Malamulo a Alima kwa mwana wake Helamani.
Yophatikiza mitu 36 ndi 37.
Mutu 36
Alima achitira umboni kwa Helamani wa kutembenuka kwake atatha kuona mngelo—Iye adazunzika mu ululu kwa mzimu wotaika; iye adaitanira pa dzina la Yesu, ndipo kenako adabadwa mwa Mulungu—Chisangalalo chokoma chidadzadza moyo wake—Iye adaona magulu a angelo akutamanda Mulungu—Otembenuka ambiri adalawa ndi ndikuona monga iye adalawira ndi kuona. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.
1 Mwana wanga, tchera khutu ku mawu anga; pakuti ndikulumbira kwa iwe, kuti monga momwe iwe udzasunge malamulo a Mulungu udzachita bwino mu dziko.
2 Ndikufuna kuti iwe uchite monga ine ndachitira, pokumbukira ukapolo wa makolo athu; pakuti iwo adali mu ukapolo, ndipo palibe amene akadawapulumutsa kupatula adali Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isaki, ndi Mulungu wa Yakobo; ndipo ndithu, iye adawapulumutsadi iwo mu masautso awo.
3 Ndipo tsopano, O mwana wanga Helamani, taona, iwe udakali mu ubwana wako, ndipo kotero, ndikukupempha iwe kuti umvere mawu anga ndi kuphunzira kwa ine; pakuti ndikudziwa kuti onse amene adzaika chikhulupiliro chake mwa Mulungu adzathandizidwa m’mayesero awo, ndi mu mavuto awo, ndi mu masautso awo, ndipo adzakwezedwa pa tsiku lomaliza.
4 Ndipo sindikufuna kuti iwe uganize kuti ine ndikudziwa mwandekha—osati mwa kuthupi koma mwauzimu, osati za maganizo achithupithupi koma a Mulungu.
5 Tsopano, taona, ndikunena ndi iwe, ngati ndidakapanda kubadwa mwa Mulungu sindikadadziwa zithu izi; koma Mulungu, mwa pakamwa pa angelo ake oyera, adadziwitsa zinthu izi kwa ine, osati chifukwa cha kuyenera kwanga.
6 Pakuti ine ndinkayendayenda ndi ana a Mosiya, kufunafuna kuwononga mpingo wa Mulungu, koma taona, Mulungu adatumiza mngelo wake oyera kudzatiletsa ife panjira.
7 Ndipo taona, iye adayankhula kwa ife, monga ngati adali mawu a bingu, ndipo dziko lonse lidagwedezeka pansi pa mapazi athu; ndipo ife tidagwa pansi, pakuti mantha a Ambuye adadza pa ife.
8 Koma taona, mawuwo adati kwa ine: Dzuka. Ndipo ndidadzuka ndi kuimilira, ndipo ndidaona mngelo.
9 Ndipo iye adati kwa ine: Ngati ukufuna mwa iwe mwini kuwonongeka, usafunenso kuwononga Mpingo wa Mulungu.
10 Ndipo zidachitika kuti ine ndidagwa pansi; ndipo kudali kwa masiku atatu, usana ndi usiku, omwe ine sindidathe kutsegula pakamwa panga, ngakhale kugwiritsa ntchito ziwalo zanga.
11 Ndipo mngeloyo adayankhula zinthu zambiri kwa ine, zimene zidamvedwa ndi abale anga, koma ine sindidazimve; pakuti pamene ndidamva mawu—Ngati iwe ukufuna kuwonongedwa mwa iwe wekha, usafunenso kuwononga mpingo wa Mulungu—ndidagwidwa ndi mantha aakulu ndi kututumuka kuopa kuti mwina ndingawonongedwe, mpaka ndidagwa pansi ndipo sindidamvenso.
12 Koma ndidasautsika ndi mazunzo amuyaya, pakuti mzimu wanga udazunzika ndi mantha aakulu ndi kusautsika ndi machimo anga onse.
13 Inde, ndidakumbukira machimo anga onse ndi mphulupulu, pakuti ndidazunzika ndi kuwawa kwa gahena; inde, ndidaona kuti ndidapandukira motsutsana ndi Mulungu, ndipo kuti sindidasunge malamulo ake oyera.
14 Inde, ndidapha ambiri a ana ake, kapena kuti ndidawatsogolera ku chiwonongeko; inde, ndipo mapeto ake zambiri zidali mphulupulu zanga, kuti ganizo lokha lobwera pamaso pa Mulungu wanga lidagwira mzimu wanga ndi kuopsya kosasimbika.
15 O, ndidaganiza ine, kuti ndikadathamangitsidwa ndi kukhala otheratu zonse mzimu ndi thupi, kuti ndisabweretsedwe kuti ndiime pamaso pa Mulungu wanga, kuti ndiweruzidwe pa ntchito zanga.
16 Ndipo tsopano, kwa masiku atatu usana ndi usiku ndidasautsidwa, ngakhale ndi ululu kwa mzimu wokanidwa.
17 Ndipo zidachitika kuti pamene ndidazunzidwa ndi mazunzo choncho, pamene ndidakhumudwitsidwa ndi chikumbutso cha machimo anga ambiri, taona, ndidakumbukiranso kuti ndidamva mawu a atate anga akunenera kwa anthu zokhudzana ndi kubwera kwa m’modzi Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, kudzatetezera ku machimo a dziko lapansi.
18 Tsopano, pamene maganizo anga adagwira pa ganizo limeneri, ndidalira mkati mwa mtima wanga: O Yesu, inu mwana wa Mulungu, ndichitireni chifundo, amene ndiri mu ndulu yowawa, ndipo ndazingidwa ndi maunyolo osatha a imfa.
19 Ndipo tsopano, taona, pamene ndidaganiza izi, sindidakumbukirenso zowawa zanga; inde, sindidazunzikenso ndi chikumbutso cha machimo anga.
20 Ndipo O, chisangalalo chotani, ndipo kuwala kodabwitsa kotani komwe ine ndidaona; inde, mzimu wanga udadzadzidwa ndi chisangalalo chachikulu monganso udaliri ululu wanga!
21 Inde, ndinena kwa iwe, mwana wanga, kuti sipangakhale kanthu kopambana ndi kowawa ngati udaliri ululu wanga. Inde, ndiponso ndikunena ndi iwe, mwana wanga, kuti ku dzanja linali, sikungakhale chinthu chokongola ndi chokoma ngati chisangalalo changa.
22 Inde, ndidaganiza ndidaona, monga ngati atate athu Lehi adaonera, Mulungu atakhala pa mpando wachifumu wake, atazunguliridwa ndi magulu a angelo osawerengeka, ali mu mchitidwe woimba ndi kutamanda Mulungu wawo; inde ndipo mzimu wanga udafunitsitsa kukhala kumeneko.
23 Koma taona, ziwalo zanga zidalandiranso mphamvu, ndipo ine ndidaimilira pamapazi anga, ndi kuonetsera kwa anthu kuti ndidabadwa mwa Mulungu.
24 Inde, ndipo kuchokera pa nthawi imeneyo kufikira tsopano, ndagwira ntchito mosalekeza, kuti ndithe kubweretsa miyoyo m’kulapa; kuti ndithe kubweretsa iwo kulawa za chisangalalo choposera chimene ine ndidalawa; kuti iwo athenso kubadwa mwa Mulungu, ndi kudzadzidwa ndi Mzimu Oyera.
25 Inde, ndipo tsopano taona, O mwana wanga, Ambuye wandipatsa ine chisangalalo chachikulu kwambiri mu chipatso cha ntchito zanga.
26 Pakuti chifukwa cha mawu amene iye wandigaila ine, taona, ambiri abadwa mwa Mulungu, ndipo alawa monga ine ndalawira, ndipo aona maso ndi maso monga ine ndaonera; kotero iwo akudziwa zinthu izi zimene ine ndanena, monga ine ndikudziwira; ndipo chidziwitso chimene ine ndiri nacho ndi cha Mulungu.
27 Ndipo ndathandizidwa pansi pa mayesero ndi mavuto amitundu yonse, inde, ndipo mu masautso amitundu yonse; inde, Mulungu wandipulumutsa ine kuchokera ku ndende, ndi ku nsinga, ndi ku imfa; inde, ndipo ndimaika chikhulupiliro changa mwa iye, ndipo iye adzandipulumutsabe ine.
28 Ndipo ndikudziwa kuti iye adzandiukitsa ine pa tsiku lomaliza, kuti ndikakhale ndi iye mu ulemelero; inde, ndipo ndidzamutamanda iye kosatha, pakuti iye wabweretsa makolo athu kuchoka ku Igupto, ndipo wameza Aigupto mu Nyanja Yofiira; ndipo iye adawatsogolera iwo mwa mphamvu yake kulowa ku dziko la lonjezano; inde, ndipo waapulumutsa iwo kutuluka mu nsinga ndi ukapolo kuchokera ku nthawi ndi nthawi.
29 Inde, ndipo wabweretsanso makolo athu kuchokera ku dziko la Yerusalemu; ndipo iye, ndi mphamvu yake yosatha, wapulumutsa iwo kuchokera ku nsinga ndi ukapolo, kuchokera ku nthawi ndi nthawi ngakhale kufikira ku tsiku la lero; ndipo ine ndakhala ndikukumbukirabe za ukapolo wawo, inde, iwenso ukuyenera kukumbukirabe, monga ine ndachitira, ukapolo wawo.
30 Koma taona, mwana wanga, izi sizokhazi; pakuti ukuyenera kudziwa monga ine ndidziwira, kuti monga momwe iwe udzasunge malamulo a Mulungu udzachita bwino pa dziko; ndipo ukuyenera kudziwanso, kuti monga momwe sudzasunga malamulo a Mulungu udzadulidwa kuchoka pamaso pake. Tsopano izi ndi molingana ndi mawu ake.