Malembo Oyera
Alima 37


Mutu 37

Mapale a Mkuwa ndi malembo oyera ena asugidwa kudzabweretsa miyoyo ku chipulumutso—Ayaredi awonongedwa chifukwa cha kuipa kwawo—Malumbiro awo achinsisi ndi mapangano awo akuyenera kubisidwa kwa anthu—Funsani kwa Ambuye mu zochita zanu zonse—Monga Liyahona lidatsogolera a Nefi, choncho mawu a Khristu amatsogolera anthu ku moyo wamuyaya. Mdzaka dza pafupifupi 74 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, mwana wanga Helamani, ndikukulamula iwe kuti utenge zolemba izi zimene zidapatsidwa kwa ine.

2 Ndiponso ndikukulamula iwe kuti usunge zolemba za anthu awa, molingana ndi m’mene ine ndachitira, pa mapale a Nefi, ndi kusunga zinthu zonsezi zopatulika zimene ine ndazisunga, monga ine ndazisungira; pakuti zili pa cholinga chanzeru kuti zisungidwe.

3 Ndipo mapale amkuwa awa, amene ali ndi zozokotedwa izi, amene ali ndi zolemba za malembo oyera pa iwo, amene ali ndi mibadwo ya makolo athu, ngakhale kuchokera pa chiyambi—

4 Taona, zidaneneredwa ndi makolo athu, kuti izo zikuyenera kudzasungidwa ndi kupatsidwa kuchokera ku m’badwo umodzi kupita ku umzake, ndipo zidzasungidwa ndi kusamalidwa ndi dzanja la Ambuye kufikira zidzapita ku pfuko lilironse, mtundu, lilime, ndi anthu, kuti iwo adziwe za zinsinsi zili m’menemo.

5 Ndipo tsopano taona, ngati zasungidwa zikuyenera kukhalabe zowala; inde, ndipo zidzasunga kuwala kwake; inde ndiponso mapale onse amene ali ndi malembo oyera.

6 Tsopano iwe ukhonza kuganiza kuti uku ndi kupusa mwa ine; koma taona ndikunena ndi iwe, kuti kudzera mu zinthu zazing’ono ndi zophweka zinthu zazikulu zimachitika; ndipo mu njira zazing’ono m’nthawi zambiri zimatsutsa anzeru.

7 Ndipo Ambuye Mulungu amagwira ntchito mu njirayi kuti akwaniritse zolinga zake zazikulu ndi zamuyaya; ndipo kudzera mu njira zazing’ono Ambuye amatsutsa anzeru ndi kubweretsa chipulumutso ku miyoyo yambiri.

8 Ndipo tsopano, mpaka pano chakhala nzeru mwa Mulungu kuti zinthu izi zikuyenera kusungidwa, pakuti taona, zakuza chikumbutso cha anthu awa, ndi kutsimikizira ambiri njira zawo zolakwika zambiri, ndi kuwabweretsa iwo ku chidziwitso cha Mulungu wawo kufika ku chipulumutso cha miyoyo yawo.

9 Inde, ndikunena ndi iwe, kukadapanda zinthu izi zimene zolemba izi zili nazo, zimene zili pa mapale awa, Amoni ndi abale ake sakadatsimikizira zikwi zambiri za Alamani za kusalondola kwa miyambo ya makolo awo; zolemba izi ndi mawu awo zidabweretsa iwo m’kulapa, ndiye kuti, adawabweretsa ku chidziwitso cha Ambuye Mulungu wawo, ndi kukondwera mwa Yesu Khristu muwomboli wawo.

10 Ndipo ndani adziwa koma chimene zidzakhale njira yobweretsera zikwi zambiri za iwo, inde ndiponso zikwi zambiri za abale athu ouma makosi, Anefi, amene tsopano alimbitsa mitima yawo mu tchimo ndi mphulupulu, ku chidziwitso cha Muwomboli wawo?

11 Tsopano zinsinsi izi sizidadziwitsidwe kwathunthu kwa ine; kotero ndidzaleka.

12 Ndipo zingakhale zokwanira ngati ndingonena kuti zasungidwa pa cholinga cha nzeru, chimene cholinga chake chikudziwika ndi Mulungu; pakuti iye amalangiza mwanzeru pantchito zake zonse, ndipo njira zake ndi zoongoka, ndipo njira yake ndi yozungulira yamuyaya.

13 O kumbukira, kumbukira, mwana wanga Helamani, ndi wokhwima chotani malamulo a Mulungu. Ndipo iye adati: Ngati iwe udzasunge malamulo anga udzachita bwino mu dziko—koma ngati iwe siudzasunga malamulo anga udzadulidwa kuchoka pamaso pake.

14 Ndipo tsopano kumbukira, mwana wanga, kuti Mulungu wakudalira iwe ndi zinthu izi, zimene zili zopatulika, zimene iye wazisunga zopatulika, ndiponso zimene iye adzazisunge ndi kuzisamala pa cholinga cha nzeru mwa iye, kuti iye athe kuonetsa mphamvu yake kwa mibadwo yamtsogolo.

15 Ndipo tsopano taona, ndikukuuza iwe kudzera mwa mzimu wa uneneri, kuti ngati ulakwire malamulo a Mulungu, taona, zinthu izi zimene zili zopatulika zidzalandidwa kwa iwe mwa mphamvu ya Mulungu, ndipo iwe udzaperekedwa kwa Satana, kuti akupete iwe ngati mankhusu pamaso pa mphepo.

16 Koma ngati usunga malamulo a Mulungu, ndi kuchita ndi zinthu izi zimene zili zopatulika molingana ndi zimene Ambuye akulamulira iwe, (pakuti ukuyenera kupempha kwa Ambuye mu zinthu zonse zimene ukuyenera kuchita nazo) taona, palibe mphamvu padziko lapansi kapena ku gahena ingathe kuzitenga kwa iwe, pakuti Mulungu ndi wamphamvu za kukwaniritsa mawu ake onse.

17 Pakuti iye adzakwaniritsa malonjezano ake onse amene adzapange kwa iwe, pakuti iye wakwaniritsa malonjezo ake amene adapanga kwa makolo athu.

18 Pakuti iye adalonjeza kwa iwo kuti adzasunga zinthu izi pa cholinga chanzeru mwa iye, kuti iye aonetsere mphamvu yake ku mibadwo yamtsogolo.

19 Ndipo tsopano taona, cholinga chimodzi iye wakwaniritsa, ngakhale kubwenzeretsa zikwi zambiri za Alamani ku chidziwitso cha choonadi; ndipo iye waonetsa mphamvu yake kwa iwo, ndiponso adzaonetserabe mphamvu yake kwa iwo kwa mibadwo yamtsogolo; kotero zidzasungidwa.

20 Kotero ndikukulamula iwe, mwana wanga Helamani, kuti ukhale wakhama pakukwaniritsa mawu anga onse, ndipo kuti ukhale wakhama pakusunga malamulo a Mulungu monga m’mene alembedwera.

21 Ndipo tsopano, ndiyankhula kwa iwe zokhudzana ndi mapale makumi awiri ndi mphambu zinayi, kuti uwasunge, kuti zinsinsi ndi ntchito za mdima, ndi ntchito zachinsinsi zawo, kapena ntchito za chinsinsi za anthu amene awonongedwa, ziwonekere kwa anthu awa; inde, kupha kwawo konse, ndi kuba, ndi kulanda, ndi kuipa kwawo konse ndi zonyansa, zikhonza kuonetseredwa kwa anthu awa; inde, ndipo kuti iwe usunge zomasulirazi.

22 Pakuti taona, Ambuye adaona kuti anthu awo adayamba kugwira ntchito mumdima, inde, kuchita zakupha mwachinsinsi ndi zonyansa; kotero Ambuye adati, ngati iwo sadalape iwo akuyenera kuwonongedwa kuchokera pa pankhope ya dziko lapansi.

23 Ndipo Ambuye adati: Ndidzakonzera kwa mtumiki wanga Gazelemu, mwala umene udzawalira mu mdima mkuyeretsa, kuti ndipeze kwa anthu anga amene amanditumikira, kuti ndipeze kwa iwo ntchito za abale awo, inde, ntchito zawo zachinsinsi, ndi ntchito zawo za mdima ndi kuipa kwawo ndi zonyansa zawo.

24 Ndipo tsopano, mwana wanga, zomasulira izi zidakonzedwa kuti mawu a Mulungu akwaniritsidwe, amane iye adayankhula, nati:

25 Ndidzatulutsa kuchoka mumdima n’kuika poyera ntchito zawo zonse zachinsinsi ndi zonyansa zawo; ndipo kupatula iwo atalapa ndidzawawononga iwo kuchoka pa nkhope ya dziko lapansi; ndipo ndidzabweretsa poyera zachinsinsi zawo zonse ndi zonyansa, kwa mtundu uliwonse umene pambuyo pake udzalandira dzikolo.

26 Ndipo tsopano, mwana wanga, tikuona kuti iwo sadalape, kotero iwo awonongedwa, ndipo motero mawu a Mulungu akwaniritsidwa; inde, zonyansa zawo zobisika zatulutsidwa kuchoka mumdima ndipo zadziwika kwa ife.

27 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikukulamula iwe kuti usunge malumbiro awo onse, ndi mapangano awo, ndi migwirizano yawo mu zinsinsi zawo zonyasa; inde, ndi zizindikiro ndi zodabwitsa zawo zonse iwe udzazisunga kwa anthu awa, kuti iwo asazidziwe, kuopa kuti mwina angagwerenso mumdima ndi kuwonongedwa.

28 Pakuti taona, pali thembelero pa dziko lonseli, kuti chiwonongeko chidzagwera pa onse ogwira ntchito za mdima, molingana ndi mphamvu ya Mulungu, pamene iwo akhwima kwathunthu; kotero ndikukhumba kuti anthu awa asawonongedwe.

29 Kotero iwe udzasunga madongosolo achinsinsiwa a malumbiro awo ndi mapangano awo kwa anthu awa, ndipo zoipa zawo zokha ndi kuphana kwawo ndi zonyansa zawo iwe udzawadziwitsa iwo; ndipo udzawaphunzitsa iwo kudana ndi zoipa zotere ndi zonyansa ndi zophana; ndipo iwe udzawaphunzitsanso iwo kuti anthu awa adawonongedwa pa nkhani ya zoipa zawo ndi zonyansa ndi kuphana kwawo.

30 Pakuti taona, adapha aneneri onse a Ambuye amene adabwera pakati pawo kudzalalika kwa iwo zokhudzana ndi kusaweruzika kwawo; ndipo mwazi wa iwo amene adawapha udalira kwa Ambuye Mulungu wawo kuti abwenzere pa iwo amene adali kuwapha; ndipo motero ziweruzo za Mulungu zidadza pa awa ochita ntchito zamdima ndi zinsinsi zonyansa.

31 Inde, ndipo likhale lotembeleredwa dzikoli kunthawi zosatha kwa iwo ochita za mdima ndi magulu a zachinsinsi, ngakhale kuchiwonongeko, pokhapokha iwo atalapa asadakhwime mwathunthu.

32 Ndipo tsopano, mwana wanga, kumbukira mawu amene ine ndayankhula kwa iwe, usapereke madongosolo azachinsinsiwo kwa anthu awa, koma uwaphunzitse iwo kudana ndi tchimo kosatha ndi kusaweruzika.

33 Ulalikire kwa iwo kulapa, ndi chikhulupiliro mwa Ambuye Yesu Khristu; uwaphunzitse kudzichepetsa wokha ndi kukhala ofatsa ndi ochidzichepetsa mumtima; uwaphunzitse kupilira m’mayesero aliwonse a mdyerekezi, ndi chikhulupiliro chawo mwa Ambuye Yesu Khristu.

34 Uwaphunzitse iwo kusatopa ndi ntchito zabwino, koma kuti akhale ofatsa ndi odzichepetsa mumtima; pakuti oterowo adzapeza mpumulo ku miyoyo yawo.

35 O, kumbukira, mwana wanga, ndi kuphunzira nzeru mu ubwana wako; inde, phunzira mu ubwana wako kusunga malamulo a Mulungu.

36 Inde, ndi kulira kwa Mulungu pa thandizo lako; inde, lora zochita zako zonse zikhale kwa Ambuye, ndipo kulikonse komwe upita lora kuti kukhale mwa Ambuye; inde, lora maganizo ako onse alunjike kwa Ambuye; inde, lora zokonda za mtima wako ziikidwe pa Ambuye kwamuyaya.

37 Funsa kwa Ambuye mu zochita zako zonse, ndipo iye adzakulondolera iwe kuzabwino; inde, pamene iwe ukugona pansi usiku, gona pansi mwa Ambuye, kuti iye akuyang’anire iwe m’tulo tako; ndipo pamene udzuka m’mawa lora mtima wako udzadze ndi chiyamiko kwa Mulungu; ndipo ngati iwe uchita zinthu izi, udzakwezedwa pa tsiku lomaliza.

38 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndili ndi zina zoti ndinene zokhudzana ndi chinthu chimene makolo athu adachitcha mpira, kapena chotsogolera—kapena makolo athu adachitcha Liyahona, chimene chili, kutanthauziridwa, kampasi; ndipo Ambuye adachikonza.

39 Ndipo taona, sipangakhale munthu aliyense angagwire ntchito mwaupangiri wopatsa chidwi chotere. Ndipo taona, chidapangidwa kuti chiwonetse makolo athu njira imene iwo akuyenera kuyenda m’chipululu.

40 Ndipo chimagwira ntchito kwa iwo molingana ndi chikhulupiliro chawo mwa Mulungu; kotero, ngati iwo adali ndi chikhulupiliro kukhulupilira kuti Mulungu akhonza kuchititsa zitsulo zopotazo ziloze njira imene iwo akuyenera kupita, taonani, zimachitika; kotero iwo adali ndi chozizwitsa chimenechi, ndiponso zozizwitsa zina zambiri zidachitidwa ndi mphamvu ya Mulungu, tsiku ndi tsiku.

41 Komabe, chifukwa cha zodabwitsa zimenezo zinkachitika mwa njira zazing’ono zidawaonetsa kwa iwo ntchito zodabwitsa. Iwo adali aulesi, ndipo adaiwala kuonetsa chikhulupiliro chawo ndi khama lawo ndipo potero ntchito zodabwitsazo zidasiya, ndipo sadapite patsogolo pa ulendo wawo;

42 Kotero, adakhalabe m’chipululu, kapena sadayende njira yolondola, ndipo adasautsika ndi njala ndi ludzu, chifukwa cha zolakwitsa zawo.

43 Ndipo tsopano, mwana wanga, ndikufuna kuti umvetsetse kuti zinthu izi siziri zopanda chithunzithunzi; pakuti monga mokolo athu adali aulesi kumvera ku kampasi imeneyi (tsopano zinthu izi zidali zakuthupi) iwo sadachite bwino; ngakhale momwemonso ndi zinthu zimene zili zauzimu.

44 Pakuti taona, kuli kophweka kumvera mawu a Khristu, amene adzalozera kwa iwe mu njira yoongoka yamuyaya, monga m’mene zidalili ndi makolo athu pomvetsera ku kampasi imeneyi, imene inkaloza kwa iwo njira yoongoka kupita ku dziko lalonjezo.

45 Ndipo tsopano ndikunena, kodi palibe chifanizo pa chinthu ichi? Pakuti monga mwandithu ngati kampasiyi idawabweretsa makolo athu, potsatira njira yake, ku dziko lalonjezo, adzakhala mawu a Khristu, ngati ife titsatira njira yawo, adzatitengera ife kupitilira chigwa cha chisonichi kufika ku dziko labwino kwambiri lalonjezo.

46 O, mwana wanga, usatilore ife tikhale aulesi chifukwa cha kuphweka kwa njira; pakuti kudatero ndi makolo athu; pakuti choncho kudakonzeredwa kwa iwo, kuti ngati iwo angayang’ane akakhale ndi moyo; ngakhale momwemonso ziliri ndi ife. Njira yakonzedwa, ndipo ngati ife tingayang’ane tidzakhala moyo kwamuyaya.

47 Ndipo tsopano mwana wanga, ona kuti ukusamalira zinthu zopatulikazi, inde, ona kuti ukuyang’ana kwa Mulungu ndi kukhala moyo. Pita kwa anthu awa ndi kulalikira mawu, ndipo khala odziletsa. Mwana wanga, tsala bwino.