kuti iye adzaukanso kwa akufa, zimene zidzabweretse chiukitso, kuti anthu onse adzaime pamaso pake, kudzaweruzidwa pa tsiku lomaliza ndi tsiku lachiweruzo, molingana ndi ntchito zawo.

23 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa, ndikukhumba kuti inu mudzale mawu awa m’mitima mwanu, ndipo pamene ayamba kufufuma monga choncho adyetsereni ndi chikhulupiliro chanu. Ndipo taonani, adzakhala mtengo, kukula mwa inu kufikira ku moyo wosatha. Ndipo Mulungu athe kudzakupatsani inu kuti zolemetsa zanu zikhale zopepuka, kudzera mu chimwemwe cha Mwana wake. Ndipo ngakhale zonsezi mungathe kuchita ngati mukufuna. Ameni