Malembo Oyera
Alima 60


Mutu 60

Moroni adandaula kwa Pahorani za kunyalanyaza kwa boma kwa ankhondo—Ambuye alolera olungama kuti aphedwe—Anefi akuyenera kugwiritsa mphamvu zawo zonse ndi njira zawo kudzipulumutsa wokha kwa adani awo—Moroni awopsyeza kulimbana ndi boma pokhapokha thandizo liperekedwe kwa ankhondo ake. Mdzaka dza pafupifupi 62 Yesu asadabadwe.

1 Ndipo zidachitika kuti iye adalemberanso kachiwiri kwa kazembe wa dzikolo, amene adali Pahorani, ndipo awa ndi mawu amene iye adalemba, kuti: Taona, ndikulembera kalata yangayi kwa Pahorani, mu mzinda wa Zarahemula, amene ali mkulu wa oweruza ndi kazembe wa dzikoli, ndiponso kwa iwo onse amene asankhidwa ndi anthu awa kuti alamulire ndi kuyendetsa zochitika za nkhondo iyi.

2 Pakuti taonani, ndili ndi zinazake zoti ndinene kwa iwo mwa njira yodzudzula; pakuti taonani, inu nokha mukudziwa kuti mwasankhidwa kuti musonkhanitse pamodzi anthu, ndi kupezera iwo malupanga, ndi zikwanje ndi zida zankhondo zosiyanasiya, ndi kutumiza motsutsana ndi Alamani, mu mbali zinazilizonse zomwe iwo angabwere mu dziko lathu.

3 Ndipo tsopano taonani, ndikunena ndi inu kuti ineyo, ndiponso anthu anga, komanso Helamani ndi anthu ake, azunzika kwambiri mazunzo aakulu; inde, ngakhale njala, ludzu, ndi kutopa, ndi masautso amitundu yosiyanasiyana.

4 Koma taonani, zonsezi zomwe ife tazunzikazi sitidang’ung’udze kapena kudandaula.

5 Koma taonani, kwakukulu kwakhala kuphedwa kwa anthu athu, inde, zikwizikwi zagwa ndi lupanga, pamene zikadakhala mwinamwake inu mukadatumiza kwa ankhondo athu mphamvu zokwanira ndi chithandizo kwa iwo. Inde, kwakukulu kwakhala kunyalanyaza kwanu pa ife.

6 Ndipo tsopano taonani, ife tikukhumba kudziwa chifukwa cha kunyalanyaza kwakukulu kumeneku; inde, tikukhumba kudziwa chifukwa cha kusaganiza kwanuku.

7 Kodi mungaganize kukhala pa mipando yanu yachifumu m’khalidwe wa kusaganizirawu, pamene adani anu akufalitsa ntchito ya imfa kuzungulira inu? Inde, pamene iwo akupha zikwi za abale anu—

8 Inde, ngakhale iwo amene akuyang’anira kwa inu pachitetezo, inde, akuyikani inu m’khalidwe woti muthe kuwathandiza iwo, inde, mukadawatumizira ankhondo kwa iwo, kukawalimbikitsa iwo, ndi kupulumutsa zikwi zawo zisagwe ndi lupanga.

9 Koma taonani, izi sizokhazo—inu mwakaniza chakudya chanu kwa iwo, kotero kuti ambiri amenyana ndi kukhetsa mwazi wa miyoyo yawo chifukwa cha chikhumbo chawo chachikulu chimene iwo adali nacho pa ubwino wa anthu awa; inde, izi iwo achita pamene adali pafupi kuwonongeka ndi njala, chifukwa cha kunyalanyaza kwanu kwakukulu kwa iwo.

10 Ndipo tsopano, abale anga okondedwa—pakuti mukuyenera kukhala okondedwa; inde, ndipo mukadayenera kudziutsa nokha mwakhama ku ubwino ndi ufulu wa anthu awa; koma taonani, mwawanyalanyaza iwo kotero kuti mwazi wa zikwi udzakhala pa mutu panu kubwenzera, inde, pakuti kudadziwika kwa Mulungu kulira kwawo konse, ndi mazunzo awo onse—

11 Taonani, kodi munkaganiza kuti mungakhale pa mipando yanu yaufumu, ndipo chifukwa cha ubwino waukulu wa Mulungu simungachite kanthu ndipo iye adzakuwombotsani? Taonani, ngati mumaganiza izi inu mwaganiza mwachabe.

12 Kodi mukuganiza kuti, chifukwa cha ambiri mwa abale anu aphedwa ndi chifukwa cha zoipa zawo? Ndikunena kwa inu, ngati mwaganiza izi mwaganiza mwachabe; pakuti ndikunena kwa inu, alipo ambiri amene agwa ndi lupanga; ndipo taonani ndiko kutsutsidwa kwanu;

13 Pakuti Ambuye amalolera olungama kuti aphedwe kuti chilungamo ndi chiweruzo chake chidzabwere pa oipa; kotero simukuyenera kuganiza kuti olungama ataika chifukwa iwo aphedwa; koma taonani, iwo alowa mu mpumulo wa Ambuye Mulungu wawo.

14 Ndipo tsopano taonani, ndikunena kwa inu, ndikuopa kwambiri kuti ziweruzo za Mulungu zidzabwera pa anthu awa, chifukwa cha ulesi waukulu, inde, ngakhale ulesi wa boma lathu, ndi kunyalanyaza kwawo kwakukulu kwa abale awo, inde, kwa iwo amene aphedwa.

15 Pakuti kukadapanda kuipa kumene kudayambira patsogolo pathu, tikadatha kulimbana ndi adani athu kuti sakadatha kupeza mphamvu pa ife.

16 Inde, kukadapanda nkhondo imene idabuka pakati pathu; inde, pakadapanda anthu amfumuwa, amene adayambitsa kukhetsana mwazi kwakukulu pakati pathu; inde, pa nthawi imene tidali kulimbana pakati pathu, tikadagwirizana mphamvu zathu monga tinkachitira; inde, pakadapanda chikhumbokhumbo cha mphamvu ndi ulamuliro umene anthu amfumu awo adali nawo pa ife; akadakhala woona mtima pa cholinga cha ufulu wathu, ndi kugwirizana nafe, ndi kupita kukamenyana ndi adani athu, m’malo motenga malupanga awo motsutsana nafe, zimene zidali chifukwa cha kukhetsa mwazi kwakukulu pakati pathu; inde, ngati tikadapita motsutsana nawo mu mphamvu ya Ambuye, tikadabalalitsa adani athu, pakuti zikadachitika, molingana ndi kukwaniritsa kwa mawu ake.

17 Koma taonani, tsopano Alamani akubwera pa ife, kulanda maiko athu, ndipo akupha anthu athu ndi lupanga, inde, azimayi athu ndi ana athu, ndiponso kuwatenga iwo ukapolo, kuwapangitsa iwo kuti azunzike masautso osiyanasiyana, ndipo izi chifukwa cha kuipa kwakukulu kwa iwo amene akufunafuna mphamvu ndi ulamuliro, inde, ngakhale anthu amfumu.

18 Koma n’chifukwa chiyani ndikuyenera kunena zambiri zokhudzana ndi nkhaniyi? Pakuti sitikudziwa koma zoti inu nomwe mukufuna ulamuliro. Ife sitikudziwa koma zoti inu ndinu achiwembu ku dziko lanu.

19 Kapena kodi ndi chifukwa choti mwatinyanyala ife chifukwa muli m’mtima wa dziko lathu ndipo mwazungilidwa ndi achitetezo, kuti inu simukutumiza chakudya kwa ife, ndiponso anthu kudzalimbitsa akhondo anthu?

20 Kodi mwaiwala malamulo a Ambuye Mulungu wanu? Inde, kodi mwaiwala ukapolo wa makolo athu? Kodi mwaiwala nthawi zambiri zomwe tapulumutsidwa kuchokera m’manja mwa adani athu?

21 Kapena mukuganiza kuti Ambuye adzatipulumutsabe ife, pamene ife titakhala pamipando yathu yachifumu ndi kusagwiritsa ntchito njira zimene Ambuye watipatsa ife?

22 Inde, kodi mudzakhala aulesi pamene mwazunguliridwa ndi zikwi za iwo, inde, makumi a zikwi, amene amakhalanso mwaulesi, pamene kuli zikwizikwi zozungulira malire a dziko amene akugwa ndi lupanga, inde, kuvulazidwa ndi kutuluka mwazi?

23 Kodi mukuganiza kuti Mulungu adzayang’ana pa inu ngati osalakwa pamene mutangokhala ndi kuyang’anira zinthu izi? Taonani, ndinena kwa inu, Ayi. Tsopano ndikufuna kuti mukumbukire kuti Mulungu wanena kuti mkati mwa mbiya mudzayeretsedwa choyamba, ndipo kenako kunja kwa mbiya kudzayeretsedwanso.

24 Ndipo tsopano, pokhapokha inu mulape pa icho chimene mwachita, ndi kuyamba kudzuka ndi kuchita, ndi kutumiza chakudya ndi anthu kwa ife, ndiponso kwa Helamani, kuti iye akathandize zigawo za dziko lathu zimene iye watenganso, ndipo kuti ife tithenso kutenganso katundu wathu otsalira mzigawo zimenezi, taonani kuzakhala koyenera kuti tisalimbanenso ndi Alamani kufikira choyamba tikatsuka mbiya zathu, inde, ngakhale mutu waukulu wa boma lathu.

25 Ndipo pokhapokha muyankhe kalata yangayi, ndi kutuluka ndi kundionetsa ine mzimu weniwenu wa ufulu, ndi kuyesetsa kulimbitsa ndi kukuza ankhondo athu, ndi kuwapatsa iwo chakudya chowathandiza, taonani, ndidzasiya gawo la anthu anga omasulidwa kuti ateteze chigawo chino cha dziko, ndipo ndidzasiya mphamvu ndi madalitso a Mulungu pa iwo, kuti palibe mphamvu ina imene ingagwire pa iwo—

26 Ndipo izi chifukwa cha chikhulupiliro chachikulu ndi kuleza mtima kwawo mu mazunzo awo—

27 Ndipo ndidzabwera kwa inu, ndipo ngati pali wina pakati panu amene ali ndi chikhumbo cha ufulu, inde, ngati pangakhale mphamvu ya ufulu yotsala, taonani ndidzayambitsa kuukira pakati panu, ngakhale kufikira iwo amene ali ndi zokhumba zolanda mphamvu ndi ulamuliro adzatheratu.

28 Inde, taonani ine sindiopa mphamvu zanu kapena ulamuliro wanu, koma ndi Mulungu amene ndimamuopa; ndipo ndi molingana ndi malamulo ake kuti ndimatenga lupanga langa kutetezera cholinga cha dziko langa, ndipo ndi chifukwa cha kusaweruzika kwanu kuti ife tazunzika chitaiko chachikulu chonchi.

29 Taonani nthawi yakwana, inde, nthawi yafika tsopano, kuti pokhapokha mudzipereke nokha kutetezera dziko lanu ndi ana aang’ono anu, lupanga lachilungamo likwezedwa pa inu; inde, ndipo lidzagwera pa inu ndi kukuyenderani inu ngakhale kukuwonongani kotheratu.

30 Taonani, ndikudikira chithandizo kwa inu; ndipo, pokhapokha mutitumikire ife ku chithandizo chathu, taonani, ndidzabwera kwa inu, ngakhale mu dziko la Zarahemula, ndi kukukanthani inu ndi lupanga, kufikira kuti simungakhale ndi mphamvu inanso yolepheletsa kupita patsogolo kwa anthu awa mu chifukwa cha ufulu wathu.

31 Pakuti taonani, Ambuye sadzalora kuti inu mukhale ndi kukula m’mphamvu mu zoipa zanu kuti muwononge anthu olungama.

32 Taonani, kodi mungaganize kuti Ambuye adzakulekani inu ndi kubwera ku chiweruzo chotsutsana ndi Alamani, pamene ndi miyambo ya makolo awo imene idayambitsa udani umenewu, inde, ndipo yawonjezeredwa ndi iwo amene adapanduka kwa ife, pamene kusaweruzika kwanu kuli pa chifukwa cha chikondi chanu cha ulemelero ndi zinthu zachabechabe za dziko lapansi?

33 Inu mukudziwa kuti mukulakwira malamulo a Mulungu, ndipo mukudziwa kuti mumawapondereza pansi pa mapanzi anu. Taonani, Ambuye anena kwa ine: Ngati iwo amene inu mwawasankha kukhala okulamulirani sakulapa pa machimo awo ndi kusaweruzika kwawo, mudzapita kunkhondo motsutsana nawo.

34 Ndipo tsopano taonani, ine, Moroni, ndine wokakamizidwa, molingana ndi pangano limene ndapanga kusunga malamulo a Mulungu wanga; kotero ndikufuna kuti mutsatire ku mawu a Mulungu, ndi kutumiza mwachangu kwa ine zakudya zanu ndi anthu anu, ndiponso kwa Helamani.

35 Ndipo taonani, ngati simuchita zimenezi ndidzabwera kwa inu mwachangu; pakuti taonani, Mulungu sadzalora kuti ife tiwonongeke ndi njala; kotero iye adzatipatsa ife chakudya chanu, ngakhale zitakhala mwa lupanga. Ndipo muone kuti mukwaniritse mawu a Mulungu.

36 Taonani, ndine Moroni, mkulu wanu wa nkhondo. Sindikufunafuna mphamvu, koma kuti ndiigwetse. Sindikufunafuna ulemu wa dziko lapansi, koma kwa ulemelero wa Mulungu, ndi ufulu ndi ubwino wa dziko langa. Ndipo motero ndikutseka kalata yanga.

Print