Malembo Oyera
Alima 44


Mutu 44

Moroni alamula Alamani kupanga chipangano cha mtendere kapena kuwonongedwa—Zerahemuna akana pemphoro, ndipo nkhondo iyambikanso—Ankhondo a Moroni agonjetsa Alamani. Mdzaka dza pafupifupi 74–73 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti iwo adaima ndi kubwelera pang’ono kwa iwo. Ndipo Moroni adati kwa Zerahemuna: Taona, Zerahemuna, kuti ife sitikufuna kukhala anthu a mwazi. Iwe ukudziwa kuti uli m’manja mwathu, komabe sitikufuna kukuphani.

2 Taona, ife sitidabwere kudzamenyana ndi inu kuti tikhetse mwazi wanu chifukwa cha mphamvu; ngakhale sitikufuna kubweretsa aliyense mu goli la ukapolo. Koma ichi ndi chifukwa chimene inu mwabwera motsutsana nafe; inde, ndipo inu mwakwiya nafe chifukwa cha chipembedzo chathu.

3 Koma tsopano, waona kuti Ambuye ali nafe; ndipo iwe waona kuti iye wakuperekani inu m’manja mwathu. Ndipo tsopano ndikufuna kuti umvetse kuti izi zachitika kwa ife chifukwa cha chipembedzo chathu ndi chikhulupiliro chathu mwa Khristu. Ndipo tsopano iwe waona kuti simungawononge chikhulupiliro chathuchi.

4 Tsopano ukuona kuti ichi ndi chikhulupiliro choonadi cha Mulungu; inde, ukuona kuti Mulungu adzathandiza, ndi kutisunga, ndi kutiteteza ife, kufikira pamene ife tikhala okhulupirika kwa iye, ndi kuchikhulupiliro chathu, ndi ku chipembedzo chathu, ndipo Ambuye sadzalora konse kuti ife tiwonongedwe pokhapokha titagwa mu kulakwitsa ndi kukana chikhulupiliro chathu.

5 Ndipo tsopano, Zerahemuna; ndikukulamula iwe, mu dzina la Mulungu wamphamvu zonse, amene walimbitsa manja athu kuti ife tapeza mphamvu pa inu, mwa chikhulupiliro chathu, ndi mwa chipembedzo chathu, ndipo mwa miyambo yathu yakupembedza, ndi mpingo wathu, ndi chithandizo chopatulika chomwe tili nacho kwa akazi athu ndi ana athu, ndi ufulu umene umatimangilira ife ku malo athu ndi dziko lathu, inde, ndiponso ndi kasamalidwe ka mawu opatulika a Mulungu, amene ife tili nawo chimwemwe chathu chonse; ndipo ndi zonse zimene zili zofunika kwambiri kwa ife—

6 Inde, ndipo izi si zonse; ndikukulamula iwe ndi zikhumbo zonse zomwe uli nazo za moyo, kuti upereke zida zako za nkhondo kwa ife, ndipo ife sitidzafunanso mwazi wanu, koma tidzakusiyirani inu moyo wanu, ngati mudzapita njira yanu ndi kusabweranso kudzamenya nkhondo ndi ife.

7 Ndipo tsopano, ngati siuchita izi, taona, iwe uli m’manja mwathu, ndipo ndidzalamula anthu anga kuti agwere pa iwe, ndi kukupatsani mabala a imfa m’matupi mwanu, kuti inu muthe kutheratu; ndipo kenako ife tidzaona amene adzakhale ndi mphamvu pa anthu awa; inde, tidzaona amene adzabweretsedwe mu ukapolo.

8 Ndipo tsopano zidachitika kuti pamene Zerahemuna adamva zonena izi adabwera patsogolo ndi kupereka lupanga lake ndi chikwanje chake, ndi uta wake m’manja mwa Moroni, ndipo adati kwa iye: Taonani, izi ndi zida zathu za nkhondo; tidzazipereka kwa inu, koma sitidzadzilora ife eni kutenga chipangano kwa iwe, chimene ife tikudziwa kuti tidzaswa, ndiponso ana athu; koma tengani zida zathu zankhondo, ndi kutilora kuti tipite m’chipululu; apo ayi tidzatenganso malupanga athu, ndipo tidzawonongeka kapena tidzapambana.

9 Taona, ife sitili achikhulupiliro chako, sitikhulupilira kuti ndi Mulungu amene watipereka ife m’manja mwanu; koma tikukhulupilira kuti ndi kuchenjera kwako kumene kwakutetezani inu ku malupanga athu. Taonani, ndi zapachifuwa zanu ndi zishango zanu zimene zakutetezani inu.

10 Ndipo tsopano pamene Zerahemuna adamaliza kuyankhula kwake mawu awa, Moroni adabweza malupangawo ndi zida zankhondozo, zimene iye adalandira, kwa Zerahemuna, nati: Taonani, timaliza nkhondoyi.

11 Tsopano sindingathe kukumbukira mawu amene ine ndanena, kotero monga Ambuye ali wamoyo, inu simudzachoka pokhapokha mutachoka ndi lumbiro kuti inu simudzabweleranso kudzamenyana nafe kunkhondo. Tsopano pamene iwe uli m’manja mwathu tidzakhetsa mwazi wanu pansi, kapena inu mudzagonjera ku zofunika zimene ine ndapempha.

12 Ndipo tsopano pamene Moroni adanena mawu awa, Zerahemuna adabwenzeretsa lupanga lake, ndipo adali okwiya ndi Moroni, ndipo adathamangira patsogolo kuti amuphe Moroni; koma pamene iye adakweza lupanga lake, taonani, m’modzi wa ankhondo a Moroni adalikantha mpaka pansi, ndipo lidathyoka chigwiliro; ndipo iye adakanthanso Zerahemuna mpaka adakhapa khungu lake lapamutu ndipo lidagwera pansi. Ndipo Zerahemuna adachoka pamaso pawo kupita pakati pa ankhondo ake.

13 Ndipo zidachitika kuti wankhondo amene adaima pambali, amene adakhapa khungu lapamutu la Zerahemuna, adanyamula khungulo kuchokera pansi ndi tsitsi, ndipo adalipachika ku nsonga ya lupanga lake, ndipo adalitambasulira kwa iwo, nati kwa iwo ndi mawu ofuula.

14 Ngakhale monga ngati khungu la pamutu ili lagwa pansi, limene liri khungu la pamutu pa mkulu wanu, choncho inunso mudzagwera pansi pokhapokha mutapereka zida zanu za nkhondo ndi kuchoka ndi pangano la mtendere.

15 Tsopano adalipo ambiri, pamene adamva mawu amenewa ndi kuona chikhungu chimene chidali pa lupangalo, amene adagwidwa ndi mantha, ndipo ambiri adabwera patsogolo ndi kuponya pansi zida zawo zankhondo pamapazi a Moroni, ndipo adalowa mu pangano la mtendere. Ndipo onse ambiri amene adalowa mu pangano iwo adawalora kuti apite m’chipululu.

16 Tsopano zidachika kuti Zerahemuna adali okwiya kwambiri, ndipo adautsira otsala a ankhondo akewo ku mkwiyo, kuti alimbane mwa mphamvu kwambiri motsutsana ndi Anefi.

17 Ndipo tsopano Moroni adakwiya, chifukwa cha makani a Alamani; kotero iye adalamula anthu ake kuti agwere pa iwo ndi kuwapha. Ndipo zidachitika kuti iwo adayamba kuwapha; inde, ndipo Alamani adalimbana ndi malupanga awo ndi nyonga zawo.

18 Koma taonani, khungu lawo lamaliseche ndi mitu yawo yosavala idaikidwa poyera ku malupanga akuthwa a Anefi; inde, taonani iwo adalasidwa ndi kukanthidwa, inde, ndipo adagwa mwansanga kwambiri pamaso pa malupanga achinefi; ndipo iwo adayamba kugwetsedwa pansi, monga momwe wankhondo wa Moroni adalosera.

19 Tsopano Zerahemuna, pamene adaona kuti adali pafupi kuwonongedwa, adafuula mwamphamvu kwa Moroni, kulonjeza kuti iye adzapangana ndiponso anthu ake limodzi nawo, ngati iwo adzawasiyira otsalirawo moyo wawo, kuti iwo sadzabweranso kunkhondo motsutsana ndi iwo.

20 Ndipo zidachitika kuti Moroni adachititsa kuti ntchito yophana iyimenso pakati pa anthu. Ndipo iye adatenga zida zankhondo kwa Alamani; ndipo atamaliza kulowa mu pangano ndi iye la mtendere adawalora kunyamuka kupita m’chipululu.

21 Tsopano chiwerengero cha akufa awo sichidawerengedwe chifukwa cha kuchuluka kwa chiwerengerocho; inde chiwerengero cha akufa awo chidali chachikulu kwambiri, mbali zonse za Anefi ndi za Alamani.

22 Ndipo zidachitika kuti iwo adaponya akufa awo mu madzi a Sidoni, ndipo adapita ndi kukwiliridwa mkuya kwa nyanja.

23 Ndipo ankhondo achinefi, kapena a Moroni, adabwelera ndi kufika ku nyumba zawo ndi malo awo.

24 Ndipo motero chidatha chaka cha khumi ndi zisanu ndi zitatu cha ulamuliro wa oweruza pa anthu a Nefi. Ndipo motero zolemba za Alima zidatha, zimene zidalembedwa pa mapale a Nefi.

Print