Malembo Oyera
Alima 28


Mutu 28

Alamani agonjetsedwa ku nkhondo yoopsa—Makumi a zikwi aphedwa—Oipa aperekedwa ku mkhalidwe wa tsoka losatha; wolungama apeza chimwemwe chosatha Mdzaka dza pafupifupi 77–76 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano zidachitika kuti anthu a Amoni atatha kukhazikika mu dziko la Yeresoni, ndipo mpingo nawonso udakhazikitsidwa mu dziko la Yeresoni, ndipo ankhondo Anefi adakhazikitsidwa mozungulira dziko la Yeresoni, inde, mu malire onse ozungulira dziko la Zarahemula; taonani ankhondo a Alamani adali atatsatira abale awo ku chipululu.

2 Ndipo choncho kudali nkhondo yoopsa; inde, monga imene siidadziwikepo pakati pa anthu onse m’dzikolo kuchokera pa nthawi yomwe Lehi adachoka ku Yerusalemu; inde, ndipo makumi a zikwi za a Alamani adaphedwa ndi kubalalitsidwira kutali.

3 Inde, ndiponso kudali kuphedwa koopsa pakati pa anthu a Nefi, komabe, Alamani adathamangitsidwa ndi kubalalitsidwa, ndipo anthu a Nefi adabwelera ku dziko lawo.

4 Ndipo tsopano iyi idali nthawi yomwe kudali chisoni ndi maliro aakulu kumveka m’dziko lonselo, pakati pa anthu wonse a Nefi—

5 Inde, kulira kwa akazi amasiye kulilira amuna awo, ndiponso abambo kulilira ana awo aamuna ndi ana aakazi kulilira alongo awo, inde, mchimwene kulilira tate wawo; ndipo motero kulira kwa chisoni kudamveka pakati pawo wonse, kulilira achibale awo amene adaphedwa.

6 Ndipo tsopano ndithu ili lidali tsiku la chisoni; inde, nthawi ya mwambo, ndi nthawi ya kusala kudya kwambiri ndi kupemphera.

7 Ndipo kotero chidatha chaka cha khumi ndi chisanu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi;

8 Ndipo iyi ndi nkhani ya Amoni ndi Abale ake, maulendo awo mu dziko la Nefi, mazunzo awo mu dzikolo, zisoni zawo, ndi masautso awo, ndi chisangalalo chawo chosamvetsetseka, ndi kulandiridwa ndi kutetezedwa kwa abale mu dziko la Yeresoni. Ndipo tsopano Ambuye, Muwomboli wa anthu onse, adalitse miyoyo yawo kwamuyaya.

9 Ndipo iyi ndi nkhani ya nkhondo ndi mikangano pakati pa Anefi, ndinso nkhondo pakati pa Anefi ndi Alamani; ndi kutha kwa dzaka khumi ndi chisanu cha ulamuliro wa oweruza.

10 Ndipo kuchokera pa chaka choyamba mpaka cha khumi ndi chisanu chabweretsa chiwonongeko cha miyoyo zikwi zochuluka; inde, zabweretsa zochitika zoopsya ndi kukhetsa mwazi.

11 Ndipo matupi a zikwi zochuluka agonekedwa pansi panthaka, pamene matupi a zikwi zambiri awunjikidwa pa nkhope ya dziko lapansi; inde, ndipo zikwi zambiri zikulira chifukwa cha kutaika kwa achibale awo, chifukwa iwo ali ndi chifukwa chochitira mantha, molingana ndi malonjezo a Ambuye, kuti iwo aperekedwa ku mkhalidwe wa tsoka losatha.

12 Pamene zikwi zochuluka za ena zikulira moonadi chifukwa cha kutaika kwa achibale awo, komanso iwo akusangalala ndi kukondwera mu chiyembekezo, ndipo ngakhale akudziwa, molingana ndi malonjezo a Ambuye, kuti iwo aukitsidwa ndi kukakhala ku dzanja lamanja la Mulungu, mu mkhalidwe wa chimwemwe chosatha.

13 Ndipo choncho tikuona m’mene kusiyana kwa munthu kuliri chifukwa cha uchimo ndi kulakwitsa, ndi mphamvu ya mdyerekezi, imene imabwera ndi dongosolo lochenjera lachinyengo limene iye adalikonza kuti akole mitima ya anthu.

14 Ndipo choncho tikuona maitanidwe aakulu a khama la anthu kuti agwire ntchito mu minda yampesa ya Ambuye; ndipo choncho tikuona chifukwa chachikulu cha chisoni, ndiponso chisangalalo—chisoni chifukwa cha imfa ndi chiwonongeko pakati pa anthu, ndipo chisangalalo chifukwa cha kuwala kwa Khristu ku moyo.