Malembo Oyera
Alima 59


Mutu 59

Moroni apempha Pahorani kuti alimbitse ankhondo a Helamani—Alamani atenga mzinda wa Nefiha—Moroni akwiya ndi boma. Mdzaka dza pafupifupi 62 Yesu asadabadwe.

1 Tsopano zidachitika mu chaka cha makumi atatu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi, pambuyo pa Moroni atalandira ndi kuwerenga kalata ya Helamani, iye adali ndi chimwemwe chachikulu chifukwa cha thandizo, inde, chipambano chachikulu chimene Helamani adali nacho, potenga maiko amene adataika.

2 Inde, ndipo iye adadziwitsa kwa anthu ake onse, mu maiko onse ozungulira mbali imene iye adali, kuti nawonso athe kukondwera.

3 Ndipo zidachitika kuti iye nthawi yomweyo adatumiza kalata kwa Pahorani, pofuna kuti iye achititse anthu ake kuti asonkhanitsidwe pamodzi kukamulimbitsa Helamani, kapena ankhondo a Helamani, kotero kuti iye akwanitse mosavuta kuteteza chigawo chimenecho cha dziko limene iye adachita nalo bwino modabwitsa pakulitenganso.

4 Ndipo zidachitika pamene Moroni adatumiza kalata imeneyi ku dziko la Zarahemula, iye adayamba kachiwiri kukonza dongosolo loti iye athe kutenga zotsalira za katundu ndi mizinda imene Alamani adawatengera.

5 Ndipo zidachitika kuti pamene Moroni adali choncho kupanga zokonzekera motero kuti apite motsutsana ndi Alamani kunkhondo, taonani, anthu a Nefiha, amene adasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mzinda wa Moroni ndi mzinda wa Lehi ndi mzinda wa Moriyantoni, adaukiridwa ndi Alamani.

6 Inde, ngakhale iwo amene adakakamizidwa kuthawa kuchokera ku dziko la Manti, ndi ochokera ku maiko ozungulira, adabwera ndi kuphatikizana ndi Alamani mugawo limeneli la dzikoli.

7 Ndipo motero pokhala ochuluka kwambiri, inde, ndi kulandira mphamvu kuchokera tsiku ndi tsiku, mwa lamulo la Amoroni iwo adabwera motsutsana ndi anthu a Nefiha, ndipo adayamba kuwapha iwo ndi kupha kochuluka kwambiri.

8 Ndipo ankhondo awo adali ochuluka mpaka otsalira a anthu a Nefiha adakakamizidwa kuthawa pamaso pawo; ndipo iwo adafika madzulo ndi kuphatikizana ndi ankhondo a Moroni.

9 Ndipo tsopano monga Moroni adaganizira kuti pakuyenera kukhala anthu atumizidwe ku mzinda wa Nefiha, kukawathandizira anthuwo kuteteza mzinda umenewo, ndi kudziwa kuti kudali kosavuta kuteteza mzindawo kuti usagwere m’manja mwa Alamani koposa kuutenganso kuchokera kwa iwo, iye adaganiza kuti auteteza mzindawo mosavuta.

10 Kotero iye adatenga ankhondo ake onse kuti ateteze malo amenewo amene iwo adawapeza.

11 Ndipo tsopano, pamene Moroni adaona kuti mzinda wa Nefiha wataika iye adali ndi chisoni chachikulu, ndipo adayamba kukaikira, chifukwa cha kuipa kwa anthuwo, ngati sangagwe m’manja mwa abale awo.

12 Tsopano izi zidali chomwechi ndi akulu ankhondo ake onse. Iwo adakaikira ndi kuzizwanso chifukwa cha kuipa kwa anthuwo, ndipo izi chifukwa cha kupambana kwa Alamani pa iwo.

13 Ndipo zidachitika kuti Moroni adali okwiya ndi boma, chifukwa cha mphwayi zawo zokhudzana ndi ufulu wa dziko lawo.