Malembo Oyera
Alima 26


Mutu 26

Amoni akondwera mwa Ambuye—Wokhulupilira alimbikitsidwa ndi Ambuye ndipo apatsidwa chidziwitso—Mwa chikhulupiliro anthu akhonza kubweretsa zikwi za miyoyo m’kulapa—Mulungu ali ndi mphamvu zonse ndipo amadziwa zinthu zonse. Mdzaka dza pafupifupi 90–77 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo tsopano, awa ndiwo mawu a Amoni kwa abale ake, amene akunena motere: Azichimwene anga ndi abale anga, taonani ndikunena ndi inu, ndi chifukwa chachikulu chotani chimene ife tili nacho cha kusangalala; pakuti kodi tikadaganiza pamene ife tidayambira kuchokera ku dziko la Zarahemula kuti Mulungu akhonza kupereka kwa ife madalitso aakulu chotere?

2 Ndipo tsopano, ine ndikufunsa, ndi madalitso aakulu ati amene iye wapereka pa ife? Kodi munganene?

3 Taonani, ndikuyankhirani; pakuti abale athu, Alamani, adali mu mdima, inde, ngakhale mu mdima wa ndiweyani, koma taonani, ndi angati mwa iwo amene abweretsedwa kudzaona kuwala kodabwitsa kwa Mulungu! Ndipo ili ndi dalitso limene laperekedwa kwa ife, kuti ife tapangidwa kukhala zida m’manja mwa Mulungu kubweretsa ntchito yaikulu yotereyi.

4 Taonani, zikwi za iwo zakondwera, ndipo zabweretsedwa mu khola la Mulungu.

5 Taonani, munda udali wakucha, ndipo odala ndi inu, pakuti mwaponya chikwakwa chanu, ndipo mwakolola ndi mphamvu zanu, inde, tsiku lonse inu mwagwira ntchito; ndipo taonani chiwerengero cha mitolo ya zokolora zanu! Ndipo iwo adzasonkhanitsidwa mu nkhokwe, kuti iwo asawonongeke.

6 Inde, iwo sadzawombedwa ndi namondwe pa tsiku lotsiriza; inde, ngakhale kumezedwa ndi mphepo ya mkuntho; koma pamene namondwe afika iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi mu malo awo, kotero namondweyo sangafike pa iwo; inde, ngakhale kuphepheluka ndi mphepo yoopsya kulikonse kumene mdani adzafuna kuwatengera iwo.

7 Koma taonani, iwo ali m’manja mwa Ambuye wa zokolora, ndipo ndi ake; ndipo iye adzawaukitsa iwo pa tsiku lotsiriza.

8 Lidalitsike dzina la Mulungu wathu; tiyeni tiyimbe matamando ake, inde tiyeni tiyamike ku dzina lake loyera, pakuti iye amachita ntchito zolungama kwa muyaya.

9 Pakuti ngati ife tikadapanda kubwera ku dziko la Zarahemula, abale athu okondedwawa, amene atikondanso ife kwambiri, akadazunzikabe mu udani ndi ife, inde, ndipo akadakhalanso achilendo kwa Mulungu.

10 Ndipo zidachitika kuti pamene Amoni adanena mawu awa, m’bale wake Aroni adamudzudzula iye, nati: Amoni, ndikuopa kuti chisangalalo chakochi chakutengera iwe mkudzitamandira.

11 Koma Amoni adati kwa iye: Sindikudzitamandira mu mphamvu zanga, kapena mu mzeru zanga; koma taona, chisangalalo changa ndi chodzadza, inde, mtima wanga wasefukira ndi chisangalalo, ndipo ndidzasangalala mwa Mulungu wanga.

12 Inde, ndikudziwa kuti ine ndili chabe; monga mwa mphamvu zanga ndili ofooka; kotero sindingadzitamandire ndekha, koma ndidzadzitamandira mwa Mulungu wanga, pakuti mu mphamvu zake ndikhonza kuchita zinthu zonse; inde, taona, zodabwitsa zazikulu zambiri ife tazichita mu dziko lino, pazimenezi ife tidzatamanda dzina lake ku nthawi zosatha.

13 Taonani, ndi zikwi zingati za abale athu amene iye wawamasula ku zowawa za gahena; ndipo abweretsedwa kuti ayimbe nyimbo ya chikondi cha chiwombolo, ndipo izi chifukwa cha mphamvu ya mawu ake amene ali mwa ife, kotero kodi ife tilibe chifukwa chokondwelera?

14 Inde, ife tilinacho chifukwa chomutamanda iye kwamuyaya, pakuti iye ndi Mulungu Wam’mwambamwamba, ndipo wamasula abale athu ku maunyolo a gahena.

15 Inde, iwo adazunguliridwa ndi mdima wamuyaya ndi chiwonongeko; koma taonani, iye wawabweretsa iwo mu kuwala kosatha, inde, mu chipulumutso chamuyaya; ndipo iwo azunguliridwa ndi chikondi chake chodzadza chosayelekezeka; inde, ndipo ife takhala zida m’manja mwake pochita ntchito yaikulu ndi yodabwitsayi.

16 Kotero, tiyeni titamandire, inde, tidzadzitamandira mwa Ambuye; tidzakondwera, pakuti chisangalalo chathu ndi chodzadza; inde, ife tidzatamanda Mulungu wathu kosalekeza. Taonani, ndindani angathe kutamandira koposa muyeso mwa Ambuye? Inde, ndani anganene moposa muyeso za mphamvu zake zazikulu ndi za chifundo chake, ndi za chipiliro chake kwa ana a anthu? Taonani, ndikunena kwa inu, sindinganene gawo lochepa la zomwe ine ndikumva.

17 Ndani akadaganiza kuti Mulungu wathu angakhale ndi chifundo mpaka kutichotsa ife kuchoka ku mkhalidwe wathu woipitsitsa, wauchimo ndi woipitsidwa?

18 Taonani, ife tidapita ngakhale mu mkwiyo, ndi kuopseza kwamphamvu kuti tiwononga mpingo wake.

19 O ndiye, bwanji iye sadatisiye ife m’chiwonongeko choopsya, inde, bwanji iye sadalore lupanga la chilungamo chake kutigwera ife, ndi kutiweruza ife mu kukhumudwa kosatha?

20 O, moyo wanga, pafupifupi ngati udali, kuthawa pa ganizo limeneli. Taonani, iye sadachite chilungamo chake pa ife, koma mu chifundo chake chachikulu watiwombotsa ife ku phompho losatha la imfa ndi chisoni, ngakhale kufikira ku chipulumutso cha miyoyo yathu.

21 Ndipo tsopano taonani, azibale anga, ndi munthu wachilengedwe otani amene amadziwa zinthu izi? Ndikunena kwa inu, palibe amene amadziwa zinthu izi, kupatula akhale wolapa.

22 Inde, iye amene amalapa ndi kukhulupirika, ndi kubweretsa ntchito zabwino ndi kupempherabe mosalekeza—kwa otere kumapatsidwa kwa iwo kuti adziwe zinsisi za Mulungu, inde, kwa otere kudzapatsidwa kuti aulure zinthu zimene sizidauliredwepo; inde, ndipo kudzapatsidwa kwa otere kubweretsa zikwi za miyoyo m’kulapa, monga momwe kudapatsidwira kwa ife kubweretsa abale athuwa m’kulapa.

23 Tsopano kodi mukukumbikira, abale anga, kuti tidati kwa abale athu mu dziko la Zarahemula, tikupita ku dziko la Nefi, kukalalika kwa abale athu, Alamani, ndipo iwo adatiseka ife monyoza?

24 Pakuti iwo adati kwa ife: Kodi mukuganiza kuti mungabweretse Alamani ku chidziwitso cha choonadi? Mukuganiza kuti mungatsimikizire Alamani za kusalondola kwa miyambo ya makolo awo, monga anthu osamvera monga iwo aliri; amene mitima yawo imakondwa mu kukhetsa mwazi; amene masiku awo adathera m’mphulupulu yopambana; m’mene njira za wolakwa zidali njira zawo kuyambira pachiyambi? Tsopano abale anga, inu mukukumbukira kuti aka kadali kayankhulidwe kawo.

25 Ndipo kuposera apo iwo adati: Tiyeni titenge zida tikamenyane nawo, kuti tiwawononge iwo ndi zoipa zawo kuwachotsa mu dzikoli, kuwopa angatipose ndi kutiwononga ife.

26 Koma taonani, abale anga, tidabwera m’chipululu osati ndi cholinga chakuwononga abale athu, koma ndi cholinga chakuti mwina tikhonza kupulumutsa ena wochepa mwa anthu awo.

27 Tsopano pamene mitima yathu idali yokhumudwa, ndipo tidali pafupi kubwelera, taonani, Ambuye adatitonthoza ife, ndipo adati: Pitani pakati pa abale anu, Alamani, ndi kukhala oleza mtima pa masautso anu, ndipo ine ndidzakupatsani inu chipambano.

28 Ndipo tsopano taonani, ife tabwera, ndipo takhala pakati pawo; ndipo takhala oleza mtima mu zowawa zathu, ndipo tazunzika mu kusowa chirichonse, inde, tayenda kuchoka nyumba ndi nyumba, kudalira pa zifundo za padziko lapansi—osati pa zifundo za padziko lapansi pokha koma pa zifundo za Mulungu.

29 Ndipo ife talowapo m’nyumba zawo ndi kuwaphunzitsa iwo, ndipo tawaphunzitsa iwo m’makwalala mwawo; inde, ndipo tawaphunzitsa iwo m’mapiri mwawo; ndiponso talowamo m’makachisi awo ndi m’ma sunagoge mwawo ndi kuwaphunzitsa iwo; ndipo tathamangitsidwa, ndi kunyozedwa, ndi kulavulidwa, ndi kumenyedwa makofi; ndipo tidagendedwa, ndipo tatengedwa ndi kumangidwa ndi zingwe zolimba, ndi kuponyedwa mu ndende, ndipo kudzera mu mphamvu ndi mnzeru ya Mulungu ife tapulumutsidwanso.

30 Ndipo ife tazunzika mitundu yonse yamasautso, ndipo zonsezi, kuti mwina tingathe kukhala njira yopulumutsira moyo wina; ndipo ife tikuganiza kuti chisangalalo chathu chidzakhala chodzadza ngati tingathe kukhala njira yopulumutsira moyo wina.

31 Tsopano taonani, kodi tingayang’ane ndi kuona zipatso za ntchito zathu; ndipo kodi ndizochepa? Ndikunena ndi inu, Ayi, ndizambiri, inde, ndipo tingathe kuchitira umboni za kuona mtima kwawo, chifukwa cha chikondi chawo kwa abale awo ndiponso kwa ife.

32 Pakuti taonani, iwo akadakonda kupereka nsembe miyoyo yawo koposa ngakhale kutenga moyo wa mdani wawo; ndipo akwilira zida zawo zankhondo mozama mu nthaka, chifukwa cha chikondi chawo kwa abale awo.

33 Ndipo tsopano taonani ndinena kwa inu, kodi pakhalapo chikondi chachikulu chotere mu dziko lonseli? Taonani, ndinena kwa inu, Ayi, sipadakhalepo, ngakhale pakati pa Anefi.

34 Pakuti taonani, iwo akadatenga zida kumenyana ndi abale awo; sakadalora iwo okha kuti aphedwe. Koma taonani ndi angati mwa iwowa ataya miyoyo yawo; ndipo tikudziwa kuti iwo apita kwa Mulungu wawo, chifukwa cha chikondi chawo ndi kudana ndi tchimo kwawo.

35 Tsopano kodi tilibe chifukwa chokondwelera? Inde, ndikunena ndi inu, sipadakhalepo anthu wokhala ndi chifukwa chokondwelera ngati ife, chiyambire dziko lapansi; inde, ndipo chisangalalo changa chanyamulidwa, ngakhale kufika podzitamandira mwa Mulungu wanga; pakuti iye ali ndi mphamvu zonse, ndi nzeru zonse, ndi luntha lonse; iye amadziwa zinthu zonse, ndipo iye ndi Munthu wachifundo, ngakhale ku chipulumutso, kwa iwo amene adzalapa ndi kukhulupilira mu dzina lake.

36 Tsopano ngati uku kuli kudzitamandira, momwemo ine ndidzadzitama; pakuti uwu ndi moyo wanga ndi kuwala kwanga, ndi chisangalalo changa ndi chipulumutso changa, ndi chiwombolo changa ku tsoka losatha. Inde, lodala ndi dzina la Mulungu wanga, amene wakhala moganizira anthu ake, amene ali nthambi ya mtengo wa Israeli, ndipo adasowekera mu thupi lake mu dziko lachilendo, ndikunena, lidalitsike dzina la Mulungu wanga, amene wakhala akutiganizira ife, woyendayenda mu dziko lachilendo.

37 Tsopano abale anga, tikuona kuti Mulungu amakumbukira anthu onse, mu dziko lirilonse lomwe iwo angakhalemo; inde, amawerengera anthu ake, ndipo zimphyo zake zachifundo zadzadza dziko lonse lapansi. Tsopano ichi ndicho chisangalalo changa, ndi kuthokoza kwanga kwakukulu; inde, ndipo ndidzayamika kwa Mulungu wanga kosalekeza. Ameni.